Mfuti—Dziko Lopanda Izo
KUCHOKERA pachiyambi pambiri ya anthu, munthu wagwiritsira ntchito chiwawa m’zochita zake ndi munthu mnzake. Kupha kunayambira m’banja loyamba pamene Kaini anapha mphwake Abele. Kuphanako kwapitirizabe kuyambira pomwepo—m’mabanja, m’mafuko, ndi pakati pa mitundu. Pamene zida zinakhala zamphamvu kwambiri, minkhole inachuluka mowonjezereka. Miyala ndi zibonga zinaloŵedwa m’malo ndi mikondo ndi mivi, iyi inaloŵedwanso m’malo ndi mfuti ndi mabomba. Kuwonongedwa kwa anthu mazana ambiri kunadzakhala zikwi zambiri; lerolino zikwi zambirizo zakhala mamiliyoni ambiri. Ndipo sizimachitika m’nthaŵi yankhondo yokha komanso mumtendere. Sikumachitidwa ndi asilikali okha komanso ndi nzika wamba. Sikumachitidwa ndi akulu okha komanso ndi ana omwe. Kodi kuchulukachuluka kwa chiwawa kudzathadi? Ngati kumadalira pa anthu, pamenepo palibe chiyembekezo.—2 Timoteo 3:1-5, 13.
Kristu Yesu ananeneratu kuti iyi ikakhala nthaŵi pamene mitundu ikawukirana ndi mitundu ina m’nkhondo zowopsya, kupha miyoyo mamiliyoni ambiri. Miliri ndi zivomezi zikapha ochuluka m’malo ambiri. Munthu akaipitsa dziko lapansi kumlingo wakuti mphamvu zadziko zochilikiza moyo zikaikidwa paupandu—asayansi ambiri tsopano akufuula mantha amenewo. Koma kukonda ndalama kwa munthu kumampangitsa kupitirizabe ndi kuipitsa kwakeko, ndipo kudzatha kokha pamene Yehova Mulungu iyemwini adzaloŵereramo “kuononga iwo akuononga dziko.”—Chibvumbulutso 11:18.
Ambiri amaseka machenjezo oterowo ndipo mwakutero akukwaniritsa mbali ina ya chizindikiro chonenedweratucho cha masiku otsizira: ‘Ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwake? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.’—2 Petro 3:3, 4.
Koma mtambo wamdima umenewu wophimba mtundu wa anthu uli ndi mapeto owala. Yesu ananeneratu kuti pa kukhalapo kwake, padzakhala “chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo [wake] wa nyanja ndi mafunde [ake]; anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.” Koma ananenanso kuti ikakhala nthaŵi yakuti ‘muweramuke, ndi kutukula mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.’—Luka 21:25-28.
Mitundu ikukomoka ndi mantha, makamu a anthu ali osokonekera, ndipo munthu payekha akuwopa zinthu zirinkudza padziko lapansi, koma iyi ndi nthaŵi ya kuwomboledwa kwa awo oyembekezera kufika kwa Ufumu wa Mulungu ndi Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu Yesu. Imeneyo idzakhala nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova Mulungu la ‘miyamba yatsopano ndi dziko latsopano mmene mudzakhala chilungamo.’—2 Petro 3:13.
Ndipo simudzakhala mfuti! Palibiretu yofunikira nkhondo. “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto [magareta ankhondo, Rotherham].”—Salmo 46:9.
Palibe idzafunikira chitetezo chaumwini. ‘Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsya; pakuti pakamwa pa Yehova wamakamu padanena.’—Mika 4:4.
Owongoka mtima okha, popanda woipa aliyense, ngwomwe adzakhalamo. ‘Pakuti owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.’ (Miyambo 2:21, 22) Pamenepo ‘ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:11.
M’maso mwa Mulungu chiwawa chikuwononga dziko. M’tsiku la Nowa ‘dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.’ (Genesis 6:11-13) Motero, Yehova analithetsa dzikolo ndi Chigumula chapadziko lonse. Yesu anafanizira motere mapeto a dziko lachiwawa la m’nthaŵi ya kukhalapo kwake iri ku mapeto a lakale lija: ‘Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.’—Mateyu 24:38, 39.
M’dziko latsopano la Mulungu aliyense wokhala ndi moyo adzakwaniritsa Marko 12:31 amene amati: “Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini.” Ndi Yesaya 11:9: ‘Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’ Ndipo chimene chidzakwaniritsidwanso m’dziko latsopano lachilungamo limenelo ndicho mikhalidwe iyi yaulemerero yolongosoledwa pa Chibvumbulutso 21:1, 4: ‘Ndipo ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa, zoyambazo zapita.’ Pamenepo kunena mwantheradi, sipadzakhala zitaganya za anthu zolimbana ndi mfuti!
Palibe ndi amodzi omwe a masinthidwe aakulu ameneŵa odalitsa anthu amene adzabweretsedwa ndi owukira maboma ndi mfuti zawo zokakala zopululutsa otsutsa. M’malo mwake, adzabweretsedwa ndi Yehova Mulungu kupyolera mwa Ufumu wake pansi pa Kristu Yesu. Motero Yesaya 9:6, 7 amati: ‘Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiŵeruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.’