Pamene Dziko Latsopano Lidzadza
DZIKO latsopano la Mulungu lidzadza litachoka limene lilipoli. Koma mungafunse kuti, ‘Kodi tingakhulupiriredi kuti dzikoli lidzatha?’ Eya, talingalirani, kodi lina linayamba lathapo?
Inde, malinga ndi umboni wotsimikizirika, dziko linathapo. Baibulo limati: “Dziko lapansi la masiku aja [m’nthaŵi ya Nowa], pomizika ndi madzi, lidaonongeka.” Mulungu “sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.”—2 Petro 2:5; 3:6.
Onani kuti linali “dziko la osapembedza,” kapena dongosolo loipa la zinthu, limene linawonongedwa. Silinali pulanetili Dziko Lapansi, miyamba yokhala ndi nyenyezi, kapena banja la anthu limene linatha. Pamene opulumuka Chigumula anawonjezereka m’chiŵerengero, dziko lina (lamakono lathuli) linakhalako. Kodi nchiyani chimene chidzalichitikira?
Litanena kuti dziko la m’tsiku la Nowa linawonongedwa, Baibulo limapitiriza kuti: “Miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto.” (2 Petro 3:7) Moto uli chizindikiro cha chiwonongeko cha dziko. Ndithudi, “dziko lapansi [limene lilipo tsopano] lipita.” (1 Yohane 2:17) Koma kodi lidzapita liti?
Atumwi a Yesu anafuna kudziŵa, motero anafunsa kuti: “Tatiuzani, kodi zinthuzi zidzachitika liti? ndipo nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kubwera kwanu, ndi cha mapeto a dzikoli?” (Mateyu 24:3, King James Version) Poyankha Yesu anapereka chizindikiro chimene chikakhozetsa anthu okhalako panthaŵi ya kukwaniritsidwa kwake kudziŵa kuti dziko lina linali pafupi kutha; kuti dziko latsopano likaliloŵa m’malo. Kodi chizindikirocho chinali chiyani?
Chizindikiro
Chizindikirocho chinaphatikizapo mbali zambiri, inde, zochitika zambiri zidanenedweratu. Kuti chizindikirocho chikwaniritsidwe, zonsezi zikayenera kuchitika mwanjira yoonekera bwino lomwe makamaka m’nthaŵi imodzimodzi, mkati mwa mbadwo umodzi. (Mateyu 24:34) Kodi zochitikazo nziti?
Zina zimene zinatchulidwa ndi Yesu ndizo: “Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akutiakuti.” “Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa. . . . Chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.”—Luka 21:10, 11; Mateyu 24:7-9, 12.
Mtumwi Paulo anatchula mikhalidwe ina imene ikasonyeza “masiku otsiriza” a dzikoli. Iye analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, . . . aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”—2 Timoteo 3:1-5.
Ndithudi, inu mwaona kapena kumva za zinthu zonsezi—mikangano ya padziko lonse yoposa nkhondo zakale, zivomezi zazikulu, miliri yofalikira kwambiri ndi kupereŵera kwa chakudya, kudedwa ndi kuzunzidwa kwa otsatira a Kristu, kuwonjezereka kwa kusayeruzika, ndi nthaŵi zovuta zosayerekezereka. Kuwonjezera pazinthu zimenezi, Baibulo limaneneratu kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (Chivumbulutso 11:18) Ndipo anthu akuwonongadi dziko tsopano lino!
M’November chaka chatha, manyuzipepala anali ndi mitu yankhani yotere: “Asayansi Opambana Akuchenjeza za Chiwonongeko cha Dziko Lapansi.” Dr. Henry Kendall, wolandira mphotho ya Nobel ndi tcheyamani wa Union of Concerned Scientists, anati: “Chenjezoli silokukumazidwa, ndipo silongowopseza.” Nkhani ina ya m’nyuzipepala inasimba kuti: “Mpambo wa asayansi okwanira 1,575 amene analemba chenjezolo uli ndi asayansi otchuka okhaokha m’chitaganya cha padziko lonse cha asayansi.” Chenjezo lawo la chiwonongeko chotheratu cha dziko lathu siliyenera kunyalanyazidwa!
Sipangakhale chikayikiro chilichonse. Chizindikirocho m’mbali zake zonse chikukwaniritsidwa, kuphatikizapo mbali yaikulu ya ulosi wa Yesu wakuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro,” inde, chimaliziro cha dziko lino. (Mateyu 24:14) Chidzafika, Yesu anatero, pamene mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu yalalikidwa padziko lonse. Ndipo kulalikidwa kumeneko kukuchitidwa tsopano ndi Mboni za Yehova pamlingo wonenedweratuwo!
Zimene Muyenera Kuchita
Motero, maumboni onse amasonyeza chenicheni chakuti dziko latsopano la Mulungu layandikira kwambiri. Komabe, ngati muti mudzapulumuke mapeto a dzikoli ndi kudzasangalala ndi moyo m’dziko latsopano, mufunikira kuchita kanthu kena. Litanena kuti “dziko lapansi lipita,” Baibulo limasonyeza chimene chili chofunika kwa inu, likumalongosola kuti: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.
Motero, mufunikira kuphunzira chifuniro cha Mulungu ndi kuchichita. Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani kuchita zimenezi. Pamenepo mukhoza kupulumuka mapeto a dzikoli ndi kusangalala kwamuyaya ndi madalitso a dziko latsopano la Mulungu.
Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Chithunzithunzi cha NASA
[Chithunzi patsamba 31]
Chisautso chachikulu chitangotha dziko latsopano lidzadza