Limbikitsanani Pamene Tsiku Likuyandikira
‘Limbikitsanani, ndipo koposatu monga momwe muwona tsiku likuyandikira.’—AHEBRI 10:25, “NW.”
1, 2. Kodi n’tsiku lotani lomwe likuyandikira, ndipo kodi maganizo a anthu a Yehova ayenera kukhala otani?
AMENE lerolino akukhala ndi phande m’kunena kuti, ‘Idzani mudzamwe madzi a moyo,’ samadzipatula okha. Pamene tsiku lalikulu la chilakiko cha Yehova likufika, iwo amagwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo wakuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi monga amachita ena, komatu tilimbikitsane, ndipo koposatu monga momwe muwona tsiku likuyandikira.”—Ahebri 10:24, 25, NW.
2 Malemba amalosera ponena za “tsiku” limenelo kukhala “tsiku la Yehova.” (2 Petro 3:10, NW) Popeza kuti Yehova ndiye Wam’mwambamwamba, Mulungu wamphamvuyonse, palibe tsiku limene lingapambane tsiku lake. (Machitidwe 2:20) Kumatanthauza kulemekezedwa kwa ufumu wake monga Mulungu pa chilengedwe chonse. Tsiku lofunika losayerekezereka limenelo likuyandikira.
3. Kodi tsiku la Yehova linkayandikira motani kwa Akristu a mzaka za zana loyamba, ndipo bwanji ponena za ife lerolino?
3 Mtumwi Paulo anauza Akristu m’zaka za zana loyamba za Nyengo Yathu ino kuti tsiku la Yehova linkayandikira. Iwo anayembekezera kudza kwa tsikulo, koma kumbuyoko, tsikulo linali zaka 1,900 kutsogolo. (2 Atesalonika 2:1-3) Mosasamala kanthu za mfundo imeneyo, iwo anafunikira kulimbikitsidwa chifukwa chakuti tsikulo linali lotsimikizirikadi kubwera, ndipo ngati Akristuwo anapitirizabe kutsata chikhulupiriro chimenecho, iwo akaloŵa m’tsiku lodalitsidwa limenelo. (2 Timoteo 4:8) Kumbuyoko, tsikulo linawonedwa likumayandikira. Ponena za ife lerolino, tsiku la Yehova layandikira kwenikweni. Kukwaniritsidwa kozizwitsa konse kwa ulosi wa Baibulo kumatsimikizira mfundo yosangalatsa imeneyi. Posachedwapa, dzina la Mulungu wathu, Yehova, lidzayeretsedwa kunthaŵi yosatha.—Luka 11:2.
Kulimbikitsidwa ndi Dzina Laumulungu
4. Mogwirizana ndi Chibvumbulutso 19:6, kodi ndani adzakhala Mfumu, ndipo dzina lake likudziŵidwa motani?
4 Dzina laumulungu liyenera kukhala nkhani yokondweretsa ku banja lonse la anthu. Today’s English Version imati: “Tamandani Mulungu! Chifukwa chakuti Ambuye, Mulungu Wamphamvuyonse, ndiye Mfumu!” (Chibvumbulutso 19:6) Mogwirizana ndi matembenuzidwe a Baibulo amenewo a m’zaka za zana la 20, iye ndiye Ambuye, Mulungu wamphamvuyonse. Matembenuzidwe amenewo, limodzinso ndi matembenuzidwe ena ambiri amakono, samapereka dzina la Munthu waumulunguyo yemwe akuyamba kulamulira monga Mfumu. Komabe, dzina laumulungu nlophatikizidwa m’kulengeza kwakuti “Aleluya!” (“Tamandani Ya” kapena, “Tamandani Yehova”) kopezedwa mu Revised Standard Version, New International Version, ndi matembenuzidwe a Moffatt a Chibvumbulutso 19:6. Kwakukulukulu m’Nyengo Yathu ino, dzina laumulungu laphimbidwa kwenikweni m’matembenuzidwe a Baibulo. Komabe, monga momwe tidzawonera, dzina limenelo lakhala lolimbikitsa kwakukulukulu kwa anthu a Mulungu, ponse paŵiri m’nthaŵi zakale ndi zamakono.
5, 6. (a) Kodi nchifukwa ninji Mose anafunikira kudziŵa dzina la Mulungu yemwe anamuimira? (b) Kodi payenera kuti panali chiyambukiro chotani kwa Aisrayeli pamene Mose anagogomezera dzina laumulungu?
