Zimene Owerenga Amafunsa . . .
Kodi Aramagedo ndi Chiyani?
▪ Anthu ambiri akamva mawu akuti “Aramagedo” amaganizira za zinthu zoopsa kwambiri monga nkhondo ya zida za nyukiliya, masoka akuluakulu achilengedwe kapenanso kusintha kwa nyengo kowononga chilengedwe. Koma Baibulo potchula mawu amenewa silitanthauza zinthu zimenezi. Ndiyeno kodi limatanthauza chiyani?
Mawu akuti “Aramagedo” (“Haramagedo”) amapezeka m’buku la m’Baibulo la Chivumbulutso. Mawu amenewa amatanthauza nkhondo yapadera kwambiri yomwe ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Panopa “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” akukonzekeretsedwa kuti amenyane ndi Mulungu pa nkhondo yomaliza imeneyi. M’Baibulo mulinso malemba ena amene amanena zinthu zina zokhudza nkhondo imeneyi.—Chivumbulutso 16:14-16; Ezekieli 38:22, 23; Yoweli 3:12-14; Luka 21:34, 35; 2 Petulo 3:11, 12.
Kodi chidzachitike n’chiyani pa nkhondo imeneyi? Buku la Chivumbulutso limatiuza mophiphiritsa kuti: ‘Mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo anasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo.’ “Wokwera pahatchi” amene akutchulidwa palembali ndi Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, yemwe anadzozedwa ndi Mulungu kuti atsogolere magulu a angelo pogonjetsa adani a Mulungu. (Chivumbulutso 19:11-16, 19-21) Lemba la Yeremiya 25:33 limasonyeza kuchuluka kwa anthu osaopa Mulungu amene adzaphedwe. Lembali limati: “Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.”
Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu adzabweretse nkhondo imeneyi? Mayiko amakana kugonjera ulamuliro wa Mulungu ndipo m’malomwake amalimbikitsa maulamuliro awo. (Salimo 24:1) Mzimu wosafuna kugonjera Mulungu umene anthu amenewa ali nawo wafotokozedwa palemba la Salimo 2:2, limene limati: “Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo, ndipo nduna zapamwamba zasonkhana pamodzi mogwirizana. Atero kuti alimbane ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.”
Anthu opanduka amenewa amakhala ngati anthu amene akukhala pamalo oti si awo n’kumawononganso malowo. Masiku ano anthu akuwononga dzikoli m’njira zosiyanasiyana ndipo akuwononganso zinthu zachilengedwe. Mawu a Mulungu analosera kuti zinthu zoipa zimenezi zidzachitika. Baibulo limati: ‘Mitundu ya anthu inakwiya, ndipo mkwiyo wa Mulungu unafika, koma Mulungu adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Mulungu adzagwiritsa ntchito Aramagedo pothetsa nkhani yokhudza amene ali woyenera kulamulira anthu onse.—Salimo 83:18.
Kodi Aramagedo idzachitika liti? Mwana wa Mulungu ananena momveka bwino kuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) Komabe ponena za Aramagedo, Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Nkhondo, anawonjezera chenjezo ili: “Taona! Ndikubwera ngati mbala. Wodala ndiye amene akhalabe maso.” (Chivumbulutso 16:15) Choncho nkhondo yapadziko lonse imeneyi idzachitika pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. Ndipo maulosi a m’Baibulo amasonyeza kuti nthawi ya kukhalapo kwa Khristuyo, ndi inoyo.
Nkhondo ya Aramagedo idzawononga anthu okhawo amene asankha kupitirizabe kuchita zoipa. Koma padzakhala “khamu lalikulu la anthu” lomwe lidzapulumuke. (Chivumbulutso 7:9-14) Anthu amenewa adzaona kukwaniritsidwa kwa mawu awa: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.
[Mawu Otsindika patsamba 10]
“Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka”