Mutu 24
Uthenga Wozuna Komanso Wowawa
Masomphenya 6—Chivumbulutso 10:1–11:19
Nkhani yake: Masomphenya a mpukutu waung’ono, zinthu zokhudza kachisi, kulizidwa kwa lipenga la 7
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira pamene Yesu anaikidwa pampando wachifumu mu 1914 mpaka pa chisautso chachikulu
1, 2. (a) Kodi tsoka lachiwiri linabweretsa chiyani, ndipo lidzatha liti? (b) Kodi kenako Yohane anaona ndani akutsika kuchokera kumwamba?
TSOKA lachiwiri linali lowononga kwambiri. Linabweretsa miliri pa Matchalitchi Achikhristu ndi atsogoleri ake, omwe ndi “gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu” ndipo anaonekera kuti ndi akufa mwauzimu. (Chivumbulutso 9:15) Pambuyo poona zimenezi, Yohane ayenera kuti ankadzifunsa kuti tsoka lachitatu likhala lotani. Komatu tsoka lachiwiri linali lisanathe. Likupitirizabe kufotokozedwa mpaka kufika pa Chivumbulutso 11:14. Koma lisanafike pamapeto pake, Yohane anaona masomphenya ena ndipo iye ankachita nawo zinthu zina m’masomphenyawo. Zimene Yohane anaona m’masomphenyawo zinali zodabwitsa kwambiri. Iye anati:
2 “Kenako, ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba, atavala mtambo. Kumutu kwake kunali utawaleza, ndipo nkhope yake inali ngati dzuwa. Miyendo yake inali ngati mizati yamoto.”—Chivumbulutso 10:1.
3. (a) Kodi ‘mngelo wamphamvu’ uja ndani? (b) Kodi utawaleza umene uli kumutu kwake ukuimira chiyani?
3 Kodi ‘mngelo wamphamvuyu’ ndani? Zikuoneka kuti ndi Yesu Khristu ali mu ulemerero wake, ndipo akugwiranso ntchito ina. Iye wavala mtambo kuti asaoneke, ndipo zimenezi zikutikumbutsa mawu amene Yohane ananena pofotokoza za Yesu m’mbuyomu, kuti: “Taonani! Akubwera ndi mitambo, ndipo diso lililonse lidzamuona, ngakhalenso anthu amene anamulasa.” (Chivumbulutso 1:7; yerekezerani ndi Mateyu 17:2-5.) Utawaleza umene unali kumutu kwake ukutikumbutsa za masomphenya ena amene Yohane anaona m’mbuyomu. Iye anaona mpando wachifumu wa Yehova, womwe unazunguliridwa ndi “utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi.” (Chivumbulutso 4:3; yerekezerani ndi Ezekieli 1:28.) Utawalezawo ukusonyeza kuti malo amene pali mpando wachifumu wa Mulungu ndi a bata ndi mtendere. Mofanana ndi zimenezi, utawaleza umene uli kumutu kwa mngeloyu ukusonyeza kuti iye ndi mthenga wapadera wamtendere, kapena kuti “Kalonga Wamtendere” wa Yehova, amene Baibulo linaneneratu kuti adzabwera.—Yesaya 9:6, 7.
4. Kodi mawu otsatirawa akutanthauza chiyani? (a) nkhope ya mngelo wamphamvuyo “inali ngati dzuwa,” (b) miyendo yake “inali ngati mizati yamoto.”
4 Nkhope ya mngelo wamphamvuyu “inali ngati dzuwa.” M’masomphenya ena a m’mbuyomu pamene Yohane anaona Yesu ali m’kachisi wa Mulungu, iye anaona kuti nkhope ya Yesu “inali yowala ngati dzuwa limene likuwala kwambiri.” (Chivumbulutso 1:16) Yesu, yemwe ndi “dzuwa la chilungamo,” amawala popeza m’mapiko mwake muli mphamvu yochiritsa anthu amene amaopa dzina la Yehova. (Malaki 4:2) Sikuti nkhope yokha ya mngeloyu ndi imene ili yaulemerero. Miyendo yakenso ndi yaulemerero, ndipo ili “ngati mizati yamoto.” Mmene iye waimiramu zikusonyeza kuti Yehova wamupatsa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.”—Mateyu 28:18; Chivumbulutso 1:14, 15.
5. Kodi Yohane anaona kuti mngelo wamphamvu uja anali ndi chiyani m’dzanja lake?
5 Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “M’dzanja lake, anali ndi mpukutu waung’ono wofunyulula. Iye anaponda panyanja ndi phazi lake lamanja, koma ndi phazi lake lamanzere anaponda pamtunda.” (Chivumbulutso 10:2) Apa tikuonanso mpukutu wina, koma tsopano unalibe chidindo chomatira. Tingayembekezere kuonera limodzi ndi Yohane zinthu zinanso zosangalatsa kwambiri zimene zili mumpukutuwo. Koma choyamba Yohane akutipatsa kaye chithunzi cha zimene zichitike.
6. (a) N’chifukwa chiyani m’poyenera kuti mapazi a Yesu aponde pamtunda ndi panyanja? (b) Kodi lemba lonse la Salimo 8:5-8 linakwaniritsidwa liti?
6 Tiyeni tibwerere kaye ku mawu amene Yohane anagwiritsa ntchito pofotokoza za Yesu. Iye anati mapazi ake angati moto anaponda pamtunda ndi panyanja, kutanthauza kuti tsopano iye ali ndi ulamuliro wonse pa dziko lapansi ndi nyanja. Zimenezi zikufanana ndi zimene zinalembedwa m’salimo lina laulosi, kuti: “[Inu Yehova] munamuchepetsa pang’ono [Yesu] poyerekeza ndi ena onga Mulungu, kenako munamuveka ulemerero ndi ulemu monga chisoti chachifumu. Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu. Mwaika zonse pansi pa mapazi ake: nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, zonse zimenezi, komanso zilombo zakutchire. Mbalame zam’mlengalenga ndi nsomba za m’nyanja, chilichonse choyenda m’njira za pansi pa nyanja.” (Salimo 8:5-8; onaninso Aheberi 2:5-9.) Salimo limeneli linakwaniritsidwa lonse mu 1914, pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo nthawi yamapeto inayamba. Choncho zimene Yohane anaona m’masomphenyawa zinayamba kukwaniritsidwa kuyambira m’chaka chimenecho.—Salimo 110:1-6; Machitidwe 2:34-36; Danieli 12:4.
Mabingu 7
7. Kodi mngelo wamphamvu uja anafuula ndi mawu otani, ndipo mawu akewo akuimira chiyani?
7 Pamene Yohane ankaganizira za mngelo wamphamvuyu, anadzidzimutsidwa ndi mawu a mngelo yemweyo. Yohane anati: “Kenako [mngeloyo] anafuula ndi mawu okweza ngati kubangula kwa mkango. Atafuula choncho, mabingu 7 analankhula, bingu lililonse ndi liwu lakelake.” (Chivumbulutso 10:3) Mosakayikira, mawu okwezawo anachititsa Yohane kuti akhale tcheru, ndipo akutsimikizira mfundo yoti Yesu ndiyedi “Mkango wa fuko la Yuda.” (Chivumbulutso 5:5) Yohane ankadziwanso kuti Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina Yehova ‘amabangula.’ Mwaulosi, kubangula kwa Yehova kunkasonyeza kuti nthawi yosonkhanitsanso Isiraeli wauzimu yafika ndiponso kuti “tsiku la Yehova” lowononga kwambiri lili pafupi. (Hoseya 11:10; Yoweli 3:14, 16; Amosi 1:2; 3:7, 8) Choncho zikuonekeratu kuti kubangula kwangati mkango kwa mngelo wamphamvuyu kukusonyeza kuti zinthu zikuluzikulu ngati zimenezi zatsalanso pang’ono kuchitika panyanja ndi padziko lapansi. Ndipo mawu obangulawa anachititsa kuti mabingu 7 alankhule.
8. Kodi ‘mawu a mabingu 7’ akuimira chiyani?
8 M’mbuyomu, Yohane anamvapo mabingu ochokera kumpando wachifumu wa Yehova. (Chivumbulutso 4:5) Mu nthawi ya Davide, nthawi zina anthu ankanena kuti bingu ndi “liwu la Yehova.” (Salimo 29:3) M’mbuyomu, Yehova analankhulapo kuchokera kumwamba pa nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake padziko lapansi, ndipo ananena kuti ankafuna kulemekeza dzina lake. Mawu ake pa nthawiyo anamveka ngati bingu kwa anthu ambiri amene anawamva. (Yohane 12:28, 29) Choncho m’pomveka kunena kuti ‘mawu a mabingu 7’ aja akuimira mawu a Yehova ofotokoza zolinga zake. Mfundo yakuti mabinguwo analipo “7” ikusonyeza kuti mawu amene Yohane anamva anali okwanira.
