Mutu 25
Mboni Ziwiri Zinaukitsidwa
1. Kodi mngelo wamphamvu uja anauza Yohane kuti achite chiyani?
TSOKA lachiwiri lisanathe, mngelo wamphamvu uja anauza Yohane kuti achite nawo zinthu zina zaulosi zokhudzana ndi kachisi. (Chivumbulutso 9:12; 10:1) Yohane ananena kuti: “Ndiyeno ndinapatsidwa bango lokhala ngati ndodo ndipo ndinauzidwa kuti: ‘Nyamuka, kayeze nyumba yopatulika ya pakachisi wa Mulungu, guwa lansembe, ndi amene akulambira mmenemo.’”—Chivumbulutso 11:1.
Nyumba Yopatulika ya Pakachisi
2. (a) Kodi ndi kachisi uti amene anali woti adzakhalapobe mpaka m’nthawi yathu ino? (b) Kodi ndani amene ali Mkulu wa Ansembe m’kachisiyu, ndipo Malo Oyera Koposa a kachisiyu n’chiyani?
2 Kachisi amene akutchulidwa palembali sangakhale kachisi weniweni wa ku Yerusalemu chifukwa chakuti kachisi womaliza anawonongedwa ndi Aroma mu 70 C.E. Komabe, mtumwi Paulo anasonyeza kuti ngakhale kachisi wa ku Yerusalemu asanawonongedwe, panali kachisi wina amene anali woti adzakhalapobe mpaka m’nthawi yathu ino. Ameneyu ndi kachisi wamkulu wauzimu amene ankaimiridwa ndi chihema ndipo patapita nthawi ankaimiridwa ndi akachisi amene anamangidwa ku Yerusalemu. Kachisi wauzimuyu ndi ‘chihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova, osati munthu,’ ndipo Mkulu wa Ansembe wa pakachisi ameneyu ndi Yesu. Ponena za Mkulu wa Ansembe ameneyu, Paulo ananena kuti ‘wakhala kale pansi kumwamba, kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka.’ Malo Oyera Koposa a kachisiyu ndi malo akumwamba kumene kuli Yehova.—Aheberi 8:1, 2; 9:11, 24.
3. Pachihema, n’chiyani chimene chinkaimiridwa ndi (a) nsalu yotchinga imene inali pakati pa Malo Oyera Koposa ndi Malo Oyera? (b) nsembe za nyama? (c) guwa lansembe?
3 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti nsalu yotchinga ya m’chihema, imene inali pakati pa Malo Oyera Koposa ndi Malo Oyera, inkachitira chithunzi thupi la Yesu. Yesu atafa monga nsembe, nsalu yotchingayi inang’ambika pakati, kutanthauza kuti thupi la Yesu silinalinso chotchinga chomulepheretsa kufika pamaso pa Yehova kumwamba. Chifukwa cha nsembe ya Yesu imeneyi, patapita nthawi, ansembe aang’ono amene anafa ali okhulupirika, nawonso anayamba kupita kumwamba. (Mateyu 27:50, 51; Aheberi 9:3; 10:19, 20) Paulo ananenanso kuti nsembe za nyama zimene anthu ankapereka nthawi zonse pachihema, zinkaimira nsembe imodzi ya Yesu, yomwe ndi moyo wake wangwiro monga munthu. Guwa lansembe limene linali m’bwalo la kachisi linkaimira zinthu zimene Yehova anakonza zogwirizana ndi chifuniro chake. Iye anakonza zoti alandire nsembe ya Yesu m’malo mwa “anthu ambiri,” omwe ndi odzozedwa ndipo patapita nthawi, m’malo mwa a nkhosa zina, amene “akumuyembekezera ndi mtima wonse kuti awapulumutse.”—Aheberi 9:28; 10:9, 10; Yohane 10:16.
4. Kodi n’chiyani chimene chinachitiridwa chithunzi ndi (a) Malo Oyera (b) bwalo?
4 Tikaona mfundo zouziridwazi, tinganene mosakayikira kuti Malo Oyera a m’chihema, akuimira kukhala woyera. Khristu ndi amene anali woyamba kukhala woyera ndipo patapita nthawi a 144,000, omwe ndi ansembe odzozedwa, nawonso anayamba kukhala oyera adakali padziko lapansi, asanadutse pa “nsalu yotchinga” ija. (Aheberi 6:19, 20; 1 Petulo 2:9) Moyenerera, Malo Oyera a m’chihemawa akuimira kuti iwo anatengedwa ndi Mulungu kukhala ana ake auzimu, monga mmene Mulungu ananenera za Yesu kuti ndi Mwana wake, Yesuyo atabatizidwa mumtsinje wa Yorodano mu 29 C.E. (Luka 3:22; Aroma 8:15) Pachihema panalinso bwalo lomwe ankaperekapo nsembe. Bwaloli linali malo okhawo a pachihema amene anali poonekera kwa Aisiraeli omwe sanali ansembe. Kodi n’chiyani chimene chinkachitiridwa chithunzi ndi bwalo limeneli? Bwaloli linkachitira chithunzi kulungama komanso ungwiro wa Yesu, zimene zinachititsa kuti akhale woyenerera kupereka moyo wake monga nsembe yowombola anthu. Komanso linkaimira kuti Mulungu amaona oyera kuti ndi olungama chifukwa cha nsembe ya Yesu. Anthu amenewa ndi otsatira a Yesu odzozedwa, ndipo Mulungu amawaona kuti ndi olungama adakali padziko lapansi.a—Aroma 1:7; 5:1.
Kuyeza Nyumba Yopatulika ya Pakachisi
5. M’maulosi a m’Malemba Achiheberi (a) kodi kuyezedwa kwa Yerusalemu kunkaimira chiyani? (b) Kodi kuyezedwa kwa kachisi wa m’masomphenya a Ezekieli kunkaimira chiyani?