5 Tikukumbukira kuti pamene Mose anatumidwa ndi Mulungu Wam’mwambamwamba kwa anthu a Israyeli okhala muukapolo mu Igupto, funso lakuti kodi ndani anamtuma linabuka m’maganizo a anthu amene Mose anatumidwako. Mose anazindikira kuti anthu Achiyuda ovutikawo akafuna kudziŵa dzina la Mulungu amene iye anamuimira. Ponena za chimenechi timaŵerenga pa Eksodo 3:15 kuti: ‘Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthaŵi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwo mibadwo.’
6 Pamene chidziŵitsochi chinagogomezeredwa kwa iwo, Aisrayeli ayenera kukhala analimbikitsidwa kwambiri. Chilanditso chawo chinatsimikiziridwa ndi Mulungu wowona yekha, Yehova. Ndipo kuyenera kukhala kunali kolimbikitsa chotani nanga kukhala ndi chiyembekezo chakuzoloŵerana ndi Mulungu pamene iye akasonyeza tanthauzo la dzina lake laumwini—osati kudzipatula modzitukumula!—Eksodo 3:13; 4:29-31.
7. (a) Kodi timadziŵa motani kuti ophunzira a Yesu anali ozoloŵerana ndi dzina laumulungu? (b) Kodi ndimotani mmene dzina la Mulungu linakankhidwira kumbuyo?
7 Ophunzira a Ambuye Yesu Kristu analimbikitsidwanso kwambiri ndi dzina laumulungu, Yehova, ndi amene linamuimira. (Yohane 17:6, 26) M’kati mwa uminisitala wa Yesu wa padziko lapansi, iye ndithudi sanakankhire kumbuyo dzina laumulungu, ndipo sichinali chifuno chake kuika dzina la iyemwini, Yesu, m’malo oyamba. Ndikokha pambuyo pa kuyambika kwa chipatuko chonenedweratu chakugwa pa chikhulupiriro chowona Chachikristu pamene dzina laumulungu linakankhidwira kumbuyo, inde, kulichotseratu m’kukambitsirana Kwachikristu. (Machitidwe 20:29, 30) Pamene dzina la Mwana wa Mulungu likayamba kupatsidwa ulemu waukulu, kuphimba lija la Atateyo, Akristu wamba akapeza kulambira kwawo Atateyo kukhala kosatsimikizirika, kopanda unansi wabanja pakati pa aŵiriwo, ndipo motero kosalimbikitsa kwenikweni.
8. Kodi kutenga dzina la Mboni za Yehova kwakhala ndi chiyambukiro chomapitirizabe chotani pa anthu a Mulungu?
8 Chotero, zinachititsa chisangalalo chosaneneka pamene International Bible Students mogwirizana ndi Watch Tower Society anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova mu 1931. Sikunali kokha kodzetsa chisangalalo komanso kunalidi kolimbikitsa. Pachifukwa chimenechi, ophunzira Baibulo opatsidwa dzina latsopanowo anatha kulimbikitsana.—Yerekezerani ndi Yesaya 43:12.
9. Kodi Akristu owona amamva motani ponena za Yemwe akumkhalira Mboni?
9 Chifukwa chake, Akristu owona lerolino amakupeza kukhala koyenerera kumdziŵikitsa Yemwe iwo ali Mboni zake zonenedweratu, mongadi momwe Yesu Kristu mtsogoleri wawo anachitira pamene anali pano padziko lapansi. (Chibvumbulutso 1:1, 2) Inde, iwo amamdziŵikitsa iye yekha kukhala yemwe dzina lake ndi Yehova.—Salmo 83:18.
Odzazidwa ndi Chimwemwe ndi Mzimu Woyera
10-12. (a) Kodi mphamvu yogwira ntchito imakhala ndi chiyambukiro chotani pa otsatira a Yesu? (b) Kodi Mboni za Yehova zodzala nchimwemwe zimafuna kuchitirana motani?
10 Yesu Kristu m’mawu ake otsazikira atumwi ake anati: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.’—Mateyu 28:19, 20.
11 Onani kuti Akristu ophunzitsidwa chatsopano anayenera kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera. Mzimu woyera umenewu simunthu koma mphamvu yogwira ntchito ya Yehova Mulungu, imene Iye amaigwiritsira ntchito kupyolera mwa Yesu Kristu. Pa Pentekoste, Yehova Mulungu, kupyolera mwa Yesu, anatsanulira mphamvu yogwira ntchito imeneyi pa otsatira odzipereka a Yesu Kristu. (Machitidwe 2:33) Iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera umenewu, ndipo chimodzi cha zisonyezero, kapena zipatso, za mzimu woyera ndicho chimwemwe. (Agalatiya 5:22, 23; Aefeso 5:18-20) Chimwemwe ndicho mkhalidwe wotsitsimula. Ophunzira ayenera kudzazidwa ndi chimwemwe cha mzimu woyera. Pemphero loperekedwa ndi mtumwi Paulo nloyenerera koposa: ‘Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya mzimu woyera.’—Aroma 15:13.
12 Pokhala zodzazidwa ndi mzimu wodzetsa chimwemwe umenewu, Mboni za Yehova lerolino, kuphatikizapo ‘khamu lalikulu,’ zidzafuna, inde, zidzasonkhezeredwa kulimbikitsana mkati mwa dongosolo lazinthu lopanda ubwenzi liripoli. Moyenerera, mtumwi Paulo ananena za ‘kutonthozana.’—Chibvumbulutso 7:9, 10; Aroma 1:12; 14:17.
Chifukwa Chokwanira Cholimbikitsidwira
13. Kodi tiri nzifukwa zotani zofunira kulimbikitsidwa ndi kumalimbikitsana?
13 Pokhala mkati mwa dongosolo lazinthu liripoli, limene wolamulira wake yemwe alidi mulungu ali wotsutsa chinthu cholungama chirichonse, Akristu adzafuna kulimbikitsana mkati mwa mpingo Wachikristu wa padziko lonse, umene umakutidwa ndi mzimu woyera wa Yehova Mulungu. (Ahebri 10:24, 25; Machitidwe 20:28) Tiri ndi chifukwa chokwanira cholimbikitsidwira. Inde, tiri achiyamikiro chotani nanga kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka chonena za Yehova ndi Mwana Wake ndi chonena za mphamvu yogwira ntchito imene iwo amaigwiritsira ntchito, ndiyo, mzimu woyera! Ha, ndife oyamikira chotani nanga kaamba ka chiyembekezo chimene akuchipereka! Chotero kulambira kwathu nkodzazidwa ndi chimwemwe. Mtumwi Paulo anauza Akristu amene anawalembera kalata kuti ayenera kumalimbikitsana ndi kumangirirana m’chikhulupiriro chawo chopatulika koposa. Iwo anayenera kumachita izi ‘monga momwe mophiphiritsira ankawona tsiku likuyandikira.’ Ndiponso, pamene maulamuliro andale a dziko lapansili asesa ndikuchotsapo Chikristu chamdzina lokha, limodzi ndi zipembedzo zonyenga zina zonse, mkhalidwewo udzafunikiritsa kuti tilimbikitsane mowonjezerekadi.
14. Kodi ndani ayenera kumalimbikitsana, ndipo motani?
14 Pamene akulu akutsogolera m’kulimbikitsa nkhosa m’mipingo yawo, Akristu onse amafunikira kumalimbikitsana, mongadi momwe Ahebri 10:25 ikulangizira. Kwenikweni, ichi nchiyeneretso Chachikristu. Ngati ndinu chiŵalo cha mpingo, kodi mumapereka chilimbikitso chimenechi? Inu mungazizwe kuti, ‘Kodi ndingatero motani? Kodi ndingachitenji?’ Choyamba, kodi abale ena onse ndi alongo samalimbikitsidwa kokha mwakupezekapo kwanu pa misonkhano ndi mwakuchirikiza kwanu makonzedwe Achikristu, monga momwedi inu mwininu mwachiwonekere mumalimbikitsidwira pamene muwona ena akumapezeka mokhulupirika pa misonkhano yampingo? Nawonso angalimbikitsidwe ndichitsanzo chanu chakupirira mokhulupirika. Mwakupitirizabe kwanu pa njira Yachikristu mosasamala kanthu za mavuto a moyo ndi zovuta zina, osaleka konse, mungakhazikitse chitsanzo chosonkhezera.