9. Kodi mawu ochokera kumwamba anamuuza chiyani Yohane?
9 Koma tsopano panamvekanso mawu ena. Mawuwo anauza Yohane kuti achite zinthu zimene ziyenera kuti zinamveka zodabwitsa kwa iye. Yohane anati: “Tsopano mabingu 7 aja atalankhula, ndinafuna kulemba. Koma ndinamva mawu kumwamba akuti: ‘Tsekera zimene mabingu 7 amenewo alankhula, usazilembe.’” (Chivumbulutso 10:4) Yohane ayenera kuti ankafunitsitsa kumva ndi kulemba zimene mabinguwo analankhula, mofanana ndi mmene Akhristu odzozedwa masiku ano akhala akudikirira mwachidwi kuti Yehova aulule zolinga zake, kuti iwo azilembe n’kuzifalitsa. Koma Yehova amaulula zimenezi pa nthawi yake imene anaiikiratu.—Luka 12:42; onaninso Danieli 12:8, 9.
Kutha kwa Chinsinsi Chopatulika
10. Kodi mngelo wamphamvu uja analumbira m’dzina la ndani, ndipo analumbira kuti chiyani?
10 Kenako Yehova anapatsa Yohane ntchito ina yoti achite. Mabingu 7 aja atamaliza kugunda, mngelo wamphamvu uja analankhulanso. Yohane anati: “Mngelo amene ndinamuona ataimirira panyanja ndi pamtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba. Iye analumbira pa Iye wokhala ndi moyo kwamuyaya, amene analenga kumwamba ndi zokhala kumeneko, ndi dziko lapansi ndi zinthu za mmenemo, ndi nyanja ndi zinthu za mmenemo. Analumbira kuti: ‘Sipakhalanso kuchedwa ayi.’” (Chivumbulutso 10:5, 6) Kodi mngelo wamphamvuyo analumbira m’dzina la ndani? Yesu, amene ali mu ulemerero wake, sanalumbire m’dzina lake, koma m’dzina la Yehova, amene ali ndi ulamuliro woposa wa wina aliyense, yemwenso ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi ndipo sangafe. (Yesaya 45:12, 18) Ndi lumbiro limeneli, mngeloyu anatsimikizira Yohane kuti Mulungu sachedwa kukwaniritsa cholinga chake.
11, 12. (a) Kodi mawu akuti “sipakhalanso kuchedwa ayi” akutanthauza chiyani? (b) Kodi n’chiyani chimene chithetsedwe?
11 Mawu achigiriki (khroʹnos) amene anawamasulira kuti “kuchedwa” palembali amatanthauza “nthawi.” Choncho anthu ena amaona kuti mawu a mngeloyu ayenera kumasuliridwa kuti: “Sipakhalanso nthawi,” ngati kuti nthawi, mmene timaidziwira masiku ano, idzatha. Koma pavesili mawuwa alembedwa m’njira yosonyeza kuti akunena za nthawi inayake yapadera, osati za nthawi basi. Choncho akutanthauza kuti Yehova sadzalola kuti padutsenso nthawi, kapena kuti pakhalenso kuchedwa. Pa Aheberi 10:37, Paulo anagwiritsira ntchito mawu ena achigiriki ochokera ku mawu omwewa (khroʹnos), ndipo anagwira mawu lemba la Habakuku 2:3, 4. Iye analemba kuti, “amene akubwerayo . . . sachedwa ayi.”
12 Mawu amene mngelo uja ananena, oti “sipakhalanso kuchedwa ayi,” ndi olimbikitsa kwambiri kwa Akhristu odzozedwa masiku ano, amene ambiri a iwo ndi okalamba. Kodi mawuwa akutanthauza chiyani? Yohane akutiuza kuti: “Koma m’masiku oliza lipenga la mngelo wa 7, mngeloyo atatsala pang’ono kuliza lipenga lake, ndithu chinsinsi chopatulika cha Mulungu chidzathetsedwa, malinga ndi uthenga wabwino umene anaulengeza kwa akapolo ake, aneneri.” (Chivumbulutso 10:7) Nthawi yoti Yehova athetse chinsinsi chake chopatulika yakwana, ndipo kutha kwake kudzakhala kosangalatsa, kwaulemerero, ndiponso kudzakwaniritsa cholinga chake.