5 Yohane anauzidwa kuti ‘ayeze nyumba yopatulika ya pakachisi wa Mulungu, guwa lansembe, ndi amene akulambira mmenemo.’ Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani? M’maulosi a m’Malemba Achiheberi, kuyeza ngati koteroko kunkatsimikizira anthu kuti chilungamo chichitika potsatira mfundo zangwiro za Yehova. M’masiku a Manase amene anali mfumu yoipa, kuyezedwa mwaulosi kwa mzinda wa Yerusalemu, unali umboni wakuti mzindawo wapatsidwa chiweruzo chosasintha chakuti udzawonongedwa. (2 Mafumu 21:13; Maliro 2:8) Koma patapita nthawi, Yeremiya anaona mzinda wa Yerusalemu ukuyezedwa, ndipo izi zinatsimikizira kuti mzindawo udzamangidwanso. (Yeremiya 31:39; onaninso Zekariya 2:2-8.) Mofanana ndi zimenezi, Ezekieli anaona m’masomphenya kachisi akuyezedwa mwatsatanetsatane ndipo zimenezi zinatsimikizira Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo kuti kulambira koona kudzabwezeretsedwa m’dziko lawo. Zimenezi zinakumbutsanso Aisiraeli kuti chifukwa cha zolakwa zawo, kuyambira pa nthawiyo ankafunika kutsatira ndendende mfundo zolungama za Mulungu.—Ezekieli 40:3, 4; 43:10.
6. Kodi Yohane atauzidwa kuti ayeze kachisi komanso ansembe olambira mmenemo, chinali chizindikiro cha chiyani? Fotokozani.
6 Choncho, Yohane atalamulidwa kuyeza kachisi komanso ansembe amene ankalambira m’kachisimo, chinali chizindikiro chakuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake chokhudza dongosolo la pakachisi ndi ogwira ntchito pakachisipo, komanso kuti cholinga chimenechi chili pafupi kukwaniritsidwa. Tsopano popeza kuti ulamuliro wonse waperekedwa kwa mngelo wamphamvu wa Yehova, ndi nthawi yoti ‘phiri la nyumba ya Yehova likhazikike pamwamba pa nsonga za mapiri.’ (Yesaya 2:2-4) Kulambira koyera kwa Yehova kunayenera kukwezedwa, pambuyo pa zaka zambiri kuchokera pamene mpatuko wa Matchalitchi Achikhristu unayamba. Komanso ndi nthawi yakuti abale okhulupirika a Yesu amene anamwalira aukitsidwe n’kulowa ‘m’Malo Opatulikitsa.’ (Danieli 9:24; 1 Atesalonika 4:14-16; Chivumbulutso 6:11; 14:4) Ndipo “akapolo a Mulungu wathu” amene anadindidwa chidindo komalizira padziko lapansi anayenera kuyezedwa mogwirizana ndi mfundo za Mulungu kuti akhale oyenerera kukalandira malo awo okhazikika m’dongosolo la kachisi, monga ana a Mulungu odzozedwa ndi mzimu. Akhristu odzozedwa masiku ano akudziwa bwino mfundo zoyera zimenezo ndipo akuyesetsa kuzitsatira.—Chivumbulutso 7:1-3; Mateyu 13:41, 42; Aefeso 1:13, 14; yerekezerani ndi Aroma 11:20.
Bwalo Linapondedwapondedwa
7. (a) N’chifukwa chiyani Yohane anauzidwa kuti asayeze bwalo? (b) Kodi mzinda woyera unapondedwapondedwa liti kwa miyezi 42? (c) Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu analephera bwanji kutsatira mfundo zolungama za Yehova kwa miyezi 42?
7 N’chifukwa chiyani Yohane analetsedwa kuyeza bwalo? Iye akutiuza chifukwa chake, kuti: “Koma bwalo lakunja kwa nyumba yopatulika ya pakachisi ulisiye, usaliyeze m’pang’ono pomwe chifukwa laperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo iwo adzapondaponda mzinda woyera kwa miyezi 42.” (Chivumbulutso 11:2) Taona kale kuti bwalo linkachitira chithunzi mfundo yakuti Mulungu amaona Akhristu odzozedwa kuti ndi olungama, Akhristuwo ali padziko lapansi. Kutsogoloku tiona kuti lembali likunena za miyezi 42 yeniyeni osati yophiphiritsa. Miyezi imeneyi inayambira mu December 1914 mpaka mu June 1918, pamene anthu onse amene ankati ndi Akhristu anayesedwa kwambiri. Kodi anthu amene ankati ndi Akhristuwo anapitiriza kutsatira mfundo zolungama za Yehova pa nthawi yankhondoyo? Ambiri sanapitirize kutsatira mfundozi. Pa nthawi imeneyi, atsogoleri onse a Matchalitchi Achikhristu ankalimbikitsa anthu kukonda kwambiri dziko lawo m’malo mowalimbikitsa kumvera malamulo a Mulungu. Kumbali zonse za magulu amene ankachita nkhondo, imene inkamenyedwa makamaka m’Mayiko Achikhristu, atsogoleri a zipembedzo ankalimbikitsa achinyamata kuti apite kunkhondo. Ndipo anthu ambiri anaphedwa. Pofika nthawi imene chiweruzo chinayamba pa nyumba ya Mulungu mu 1918, dziko la United States linalinso litalowerera nkhondo yoopsayo, ndipo atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu onse anali ndi mlandu wa magazi. Magaziwa akufuulabe mpaka pano kuti Mulungu abwezere adani awo. (1 Petulo 4:17) Atsogoleriwo aponyedwa kunja ndipo adzakhala kumeneko mpaka kalekale.—Yesaya 59:1-3, 7, 8; Yeremiya 19:3, 4.
8. Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, kodi Ophunzira Baibulo ambiri anazindikira chiyani, koma iwo sankamvetsa bwino mfundo iti?
8 Koma kodi zinthu zinali bwanji kwa gulu laling’ono la Ophunzira Baibulo? Kodi iwo ankafunikira kuyezedwa nthawi yomweyo mu 1914 pofuna kuona ngati ankatsatira mfundo za Mulungu? Ayi. Mofanana ndi anthu a m’Matchalitchi Achikhristu amene ankati ndi Akhristu enieni, iwonso ankafunika kuyesedwa kaye choyamba asanayezedwe. Choncho iwo ‘anaperekedwa kwa anthu a mitundu ina’ kapena kuti anaponyedwa kunja, kuti ayesedwe ndi kuzunzidwa kwambiri. Ambiri mwa iwo ankadziwa kuti sayenera kupita kunkhondo ndi kupha anthu anzawo. Komabe pa nthawiyi iwo anali asanamvetse bwino mfundo yoti Akhristu sayenera kulowerera nkhondo. (Mika 4:3; Yohane 17:14, 16; 1 Yohane 3:15) Choncho Akhristu ena anachita zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro chawo chifukwa chokakamizidwa ndi anthu a mitundu ina.
