Mutu 28
Kulimbana ndi Zilombo Ziwiri Zoopsa
Masomphenya 8—Chivumbulutso 13:1-18
Nkhani yake: Chilombo cha mitu 7, chilombo cha nyanga ziwiri ndiponso chifaniziro cha chilombo
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira nthawi ya Nimurodi mpaka pa chisautso chachikulu
1, 2. (a) Kodi Yohane ananena chiyani za chinjoka chija? (b) Pofotokoza mophiphiritsa, kodi Yohane anati chiyani za gulu looneka limene chinjoka chikugwiritsa ntchito?
CHINJOKA chachikulu chija chinaponyedwa kudziko lapansi. Pophunzira buku la Chivumbulutso, taona kuti Njoka, yomwe ndi Satana, ndiponso ziwanda zake sizidzaloledwanso kubwerera kumwamba. Komatu sitinamalize kuphunzira za njoka imeneyi, “iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Nkhaniyi ifotokoza mwatsatanetsatane njira imene Satana akugwiritsa ntchito polimbana ndi ‘mkazi uja ndi mbewu yake.’ (Chivumbulutso 12:9, 17) Ponena za chinjokacho, Yohane anati: “Ndiyeno chinjokacho chinangoima pamchenga wa m’mbali mwa nyanja.” (Chivumbulutso 13:1a) Tsopano tiyeni tione njira zimene chinjokachi chimagwiritsira ntchito pokwaniritsa zolinga zake.
2 Panopa Satana ndi ziwanda zake sakusokonezanso kumwamba koyera. Mizimu yoipayi inathamangitsidwa kumwambako n’kuponyedwa kudziko lapansi kumene singathenso kuchokako. Sitikukayikira kuti zimenezi n’zomwe zachititsa kuti masiku ano anthu ambiri azichita zinthu zamizimu. Njoka yochenjerayi ikuyendetsabe gulu lake lauzimu lomwe ndi loipa kwambiri. Koma kodi ikugwiritsanso ntchito gulu looneka pofuna kusocheretsa anthu? Yohane akutiuza kuti: “Kenako ndinaona chilombo chikutuluka m’nyanja. Chinali ndi nyanga 10 ndi mitu 7. Kunyanga yake iliyonse kunali chisoti chachifumu. Koma pamitu yake panali mayina onyoza Mulungu. Chilombo chimene ndinaonacho chinali ngati nyalugwe, koma mapazi ake anali ngati a chimbalangondo, ndipo pakamwa pake panali ngati pa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chilombocho mphamvu yake, mpando wake wachifumu, komanso ulamuliro wake waukulu.”—Chivumbulutso 13:1b, 2.
3. (a) Kodi mneneri Danieli anaona zilombo ziti zoopsa m’masomphenya? (b) Kodi zilombo zikuluzikulu zotchulidwa pa Danieli 7 zikuimira chiyani?
3 Kodi chilombo chodabwitsachi n’chiyani? Baibulo likuyankha funso limeneli. Ufumu wa Babulo usanawonongedwe mu 539 B.C.E., mneneri wachiyuda Danieli anaona masomphenya okhudza zilombo zoopsa. Pa Danieli 7:2-8 iye anafotokoza zilombo zinayi zimene zinkatuluka m’nyanja. Chilombo choyamba chinali chofanana ndi mkango, chachiwiri chinali chofanana ndi chimbalangondo, ndipo chachitatu chinali chofanana ndi kambuku, kapena kuti nyalugwe. Iye anapitiriza kufotokoza kuti: ‘Kenako ndinaonanso chilombo chachinayi, choopsa kwambiri ndiponso chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri ndipo chinali ndi nyanga 10.’ N’zochititsa chidwi kuti cha mu 96 C.E., Yohane anaona chilombo chofanana ndi zilombo zimenezi. Chilombo chimene anaonacho chinali ndi maonekedwe ofanana ndi mkango, chimbalangondo ndi kambuku ndipo chinali ndi nyanga 10. Koma kodi zilombo zikuluzikulu zimene Danieli anaonazi zikuimira chiyani? Iye akutiuza kuti: ‘Zilombo zikuluzikulu zimenezi zikuimira mafumu anayi amene adzauka padziko lapansi.’ (Danieli 7:17) N’zoonadi, zilombo zimenezi zikuimira “mafumu,” kapena kuti maulamuliro andale padziko lapansili.
4. (a) Kodi nkhosa yamphongo ndi mbuzi yamphongo zotchulidwa mu Danieli 8 zikuimira chiyani? (b) Kodi zinatanthauza chiyani pamene nyanga yaikulu ya mbuzi yamphongo ija inathyoledwa, pamalo pakepo n’kumera nyanga zina zinayi?
4 M’masomphenya ena, Danieli anaona nkhosa yamphongo yanyanga ziwiri imene inamenyedwa n’kugwetsedwa pansi ndi mbuzi yamphongo imene inali ndi nyanga yaikulu. Mngelo Gabirieli anauza Danieli tanthauzo la zimenezi. Iye anati: “Nkhosa yamphongo . . . ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya. Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi.” Popitiriza kufotokoza, Gabirieli analosera kuti nyanga yaikulu ya mbuziyo idzathyoledwa ndipo pamalo pake padzamera nyanga zina zinayi. Patapita zaka zoposa 200, zimenezi zinachitikadi pamene Alekizanda Wamkulu anamwalira. Ufumu wakewo unagawanika n’kukhala maufumu anayi omwe ankalamuliridwa ndi akuluakulu anayi a asilikali ake.—Danieli 8:3-8, 20-25.a
5. (a) Kodi munthu akamva mawu achigiriki amene anawamasulira kuti chilombo angaganize chiyani? (b) Kodi chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1, 2, komanso mitu yake 7, zikuimira chiyani?
5 Apa n’zoonekeratu kuti Yehova, yemwe ndi Mlembi Wamkulu wa Baibulo louziridwali, amaona kuti maulamuliro andale apadziko lapansi ali ngati zilombo. Kodi amawaona kuti iwo ali ngati zilombo zotani? Katswiri wina wa nkhani za m’Baibulo ananena kuti chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1, 2 “n’choopsa” kwambiri. Kenako ananena kuti: “Tikuvomereza kuti zonse zimene munthu amaganiza akamva mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘chilombo,’ n’zolondola. Munthu angaganize za chilombo chankhanza, chowononga, choopsa, cholusa ndi zina zotero.”b Izi zikugwirizanadi ndi mmene olamulira andale amene m’manja mwawo muli magazi, akuponderezera anthu. Iwo amachita zinthu zoipazi chifukwa akutsogoleredwa ndi Satana. Ndipo mitu 7 ya chilombo chija ikuimira maulamuliro 7 amphamvu kwambiri padziko lonse. Zochitika zambiri zolembedwa m’Baibulo zinachitika pa nthawi ya maulamuliro 6 mwa maulamuliro amenewa, omwe analamulira mpaka kudzafika m’nthawi ya Yohane. Maulamuliro amenewa anali Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi, ndiponso Roma. Ulosi unasonyeza kuti ulamuliro wa 7 udzabwera m’tsogolo.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 17:9, 10.
6. (a) Kodi mitu 7 ya chilombo chija yatsogolera pochita chiyani? (b) Kodi Yehova anagwiritsira ntchito bwanji ufumu wa Roma popereka chiweruzo chake kwa Ayuda, ndipo Akhristu a ku Yerusalemu zinawayendera bwanji?