13. Kodi chinsinsi chopatulika cha Mulungu n’chiyani?
13 Kodi chinsinsi chopatulika chimenechi n’chiyani? Chikukhudza mbewu imene inalonjezedwa choyamba mu Edeni, ndipo Yesu Khristu anadzakhala mbali yake yoyamba. (Genesis 3:15; 1 Timoteyo 3:16) Chikukhudzanso mkazi amene mwa iye munachokera Mbewuyo. (Yesaya 54:1; Agalatiya 4:26-28) Chinsinsi chopatulikachi chikukhudzanso anthu amene akupanga mbali yachiwiri ya mbewu ndiponso Ufumu umene ukulamulidwa ndi Mbewuyo. (Luka 8:10; Aefeso 3:3-9; Akolose 1:26, 27; 2:2; Chivumbulutso 1:5, 6) Choncho uthenga wabwino wonena za Ufumu wakumwamba wapaderawu, uyenera kulengezedwa padziko lonse mu nthawi yamapeto ino.—Mateyu 24:14.
14. Kodi n’chifukwa chiyani tsoka lachitatu likukhudzana ndi Ufumu wa Mulungu?
14 Ndithudi, umenewu ndi uthenga wabwino kwambiri. Komabe, pa Chivumbulutso 11:14, 15, tsoka lachitatu likukhudzana ndi Ufumu umenewu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kulengezedwa kwa uthenga wabwino woti chinsinsi chopatulika cha Mulungu chathetsedwa, kapena kuti Ufumu wa Mulungu womwe wolamulira wake ndi Mesiya wakhazikitsidwa, ndi nkhani yoipa kwambiri kwa anthu amene amakonda dziko la Satanali. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:16.) Uthenga umenewu ukutanthauza kuti dzikoli pamodzi ndi zinthu zake zonse zimene anthuwo amazikonda kwambiri, latsala pang’ono kuwonongedwa. Mawu a mabingu 7 aja, ali ndi uthenga wonena za kuyandikira kwa chiwonongeko chimenecho. Chiwonongekochi chili ngati mphepo yamkuntho yoopsa, ndipo mawu a mabinguwo akumveka bwino kwambiri ndiponso akukwererakwerera pamene tsiku lalikulu la mkwiyo wa Yehova likuyandikira.—Zefaniya 1:14-18.
Mpukutu Wofunyulula
15. Kodi mawu ochokera kumwamba komanso mngelo wamphamvu uja anauza Yohane kuti achite chiyani, ndipo chinamuchitikira n’chiyani atachita zimenezo?
15 Pamene Yohane ankadikira kuti lipenga la 7 lilizidwe, ndiponso kuti chinsinsi chopatulika cha Mulungu chithetsedwe, anapatsidwanso ntchito ina. Iye anati: “Kenako, mawu amene ndinawamva kuchokera kumwamba aja, analankhulanso ndi ine kuti: ‘Pita, katenge mpukutu wofunyulula umene uli m’dzanja la mngelo amene waimirira panyanja ndi pamtunda uja.’ Choncho, ndinapita kwa mngeloyo n’kumuuza kuti andipatse mpukutu waung’onowo. Iye anandiuza kuti: ‘Tenga mpukutuwu udye. Ukupweteketsa m’mimba, koma m’kamwa mwako ukhala wozuna ngati uchi.’ Chotero ndinatenga mpukutu waung’onowo m’dzanja la mngeloyo n’kuudya. M’kamwa mwanga, unali wozuna ngati uchi, koma nditaudya, unandipweteketsa m’mimba. Ndiye iwo anandiuza kuti: ‘Uyenera kuneneranso zokhudza mitundu ya anthu, mayiko, zinenero, ndi mafumu ambiri.’”—Chivumbulutso 10:8-11.
