Mdyerekezi Alipo Si Nthano Chabe
“Chipangano Chatsopano chonse chimasimba za nkhondo yaikulu pakati pa magulu a Mulungu ndiponso a khalidwe labwino kulimbana ndi magulu oipa otsogozedwa ndi Satana. Ameneŵa simalingaliro a wolemba Baibulo mmodzi kapena aŵiri okha ayi. . . . Choncho, umboni wa Chipangano Chatsopano n’ngomveka bwino. Satana woipayo alipodi , ndipo nthaŵi zonse amadana ndi Mulungu ndiponso anthu Ake,” likutero buku lakuti “The New Bible Dictionary.”
NANGANO n’chifukwa chiyani anthu ambiri odzinenera kuti ndi Akristu ndiponso amene amati amakhulupirira Baibulo amatsutsa zoti Mdyerekezi alipo? Kunena zoona, n’chifukwa chakuti savomereza kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. (Yeremiya 8:9) Iwo amanena kuti amene analemba Baibulo anaphatikizamo malingaliro a filosofi ya anthu omwe ankakhala nawo ndipo sanalembe choonadi chochokera kwa Mulungu molondola. Mwachitsanzo, Mkatolika wina wamaphunziro apamwamba azaumulungu dzina lake Hans Küng analemba m’buku lake lakuti On Being a Christian kuti: “Malingaliro a Satana pamodzi ndi a ziwanda opezeka m’nthano . . . analoŵa m’Chiyuda choyambirira ndipo kenako m’Chipangano Chatsopano kuchokera m’nthano za Ababulo.”
Komabe, Baibulo ndi Mawu ouziridwa a Mulungu osati a anthu. Choncho, n’kwanzeru kuona zomwe Baibulo limanena zokhudza Mdyerekezi kukhala zenizeni.—2 Timoteo 3:14-17; 2 Petro 1:20, 21.
Kodi Yesu Ankaganiza Bwanji za Nkhaniyi?
Yesu Kristu ankakhulupirira kuti Mdyerekezi alipodi. Yesu sanayesedwe ndi zinthu zoipa za m’thupi lake lomwe. Anaukiridwa ndi munthu weniweni yemwe Yesu kenako anamutcha kuti “mkulu wa dziko lapansi.” (Yohane 14:30; Mateyu 4:1-11) Ankakhulupiriranso kuti zolengedwa zina zauzimu zinagwirizana ndi Satana pa zolinga zake zoipazo. Yesu anachiritsa anthu ‘ogwidwa ndi ziwanda.’ (Mateyu 12:22-28) Ngakhale buku la okana Mulungu lakuti A Rationalist Encyclopædia limatchula mfundo imeneyi mwa kunena kuti: “Anthu amaphunziro apamwamba azaumulungu sakumvetsa chifukwa chake Yesu wa m’Mauthenga Abwino anavomereza kuti kunja kuno kuli mizimu yoipa.” Pamene Yesu ankanena za Mdyerekezi ndi ziwanda zake, sanali kungonena za zikhulupiriro zozikidwa pa nthano za Ababulo. Iye ankadziŵa kuti alipodi.
Timaphunzira zambiri zokhudza Mdyerekezi pamene tipenda mawu a Yesu kwa aphunzitsi achipembedzo a m’nthaŵi yake. Iye anati: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.
Mogwirizana ndi mawu ameneŵa, Mdyerekezi (dzina lomwe m’Chigiriki limatanthauza ‘woneneza’) anali “wabodza, ndi atate wake wa bodza.” Anali cholengedwa choyamba kunamizira Mulungu ndipo anachita zimenezo kalekale m’munda wa Edene. Yehova anali atauza makolo athu oyambawo kuti ‘adzafa ndithu’ ngati adzadya zipatso zamtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa. Mwakugwiritsira ntchito pakamwa pa njoka, Satana ananena kuti mawu amenewo anali abodza. (Genesis 2:17; 3:4) N’chifukwa chake moyenerera amatchedwa “njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana.”—Chivumbulutso 12:9.