6 N’zoona kuti kuwonjezera pa maulamuliro 7 amenewa, panalinso maulamuliro ena amphamvu kwambiri padziko lonse. Izi zikugwirizana ndi mfundo yakuti chilombo chimene Yohane anaona chinali ndi thupi komanso mitu 7 ndi nyanga 10. Koma mitu 7 ikuimira maulamuliro 7 amphamvu kwambiri, amene atsogolera pozunza anthu a Mulungu pa nthawi ya ulamuliro wawo. Mwachitsanzo, mu 33 C.E., pamene ulamuliro wa Roma unali wamphamvu kwambiri padziko lonse, Satana anagwiritsira ntchito mutu wa chilombo umenewu popha Mwana wa Mulungu. Pa nthawiyi, Mulungu sankaonanso Ayuda osakhulupirika ngati anthu ake apadera ndipo kenako mu 70 C.E., anagwiritsa ntchito Aroma popereka chiweruzo chake ku mtundu umenewu. Koma n’zosangalatsa kuti Isiraeli weniweni wa Mulungu, yemwe ndi mpingo wa Akhristu odzozedwa, anali atachenjezedwa, ndipo Akhristu amene anali mu Yerusalemu ndi mu Yudeya anathawira kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano.—Mateyu 24:15, 16; Agalatiya 6:16.
7. (a) Kodi n’chiyani chimene chinachitika kumayambiriro kwa mapeto a nthawi yathu ino, pamene tsiku la Ambuye linayamba? (b) Kodi n’chiyani chinakhala mutu wa 7 wa chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1, 2?
7 Koma chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, Akhristu ambiri mumpingo woyambirirawo anasiya choonadi, ndipo tirigu weniweni, kapena kuti Akhristu oona, omwe ndi “ana a ufumu,” anasokonezedwa kwambiri ndi namsongole, yemwe ndi “ana a woipayo.” Koma kumayambiriro kwa mapeto a nthawi yathu ino, Akhristu odzozedwa anaonekeranso monga gulu logwirizana. Baibulo linaneneratu kuti m’tsiku la Ambuye, anthu olungama “adzawala kwambiri ngati dzuwa.” Choncho mpingo wachikhristu unakonzedwanso kuti ugwire ntchito yapadera. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Pa nthawiyi n’kuti Ufumu wa Roma utatha, ndipo Ufumu Waukulu wa Britain, limodzi ndi dziko lamphamvu la United States, ndi amene ankalamulira dziko lonse. Ufumu wamphamvu kwambiri padziko lonse umenewu, wopangidwa ndi mayiko awiriwa, ndi umene unakhala mutu wa 7 wa chilombo chija.
8. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuona ngati chipongwe kuti Mulungu amagwiritsira ntchito chilombo monga chizindikiro cha ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse, wa Britain ndi United States?
8 Kodi si chipongwe kuyerekezera olamulira a ndale ndi chilombo? Zimenezi n’zimene anthu ena odana ndi Mboni za Yehova ankanena pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Iwo ankatsutsa zimene anthu a Mboni ankafalitsa pa nkhani imeneyi, ndipo ankawaimba milandu m’makhoti osiyanasiyana padziko lonse, chifukwa chokana kulowerera nawo nkhondo komanso ndale. A Mboniwo ankaimbidwa milandu monga gulu komanso aliyense payekha. Koma taganizirani kaye mofatsa. Kodi si paja mayiko ena amagwiritsira ntchito zilombo kapena zinyama zina monga zizindikiro za mayiko awo? Mwachitsanzo, dziko la Britain limagwiritsira ntchito mkango monga chizindikiro cha dzikolo, pamene dziko la United States limagwiritsira ntchito chiwombankhanga, ndipo la China limagwiritsira ntchito chinjoka. Ndiye n’chifukwa chiyani wina angadandaule poona kuti Mulungu, amene ndiye Mlembi Wamkulu wa Baibulo Lopatulika, nayenso amagwiritsira ntchito zilombo monga zizindikiro za maulamuliro amphamvu kwambiri a padziko lonse?
9. (a) N’chifukwa chiyani munthu sayenera kukwiya ndi zimene Baibulo limanena zoti Satana ndi amene akupereka mphamvu kwa chilombochi? (b) Kodi Satana akufotokozedwa bwanji m’Baibulo, ndipo akuchititsa bwanji maboma kuyendera mfundo zake?
9 Ndipo n’chifukwa chiyani munthu angakwiye ndi zimene Baibulo limanena, zoti Satana ndi amene akupereka mphamvu kwa chilombochi? Mfundo imeneyi ikuchokera kwa Mulungu, ndipo kwa iye ‘mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko, ndiponso ili ngati fumbi.’ Zingakhale bwino ngati mitundu ya anthuyi itachita zinthu zoyenera kuti Mulungu aziikonda m’malo mokwiya ndi mmene Mawu ake aulosi akuifotokozera. (Yesaya 40:15, 17; Salimo 2:10-12) Satana si munthu wongoyerekezera amene ena amakhulupirira kuti amazunza mizimu ya anthu omwalira kumalo amene kuli moto wosazima, chifukwa kulibe malo oterowo. Koma Malemba amanena kuti Satana “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” Iye ndi tate wachinyengo amene amatsogolera kwambiri zochita za anthu a ndale.—2 Akorinto 11:3, 14, 15; Aefeso 6:11-18.
10. (a) Kodi mfundo yakuti nyanga 10 zija zinali ndi chisoti chachifumu kunyanga iliyonse ikutanthauza chiyani? (b) Kodi nyanga 10 ndi zisoti zachifumu 10 zikuimira chiyani?
10 Chilombochi chinali ndi nyanga 10 pamitu yake 7. Mwina mitu inayi inali ndi nyanga imodziimodzi ndipo mitu itatu inali ndi nyanga ziwiriziwiri. Komanso kunyanga zimenezi kunali zisoti 10 zachifumu. Buku la Danieli likutchulanso zilombo zochititsa mantha kwambiri, ndipo chiwerengero cha nyanga za zilombozi ndi chenicheni, osati chophiphiritsa. Mwachitsanzo, nyanga ziwiri za nkhosa yamphongo zinkaimira ufumu wamphamvu kwambiri padziko lonse umene unali mgwirizano wa Mediya ndi Perisiya. Ndipo nyanga zinayi za mbuzi ija zinkaimira maufumu anayi amene anapangidwa pamene ufumu wa Girisi, womwe wolamulira wake anali Alekizanda Wamkulu, unagawanika. (Danieli 8:3, 8, 20-22) Koma tikanena za chilombo chimene Yohane anaona, zikuoneka kuti chiwerengero cha nyanga zake 10 n’chophiphiritsa. (Yerekezerani ndi Danieli 7:24; Chivumbulutso 17:12) Nyanga zimenezi zikuimira kuti maboma onse amene akupanga gulu landale la Satana ndi okwanira bwino. Nyanga zonsezi n’zankhanza komanso zaukali. Koma monga mmene mitu 7 ija ikusonyezera, maulamuliro onse amphamvu padziko lonse sakulamulira pa nthawi yofanana, koma uliwonse ukulamulira pa nthawi yakeyake. Komanso zisoti zachifumu zokwanira 10 zikusonyeza kuti maboma ena onse padzikoli adzakhala akulamulira pa nthawi yomweyomweyo imene ulamuliro wamphamvu padziko lonse udzakhalenso ukulamulira.
11. Kodi mfundo yakuti “pamitu [ya chilombo chija] panali mayina onyoza Mulungu,” ikusonyeza chiyani?
11 “Pamitu [ya chilombo chija] panali mayina onyoza Mulungu,” chifukwa chimanena zinthu zodzitamandira zimene zimasonyeza kuti sichilemekeza Yehova Mulungu ndi Khristu Yesu ngakhale pang’ono. Chilombochi chagwiritsira ntchito mwachinyengo mayina a Mulungu ndi Khristu pofuna kupititsa patsogolo zolinga zake zandale. Komanso chimagwirizana kwambiri ndi zipembedzo zonyenga ndipo chalola kuti atsogoleri a zipembedzozo azikhala ndi maudindo m’ndale zake. Mwachitsanzo, m’nyumba ya malamulo ya ku England mulinso mabishopu. Ku France ndi ku Italy, makadinala achikatolika ali ndi maudindo akuluakulu a ndale, ndipo posachedwapa, ansembe apatsidwa maudindo a ndale kumayiko a ku Latin America. Komanso maboma osiyanasiyana amalemba mawu achipembedzo pandalama zawo zapepala, monga akuti, “TIMADALIRA MULUNGU,” ndipo pandalama zawo zachitsulo amalembapo mawu osonyeza kuti atsogoleri awo anachita kusankhidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, iwo amalemba kuti atsogoleriwa anasankhidwa “mwa chisomo cha Mulungu.” Koma onsewa ndi mawu onyoza Mulungu, chifukwa angachititse anthu kuganiza kuti Mulungu ndi amene akuyendetsa ndale za dzikoli, zomwe zimachititsa anthu kukonda kwambiri dziko lawo ndiponso kuchita zinthu zambiri zoipa.
12. (a) Kodi mfundo yakuti chilombo chija chikutuluka “m’nyanja” ikutanthauza chiyani, ndipo chinayamba liti kutuluka m’nyanjamo? (b) Kodi mfundo yakuti chinjoka chinapatsa chilombo chophiphiritsacho mphamvu zake zazikulu, ikutanthauza chiyani?
12 Chilombochi chikutuluka “m’nyanja.” Chimenechi ndi chizindikiro choyenerera cha mitundu ya anthu omwe akuwinduka ngati mafunde a m’nyanja, ndipo maboma olamulira amapangidwa kuchokera mwa anthu amenewa. (Yesaya 17:12, 13) Chilombo chimenechi chinayamba kutuluka m’nyanja, yomwe ikuimira anthu owinduka ngati mafunde, kale kwambiri m’nthawi ya Nimurodi (cha m’ma 2000 B.C.E.). Pa nthawi imeneyi, anthu amene anakhalapo Chigumula cha Nowa chitachitika, anayamba kuchita zinthu zotsutsana ndi Yehova. (Genesis 10:8-12; 11:1-9) Koma m’tsiku la Ambuye m’pamene mutu womaliza pa mitu 7 ya chilombo chija waonekera bwino kwambiri. Tikuonanso kuti “chinjoka chija chinapatsa chilombocho mphamvu yake, mpando wake wachifumu, komanso ulamuliro wake waukulu.” (Yerekezerani ndi Luka 4:6.) Chilombo chimenechi chikuimira maulamuliro a ndale amene Satana amayambitsa pakati pa anthu. Chotero Satana ndiyedi “wolamulira wa dzikoli.”—Yohane 12:31.
Bala Limene Chilombocho Chikanafa Nalo
13. (a) Kodi chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, chilombo chija chinaona zotani? (b) N’chifukwa chiyani chilombo chonsecho chinavutika ngakhale kuti mutu umodzi wokha ndi umene unavulazidwa?
13 Chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, chilombo chija chinaona zakuda. Yohane analemba kuti: “Ndiyeno ndinaona mutu wake umodzi ukuoneka kuti wavulazidwa kwambiri. Koma ngakhale kuti balalo linali loti chikanafa nalo, linapola. Ndipo dziko lonse lapansi linatsatira chilombocho pochita nacho chidwi.” (Chivumbulutso 13:3) Vesili likunena kuti mutu umodzi wa chilombocho ndi umene unavulazidwa kwambiri, koma vesi 12 likusonyeza kuti chilombo chonsecho chinavutika. Kodi n’chifukwa chiyani zinali choncho? Mitu ya chilombochi sikuti yonse inkalamulira pa nthawi imodzi. Mutu uliwonse unali ndi nthawi yake yolamulira ndi kupondereza anthu, makamaka atumiki a Mulungu. (Chivumbulutso 17:10) Chotero pamene tsiku la Ambuye linkayamba, panali mutu umodzi wokha, wa 7, umene unkalamulira, ndipo unali ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse. Choncho mutu umenewo utavulazidwa, chilombo chonsecho chinavutika kwambiri.
14. Kodi chilombo chinavulazidwa liti ndi lupanga, ndipo mkulu wina wa asilikali anafotokoza bwanji mmene zimenezo zinakhudzira chilombo cha Satanachi?
14 Kodi bala limene chilombocho chikanafa nalo linali chiyani? M’vesi lina kutsogoloku bala limeneli likutchedwa bala la lupanga, ndipo lupanga ndi chizindikiro cha nkhondo. Chilombochi chinavulazidwa ndi lupanga limeneli kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye. Choncho balali liyenera kuti likukhudzana ndi nkhondo yoyamba yapadziko lonse, imene inawononga ndi kusowetsa mtendere kwambiri chilombo cha ndale chotsogoleredwa ndi Satana chimenechi. (Chivumbulutso 6:4, 8; 13:14) Munthu wina wolemba mabuku, dzina lake Maurice Genevoix, amenenso anali mkulu wa asilikali pa nthawi ya nkhondo yoyamba padziko lonse, ananena kuti: “Aliyense amavomereza kuti m’mbiri yonse ya anthu, tsiku la August 2, 1914 ndi limodzi mwa masiku osaiwalika. Pa tsikuli ku Ulaya kunayambika nkhondo ndipo posapita nthawi, pafupifupi mitundu yonse ya anthu inapezeka kuti ikumenya nawo nkhondo yoopsayi. Zinthu zonse zimene anthu ankadalira zinagwedezeka, kaya ndi zigamulo, mapangano kapena malamulo okhudza makhalidwe. Tsiku lililonse pankakhala zinthu zimene anthu ankayamba kuzikayikira. Ndipo nkhondoyi inayambitsa mavuto odetsa nkhawa kuposa mmene anthu ankayembekezera. Nkhondoyi inakhudza mayiko ambiri, inabweretsa chisokonezo, ndipo inali yowononga kwambiri, moti mpaka lero tikuvutikabe chifukwa cha zotsatirapo zake.”—Maurice Genevoix anali wa m’bungwe la Académie Française, ndipo mawu akewa akupezeka m’buku lotchedwa Promise of Greatness (1968).