Limbanani ndi Kulefula Kwa Mdyerekezi
15. Kodi nchifukwa ninji Mdyerekezi ali ndi ‘udani waukulu,’ ndipo motsutsana ndi yani?
15 Sindife tokha amene tikudziŵa kuti tsiku la Yehova layandikira. Satana Mdyerekezi amadziŵanso. Chibvumbulutso 12:12 chimatiuza kuti tsopano pali tsoka kwa dziko lapansi ‘chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.’ Monga momwe Chibvumbulutso 12:17 chikusonyezera, mkwiyo wake waukulu ukulunjikitsidwa motsutsana ndi awo ‘amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.’ Nzosakaikiritsa—Mdyerekezi akufuna kutilefula! Ndipo amadziŵa mmene angayesere kuchita motero. Amadziŵa zifooko zathu ndi mavuto, ndipo iye amagwirira ntchito pa zimenezi.
16. Kodi nchifukwa ninji Satana amagwiritsira ntchito kulefula monga chida?
16 Kodi nchifukwa ninji Mdyerekezi amagwiritsira ntchito kulefula monga chida? Chifukwa chakuti kaŵirikaŵiri kumagwira ntchito. Ngakhale munthu amene wapirira chitsutso champhamvu ndi chizunzo angakhale mnkhole wa kulefuka. Satana amafuna kutonza Yehova Mulungu ndikuyesa kutsimikizira kuti atha kutembenuza anthu kuleka kumtumikira Iye. (Miyambo 27:11; yerekezerani ndi Yobu 2:4, 5; Chibvumbulutso 12:10.) Ngati angathe kukulefulani, angakuchititseni kubwerera m’mbuyo muutumiki wanu kwa Mulungu; angakuchititsenidi kuleka, kukhala wosakangalika m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.—2 Akorinto 2:10, 11; Aefeso 6:11; 1 Petro 5:8.
17. Kodi ziyambukiro zoipa za kulefuka zidawonekera motani m’tsiku la Mose?
17 Ziyambukiro zoipa za kulefuka zingawonedwe m’chochitika cha Aisrayeli mu Igupto wakale. Mose atalakhula ndi Farao, munthu wankhalweyo anawonjezera mokulira mavuto awo ndi kuwapondereza kwake. Mulungu anauza Mose kutsimikiziritsa Aisrayeli kuti Iye akawalanditsadi iwo, kuwapanga kukhala anthu Ake, kuwapulumutsa, ndi kuwaloŵetsa m’dziko lolonjezedwa. Mose analankhula zimenezi kwa ana a Israyeli. Koma Eksodo 6:9 akusimba kuti: ‘Sanamvera Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.’ Izi zinamlefuladi Mose kuti akalankhule ndi Farao monga momwe analamulidwa, mpaka pamene Yehova anamkhutiritsa Mose ndikumlimbikitsa.—Eksodo 6:10-13.
18. Kodi nchifukwa ninji pali kufunika kwakukulu kwakuti anthu a Mulungu alimbane ndi kulefula kwa Mdyerekezi?
18 Satana Mdyerekezi amadziŵa bwino lomwe ziyambukiro zoipa zimene kulefuka kungakhale nazo pa mtumiki wa Mulungu. Monga momwe Miyambo 24:10 ikunenera kuti: ‘Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.’ Popeza kuti tikukhala mkati mwenimweni mwa nthaŵi ya mapeto, tifunikira kukhala amphamvu ndi olimba mwauzimu. Nzoipadi kuti tifunikira kulimbana ndi kupanda ungwiro kwathu, zifooko, ndi zolakwa zimene zingatibweze m’mbuyo; koma kukhalanso ndi Satana akumayesayesa kugwiritsira ntchito zifooko zimenezi, timafunikira thandizo.
Dalirani Zolimba pa Nsembe ya Kristu
19. Kodi nchiyani chidzatithandiza kulimbana ndi kulefuka, ndipo chifukwa ninji?
19 Thandizo lalikulu m’nkhani imeneyi ndilo makonzedwe a dipo amene Yehova anawatheketsa kupyolera mwa Yesu Kristu. Tingakhale olakika mwakudalira molimba pa dipolo. Nkwangozi kuwachepsa makonzedwe ameneŵa. Inde, tidzalakwabe, kapena kuchimwa, malinga ngati tiri opanda ungwiro. Koma sitiyenera kulefuka ndikuleka, tikumalingalira kuti tiribenso chiyembekezo, ndipo mwakutero nkugwidwa mumsampha wa Satana. Timadziŵa kuti tiri ndi nsembe yokwanira kaamba ka tchimo. Dipolo likhoza kuchotsa machimo. Ngati tiri wa ‘khamu lalikulu,’ tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chokwanira ndi chitsimikizo chakuti titha kuchapa minjiro yathu ndikuiyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.—Chibvumbulutso 7:9, 14.