16. (a) Kodi zimene zinamuchitikira mneneri Ezekieli zinali zofanana bwanji ndi zimene zinamuchitikira Yohane? (b) N’chifukwa chiyani mpukutu waung’onowo unali wozuna m’kamwa mwa Yohane, koma n’chifukwa chiyani unamupweteketsa m’mimba n’kulephera kuugaya?
16 Zimene zinamuchitikira Yohanezi n’zofanana ndi zimene zinamuchitikira mneneri Ezekieli pa nthawi imene anali pa ukapolo ku Babeloniya. Nayenso anauzidwa kuti adye mpukutu umene ankaumva kutsekemera m’kamwa mwake. Koma utafika m’mimba mwake, unamuchititsa kuti anenere zinthu zowawa zomwe zidzagwere nyumba yopanduka ya Isiraeli. (Ezekieli 2:8–3:15) Mpukutu wofunyulula umene Yesu Khristu ali mu ulemerero wake anapatsa Yohane, nawonso unali ndi uthenga wochokera kwa Mulungu. Yohane anauzidwa kuti ayenera kulalikira zinthu zokhudza “mitundu ya anthu, mayiko, zinenero, ndi mafumu ambiri.” Mpukutu umenewu unali wozuna m’kamwa mwa Yohane chifukwa unali wochokera kwa Mulungu. (Yerekezerani ndi Salimo 119:103; Yeremiya 15:15, 16.) Koma unamupweteketsa m’mimba n’kulephera kuugaya chifukwa unaneneratu zinthu zowawa zomwe zidzagwere anthu opanduka, ngatinso mmene zinalili ndi Ezekieli.—Salimo 145:20.
17. (a) Kodi ndani anauza Yohane kuti ‘anenerenso’ ndipo zimenezi zikutanthauza chiyani? (b) Kodi masomphenya ochititsa chidwi amene Yohane anaona anayamba liti kukwaniritsidwa?
17 N’zosakayikitsa kuti amene anauza Yohane kuti anenerenso anali Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. Ngakhale kuti Yohane anali mkaidi pachilumba cha Patimo, iye anali atanenera kale zinthu zokhudza mitundu ya anthu, mayiko, zinenero, ndi mafumu, kudzera mu zinthu zimene takambirana kale kufika pano m’buku la Chivumbulutso. Mawu akuti ‘anenerenso’ akusonyeza kuti iye anayenera kulemba ndi kufalitsa mfundo zimene zalembedwa kumbali yotsala ya buku la Chivumbulutso. Koma kumbukirani kuti pa nthawiyi Yohane ankachita nawo zinthu zina zimene zinkachitika m’masomphenya aulosiwa. Zimene analembazi ndi ulosi umene unayamba kukwaniritsidwa pambuyo pa chaka cha 1914, pamene mngelo wamphamvu uja anaponda pamtunda ndi panyanja. Choncho, kodi masomphenya ochititsa chidwiwa akutanthauza chiyani kwa Akhristu odzozedwa masiku ano?
Tanthauzo la Mpukutu Waung’ono Masiku Ano
18. Kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, kodi Akhristu odzozedwa anasonyeza bwanji kuti ankafunitsitsa kumvetsa buku la Chivumbulutso?
18 Zimene Yohane anaona zinachitira bwino chithunzi zinthu zimene zinachitikira Akhristu odzozedwa kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye. Pa nthawiyo, iwo sankamvetsa bwino zolinga za Yehova, kuphatikizapo tanthauzo la mabingu 7 aja. Komabe, iwo ankafunitsitsa kumvetsa buku la Chivumbulutso, ndipo pamene Charles Taze Russell anali ndi moyo, anathirira ndemanga pa mavesi ambiri a m’bukuli. Iye atamwalira mu 1916, mfundo zambiri zimene analemba zinasonkhanitsidwa pamodzi ndipo zinafalitsidwa m’buku latsopano lachingelezi lamutu wakuti The Finished Mystery. Koma patapita nthawi, zinaoneka kuti bukuli silinafotokozere mokwanira buku la Chivumbulutso. Abale ake a Khristu amene anali padziko lapansi pa nthawiyo anafunika kudikirabe kuti amvetse molondola buku louziridwa limeneli, kufikira pamene masomphenyawo anayamba kukwaniritsidwa.
19. (a) Kodi Yehova Mulungu anawagwiritsira ntchito bwanji Akhristu odzozedwa ngakhale mawu a mabingu 7 aja asanafalitsidwe onse? (b) Kodi Akhristu odzozedwa anapatsidwa liti mpukutu waung’ono wofunyulula, ndipo zimenezi zinatanthauza chiyani kwa iwo?
19 Komabe, mofanana ndi mmene anamugwiritsira ntchito Yohane, Yehova anagwiritsiranso ntchito Akhristu odzozedwawa ngakhale mawu a mabingu 7 aja asanafalitsidwe onse. Iwo analalikira mwakhama kwa zaka 40 chaka cha 1914 chisanafike, ndipo anayesetsa kulalikirabe pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, ngakhale kuti zimenezi zinali zovuta. Pamene mbuye anafika, iwo ndi amene anapezeka kuti anali kupereka chakudya pa nthawi yoyenera kwa antchito ake apakhomo. (Mateyu 24:45-47) Choncho mu 1919, iwo ndi amene anapatsidwa mpukutu waung’ono wofunyulula uja, kapena kuti uthenga wosapita m’mbali woti alalikire kwa anthu. Mofanana ndi Ezekieli, iwo anali ndi uthenga wopita ku gulu losakhulupirika kwa Mulungu, lomwe ndi Matchalitchi Achikhristu. Gulu limeneli linkanena kuti likutumikira Mulungu, koma zoona zake zinali zoti silinkachita zimenezi. Mofanana ndi Yohane, iwo anayenera kulalikiranso zinthu zina zokhudza “mitundu ya anthu, mayiko, zinenero, ndi mafumu ambiri.”
20. Kodi mfundo yoti Yohane anadya mpukutu uja ikuchitira chithunzi chiyani?
20 Mfundo yakuti Yohane anadya mpukutu uja ikuchitira chithunzi mfundo yakuti abale ake a Yesu anavomera ntchito imeneyi. Mpukutuwo unakhala ngati mbali ya thupi lawo mpaka kufika poti iwo ankadziwika ndi uthenga umene unali m’mbali imeneyi ya Mawu a Mulungu ouziridwa, komanso uthengawu unkawapatsa mphamvu. Koma uthenga umene ankalalikira unali ndi mfundo zina zonena za chiweruzo cha Yehova zimene zinali zowawa kwa anthu ambiri. Zina mwa mfundo zimenezi zinali zokhudza miliri yomwe inaloseredwa m’chaputala 8 cha buku la Chivumbulutso. Koma kwa Akhristu oonawa, kudziwa za chiweruzo chimenechi, komanso kuzindikira kuti Yehova akuwagwiritsiranso ntchito kuti alengeze chiweruzochi, kunali kozuna.—Salimo 19:9, 10.
21. (a) Kodi uthenga wa mumpukutu waung’ono uja wakhalanso bwanji wozuna kwa anthu a khamu lalikulu? (b) N’chifukwa chiyani uthenga wabwino uli uthenga woipa kwa anthu otsutsa?
21 Patapita nthawi, uthenga wa mumpukutu uja unakhalanso wozuna kwa “khamu lalikulu . . . lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” Anthu a m’khamu limeneli anapezeka kuti anali kuusa moyo chifukwa cha zinthu zonyansa zimene anaona zikuchitika m’Matchalitchi Achikhristu. (Chivumbulutso 7:9; Ezekieli 9:4) Anthu a khamu lalikuluwa nawonso amalengeza mwakhama uthenga wabwino, ndipo amagwiritsira ntchito mawu ozuna ndi achisomo pofotokoza zinthu zosangalatsa zimene Yehova wakonzera Akhristu amene ali ngati nkhosa. (Salimo 37:11, 29; Akolose 4:6) Koma kwa anthu otsutsa, umenewu ndi uthenga woipa. Chifukwa chiyani? Chifukwa ukutanthauza kuti dziko limene amalidalirali, limenenso mwina linawabweretserako chimwemwe kwakanthawi, liyenera kuwonongedwa. Choncho kwa iwo, uthenga wabwinowu ukusonyeza kuti chiwonongeko chawo chatsala pang’ono.—Afilipi 1:27, 28; yerekezerani ndi Deuteronomo 28:15; 2 Akorinto 2:15, 16.
[Zithunzi patsamba 160]
Akhristu odzozedwa pamodzi ndi anzawo a khamu lalikulu akulengeza kwa anthu a mitundu yonse uthenga wozuna komanso wowawa