9. Kodi mzinda woyera umene unapondedwapondedwa ndi anthu a mitundu ina n’chiyani, ndipo padziko lapansi pano, ndani akuimira mzinda umenewu?
9 Koma kodi anthu a mitundu ina anapondaponda bwanji mzinda woyera? N’zoonekeratu kuti mzinda umenewu sunali Yerusalemu weniweni chifukwa pamene buku la Chivumbulutso linkalembedwa, panali patapita zaka zoposa 25 mzindawu utawonongedwa. M’malomwake, mzinda woyerawu ndi Yerusalemu Watsopano umene wafotokozedwa m’buku la Chivumbulutso kutsogoloku. Panopa mzindawu ukuimiridwa ndi Akhristu odzozedwa amene adakali ndi moyo padziko lapansi m’bwalo lamkati la kachisi. M’tsogolo muno, Akhristu amenewa adzakhalanso mbali ya mzinda woyerawu. Choncho kupondaponda Akhristu amenewa n’chimodzimodzi ndi kupondaponda mzindawo.—Chivumbulutso 21:2, 9-21.
Mboni Ziwiri
10. Kodi mboni zokhulupirika za Yehova zinachita chiyani pamene zinkapondedwapondedwa?
10 Ngakhale pamene Akhristu okhulupirikawa ankapondedwapondedwa, iwo anapitirizabe kukhala mboni zokhulupirika za Yehova. Choncho ulosiwu ukupitiriza kuti: “‘Ndiyeno ndidzachititsa mboni zanga ziwiri kunenera kwa masiku 1,260, zitavala ziguduli.’ Mboni zimenezi zikuimiridwa ndi mitengo iwiri ya maolivi, ndi zoikapo nyale ziwiri, ndipo mbonizo zaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:3, 4.
11. Kodi zinatanthauza chiyani pamene Akhristu odzozedwa okhulupirika ankanenera ‘atavala ziguduli’?
11 Akhristu odzozedwa okhulupirikawa anafunika kukhala opirira chifukwa ankayenera kunenera ‘atavala ziguduli.’ Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani? Kalelo kuvala ziguduli kunkasonyeza kuti munthu ali pa chisoni kapena mavuto aakulu. (Genesis 37:34; Yobu 16:15, 16; Ezekieli 27:31) Aneneri a Mulungu akamalengeza uthenga wachisoni kapena tsoka limene lidzagwere anthuwo m’tsogolo nthawi zina ankavala ziguduli, komanso anthu ena akamva uthengawo ankavala ziguduli. (Yesaya 3:8, 24-26; Yeremiya 48:37; 49:3) Ndiponso munthu akavala chiguduli ankasonyeza kuti wadzichepetsa kapena walapa pambuyo pochenjezedwa ndi Mulungu. (Yona 3:5) Ziguduli zimene mboni ziwirizo zinavala zikuoneka kuti zinkaimira mfundo yakuti iwo anapirira modzichepetsa polengeza uthenga wa chiweruzo cha Yehova. Iwo anali mboni zolengeza tsiku la Yehova lobwezera chilango limene lidzabweretse chisoni kwa anthu a mitundu ina.—Deuteronomo 32:41-43.
12. N’chifukwa chiyani nthawi imene mzinda woyera unapondedwapondedwa ikuoneka kuti si yophiphiritsa?
12 Akhristu odzozedwa ankayenera kulalikira uthenga umenewu kwa nthawi yodziwika bwino, yomwe ndi masiku 1,260 kapena kuti miyezi 42. Nthawi imeneyi ndi yofanana ndi nthawi imene mzinda woyera unayenera kupondedwapondedwa. Zikuoneka kuti nthawi imeneyi si yophiphiritsa chifukwa yatchulidwa m’njira ziwiri. Choyamba aitchula m’miyezi ndipo kenako m’masiku. Kuwonjezera pamenepo, kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, panali nthawi yodziwika bwino ya zaka zitatu ndi hafu pamene anthu a Mulungu anakumana ndi mavuto amene akugwirizana ndi ulosi wa palembali. Nthawi imeneyi inayambira mu December 1914 mpaka mu June 1918. (Chivumbulutso 1:10) Akhristu amenewa analalikira atavala “ziguduli” uthenga wokhudza chiweruzo cha Yehova pa Matchalitchi Achikhristu ndi pa dzikoli.
13. (a) Kodi mfundo yakuti Akhristu odzozedwa akuimiridwa ndi mboni ziwiri ikutanthauza chiyani? (b) Kodi zimene Yohane ananena kuti mboni ziwiri zikuimiridwa ndi “mitengo iwiri ya maolivi, ndi zoikapo nyale ziwiri,” zikutikumbutsa ulosi uti wa Zekariya?
13 Mfundo yakuti Akhristuwo ankaimiridwa ndi mboni ziwiri ikutitsimikizira kuti uthenga wawo unali wolondola komanso wodalirika. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 17:6; Yohane 8:17, 18.) Yohane ananena kuti iwo ndi “mitengo iwiri ya maolivi, ndi zoikapo nyale ziwiri” komanso anati iwo ‘aimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.’ Mwina Yohane ataona zimenezi anakumbukira ulosi wa Zekariya, amene anaona choikapo nyale cha nthambi 7 komanso mitengo iwiri ya maolivi. Timawerenga kuti mitengo ya maoliviyo ikuimira “odzozedwa awiri,” amene ndi Bwanamkubwa Zerubabele ndi Mkulu wa Ansembe Yoswa, ndipo iwo “amaimirira kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.”—Zekariya 4:1-3, 14.
14. (a) Kodi masomphenya a Zekariya a mitengo iwiri ya maolivi ankatanthauza chiyani? Nanga choikapo nyale chinkatanthauza chiyani? (b) Kodi n’chiyani chimene Akhristu odzozedwa anachita pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse?
14 M’nthawi ya Zekariya panali ntchito yomanganso kachisi, ndipo masomphenya ake a mitengo iwiri ya maolivi anatanthauza kuti Zerubabele ndi Yoswa adzadalitsidwa ndi mzimu woyera wa Yehova kuti athe kulimbikitsa anthu kugwira ntchitoyo. Ndipo masomphenya a choikapo nyale anakumbutsa Zekariya kuti sayenera ‘kunyoza zinthu zochepa zoyamba.’ Iye sanayenera kunyoza zinthu zimenezi chifukwa cholinga cha Yehova wa makamu kuti chichitike, Yehovayo anati: “Sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga.” (Zekariya 4:6, 10; 8:9) Mofanana ndi zimenezi, pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, gulu laling’ono la Akhristu limene linkalengeza mwakhama choonadi chimene chinali ngati kuwala, linagwiritsidwa ntchito yomanganso kachisi mwauzimu. Iwo analimbikitsa ena, ndipo ngakhale kuti analipo ochepa, anaphunzira kudalira mphamvu za Yehova komanso sankanyoza zinthu zochepa zoyamba.
15. (a) Kodi mfundo yakuti Akhristu odzozedwa akuimiridwa ndi mboni ziwiri zija ikutikumbutsanso za chiyani? Fotokozani. (b) Kodi mboni ziwirizo zinapatsidwa mphamvu zochita zizindikiro zotani?
15 Mfundo yakuti Akhristu odzozedwa akuimiridwa ndi mboni ziwiri ikutikumbutsanso za kusandulika kwa Yesu. M’masomphenya amenewo, atumwi atatu a Yesu anamuona ali mu ulemerero wa Ufumu wake, ndipo anali limodzi ndi Mose komanso Eliya. Zimenezi zinaimira nthawi imene Yesu anakhala pampando wachifumu waulemerero mu 1914 kuti agwire ntchito imene ikuimiridwa ndi mboni ziwirizo. (Mateyu 17:1-3) M’pake kuti Yohane anaona mboni ziwirizo zikuchita zizindikiro zofanana ndi za Mose ndi Eliya. Mwachitsanzo, ponena za mbonizo, Yohane anati: “Ngati wina aliyense akufuna kuzivulaza, moto umatuluka m’kamwa mwawo ndi kupsereza adani awo. Ngati wina angafune kuzivulaza, ayenera kuphedwa mwanjira imeneyi. Mboni zimenezi zili ndi ulamuliro wotseka kumwamba kuti mvula isagwe m’masiku onse amene zikunenera.”—Chivumbulutso 11:5, 6a.
16. (a) Kodi chizindikiro cha moto chikugwirizana bwanji ndi zimene zinachitika m’nthawi ya Isiraeli pamene anthu anatsutsa ulamuliro wa Mose? (b) Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu ananyoza bwanji Ophunzira Baibulo ndi kuwayambitsira mavuto m’nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, ndipo Ophunzira Baibulowa anapitiriza bwanji kumenya nkhondo?
16 Izi zikutikumbutsa zimene zinachitika mu nthawi ya Isiraeli pamene anthu anatsutsa ulamuliro wa Mose. Mneneri ameneyu ananena mawu achiweruzo okhala ngati moto, ndipo Yehova anawononga anthu amene anagalukira ulamuliro wa Mose. Moto weniweni wochokera kumwamba unapsereza anthu 250 mwa anthu opandukawo. (Numeri 16:1-7, 28-35) Mofanana ndi zimenezi, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu ankanyoza Ophunzira Baibulo powanena kuti sanapite kumakoleji ophunzitsa Baibulo. Koma mboni za Mulungu zinali ndi zinthu zonse zowayenereza kukhala atumiki. Zinthuzo ndi anthu odzichepetsa amene anamvetsera uthenga wawo wa m’Malemba. (2 Akorinto 3:2, 3) Mu 1917 Ophunzira Baibulo anatulutsa buku latsopano lachingelezi. (The Finished Mystery) Buku limeneli linafotokozera momveka bwino mavesi a m’mabuku a m’Baibulo a Chivumbulutso ndi Ezekieli. Kenako Ophunzira Baibulowo anafalitsa timapepala ta masamba anayi (The Bible Students Monthly) tokwana 10 miliyoni. Timapepala timeneti tinali ndi nkhani yamutu wakuti “Kugwa kwa Babulo, Chifukwa Chake Matchalitchi Achikhristu Akuyenera Kuvutika Ndiponso Mmene Zonsezi Zidzathere,” (The Fall of Babylon—Why Christendom Must Now Suffer—the Final Outcome). Ku United States, atsogoleri a zipembedzo omwe anali okwiya anapezerapo mwayi pa nkhondo yomwe inkachitika pa nthawiyo ndipo analimbikitsa boma kuti liletse kufalitsidwa kwa buku lija. M’mayiko ena bukuli ankaliunika kaye asanalole kuti lifalitsidwe. Komabe, atumiki a Mulungu anapitiriza kumenya nkhondo pofalitsa nkhani zosiyanasiyana zodzudzula atsogoleri a zipembedzowo mosapita m’mbali. Nkhanizi zinkatuluka m’kapepala ka masamba anayi kamutu wakuti Uthenga wa Ufumu. Pamene tsiku la Ambuye likupitirira, pakhala pakutuluka mabuku ena amene apereka umboni womveka bwino wosonyeza kuti Matchalitchi Achikhristu ndi akufa mwauzimu.—Yerekezerani ndi Yeremiya 5:14.
17. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti kukhale chilala komanso kugwe moto wochokera kumwamba m’nthawi ya Eliya? (b) Kodi moto unatuluka bwanji m’kamwa mwa mboni ziwiri zija, ndipo kunachitika chilala chotani?
17 Nanga bwanji za Eliya? M’masiku a mafumu a Isiraeli, mneneri ameneyu analosera kuti kudzakhala chilala chimene chidzayambe chifukwa chakuti Yehova anakwiyira Aisiraeli olambira Baala. Chilalacho chinachitika kwa zaka zitatu ndi hafu. (1 Mafumu 17:1; 18:41-45; Luka 4:25; Yakobo 5:17) Kenako Ahaziya, amene anali mfumu yosakhulupirika, atatumiza asilikali kuti akaumirize Eliya kuti akaonane ndi mfumuyo, mneneriyu anapemphera kuti moto ubwere kuchokera kumwamba ndi kunyeketsa asilikaliwo. Eliya sanavomere kupita mpaka pamene mtsogoleri wina wa asilikaliwo anachita zinthu zomulemekeza monga mneneri. (2 Mafumu 1:5-16) Mofanana ndi zimenezi, kuyambira m’chaka cha 1914 mpaka mu 1918, Akhristu odzozedwa amene anali ndi moyo padziko lapansi pa nthawiyo, ankalalikira molimba mtima za chilala chimene chili m’Matchalitchi Achikhristu. Iwo ankachenjezanso anthu za chiweruzo chokhala ngati moto chimene chidzagwere anthuwo pa “tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha” limene likubwera.—Malaki 4:1, 5; Amosi 8:11.
