-
“Nkhani Zosangalatsa” za M’chivumbulutsoNsanja ya Olonda—1999 | December 1
-
-
3. Kodi utumiki wapoyera wa Mboni za Yehova ukugwirizana ndi ntchito iti?
3 Pokhala olengeza nkhani zosangalatsa zimenezi, Mboni za Yehova zili kwenikweni zolankhulira za mthenga wophiphiritsa wakumwamba amene ntchito yake ikulongosoledwanso m’buku la Chivumbulutso. “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) “Uthenga Wabwino wosatha” ukuphatikizapo chilengezo chakuti “Ufumu [kapena, ulamuliro] wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake” ndi kuti “nthaŵi” ya Yehova yafika ya “kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:15, 17, 18) Kodi umenewo si uthenga wabwinodi?
-
-
“Nkhani Zosangalatsa” za M’chivumbulutsoNsanja ya Olonda—1999 | December 1
-
-
6. Kodi masomphenya olembedwa m’chaputala 4 amathandiza anthu kumvetsa chiyani?
6 Chaputala 4 chikusimba za masomphenya ochititsa nthumanzi a mpando wachifumu wakumwamba wa Yehova Mulungu. Pamlingo waung’ono chikusonyeza ulemerero wa malo a Yehova ndi olamulira akumwamba amene iye adzagwiritsa ntchito. Olamulira ovala akorona ameneŵa, amene mipando yawo yachifumu imazungulira mpando wachifumu waukulu m’chilengedwe chonse, amagwadira Yehova ndi kulengeza kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”—Chivumbulutso 4:11.
7. (a) Kodi mngelo akulamula okhala padziko lapansi kuti achite chiyani? (b) Kodi mbali yofunika ya ntchito yathu ndiyo kuchitanji?
7 Kodi zimenezi zili ndi tanthauzo lililonse kwa anthu lerolino? Ndithudi zilinalo. Ngati akufuna moyo mu Ufumu wa Zaka Chikwi, ayenera kumvera zimene ‘mngelo wouluka pakati pa mlengalenga’ akulengeza kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.” (Chivumbulutso 14:6, 7) Chimodzi mwa zolinga za ntchito yophunzitsa Baibulo imene Mboni za Yehova zikuchita ndicho kuthandiza “iwo akukhala padziko” kuti adziŵe ndi kulambira Yehova, kuvomereza kuti ndiye Mlengi, ndi kugonjera uchifumu wake wolungama modzifunira.
-