Mkazi Wachigololo wa Mbiri Yoipa—Kugwa Kwake
“Iye wagwa! Babulo Wamkulu wagwa, iye amene anapangitsa mitundu yonse kumwako ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake!”—CHIBVUMBULUTSO 14:8, NW.
Nkhani iyi ndi yotsatira zinapanga nkhani yomalizira yosiirana yokhala ndi mutu wakuti “Nthaŵi Zoikidwiratu Ziri Pafupi,” yoperekedwa mkati mwa Misonkhano Yachigawo ya 1988 ya Chilungamo Chaumulungu ya Mboni za Yehova.
1. Ndani yemwe ali “mkazi wachigololo,” wa mbiri yoipa, ndipo nchifukwa ninji timafunikira kudziŵa ponena za iye?
“MKAZI wachigololo” wa mbiri yoipa—kodi iye ndani? Nchifukwa ninji tikufunikira kulankhula ponena za iye? Kodi olemba manovel osangalatsa, akanema, TV, ndi mavideo samatumikira mlingo wokwanira woipitsitsa wa chisembwere? Zowonadi! Koma uyu sali kokha mkazi wamba wa madzulo. Iye ali, m’chenicheni, wokopa kwenikweni, wosamva kwenikweni, wachigololo wakupha kwenikweni m’mbiri yonse yakale. Ndipo wakhala akugulitsa ziyanjo zake kwa zaka zoposa 4,000! Tifunikira kudziŵa ponena za iye kaamba ka chinjirizo lathu. Pa Chibvumbulutso 14:8, mngelo wakumwamba akutcha mkazi wokhala ndi kutchuka koipa ameneyu kukhala “Babulo Wamkulu” ndi kumulongosola iye kukhala wonyenga wa mitundu. Popeza kuti ali wowopsya chotero, tiyenera kukhala achimwemwe kudziŵa kuti “nthaŵi zoikidwiratu [za Yehova] ziri pafupi” za kupereka chiweruzo pa iye.—Chibvumbulutso 1:3, NW.
2. Ndi kuchokera kuti kumene mkazi wachigololo ameneyu watenga dzina lake, ndipo ndimotani mmene ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga unayambira?
2 Mkazi wachigololo ameneyu amatenga dzina lake kuchokera ku Babulo wakale, mzinda wonyada wokhazikitsidwa mu Mesopotamiya zaka zoposa 4,000 zapitazo ndi Nimrode, “mpalu wamkulu motsutsana ndi Yehova.” Pamene Ababulo anayamba kumanga nsanja ya chipembedzo chakunja, Yehova anasokoneza chinenero chawo ndi kuwabalalitsira iwo kumalekezero a dziko lapansi. Iwo anatenga chipembedzo chawo limodzi nawo, ndipo mmenemo ndi mmene ulamuliro wa dziko wa chipembedzo cha Chibabulo unayambira. Zowonadi, iwo uli Babulo WAMKULU. (Genesis 10:8-10; 11:1-9) Kutsikira kufika m’nthaŵi yathu, zinsinsi za Babulo wakale zawunikiridwa m’zikhulupiriro ndi machitachita a zipembedzo za dziko. (Chibvumbulutso 17:7) Dzina Lachihebri kaamba ka mzinda, Babele, limatanthauza “Kusokonezeka,” dzina lolondola kaamba ka chipembedzo chonyenga chosanganizana cha lerolino!
3. (a) Ndi kwa utali wotani umene Babulo anasunga anthu a Mulungu mu ukapolo, kuwaika iwo pafupi ndi chiyani? (b) Ndiliti pamene Babulo anavutika ndi kugwa kwatsoka, ndipo nchifukwa ninji matsiriziro ake sanadze pa nthaŵi imeneyo?
3 Babulo wakale anachira kuchoka ku kubwerera m’mbuyo koyamba kumeneko ndipo, ndi kugwetsedwa kwa Asuri mu 632 B.C.E., anakhala mphamvu ya dziko yachitatu ya mbiri yakale ya Baibulo. Ulemerero wake monga woterowo unali wosakhalitsa—wochepera pa zaka zana limodzi—koma kwa chifupifupi zaka 70 za zimenezo, iye anasunga anthu a Mulungu Israyeli mu ukapolo. Ichi chinawaika iwo moyandikana ndi akachisi zikwi zingapo a Babulo ndi malo opempherera, milungu yake ya utatu ndi adyerekezi ake a utatu, kulambira kwake kwa mayi ndi mwana, ndi kupenda kwake nyenyezi komwe kunapanga mafano milungu yolingaliridwa kukhala yosakhoza kufa. Chotero, Aisrayeli a mu ukapolo anali pafupi pa malo apakati a dziko lonse a chipembedzo chonyenga pamene, mu 539 B.C.E., mzinda wa Babulo unavutika ndi kugwa kwatsoka. Koma mathedwe ake anali asanakhale! Ogonjetsa ake anapitirizabe kugwiritsira ntchito iye kukhala malo apakati a chipembedzo otchuka.
Ulamuliro wa Chipembedzo wa Chiwunda Chonse
4. (a) Nchiyani chomwe aneneri a Yehova analengeza ponena za Babulo, ndipo nchiyani chomwe chinachitika kwa Babulo? (b) Ndi Babulo wina uti yemwe adakali ndi moyo, ku kuipsya kwa anthu a dziko lapansi?