18. (a) Kodi mboni ziwiri zija zinapatsidwa ulamuliro wotani, ndipo ulamulirowu unali wofanana bwanji ndi umene Mose anapatsidwa? (b) Kodi mboni ziwiri zija zinaulula bwanji chinyengo cha Matchalitchi Achikhristu?
18 Yohane anapitiriza kufotokoza za mboni ziwirizo kuti: “Zilinso ndi ulamuliro pamadzi, woti ziwasandutse magazi. Komanso zili ndi ulamuliro wokantha dziko lapansi ndi mliri wamtundu uliwonse, maulendo ambirimbiri mogwirizana ndi mmene zingafunire.” (Chivumbulutso 11:6b) Pofuna kukakamiza Farao kuti alole Aisiraeli kuchoka m’dziko la Iguputo, Yehova anagwiritsa ntchito Mose pokantha Aiguputo ankhanzawo ndi miliri, monga kusandutsa madzi kukhala magazi. Patapita zaka zambiri, Afilisiti, omwe anali adani a Aisiraeli, ankakumbukirabe zimene Yehova anachitira Aiguputo. Afilisitiwo anafuula kuti: “Adzatipulumutsa ndani m’manja mwa Mulungu wamkuluyu? Ameneyu ndi Mulungu amene anakantha Iguputo ndi masautso amtundu uliwonse m’chipululu.” (1 Samueli 4:8; Salimo 105:29) Mose ankaimira Yesu, ndipo Yesuyo anali ndi ulamuliro wolengeza uthenga wa chiweruzo cha Mulungu kwa atsogoleri a zipembedzo a m’nthawi yake. (Mateyu 23:13; 28:18; Machitidwe 3:22) Ndipo nkhondo yoyamba yapadziko lonse ili mkati, abale ake a Khristu, omwe ndi mboni ziwiri, anaulula kuti “madzi” amene Matchalitchi Achikhristu ankapatsa nkhosa zawo anali akupha.
Mboni Ziwiri Zija Zinaphedwa
19. Malinga ndi zimene buku la Chivumbulutso limanena, kodi chinachitika n’chiyani mboni ziwiri zija zitamaliza kuchitira umboni?
19 Mliri umene unagwera Matchalitchi Achikhristu unali wowawa kwambiri moti mboni ziwirizo zitanenera zitavala ziguduli kwa miyezi 42, Matchalitchi Achikhristuwo anagwiritsira ntchito mphamvu zimene ali nazo m’dzikoli kuti mbonizo ‘ziphedwe.’ Yohane analemba kuti: “Zikamaliza kuchitira umboni wawo, chilombo chotuluka muphompho chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa ndi kuzipha. Mitembo yawo idzagona pamsewu waukulu mumzinda waukulu, umene mophiphiritsira ukutchedwa Sodomu ndi Iguputo, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwa. Mitundu ya anthu, mafuko, zinenero, ndi mayiko, adzayang’anitsitsa mitembo yawo masiku atatu ndi hafu, ndipo sadzalola kuti mitemboyo iikidwe m’manda. Okhala padziko lapansi adzakondwera kwambiri ndi imfa yawoyo. Iwo adzatumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiriwa anazunza okhala padziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:7-10.
20. Kodi “chilombo chotuluka muphompho” n’chiyani?
20 Buku la Chivumbulutso latchula kambirimbiri za chilombo. Kutsogoloku tikambirana mwatsatanetsatane za chilombo chotuluka m’phomphochi ndi zilombo zina. Koma padakali pano tingodziwa kuti “chilombo chotuluka muphompho” chija chikukhudzana ndi ndale zadzikoli zomwe zikutsogoleredwa ndi Satana.b—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 13:1; Danieli 7:2, 3, 17.
21. (a) Kodi adani a mboni ziwiri zija anapezerapo bwanji mwayi pa zimene zinkachitika pa nthawi ya nkhondo? (b) Kodi mfundo yakuti mitembo ya mboni ziwirizo sinaikidwe m’manda ikusonyeza chiyani? (c) Kodi nthawi yokwana masiku atatu ndi hafu tiyenera kuiona motani? (Onani mawu a m’munsi.)
21 Kuyambira mu 1914 mpaka mu 1918 mayiko anatanganidwa ndi nkhondo yoyamba yapadziko lonse. Anthu ankasonyeza kwambiri mtima wokonda dziko lawo, ndipo kumayambiriro kwa chaka cha 1918, anthu a chipembedzo amene anali adani a mboni ziwiri zija anapezerapo mwayi pa zimenezi. Iwo anagwiritsa ntchito molakwika malamulo adziko la America kuti atumiki amene ankatsogolera Ophunzira Baibulo amangidwe pa milandu yowanamizira yoti akuukira boma. Anthu okhulupirika amene ankagwira ntchito limodzi ndi abale amene ankatsogolera Ophunzira Baibulowo anathedwa nzeru ndipo ntchito yolengeza za Ufumu inangotsala pang’ono kuimiratu. Zinangokhala ngati kuti ntchito yolalikira yafa. M’nthawi ya Yohane zinali zochititsa manyazi kwambiri kuti mtembo usaikidwe m’manda. (Salimo 79:1-3; 1 Mafumu 13:21, 22) Choncho kusiya mitembo ya mboni ziwirizo pamtunda osaziika m’manda, chinali chipongwe chachikulu. Ku Palesitina n’kotentha kwambiri ndipo mtembo umene uli pamtunda ungayambedi kununkha patangotha masiku atatu ndi hafu.c (Yerekezerani ndi Yohane 11:39.) Motero mfundo ya mu ulosiwu ikusonyeza kuti mboni ziwirizo zinapirira zinthu zochititsa manyazi kwambiri. Ophunzira Baibulo amene anamangidwa aja anakanizidwa kuti atuluke pa belo ngakhale kuti anachita apilo mlanduwo. Iwo anachititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse kwa nthawi yaitali ndithu moti anthu a “mumzinda waukulu” uja ankawaona kuti akununkha. Koma kodi ‘mzinda waukulu’ umenewu n’chiyani?