15. Kodi chinachitika n’chiyani kuti mutu wa 7 ukhale ndi bala limene chilombocho chikanatha kufa nalo?
15 Nkhondo imeneyi inabweretsa mavuto aakulu ku mutu wa 7 wa chilombocho, umene unali wamphamvu kwambiri. Anyamata ambirimbiri a ku Britain komanso a m’mayiko ena a ku Ulaya anafa pa nkhondoyi. Mwachitsanzo, pa nkhondo imodzi yokha imene inkachitikira kumtsinje wa Somme mu 1916, panali anthu oposa 1,000,000 amene anafa kapena kuvulazidwa. Pa anthu amenewa, 420,000 anali a ku Britain, 194,000 anali a ku France ndipo 440,000 anali a ku Germany. Chuma cha ku Britain komanso cha m’mayiko ena onse ku Ulaya chinalowa pansi kwambiri. Zimenezi zinabweretsa mavuto oopsa mu Ufumu Waukulu wa Britain ndi mayiko amene ankalamuliridwa ndi ufumuwo ndipo mavutowo sanatheretu mpaka pano. Zoonadi, nkhondo imeneyi, imene inkachitika pakati pa mayiko akuluakulu okwana 28, inabweretsa mavuto aakulu padziko lonse, zimene zinali ngati bala loti akanatha kufa nalo. Pa August 4, 1979, patangopita zaka 65 zokha kuchokera pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayambika, magazini ina ya ku London, m’dziko la England, inati: “Mu 1914 mgwirizano umene unalipo padzikoli unatha, ndipo sunabwererenso.”—The Economist.
16. Pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, kodi dziko la United States linasonyeza bwanji kuti ndi limodzi mwa mayiko awiri amene akupanga ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse?
16 Komanso nkhondo imeneyi, yomwe pa nthawiyo inkadziwika kuti Nkhondo Yaikulu, inachititsa kuti dziko la United States ligwirizane kwambiri ndi dziko la Britain ndipo mayikowa anapanga ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse. M’zaka zoyambirira za nkhondoyi, anthu a m’dziko la United States ankakana kuti dziko lawo lilowerere nkhondoyo. Koma katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Esmé Wingfield-Stratford, analemba kuti: “Nkhani inali yakuti, kodi pa nthawi yovutayi, mayiko a Britain ndi United States amvana chimodzi pozindikira kuti onse amagwirizana pa mfundo zina zikuluzikulu ndiponso kuti onse ali ndi udindo umodzi?” Zimene zinachitika zikusonyeza kuti iwo anamvanadi chimodzi. Mu 1917 dziko la United States linatumiza chuma komanso asilikali kuti akathandize dziko la Britain ndi mayiko amene ankagwirizana nalo, omwe zinthu sizinkawayendera bwino pa nkhondoyo. Choncho mutu wa 7 wa chilombo chija, womwe ukuimira ulamuliro wa Britain ndi United States, unapambana pa nkhondoyo.
17. Kodi chinachitikira dziko la Satanali n’chiyani nkhondo itatha?
17 Nkhondo itatha, zinthu zinasintha kwambiri padziko lonse. Dziko la Satanali, ngakhale kuti linavulazidwa ndi bala limene chilombo chija chikanatha kufa nalo, linatsitsimuka n’kukhalanso lamphamvu kwambiri kuposa kale. Zimenezi zinachititsa kuti anthu azichita chidwi ndi dzikoli chifukwa chakuti linatha kuchira bwinobwino.
18. Kodi anthu ‘atsatira bwanji chilombocho pochita nacho chidwi’?
18 Katswiri winanso wa mbiri yakale, dzina lake Charles L. Mee, Jr., analemba kuti: “Zinali zofunika kuti dongosolo lakale lochitira zinthu lithe [chifukwa cha nkhondo yoyamba ya padziko lonse] popeza zimenezi zinathandizira kuti mayiko ayambe kudzilamulira okha. Zinathandiziranso kuti mayiko ndiponso magulu ena a anthu achoke mu ukapolo, kuti anthu apeze ufulu wowonjezereka ndiponso kuti akhale odziimira paokha.” Mutu wa 7 wa chilombo chija, womwe tsopano unali utachira, ndi umene unkatsogolera zinthu zonse zokhudzana ndi chitukuko nkhondo itatha, ndipo dziko la United States linayamba kukhala lamphamvu kwambiri pa mayiko awiri aja. Mayiko awiri amenewa, omwe akupanga ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse, ndi amene anatsogolera pokhazikitsa bungwe la League of Nations komanso la United Nations. Pofika chaka cha 2010, dziko la United States ndi limene linkatsogolera mayiko olemera potukula anthu kuti azikhala moyo wabwino, polimbana ndi matenda ndiponso popititsa patsogolo luso la zopangapanga. Komanso dzikoli linatumiza anthu 12 kumwezi. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ‘atsatira chilombocho pochita nacho chidwi.’
19. (a) Kodi anthu achita zotani kuwonjezera pa kuchita chidwi ndi chilombocho? (b) Kodi ndani amene akulamulira maufumu onse a dziko lapansi, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (c) Kodi Satana wapereka bwanji mphamvu kwa chilombo, ndipo zimenezi zakhudza bwanji anthu ambiri?
19 Anthu achita zambiri kuwonjezera pa kuchita chidwi ndi chilombocho. Yohane ananena kuti: “Iwo analambira chinjoka chija chifukwa chinapatsa chilombo ulamuliro. Ndipo analambira chilombocho ndi mawu awa: ‘Ndani ali ngati chilombo, ndipo ndani angamenyane nacho?’” (Chivumbulutso 13:4) Satana ananena kuti ali ndi ulamuliro pa maufumu onse a padziko lapansi. Iye ananena zimenezi pamene Yesu anali padzikoli. Yesu sanatsutse zimenezi, ndipo ananena kuti Satana ndi wolamulira wa dzikoli, moti anakana kulowerera ndale za pa nthawiyo. Patapita nthawi, Yohane analembera Akhristu oona, kuti: “Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu, koma dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19; Luka 4:5-8; Yohane 6:15; 14:30) Satana ndi amene amapereka mphamvu kwa chilombo chija, ndipo amachita zimenezi popereka mphamvu zolamulira ku dziko lililonse. Choncho m’malo mokonda Mulungu n’kukhala ogwirizana, anthu agawanika chifukwa chokonda kwambiri mtundu wawo, fuko lawo kapena dziko lawo. Izi zachititsa kuti anthu ambiri azilambira dziko lawo, lomwe ndi mbali ya chilombo chija. Chotero anthu akuchita chidwi ndi chilombo chonsecho komanso kuchilambira.
20. (a) Kodi anthu amalambira bwanji chilombo? (b) N’chifukwa chiyani Akhristu amene amalambira Yehova Mulungu salambira nawo chilombocho, ndipo amatsanzira ndani?
20 Kodi anthu amalambira bwanji chilombocho? Amachilambira pokonda kwambiri dziko lawo m’malo mokonda Mulungu. Ndipo anthu ambiri amanyadira kwambiri dziko lawo. Akhristu oona ndi nzika zabwino ndipo amalemekeza olamulira komanso zizindikiro za boma za m’dziko limene akukhala. Iwo amamvera malamulo ndipo amathandiza m’njira zina m’dera limene akukhala komanso amathandiza anthu anzawo. (Aroma 13:1-7; 1 Petulo 2:13-17) Koma iwo satengeka ndi maganizo akuti dziko lawo ndi lofunika kwambiri kuposa mayiko ena onse. Mfundo yakuti “ndimakonda dziko langa, kaya lizichita zabwino kapena zoipa” si yachikhristu. Choncho Akhristu amene amalambira Yehova Mulungu sangachite nawo zinthu zosonyeza kuti amakonda kwambiri dziko lawo, chifukwa kuchita zimenezi kungakhale ngati kulambira mbali ina ya chilombo chija. Komanso ngati atachita zimenezi ndiye kuti akulambira chinjoka chija, chimene chimapereka mphamvu kwa chilombocho. Iwo sangafunse monyadira kuti: “Ndani ali ngati chilombo?” M’malomwake iwo amasonyeza kuti Yehova yekha ndiye woyenera kulamulira ndipo amatsanzira Mikayeli, amene dzina lake limatanthauza kuti “Ndani Ali Ngati Mulungu?” Pa nthawi imene Mulungu anaikiratu, Mikayeli, yemwe ndi Khristu Yesu, adzamenya nkhondo ndi chilombo n’kuchigonjetsa ngati mmene anagonjetsera Satana n’kumuchotsa kumwamba.—Chivumbulutso 12:7-9; 19:11, 19-21.
Chilombocho Chinachita Nkhondo ndi Oyerawo
21. Kodi Yohane anafotokoza kuti Satana amagwiritsa ntchito bwanji chilombo chija pofuna kukwaniritsa zolinga zake?
21 Satana, yemwe ndi wochenjera kwambiri, amagwiritsa ntchito chilombo chija pofuna kukwaniritsa zolinga zake. Yohane anafotokoza kuti: “Chilombocho [cha mitu 7 chija] chinapatsidwa pakamwa polankhula zinthu zodzitukumula ndi zonyoza. Chinapatsidwanso mphamvu yochita ulamuliro kwa miyezi 42. Chilombocho chinatsegula pakamwa pake n’kumanyoza Mulungu, dzina lake ndi malo ake okhala, ndiponso amene akukhala kumwamba. Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyerawo ndi kuwagonjetsa. Chinapatsidwanso ulamuliro pa anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chinenero chilichonse ndi dziko lililonse. Ndipo onse okhala padziko lapansi adzachilambira. Anthu onsewa mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo, umene Mwanawankhosa amene anaphedwa, ndiye mwiniwake. Mpukutuwo unakonzedwa kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”—Chivumbulutso 13:5-8.
22. (a) Kodi miyezi 42 ikuimira nthawi iti? (b) Kodi Akhristu odzozedwa ‘anagonjetsedwa’ bwanji pa miyezi 42 imeneyi?
22 Zikuoneka kuti miyezi 42 yomwe yatchulidwa palembali n’chimodzimodzi ndi zaka zitatu ndi hafu zimene oyera anazunzidwa ndi nyanga ya chilombo china cha mu ulosi wa Danieli. (Danieli 7:23-25; onaninso Chivumbulutso 11:1-4.) Choncho kuyambira kumapeto kwa 1914 mpaka mu 1918, pamene mayiko amene anali pa nkhondo ankakhadzulana ngati zilombo, anthu a m’mayiko amenewo ankakakamizika kulambira chilombo. Iwo ankakakamizikanso kuchita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo, zimene zinali ngati chipembedzo, ngakhalenso kukhala okonzeka kufera dziko lawo. Zimenezi zinabweretsa mavuto aakulu kwa Akhristu ambiri odzozedwa, amene ankaona kuti ayenera kumvera kwambiri Yehova Mulungu ndi Mwana wake Khristu Yesu, kuposa wina aliyense. (Machitidwe 5:29) Mayesero awo anafika pachimake mu June 1918, pamene ‘anagonjetsedwa.’ Mwachitsanzo, m’dziko la United States, anthu amene ankatsogolera bungwe la Watch Tower Society ndi akuluakulu ena anatsekeredwa m’ndende pa milandu yongowanamizira, ndipo ntchito yolalikira imene abale awo achikhristu ankagwira inasokonezedwa kwambiri. Chilombochi chinapondereza ntchito ya Mulungu padziko lonse, popeza chili ndi ulamuliro “pa anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chinenero chilichonse ndi dziko lililonse.”
23. (a) Kodi ‘mpukutu wa moyo, umene Mwanawankhosa ndiye mwiniwake,’ n’chiyani, ndipo n’chiyani chimene chakhala chikuchitika kuyambira mu 1918? (b) Ngakhale kuti Satana ndi gulu lake anaoneka ngati apambana polimbana ndi “oyerawo,” n’chifukwa chiyani zimenezi zili zosathandiza?
23 Apa zinaoneka ngati Satana ndi gulu lake anapambana. Koma kupambana kumeneku sikunali kokhalitsa chifukwa m’gulu la Satana looneka ndi maso mulibe aliyense amene dzina lake linalembedwa “mumpukutu wa moyo, umene Mwanawankhosa . . . ndiye mwiniwake.” Mophiphiritsa, mumpukutu umenewu muli mayina a anthu amene akalamulire limodzi ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba. Mayina oyambirira analembedwa mumpukutu umenewu pa Pentekosite mu 33 C.E. Kwa zaka zambiri kuchokera pa nthawi imeneyo, mayina ambirimbiri akhala akulembedwa mumpukutuwu. Kuchokera mu 1918, anthu ena a 144,000 amene adzalamulire mu Ufumu wa Mulungu, akhala akudindidwa chidindo mpaka chiwerengero chawo chitakwanira. Posachedwapa, mayina awo onse adzalembedwa mumpukutu wa moyo, umene Mwanawankhosa ndiye mwiniwake, ndipo sadzafufutidwamo. Koma wotsutsa aliyense, amene amalambira chilombocho, dzina lake silidzalembedwa mumpukutuwu. Choncho ngakhale kuti otsutsawa anaoneka ngati apambana polimbana ndi “oyerawo,” kupambana kumeneko n’kosathandiza komanso n’kosakhalitsa.
24. Kodi Yohane anapempha anthu ozindikira kuti amvetsere mawu otani, ndipo mawuwo akutanthauza chiyani kwa anthu a Mulungu?
24 Tsopano Yohane anapempha anthu ozindikira kuti amvetsere mwatcheru kwambiri. Iye anati: “Aliyense amene ali ndi makutu amve.” Kenako anapitiriza kuti: “Ngati wina akuyenera kutengedwa ukapolo, adzapitadi ku ukapoloko. Ngati wina adzapha ndi lupanga, adzaphedwa ndi lupanga. Apa m’pamene oyera akufunika kupirira ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.” (Chivumbulutso 13:9, 10) Chaka cha 607 B.C.E. chitatsala pang’ono kufika, Yeremiya analemba mawu ofanana ndi amenewa posonyeza kuti chiweruzo cha Yehova pa mzinda wosakhulupirika wa Yerusalemu sichidzasintha. (Yeremiya 15:2; onaninso Yeremiya 43:11; Zekariya 11:9.) Komanso pa nthawi imene Yesu ankazunzidwa kwambiri, ananena momveka bwino kuti otsatira ake sayenera kugonja akamayesedwa. Iye anati: “Onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Mofanana ndi zimenezi, pa nthawi ino m’tsiku la Ambuye, anthu a Mulungu ayenera kutsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo. Anthu osalapa amene akulambira chilombo chija sadzapulumuka. Tonsefe tikufunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso kupirira kuti tidzapambane pozunzidwa ndiponso poyesedwa m’tsogolomu.—Aheberi 10:36-39; 11:6.