Mdyerekezi ananenanso bodza lokhudza mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa. Ananena kuti panalibe chifukwa choletsera kudya za mumtengo umenewo ndipo kuti kuletsako kunali kugwiritsa ntchito molakwa ulamuliro. Iye anauza Adamu ndi Hava kuti ‘adzakhala ngati Mulungu,’ akumadziŵa okha zabwino ndi zoipa. Ndi mawu ameneŵa, Satana anatanthauza kuti monga anthu okhala ndi ufulu wodzisankhira anayenera kukhala odzidalira kotheratu. (Genesis 3:1-5) Kutsutsa kumeneku kwakuti Mulungu sayenera kulamulira anthu ndiponso kuti njira zake za ulamuliro n’zosayenera kunadzutsa nkhani yaikulu kwambiri. Choncho Yehova wapereka mpata woti nkhani imeneyi ithetsedwe. N’chifukwa chake Satana waloledwa kukhalabe ndi moyo kwakanthaŵi. Nthaŵi yake yokhala ndi polekezera tsopano yatsala pang’ono kutha. (Chivumbulutso 12:12) Komabe, iye akupitiriza kupatutsa anthu kwa Mulungu mwakugwiritsa ntchito bodza ndi chinyengo. Akugwiritsanso ntchito anthu ofanana ndi alembi ndi Afarisi a nthaŵi ya Yesu kufalitsa ziphunzitso zake.—Mateyu 23:13, 15.
Yesu ananenanso kuti Mdyerekezi anali “wambanda kuyambira pachiyambi” ndipo kuti “sanaima m’choonadi.” Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova analenga Mdyerekezi monga “wambanda.” Baibulo siliphunzitsa kuti Mdyerekezi analengedwa kuti akhale chilombo choyang’anira malo oyaka moto ndi ozunzirako aliyense amene amatsutsana ndi Mulungu. Ndiponso Baibulo siliphunzitsa n’komwe kuti kuli malo oterowo. Baibulo limasonyeza kuti akufa ali m’manda a anthu onse osati kumalo oyaka moto kapena m’manja mwa Satana.—Machitidwe 2:25-27; Chivumbulutso 20:13, 14.
Pachiyambi Mdyerekezi ‘anali m’choonadi.’ Anali m’banja la Yehova lakumwamba monga mwana wangwiro wauzimu wa Mulungu. Koma iye “sanaima m’choonadi.” Anasankha kutsatira njira ndiponso mfundo zake zabodza. Choncho, iye analengedwa monga mwana waungelo wa Mulungu ndithu, koma anakhala Mdyerekezi komanso wambanda atapandukira Yehova mwakufuna kwake ndiponso kunena bodza kwa Adamu ndi Hava. Mdyerekezi ali ngati anthu amene anapandukira Yehova m’nthaŵi ya Mose. Ponena za iwo, timaŵerenga kuti: “Anam’chitira zovunda sindiwo ana ake, chirema n’chawo.” (Deuteronomo 32:5) Ndi mmene zililinso ndi Satana. Anakhala “wambanda” pamene anapanduka ndi kuchititsa kuti Adamu ndi Hava, komanso anthu onse azifa.—Aroma 5:12.
Angelo Osamvera
Angelo enanso anagwirizana ndi Satana n’kupanduka. (Luka 11:14, 15) M’nthaŵi ya Nowa, angelo ameneŵa “anasiya pokhala pawopawo”, n’kuvala matupi aumunthu kuti akakwatire “ana aakazi a anthu.” (Yuda 6; Genesis 6:1-4; 1 Petro 3:19, 20) “Magawo atatu a nyenyezi zam’mwamba,” kutanthauza kuti zolengedwa zochepa zauzimu, ndizo zinachita zimenezi.—Chivumbulutso 12:4.