22. (a) Kodi mzinda waukulu n’chiyani? (b) Kodi mabungwe ofalitsa nkhani anagwirizana bwanji ndi atsogoleri a zipembedzo posangalala kuti asokoneza ntchito ya mboni ziwiri zija? (Onani bokosi.)
22 Yohane anatchula mfundo zina zotithandiza kudziwa mzinda umenewu. Iye ananena kuti Yesu anapachikidwa mumzindawu. Zimenezi zikutichititsa kuganizira mwamsanga za Yerusalemu. Koma iye ananenanso kuti mzinda waukuluwu ukutchedwa Sodomu ndi Iguputo. N’zoonadi, nthawi inayake mzinda weniweni wa Yerusalemu unkatchedwa Sodomu chifukwa cha makhalidwe oipa amene ankachitika mmenemo. (Yesaya 1:8-10; yerekezerani ndi Ezekieli 16:49, 53-58.) Komanso dziko la Iguputo, lomwe linali ulamuliro woyamba wamphamvu padziko lonse, nthawi zina limaimira dziko lonse la Satanali. (Yesaya 19:1, 19; Yoweli 3:19) Choncho mzinda waukulu ukuimira mzinda woipa wa “Yerusalemu” umene anthu ake amanena kuti amalambira Mulungu ngakhale kuti amakonda kuchita machimo komanso zinthu zoipa zambiri ngati anthu a ku Sodomu. Ndipo mzinda umenewu ndi mbali ya dziko la Satanali, ngati mmene zinalili ndi dziko la Iguputo. Mzindawu ukuimira Matchalitchi Achikhristu, amene masiku ano ali ngati Yerusalemu wosakhulupirika. Anthu a m’matchalitchiwa anasangalala kwambiri pamene anasokoneza ntchito yolalikira ya mboni ziwiri zija, imene inkawasowetsa mtendere.
Mboni Zija Zinaukitsidwa
23. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira mboni ziwiri zija patatha masiku atatu ndi hafu, ndipo zimenezi zinakhudza bwanji adani awo? (b) Kodi ulosi wa pa Chivumbulutso 11:11, 12, ndi wa m’buku la Ezekieli wonena kuti Yehova anauzira mpweya pamafupa ouma amene anali m’chigwa, unakwaniritsidwa liti m’nthawi yathu ino?
23 Mabungwe ofalitsa nkhani anagwirizana ndi atsogoleri a zipembedzo ponyoza anthu a Mulungu. Mwachitsanzo, nyuzipepala ina inati: “Buku lakuti The Finished Mystery laona zakuda.” Koma zimenezi sizinali zoona. Mboni ziwirizo sizinakhale zakufa mpaka kalekale. Timawerenga kuti: “Masiku atatu ndi hafu aja atatha, mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu unalowa mwa mboni zija. Ndiyeno mbonizo zinaimirira, ndipo amene anali kuziona anagwidwa ndi mantha aakulu. Kenako mbonizo zinamva mawu ofuula ochokera kumwamba akuziuza kuti: ‘Kwerani kuno.’ Ndipo zinakwera kumwamba mumtambo, moti adani awo anaziona.” (Chivumbulutso 11:11, 12) Choncho zimene zinachitikira mbonizi zikufanana ndi zimene zinachitikira mafupa ouma amene anali m’chigwa chinachake, omwe Ezekieli anaona m’masomphenya. Yehova anauzira mpweya pamafupawo ndipo anakhala ndi moyo. Zimenezi zinachitira chithunzi kubadwanso kwa mtundu wa Isiraeli pambuyo pa zaka 70 za ukapolo ku Babulo. (Ezekieli 37:1-14) Maulosi awiriwa, wa pa Ezekieli ndi wa pa Chivumbulutso, anakwaniritsidwa mochititsa chidwi m’nthawi yathu ino mu 1919, pamene Yehova anaukitsa mboni zake zimene zinali ngati zakufa, kuti ziyambirenso kugwira ntchito yawo mwakhama.
24. Kodi mboni ziwiri zija zitakhalanso ndi moyo, atsogoleri a zipembedzo omwe ankazunza mbonizo anamva bwanji?
24 Anthu amene ankazunza mbonizi anadabwa kwambiri. Mosayembekezera, mboni zakufazo zinakhalanso ndi moyo n’kuyambanso kugwira ntchito mwakhama. Zimenezi zinali zowawa kwambiri kwa atsogoleri a zipembedzo, makamaka chifukwa iwo ndi amene anachititsa kuti atumiki achikhristuwa amangidwe, koma tsopano anali atamasulidwa ndipo milandu yawo yonse inali itatsala pang’ono kuthetsedwa. Ndipo atsogoleri a zipembedzowa ayenera kuti anadabwa kwambiri mu September 1919, pamene Ophunzira Baibulo anachita msonkhano ku Cedar Point, m’chigawo cha Ohio, m’dziko la United States. Pamsonkhanowu J. F. Rutherford, amene anali atangotulutsidwa kumene m’ndende, analimbikitsa anthu kwambiri ndi nkhani yakuti “Kulengeza za Ufumu,” imene inachokera pa Chivumbulutso 15:2 ndi Yesaya 52:7. Akhristu odzozedwa anayambiranso “kunenera” kapena kuti kulalikira. Iwo anapitiriza kulalikira molimba mtima ndipo ankaulula chinyengo cha Matchalitchi Achikhristu mopanda mantha.
25. (a) Kodi mboni ziwiri zija zinauzidwa liti kuti, “Kwerani kuno,” ndipo zinakwera bwanji? (b) Kodi kukwezedwa kwa mboni ziwirizo kunakhudza bwanji mzinda waukulu?