Chilombo cha Nyanga Ziwiri
25. (a) Kodi Yohane anafotokoza bwanji chilombo china chophiphiritsa chimene anachiona? (b) Kodi mfundo yakuti chilombo chatsopanochi chili ndi nyanga ziwiri komanso chikutuluka pansi pa dziko lapansi ikusonyeza chiyani?
25 Kenako panabweranso chilombo china. Yohane anati: “Kenako ndinaona chilombo china chikutuluka pansi pa dziko lapansi. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa, koma chinayamba kulankhula ngati chinjoka. Chilombocho chinalamulira ndi mphamvu zonse za chilombo choyambacho pamaso pa chilombo choyambacho. Chinachititsa dziko lapansi ndi okhalamo kulambira chilombo choyamba chija, chimene bala lake limene chinayenera kufa nalo, linapola. Chinachitanso zizindikiro zazikulu, moti chinapangitsa ngakhale moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuona.” (Chivumbulutso 13:11-13) Chilombo chimenechi chili ndi nyanga ziwiri, kusonyeza mgwirizano wa mayiko awiri pa ndale. Yohane anaona chilombocho chikutuluka pansi pa dziko lapansi, osati m’nyanja. Izi zikusonyeza kuti chikuchokera m’dziko la Satana limene linali kale ndi maulamuliro ake. Chilombo chimenechi chiyenera kuti chikuimira ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse, umene unalipo kale ndipo ukukula mphamvu m’tsiku la Ambuye.
26. (a) Kodi chilombo cha nyanga ziwiri chikuimira chiyani, ndipo chikugwirizana bwanji ndi chilombo choyamba chija? (b) Kodi nyanga ziwiri za chilombochi zinali ngati za mwana wa nkhosa m’njira yotani, ndipo chikamalankhula chikufanana bwanji ndi “chinjoka” chija? (c) Kodi anthu okonda kwambiri dziko lawo akulambira chiyani kwenikweni, ndipo kukonda kwambiri dziko kwayerekezeredwa ndi chiyani? (Onani mawu a m’munsi.)
26 Kodi ulamuliro umenewu ndi uti? Umenewu ndi ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse wa Britain ndi America, umenenso ukuimiridwa ndi mutu wa 7 wa chilombo choyamba chija. Koma pamene ukuimiridwa ndi chilombochi, ulamulirowu ukuchita zinthu zapadera zosiyana ndi poyamba paja. Popeza kuti chilombochi achitchula pachokha m’masomphenyawa, zikutithandiza kuona bwino mmene chikuchitira zinthu pachokha m’dzikoli. Chilombo chophiphiritsa cha nyanga ziwiri chimenechi chikuimira maulamuliro awiri andale omwe akulamulira pa nthawi imodzi m’mayiko osiyana, koma akuchita zinthu mogwirizana. Mfundo yakuti chili ndi nyanga ziwiri zomwe zinali ngati za “mwana wa nkhosa,” ikusonyeza kuti chimadzionetsa ngati chofatsa komanso chopanda nkhanza. Ikusonyezanso kuti chimadzionetsa ngati chimalamulira mokomera aliyense ndipo chimafuna kuti dziko lonse lizitsanzira ulamuliro wakewo. Koma chimalankhula ngati “chinjoka” chija. Izi zikutanthauza kuti chimakakamiza anthu komanso kuwaopseza kuti avomereze kalamuliridwe kake, ndipo ngati sakutero chimawachitira zankhanza. Chilombo chimenechi sichilimbikitsa anthu kuti azigonjera Ufumu wa Mulungu umene wolamulira wake ndi Mwanawankhosa wa Mulungu. M’malomwake, chimawalimbikitsa kuti azichita zofuna za Satana, chinjoka chachikulu chija. Chilombo cha nyanga ziwirichi chalimbikitsa kwambiri anthu kuti azikonda kwambiri dziko lawo ndiponso kuti azidana. Anthu akamachita zimenezi, amakhala akulambira chilombo choyamba chija.c
27. (a) Kodi mfundo yakuti chilombo cha nyanga ziwiricho chinachititsa kuti moto ugwe kuchokera kumwamba, ikusonyeza kuti chimadziona bwanji? (b) Kodi anthu ambiri amaona bwanji chilombo cha nyanga ziwiri cha masiku ano?
27 Chilombo cha nyanga ziwirichi chinachita zizindikiro zazikulu, moti chinachititsa kuti moto ugwe kuchokera kumwamba. (Yerekezerani ndi Mateyu 7:21-23.) Chizindikiro chamotochi chikutikumbutsa Eliya, mneneri wakale wa Mulungu amene analimbana ndi aneneri a Baala. Eliya anapempha Yehova kuti agwetse moto kuchokera kumwamba, ndipo zinachitikadi. Zimenezi zinali umboni wamphamvu wakuti iye ndi mneneri woona ndipo zinasonyeza kuti aneneri a Baala anali onyenga. (1 Mafumu 18:21-40) Mofanana ndi aneneri a Baala amenewo, chilombo cha nyanga ziwiricho chimaona kuti chili ndi zonse zochiyenereza kukhala mneneri. (Chivumbulutso 13:14, 15; 19:20) Ndipotu chilombo chimenechi chimanena kuti pa nkhondo ziwiri za padziko lonse, chinafafaniza adani ake amene chinkawaona kuti ndi oipa. Komanso chimanena kuti chinagonjetsa ulamuliro wa chikomyunizimu, womwe chinkati unali wosaopa Mulungu. Anthu ambiri amaona kuti chilombo cha nyanga ziwiri cha masiku anochi chikuteteza ufulu wa anthu komanso chimabweretsa zinthu zambiri zabwino.
Chifaniziro cha Chilombo
28. Kodi Yohane anasonyeza bwanji kuti chilombo cha nyanga ziwiricho chikuchitanso zoipa, mosiyana ndi tanthauzo la nyanga zake zokhala ngati za mwana wa nkhosa zija?
28 Kodi chilombo cha nyanga ziwiricho chikuchita zinthu zabwino zogwirizana ndi tanthauzo la nyanga zake zokhala ngati za mwana wa nkhosazo? Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Chilombocho chinasocheretsa okhala padziko lapansi chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Ndipo chinauza okhala padziko lapansi kupanga chifaniziro cha chilombo chimene chinali ndi bala la lupanga chija, koma chimene chinapulumuka. Ndipo chinaloledwa kupereka mpweya ku chifaniziro cha chilombo chija, kuti chifaniziro cha chilombocho chithe kulankhula, ndi kuchititsa kuti onse amene mwa njira iliyonse salambira chifaniziro cha chilombocho, aphedwe.”—Chivumbulutso 13:14, 15.
29. (a) Kodi cholinga cha chifaniziro cha chilombo chija n’chiyani, ndipo chinapangidwa liti? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti chifaniziro cha chilombocho si chopanda moyo?
29 Kodi “chifaniziro cha chilombo” chimenechi n’chiyani ndipo cholinga chake n’chiyani? Cholinga chake ndi kulimbikitsa anthu kuti azilambira chilombo cha mitu 7 chija chimene chifanizirochi chikuimira, kuti anthuwo adziwe kuti chilombocho chidakalipobe. Chifaniziro chimenechi chinapangidwa pamene bala la lupanga la chilombo cha mitu 7 chija linapola, kutanthauza kuti chinapangidwa nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha. Sikuti chifaniziro chimenechi n’chopanda moyo ngati chifaniziro chimene Nebukadinezara anaimika m’chigwa cha Dura. (Danieli 3:1) Chilombo cha nyanga ziwiri chija chinauzira mpweya chifanizirocho kuti chikhale ndi moyo ndi kuchita zinthu zosiyanasiyana m’dzikoli.