20. Kodi ndimotani mmene Chibvumbulutso 12:11 chimasonyezera kuti wolefula wamkuluyo, Mdyerekezi, angalakidwe?
20 Pa Chibvumbulutso 12:10 Satana akulongosoledwa kukhala “wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.” Kodi tingamlake motani woneneza woipa woteroyo ndi wolefula wauchiŵanda? Vesi 11 la chaputala chimenecho limapereka yankho kuti: ‘Iwo anamlaka iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mawu a umboni wawo; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.’ Chotero anthu a Yehova afunikira kusunga chidaliro chokwanira m’nsembe yadipo, mwazi wa Mwanawankhosayo. Sungani chilimbikitso chochokera ku kuchitira umboni kukhala cholimba, mukumagaŵana mokhazikika mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi aliyense amene mungathe.
21. Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi phande mosadziŵa m’ntchito ya Mdyerekezi yolefula abale athu?
21 Nthaŵi zina, ngakhale mosadziŵa, tingakhale ndi phande m’ntchito ya Mdyerekezi yolefula abale athu. Motani? Mwakukhala wosuliza mopambanitsa, kukhala wofuna zopambanitsa, kapena kukhala wolungama mopambanitsa. (Mlaliki 7:16) Tonsefe tiri ndi zopereŵera ndi zifooko. Tisazigwiritsiretu ntchito monga momwe Mdyerekezi amachitira. Mmalo mwake, tiyeni tilankhule molimbikitsa ponena za abale athu ndi anthu a Yehova monga gulu lolinganizidwa. Timafuna kupitirizabe kumatonthozana mtima ndikupeŵa kukhwethemulana.
Kulimbikitsana Pamene Tsiku Likuyandikira
22, 23. (a) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kungosiira akulu kukhala magwero a chilimbikitso? (b) Kodi ndimotani mmene oyang’anira mumpingo Wachikristu angalefulidwire?
22 Tiyenera kuchipanga chitsimikizo cholimba chofuna kumalimbikitsana nthaŵi zonse pamene tsiku likuyandikira. Limbikitsani ena ndichitsanzo chanu chokhulupirika ndi mawu otonthoza. Tsanzirani Yehova ndi Ambuye Yesu Kristu m’zimenezi. Musazisiire akulu ampingo okha kukhala magwero a chilimbikitso. Eya, akulu nawonso amafunikira chilimbikitso. Iwo ali ndi zifooko ndi zophophonya mofanana ndi nkhosa zina zonse, ndipo afunikira kulaka mavuto ofananawo m’kupezera mabanja awo zofunika m’dziko lowolali. Kuwonjezera pazimenezo, ali ndi chimene Paulo analongosola kukhala nkhaŵa kaamba ka mpingo. (2 Akorinto 11:28, 29) Ntchito yawo njolimba—amafunikira chilimbikitso.
23 Inuyo mungalimbikitse okhala m’maudindo auyang’aniro mumpingo Wachikristu mwakugwirizana nawo. Pamenepo mudzakhala mukutsatira uphungu wa Ahebri 13:17 wakuti: ‘Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.’
24. M’tsiku lino la kulefuka, kodi tiyenera kumachita chiyani, ndipo chifukwa ninji?
24 Tikukhala m’tsiku la kulefuka. Mitima ya anthu ikukomokadi ndi mantha ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza padziko lapansi lokhalidwa ndi anthu, monga momwe Yesu ananeneratu. (Luka 21:25, 26) Pokhala ndi mavuto ambiri choncho amene amapsinja ndi kuziziritsa mmawondo, ‘limbikitsanani ndipo koposatu, monga momwe muwona tsiku likuyandikira.’ Tsatirani uphungu wabwino wa mtumwi Paulo pa 1 Atesalonika 5:11 wakuti: ‘Chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.’
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kumalimbikitsana, koposadi ndikale lonse?
◻ Kodi ndimotani mmene kudziŵa dzina laumulungu kwakhalira kolimbikitsa kwa anthu a Yehova?
◻ Kodi ndi m’njira ziti zimene tingalimbikitsirane paumwini?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupewa kukhala ndi phande m’ntchito ya Mdyerekezi yolefula abale athu?
[Chithunzi patsamba 17]
Akulu amatsogolera m’kulimbikitsa nkhosa m’mipingo yawo