25 Matchalitchi Achikhristu anayesa mobwerezabwereza kuti aikenso m’mavuto atumiki a Mulungu ngati mmene anachitira mu 1918. Pofuna kusokoneza ntchito yawo, matchalitchiwa ankagwiritsa ntchito magulu a anthu achiwawa, ankakhotetsa malamulo a boma, ndiponso ankachititsa kuti Akhristuwa atsekeredwe m’ndende kapena aphedwe, komabe sanaphule kanthu. Koma kuyambira mu 1919, mboni ziwiri zija zinakhala pamalo auzimu oti Matchalitchi Achikhristuwo sakanakwanitsa kuzizunza. M’chaka chimenechi, Yehova anauza Akhristuwo kuti: “Kwerani kuno,” ndipo iwo anakwera pamalo auzimu apamwamba pamene adani awo ankatha kuwaona koma sakanatha kuwakhudza. Yohane anafotokoza mmene mzinda waukulu unadabwira ndi kukwezedwa kwa mboni zija. Iye anati: “Mu ola limenelo, kunachitika chivomezi chachikulu, ndipo gawo limodzi mwa magawo khumi a mzindawo linagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomezicho, ndipo ena onse anachita mantha n’kupereka ulemerero kwa Mulungu wakumwamba.” (Chivumbulutso 11:13) Zoonadi, zipembedzo zinagwedezeka kwambiri. Atsogoleri a matchalitchi akuluakulu ankaona ngati nthaka ikugwedezeka pamene Akhristu opatsidwanso mphamvuwa anayambiranso kugwira ntchito yawo. Gawo limodzi mwa magawo khumi a mzinda wawo, limene mophiphiritsa likuimira anthu 7,000, linakhudzidwa kwambiri. Ndipo Baibulo limanena kuti anthu 7,000 amenewo anaphedwa.
26. Kodi ndani amene akuimiridwa ndi “gawo limodzi mwa magawo khumi a mzindawo” komanso anthu “7,000” otchulidwa pa Chivumbulutso 11:13? Fotokozani.
26 Mawu akuti “gawo limodzi mwa magawo khumi a mzindawo” akutikumbutsa zimene Yesaya analosera zokhudza mzinda wa Yerusalemu. Iye analosera kuti chakhumi chidzapulumuka pamene mzindawo uzidzawonongedwa, ndipo chidzakhala mbewu yopatulika. (Yesaya 6:13) Komanso chiwerengero cha 7,000 chikutikumbutsa kuti pamene Eliya ankaona kuti watsala yekha wokhulupirika mu Isiraeli, Yehova anamuuza kuti panali anthu enanso 7,000 amene sanagwadirepo Baala. (1 Mafumu 19:14, 18) M’nthawi ya atumwi, mtumwi Paulo ananena kuti anthu 7,000 amenewa akuimira Ayuda amene analabadira uthenga wabwino wonena za Khristu. (Aroma 11:1-5) Choncho malemba amenewa akutithandiza kumvetsa kuti “7,000” komanso “gawo limodzi mwa magawo khumi a mzindawo” otchulidwa pa Chivumbulutso 11:13, ndi anthu amene anamvera uthenga wa mboni ziwiri zimene zinakwezedwa zija, ndipo anachoka mumzinda waukulu wochimwa uja. Iwo amakhala ngati afa ku Matchalitchi Achikhristu ndipo mayina awo amafafanizidwa pa mndandanda wa anthu a m’matchalitchimo. Matchalitchiwo amaona kuti anthu amenewa kulibenso.d
27, 28. (a) Kodi ‘ena onse anapereka bwanji ulemerero kwa Mulungu wakumwamba’? (b) Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anakakamizika kuvomereza chiyani?
27 Koma kodi ‘ena onse [m’Matchalitchi Achikhristu] anapereka bwanji ulemerero kwa Mulungu wakumwamba’? Iwo sanachite zimenezi pochoka m’zipembedzo zawo zampatukozo n’kukhala atumiki a Mulungu. Koma anachita zimenezi m’njira imene inafotokozedwa m’buku lina lofotokozera mawu a m’Baibulo. Pofotokoza mawu akuti “n’kupereka ulemerero kwa Mulungu wakumwamba,” bukuli linati: “Mawuwa sakutanthauza kuti anthuwo anatembenuka, kulapa kapena kuyamika Mulungu, koma akungotanthauza kuti anazindikira. M’malemba kawirikawiri mawu amenewa amatanthauza zimenezi. Yerekezerani ndi Yoswa 7:19 (Septuagint). Yohane 9:24; Machitidwe 12:23; Aroma 4:20.” (Word Studies in the New Testament, lolembedwa ndi Vincent) Matchalitchi Achikhristu anakakamizika kuvomereza kuti Mulungu wa Ophunzira Baibulo anachita zodabwitsa pothandiza Akhristu amenewa kuti ayambirenso kugwira ntchito yawo.
28 N’kutheka kuti atsogoleri a zipembedzowa anangovomereza zimenezi mumtima mwawo. Palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti mtsogoleri wina aliyense wa chipembedzo anavomereza poyera kuti Mulungu wa mboni ziwirizo ndi wamphamvu. Koma ulosi umene Yehova ananena kudzera mwa Yohane ukutithandiza kuzindikira zimene zinali mumtima mwawo komanso mmene anachitira manyazi mu 1919. Kuyambira m’chaka chimenechi, pamene anthu “7,000” aja anayamba kuchoka m’Matchalitchi Achikhristu ngakhale kuti matchalitchiwo ankayesetsa kuti nkhosa zawo zisawathawe, atsogoleri a zipembedzo anakakamizika kuvomereza kuti Mulungu wa Akhristu odzozedwa ndi wamphamvu kuposa mulungu wawo. Patapita nthawi, iwo anazindikira bwino zimenezi, pamene anthu ambiri a m’gulu la nkhosa zawo anayamba kuchokamo. Anthuwa anagwirizana ndi zimene anthu ena ananena Eliya atagonjetsa anthu olambira Baala paphiri la Karimeli, kuti: “Yehova ndiye Mulungu woona! Yehova ndiye Mulungu woona!”—1 Mafumu 18:39.
29. Kodi Yohane ananena kuti n’chiyani chimene chikubwera mofulumira, ndipo Matchalitchi Achikhristu akuyembekezera kugwedezekanso motani?