30, 31. (a) Kodi zomwe zakhala zikuchitika m’mbiri ya anthu zikusonyeza kuti chifaniziro chimenechi n’chiyani? (b) Kodi pali aliyense amene waphedwa chifukwa chokana kulambira chifanizirochi? Fotokozani.
30 Zimene zachitika m’mbiri ya anthu zasonyeza kuti chifaniziro chimenechi ndi bungwe limene linakhazikitsidwa ndi kuthandizidwa ndi dziko la Britain komanso United States, ndipo poyamba linkadziwika ndi dzina lakuti League of Nations. Kutsogoloku mu Chivumbulutso chaputala 17, tiona chilombo china choima pachokha, chofiira kwambiri komanso chamoyo, chimene chikuimiranso bungwe lomweli. Bungwe la padziko lonse limeneli ‘limalankhula,’ kutanthauza kuti limanena modzitama kuti ndi bungwe lokhali limene lingabweretse bata ndi mtendere kwa anthu. Koma kwenikweni bungwe limeneli langokhala chida chimene mayiko akugwiritsa ntchito pokangana ndi kunyozana. Bungweli limaopseza mayiko kapena anthu amene sakugonjera ulamuliro wake, kuti lisiya kuwathandiza kapena liziwasala, komwe kuli ngati kuwapha. Ndipotu bungwe la League of Nations linachotsa m’bungweli mayiko amene sankatsatira mfundo zake. Chisautso chachikulu chikadzangoyamba, “nyanga” za chifaniziro cha chilombochi, zomwe zili ndi magulu amphamvu a asilikali, zidzagwira ntchito yowononga kwambiri.—Chivumbulutso 7:14; 17:8, 16.
31 Kuchokera pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, chifaniziro cha chilombochi, chomwe panopa chikudziwika kuti United Nations, chapha kale anthu ambirimbiri. Mwachitsanzo, mu 1950 asilikali a United Nations analowerera nkhondo ya pakati pa dziko la North Korea ndi la South Korea. Asilikali a bungweli mogwirizana ndi asilikali a ku South Korea, anapha anthu pafupifupi 1,420,000 a ku North Korea ndi ku China. Komanso kuyambira mu 1960 mpaka mu 1964, asilikali a United Nations ankamenya nawo nkhondo ya ku Democratic Republic of Congo. Ndipo atsogoleri otchuka m’dzikoli, kuphatikizapo Papa Paulo wa 6 ndi Papa Yohane Paulo Wachiwiri, akhala akunena motsimikiza kuti chifaniziro chimenechi n’chokhacho chimene anthu angadalire kuti chidzabweretsa mtendere. Iwo amanena motsimikiza kuti anthu akadzalephera kutumikira chifanizirochi ndiye kuti mtundu wa anthu udzathera pamenepo. Choncho mophiphiritsa iwo akuchititsa kuti anthu onse amene akana kutsatira zofuna za chilombocho kapena kuchilambira aziphedwa.—Deuteronomo 5:8, 9.
Chizindikiro cha Chilombo
32. Kodi Yohane anafotokoza kuti Satana akugwiritsa ntchito bwanji magulu andale, omwe ndi mbali yooneka ndi maso ya gulu lake, pobweretsa mavuto aakulu kwa anthu amene akupanga mbewu ya mkazi wa Mulungu amene adakali padziko lapansi?
32 Tsopano Yohane anaona mmene Satana akugwiritsira ntchito magulu andale, omwe ndi mbali yooneka ndi maso ya gulu lake, pobweretsa mavuto aakulu kwa anthu amene akupanga mbewu ya mkazi wa Mulungu, omwe adakali padziko lapansi. (Genesis 3:15) Iye anapitiriza kufotokoza “chilombo” chija kuti: “Chilombocho chinakakamiza anthu onse, olemekezeka ndi onyozeka, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti apatsidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo. Chinachita izi kuti aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho, dzina la chilombo, kapena nambala ya dzina lake. Apa ndiye pofunika nzeru: Amene ali ndi nzeru awerengere nambala ya chilombocho, pakuti ndi nambala ya munthu. Nambala yake ndi 666.”—Chivumbulutso 13:16-18.
33. (a) Kodi dzina la chilombochi n’chiyani? (b) Kodi nambala ya 6 imakhudzana kwambiri ndi chiyani? Fotokozani.
33 Chilombochi chili ndi dzina, ndipo dzina limeneli ndi nambala ya 666. Nambala ya 6 imakhudzana kwambiri ndi adani a Yehova. Mwachitsanzo, Mfilisiti wina amene anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai, anali “wa msinkhu waukulu modabwitsa,” ndipo “anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse.” (1 Mbiri 20:6) Nayenso Mfumu Nebukadinezara anaimika fano lagolide lomwe m’lifupi mwake linali mikono 6, ndipo linali lalitali mikono 60. Iye anachita zimenezi kuti akuluakulu onse a boma lake azilambira fanoli mogwirizana. Atumiki a Mulungu atakana kulambira fano lagolideli, mfumuyo inalamula kuti atumikiwo aponyedwe m’ng’anjo yamoto. (Danieli 3:1-23) Nambala ya 6 ndi yosakwana 7, amene amaimira chinthu chokwanira pamaso pa Mulungu. Choncho ma 6 atatu akuimira kupanda ungwiro kodetsa nkhawa.
34. (a) Kodi mfundo yakuti nambala ya chilombochi ndi “nambala ya munthu,” ikutanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani 666 lili dzina loyenerera la ndale za dziko la Satanali?
34 Dzina limasiyanitsa munthu ndi anthu ena. Kodi nambala imeneyi ikusiyanitsa bwanji chilombo chimenechi ndi zilombo zina? Yohane ananena kuti nambalayi ndi “nambala ya munthu,” osati ya cholengedwa chauzimu. Choncho dzinali likutsimikizira kuti chilombochi ndi cha padziko lapansi, ndipo chikuimira maboma a anthu. Popeza kuti 6 ndi woperewera ndipo sakukwana 7, ndiye kuti 666 kapena kuti ma 6 atatu, ndi dzina loyenera la magulu onse andale padziko lonse amene akuperewera modetsa nkhawa pa muyezo wolungama wa Mulungu. Pamene chilombo chandalechi chikulamulira dziko lonse, chikudziwika ndi dzina lakuti 666. Ndipo mayiko amphamvu pandale, zipembedzo zikuluzikulu komanso magulu akuluakulu a zamalonda, ndi amene akuthandiza chilombochi kuti chipitirize kupondereza anthu ndi kuzunza anthu a Mulungu.
