666—Si Nambala Yongodabwitsa Chabe
“Munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo, ndilo dzina la chilombo, kapena chiŵerengero cha dzina lake. Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziŵitso aŵerenge chiŵerengero cha chilombocho; pakuti chiŵerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiŵerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.”—Chivumbulutso 13:17, 18.
NDI nkhani zochepa chabe za m’Baibulo zimene anthu amachita nazo chidwi ndiponso kuda nazo nkhaŵa monga momwe amachitira ndi ulosi wa chilembo, kapena kuti chizindikiro chodabwitsa cha “chilombo”—nambala ya 666. Pawailesi za kanema ndiponso pa Intaneti, komanso m’mavidiyo, m’mabuku, ndi m’magazini, anthu akhala akupereka maganizo osiyanasiyana pankhani ya chizindikiro cha chilombo.
Anthu ena amakhulupirira kuti 666 ndi chizindikiro cha okana Kristu otchulidwa m’Baibulo. Ena amati nambalayi imasonyeza chizindikiro chinachake chomwe anthu angapatsidwe mokakamizidwa. Amati ingathe kukhala chidindo kapena kachipangizo ka kompyuta kamene angakaike pathupi la munthu kosonyeza kuti iye akutumikira chilombo. Enanso amakhulupirira kuti 666 ndi chizindikiro cha papa wa Katolika. Zilembo za dzina laulemu la papa lakuti Vicarius Filii Dei (Woimira Mwana wa Mulungu) akazipatsa manambala malinga ndi kalembedwe ka manambala achiroma, ndiyeno n’kuŵerengetsera manambalawo, amapeza nambala ya 666. Anthu enanso amanena kuti nambalayi ingapezeke mwa kuchita masamu ndi dzina lachilatini la mfumu Diocletian ya Roma ndiponso ndi dzina lachihebri la Kaisara Nero.a
Komabe malingaliro ongopanga anthu ameneŵa akusiyana kwambiri ndi zimene Baibulo limanena zokhudza chizindikiro cha chilombo, malinga ndi zimene tione m’nkhani yotsatirayi. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzawononga anthu omwe ali ndi chizindikiro pamene iye azidzawononga dzikoli. (Chivumbulutso 14:9-11; 19:20) Motero, kudziŵa tanthauzo la 666 n’kofunika kwambiri, kuposa kungopeza yankho la samu yongoimitsa mutu chabe. N’zosangalatsa kuti Yehova Mulungu, yemwe ndi chitsanzo chachikulu cha chikondi ndiponso Gwero la kuunika kwauzimu, sanasiye atumiki ake mu mdima pankhani yofunikayi.—2 Timoteo 3:16; 1 Yohane 1:5; 4:8.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve za nkhani yokhudza chikhulupiriro chakuti manambala amatha kudziŵitsa zinthu zinazake, onani Galamukani! ya September 8, 2002.