29 Koma tsopano tamvani zimene Yohane akutiuza. Iye akuti: “Tsoka lachiwiri linapita. Koma tsoka lachitatu linali kubwera mofulumira.” (Chivumbulutso 11:14) Ngati Matchalitchi Achikhristu anagwedezeka ndi zimene takambiranazi, kodi chiwachitikire n’chiyani tsoka lachitatu likalengezedwa, mngelo wa 7 akaliza lipenga lake, komanso chinsinsi chopatulika cha Mulungu chikathetsedwa?—Chivumbulutso 10:7.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve mwatsatanetsatane nkhani ya kachisi wamkulu wauzimu, onani nkhani yakuti “Kachisi Wauzimu Wamkulu wa Yehova” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1996, patsamba 14, komanso bokosi la mutu wakuti “Mmene Mzimu Woyera Unaululira Tanthauzo la Kachisi Wauzimu,” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2010, patsamba 22.
b Mawu akuti ‘phompho’ (Chigiriki, aʹbys·sos; Chiheberi, tehohmʹ) amatanthauza malo ophiphiritsa amene munthu kapena chinthu chomwe chili kumeneko sichingathe kuchita chilichonse. (Onani Chivumbulutso 9:2.) Koma mawuwa angatanthauzenso nyanja yaikulu. Mawu achiheberiwo kawirikawiri amawamasulira kuti “madzi akuya.” (Salimo 71:20; 106:9; Yona 2:5) Choncho “chilombo chotuluka muphompho” n’chimodzimodzi ndi ‘chilombo chotuluka m’nyanja.’—Chivumbulutso 11:7; 13:1.
c Tikafufuza zimene zinachitikira anthu a Mulungu pa nthawiyi, zikuoneka kuti masiku atatu ndi hafu amenewa si nthawi yeniyeni ya maola 84, ngakhale kuti miyezi 42 ikuimira zaka zenizeni zitatu ndi hafu. N’kutheka kuti nthawi ya masiku atatu ndi hafu, yomwe inayamba zaka zitatu ndi hafu zitatha, yatchulidwa kawiri (pa vesi 9 ndi 11) posonyeza kuti ndi nthawi yaifupi poyerekezera ndi zaka zenizeni zitatu ndi hafu zimene mbonizo zinkagwira ntchito zili pa mavuto ambiri.
d Yerekezerani ndi mmene mawu akuti “akufa,” “anafa,” komanso “amoyo” agwiritsidwira ntchito pa Aroma 6:2, 10, 11; 7:4, 6, 9; Agalatiya 2:19; Akolose 2:20; 3:3.
[Bokosi patsamba 168]
Kukondwera Kotchulidwa pa Chivumbulutso 11:10
M’buku limene Ray H. Abrams analemba mu 1933, lakuti Alaliki Akulimbikitsa Nkhondo (Preachers Present Arms), iye ananena kuti atsogoleri a zipembedzo ankatsutsa kwambiri buku la Ophunzira Baibulo lakuti The Finished Mystery. Iye anafotokoza zimene atsogoleri a zipembedzo ankachita pofuna kufafaniza Ophunzira Baibulo kuti asiye “ntchito yawo yokopa anthu, imene inali ngati mliri.” Zimenezi zinachititsa kuti pakhale mlandu umene pamapeto pake J. F. Rutherford ndi anzake ena 7 anaweruzidwa kuti akakhale m’ndende kwa zaka zambiri. Dr. Abrams anapitiriza kufotokoza kuti: “Tikaunika mmene mlandu wonsewo unayendera, timaona kuti matchalitchi komanso atsogoleri a zipembedzo ndi amene anakonza chiwembu chofuna kufafaniza anthu otsatira Russell. Mwachitsanzo, m’dziko la Canada, mu February, 1918, atsogoleri a zipembedzowa anayamba ntchito imene anaikonzekera bwino yolimbana ndi anthu otsatira Russell komanso mabuku awo, makamaka buku lakuti The Finished Mystery. Malinga ndi zimene nyuzipepala ina inanena (Winnipeg Tribune), . . . anthu ankakhulupirira kuti ‘atsogoleri enaake a zipembedzo’ ndi amene anachititsa kuti buku limeneli likhale loletsedwa m’mayiko ena.”
Dr. Abrams anapitiriza kufotokoza kuti: “Anthu olemba nkhani zachipembedzo atamva kuti otsatira Russell aja alamulidwa kuti akakhale m’ndende zaka 20, zomwe analemba m’mabuku ndi manyuzipepala awo, otchuka ndi osatchuka omwe, zinasonyeza kuti iwo anasangalala kwambiri. M’magazini onse a zipembedzo zikuluzikulu sindinapezemo mawu osonyeza kuti olemba magaziniwo ankamva chisoni ndi chigamulo chimenechi. Wolemba nkhani wina, dzina lake Upton Sinclair, ananena kuti ‘n’zosachita kufunsa kuti chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kuti anthu amenewa ayambe kuzunzidwa chinali chakuti . . . magulu a zipembedzo zikuluzikulu ankadana nawo kwambiri.’ Pamenepatu zinaoneka kuti zimene boma linachitazi n’zimene matchalitchi onse mogwirizana ankafuna kuti achite, koma ankalephera paokha.” Wolemba bukuli atagwira mawu ndemanga zina zonyoza zimene zinalembedwa m’mabuku ena azipembedzo, ananena za kusinthidwa kwa chigamulo chija m’Khoti la Apilo ndipo kenako anati: “Chigamulochi chitasinthidwa, matchalitchi sananene chilichonse.”
[Chithunzi patsamba 163]
Yohane anayeza kachisi wauzimu, kutanthauza kuti ansembe odzozedwa akuyenera kutsatira ndendende mfundo za Mulungu
[Zithunzi patsamba 165]
Ntchito yomanganso imene Zerubabele ndi Yoswa ankagwira inasonyeza kuti poyamba m’tsiku la Ambuye, Mboni za Yehova zidzakhala zochepa koma kenako zidzachuluka kwambiri. Malo awo ngati amene ali pamwambawa, omwe ali ku Brooklyn, New York, anafunika kuwawonjezera kwambiri chifukwa cha kukula kwa ntchito yawo
[Zithunzi patsamba 166]
Mauthenga achiweruzo oyaka ngati moto amene mboni ziwiri zija zinkalengeza anachitiridwa chithunzi ndi ntchito yaulosi imene Mose ndi Eliya ankagwira
[Zithunzi patsamba 169]
Mofanana ndi mafupa ouma a mu Ezekieli chaputala 37, mboni ziwiri zinapatsidwanso mphamvu kuti ziyambirenso kugwira ntchito yolalikira masiku ano