Buku la Chivumbulutso lomwe limasimba zinthu mophiphiritsa limatchula Mdyerekezi kuti “chinjoka chofiira, chachikulu.” (Chivumbulutso 12:3) Chifukwa chiyani? Osati chifukwa chakuti amaoneka wofiira ndi wonyansa ayi. Sitikudziŵa kuti zolengedwa zauzimu zili ndi matupi otani, koma mwachionekere thupi la Satana silisiyana ndi la zolengedwa zina zaungelo. Komabe, kunena kuti Satana ndi “chinjoka chofiira, chachikulu” n’koyenereradi chifukwa cha mtima wake wolusa, woopsa, wamphamvu, ndiponso wowononga.
Tsopano Satana ndi ziwanda alibenso mpata wochita zinthu zina. Sangavalenso matupi aumunthu monga anachitira. Ufumu wa Mulungu utaperekedwa m’manja mwa Kristu mu 1914, Satana ndi ziwanda anaponyedwa pansi kudziko.—Chivumbulutso 12:7-9.
Mdyerekezi Ndi Mdani Wamphamvu
Ngakhale kuti anaponyedwa pansi kudziko, Mdyerekezi akadali mdani wamphamvu. Iye “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire.” (1 Petro 5:8) Mdyerekezi sikhalidwe linalake loipa limene limakhala m’thupi lathu lopanda ungwiroli ayi. N’zoonadi kuti tsiku ndi tsiku timalimbana ndi zofuna za thupi lathu lopanda ungwiroli. (Aroma 7:18-20) Komabe, nkhondo yaikulu timalimbana ndi “akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a choipa m’zakumwamba.”—Aefeso 6:12.
Kodi mphamvu ya Mdyerekezi yafala kwambiri motani? Mtumwi Yohane anati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) N’zoona kuti sitifunikira kuda nkhaŵa ndi Mdyerekezi kapena kulola mantha onkitsa kutifooketsa. Komabe, n’kwanzeru kukhalabe atcheru ndi zolinga zake zofuna kutiphimba m’maso kuti tisaone choonadi ndi kuti tisiye kukhulupirira Mulungu.—Yobu 2:3-5; 2 Akorinto 4:3, 4.
Mdyerekezi sagwiritsa ntchito njira za nkhanza nthaŵi zonse poukira anthu ofuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Nthaŵi zina amadzionetsa ngati “mngelo wa kuunika.” Mtumwi Paulo anachenjeza Akristu za ngozi imeneyi polemba kuti: “Ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Hava ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.”—2 Akorinto 11:3, 14.
Choncho tifunikira kukhala odzisungira, atcheru, kulimbana naye kwambiri Mdyerekezi ndi kukhala olimba m’chikhulupiriro. (1 Petro 5:8, 9; 2 Akorinto 2:11) Tipeŵe kusewera m’manja mwa Satana pochita chidwi ndi zilizonse zokhudzana ndi mizimu. (Deuteronomo 18:10-12) Phunzirani Mawu a Mulungu mwakhama, mukumakumbukira kuti Yesu Kristu anatchula mobwerezabwereza Mawu a Mulungu pamene anali kuyesedwa ndi Mdyerekezi. (Mateyu 4:4, 7, 10) Pemphani mzimu wa Mulungu. Zipatso za mzimu zingakuthandizeni kupeŵa ntchito zathupi zomwe Satana amalimbikitsa kwambiri. (Agalatiya 5:16-24) Ndiponso, pempherani moona mtima kwa Yehova pamene mukuvutitsidwa mwanjira inayake ndi Mdyerekezi ndi ziwanda zake.—Afilipi 4:6, 7.
Palibe chifukwa chochitira mantha ndi Mdyerekezi. Yehova akulonjeza motsimikiza kuti adzatiteteza ku chilichonse chomwe Satana angachite. (Salmo 91:1-4; Miyambo 18:10; Yakobo 4:7, 8) Mtumwi Paulo anati: “Tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.” Mukatero, ‘mudzakhoza kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.’—Aefeso 6:10, 11.
[Chithunzi patsamba 5]
Yesu ankadziŵa kuti Mdyerekezi anali munthu weniweni
[Chithunzi patsamba 6]
“Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo”
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi cha NASA
[Zithunzi patsamba 7]
Limbanani ndi Mdyerekezi mwa kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kupemphera nthaŵi zonse