35. Kodi anthu akuikidwa bwanji chizindikiro cha dzina la chilombo chija pamphumi kapena padzanja lawo lamanja?
35 Kodi anthu akuikidwa bwanji chizindikiro cha dzina la chilombo chija pamphumi kapena padzanja lawo lamanja? Yehova atapereka Chilamulo kwa Aisiraeli, anawauza kuti: “Mawu angawa muwasunge m’mitima yanu ndi kuwatsatira m’moyo wanu. Muwamange monga chizindikiro padzanja lanu, ndipo akhale ngati chomanga pamphumi panu.” (Deuteronomo 11:18) Zimenezi zinatanthauza kuti Aisiraeliwo ankafuna kusunga Chilamulocho pafupi nthawi zonse, kuti zochita zawo zonse komanso maganizo awo onse zizigwirizana ndi Chilamulocho. Baibulo limanena kuti pamphumi pa a 144,000 odzozedwa panalembedwa dzina la Atate ndi la Yesu. Zimenezi zimasonyeza kuti odzozedwawa ndi a Yehova Mulungu komanso a Yesu Khristu. (Chivumbulutso 14:1) Pofuna kutengera zimenezi, nayenso Satana akugwiritsa ntchito chizindikiro choipa cha chilombo chija. Zimenezi zachititsa kuti aliyense amene akuchita zinthu za masiku onse monga kugula ndi kugulitsa, akakamizike kuchita zinthu mofanana ndi mmene chilombocho chimachitira, monga kukondwerera maholide. Satana amafuna kuti anthu azilambira chilombochi ndi kulolera kuti chizilamulira zochita zawo, chifukwa amadziwa kuti akatero alandira chizindikiro cha chilombocho.
36. Kodi anthu amene akana kulandira chizindikiro cha chilombocho akumana ndi mavuto otani?
36 Anthu amene amakana kulandira chizindikiro cha chilombocho, amakumana ndi mavuto nthawi zonse. Mwachitsanzo, kuyambira m’ma 1930 anthu omwe akhala akukana kulandira chizindikirochi anafunika kumenyera ufulu wawo m’makhoti. Komanso anafunika kupirira pamene anthu ankawachitira ziwawa ndi kuwazunza m’njira zina. M’mayiko amene munali ulamuliro wankhanza, iwo ankaikidwa m’ndende zozunzirako anthu ndipo ambiri a iwo anafera m’ndende zimenezi. Kuyambira pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, achinyamata ambirimbiri anaikidwa m’ndende mmene anakhalamo kwa nthawi yaitali. Ena achitiridwa zinthu zankhanza mpaka kuphedwa, chifukwa chokana kupita kunkhondo kapena kuchita zinthu zina zosemphana ndi chikhulupiriro chawo chachikhristu. M’mayiko ena Akhristu sangathedi kugula kapena kugulitsa malonda. Ena amakanizidwa kukhala ndi malo kapena katundu wina, agwiriridwa, kuphedwa kapena kuthamangitsidwa m’dziko lawo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti chikumbumtima chawo sichiwalola kugula khadi la chipani cha ndale.d—Yohane 17:16.
37, 38. (a) N’chifukwa chiyani moyo uli wovuta kwambiri m’dzikoli kwa anthu amene akukana kulandira chizindikiro cha chilombo chija? (b) Ndani akutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, ndipo iwo ndi otsimikiza ndi mtima wonse kuti achite chiyani?
37 M’madera ena a dziko lapansili, chipembedzo ndi mbali ya moyo watsiku ndi tsiku wa anthu moti munthu amene wayamba kutsatira mfundo za choonadi cha m’Baibulo amanyozedwa kwambiri ndi achibale ake komanso anthu amene kale ankagwirizana nawo. Kuti munthu athe kupirira zonsezi amafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Mateyu 10:36-38; 17:22) M’dziko lino, limene anthu ambiri amalambira chuma ndipo ambiri amakonda kuchita zinthu zachinyengo, nthawi zonse Akhristu oona amafunika kudalira Yehova kuti awathandize kutsatira mfundo zake zolungama. (Salimo 11:7; Aheberi 13:18) M’dziko limene anthu ambiri akukonda kuchita chiwerewere, Mkhristu amafunika kulimba mtima kwambiri kuti akhalebe woyera. Akhristu akadwala, kawirikawiri amakakamizidwa ndi madokotala komanso manesi kuti aphwanye malamulo a Mulungu pa nkhani yokhudza kupatulika kwa magazi. Akhristuwo amafunikanso kulimba mtima kuti asachite zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro chawo zimene makhoti amalamula nthawi zina. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Petulo 4:3, 4) Chifukwa cha kusowa kwa ntchito masiku ano, n’zovuta kwambiri kuti Mkhristu woona apeze ntchito imene singamulepheretse kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika.—Mika 4:3, 5.
38 N’zoonadi, kwa anthu amene alibe chizindikiro cha chilombo chija, moyo ndi wovuta kwambiri m’dzikoli. Anthu amene akupanga mbali ya mbewu ya mkazi, amene adakali padziko lapansi komanso anthu a khamu lalikulu oposa 7 miliyoni, akutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika ngakhale kuti amakumana ndi zovuta zambiri poyesetsa kuti asaphwanye malamulo a Mulungu. Zimenezi ndi umboni wakuti Yehova akuwapatsa mphamvu ndi kuwadalitsa. (Chivumbulutso 7:9) Tiyeni tonse mogwirizana padziko lonse lapansi, tipitirize kulemekeza Yehova ndi kutsatira njira zake zolungama, pokana kulandira chizindikiro cha chilombo chija.—Salimo 34:1-3.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! tsamba 165 mpaka 179, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b The Interpretation of St. John’s Revelation, lolembedwa ndi R. C. H. Lenski, tsamba 390 mpaka 391.
c Olemba nkhani ena anenapo kuti kukonda kwambiri dziko lako kuli ngati chipembedzo. Choncho anthu amene amakonda kwambiri dziko lawo kwenikweni amakhala akulambira chilombo chija, chimene chikuimiridwa ndi dziko lawolo. Pofotokoza zimene anthu okonda kwambiri dziko lawo amachita ku United States, katswiri wina wa mbiri yakale anati: “Kukonda kwambiri dziko lako, kumene kuli ngati chipembedzo, n’kofanana kwambiri ndi zipembedzo zina zikuluzikulu zakale . . . Anthu amene amakonda kwambiri dziko lawo masiku ano, amalidalira kwambiri moti amaliona ngati mulungu wawo. Iwo amaona kuti dziko lawolo lili ndi mphamvu zowathandiza pa chilichonse. Amaona kuti lingawathandize kukhala ndi moyo wabwino kwambiri ndiponso wosangalala. Popeza kukonda kwambiri dziko lawo kuli ngati chipembedzo chawo, iwo amagonjera kwambiri dzikolo . . . ndipo amaona kuti lidzakhalapo mpaka kalekale. Komanso achinyamata akamafera dzikolo mokhulupirika, anthu amenewa amaona kuti dziko lawolo ndi lotchuka ndiponso laulemerero kwambiri.”—Mawu a Carlton J. F. Hayes, amene akupezeka patsamba 359 m’buku lakuti What Americans Believe and How They Worship, lolembedwa ndi J. Paul Williams.
d Mwachitsanzo, onani kabuku kakuti Mboni za Yehova m’Malaŵi—Nkhani ya Kukhulupirika Kwawo, tsamba 20 mpaka 51. Komanso onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1996, tsamba 24 mpaka 28; March 15, 1996, tsamba 7; January 15, 1994, tsamba 5; April 1, 2000, tsamba 26 ndi 27.
[Chithunzi patsamba 195]
Chilombocho chinapatsidwa mphamvu yopereka mpweya kwa chifaniziro cha chilombo chija