4 Aneneri a Yehova anali atalengeza chiweruzo chake kuti Babulo akafunikira kusesedwa “ndi tsache la chiwonongeko”—“monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.” Kodi maulosi amenewo pambuyo pake anakwaniritsidwa? Inde, ku tsatanetsatane wotsirizira! M’kupita kwa nthaŵi, Babulo wakale anakhala mulu wa zapadzala—wosakhalidwapo ndi anthu kusiyapo zokwawa ndi nyama zakuthengo—ndendende monga momwe kunanenedweratu! (Yesaya 13:9, 19-22; 14:23; Yeremiya 50:35, 38-40) Ngakhale kuli tero, Babulo wina uja, Babulo Wamkulu wamakono, adakali ndi moyo. Monga ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga, iye amapitirizabe ndi ziphunzitso zakale za Babulo ndi mzimu wodzitukumula. Iye ali chiwiya chachikulu cha Satana kaamba ka kuchititsa khungu anthu ku zifuno za Ufumu wa Yehova.—2 Akorinto 4:3, 4.
5. (a) Ndi zipembedzo ziti zomwe zinayambitsidwa pamene Babulo anali pachimake cha ulemerero wake, koma kodi nchifukwa ninji Satana sanapambane kumwereketsa dziko lonse ndi chipembedzo chonyenga? (b) Ndimotani mmene Satana anagwiritsira ntchito chipembedzo chonyenga pambuyo pa kuyambitsa Chikristu?
5 Podzafika m’zana lachisanu ndi chimodzi Kristu asanadze, pamene Babulo mphamvu ya dziko anali pachimake pa ulemerero wake, chipembedzo cha Chihindu, Chibuda, Chikonfyushani, ndi Chishinto zinadzatulukiranso. Koma kodi Satana anapambana m’kusintha dziko lonse ndi chipembedzo chonyenga? Ayi, popeza kuti otsalira a mboni zakale za Yehova anabwerera kuchokera ku Babulo kupita ku Yerusalemu kukakhazikitsanso kulambira kwa Yehova. Chotero, Ayuda okhulupirika anali okonzekera kumeneko, mazana asanu ndi limodzi pambuyo pake, kulandira Mesiya ndi kukhala ziŵalo zoyambirira za mpingo Wachikristu. Chipembedzo chonyenga chinabweretsa kuphedwera chikhulupiriro kwa Mwana wa Mulungu ndipo chinakhala chiwiya cha Satana kaamba ka kutsutsa Chikristu chowona, mongadi mmene Yesu ndi atumwi ake anachenjezera.—Mateyu 7:15; Machitidwe 20:29, 30; 2 Petro 2:1.
6. (a) Ndimotani mmene Satana anaipitsira ziphunzitso Zachikristu, ndipo ndi ziphunzitso zosalemekeza Mulungu zotani zomwe zinayambika? (b) Nchiyani chomwe chinachitika ku zikwi zingapo zomwe zinakonda zowonadi za Baibulo kuposa chiphunzitso choikidwiratu cha Chibabulo?
6 Makamaka pambuyo pa chiwonongeko chachiŵiri cha Yerusalemu mu 70 C.E., ndi pamene Satana anagwiritsira ntchito atumwi onama kuipitsa ziphunzitso Zachikristu, kusanganiza zimenezi ndi nthano za Chibabulo ndi nthanthi zakudziko za Chigriki. Chotero, ‘umulungu wa mbali zitatu,’ Utatu, unaloŵa m’malo “Yehova mmodzi” wa m’Baibulo. (Deuteronomo 6:4; Marko 12:29; 1 Akorinto 8:5, 6) Ndipo chiphunzitso cha kusafa kwa moyo wa munthu, monga momwe chinaphunzitsidwira ndi Plato wanthanthi zakunja, chinabweretsedwa kuipitsa ziphunzitso zofunika za Baibulo za dipo la Kristu ndi chiwukiriro. Ichi chinatsegula njira kaamba ka chikhulupiriro mu moto wa helo ndi purigatoriyo wa moto wochepera. (Salmo 89:48; Ezekieli 18:4, 20) Ziphunzitso zosalemekeza Mulungu zoterozo zomwe zimachita mbali yake pa mantha a anthu zathandiza kudzaza mosungiramo zamtengo wapatali mwa matchalitchi. Kuwonjezerapo, m’masiku a Kufufuzafufuza ndi Kukonzanso, atsogoleri achipembedzo sakakhoza kuyembekezera kaamba ka malaŵi a moto wa helo kuti achite kuzunzako. Zikwi zingapo zomwe zinakonda zowonadi za Baibulo kuposa chiphunzitso choikidwiratu cha Chibabulo anatenthedwa amoyo pa mtengo ndi ponse paŵiri Akatolika ndi Aprotesitanti. Koma monga mmene tidzawonera, chigololo cha Babulo Wamkulu chimapita patali kupyola pa kuchirikiza chinyengo.
Tsiku la Yehova la Chiweruzo
7. (a) Ndi liti ndipo ndimotani mmene Yehova anayambira kubwezeretsanso zowonadi zenizeni za Baibulo ndi kuvumbula ziphunzitso zonyenga, za Chibabulo? (b) Ndi zowonadi zenizeni za Baibulo ziti zimene Ophunzira Baibulo anabwezeretsa?
7 Tsiku la Yehova la chiweruzo cha mkazi wachigololo ameneyu linafunikira kudza! (Ahebri 10:30) Panali nyengo yokonzekera, yoyamba mu ma 1870, pamene Yehova anatumiza “mthenga” wake—gulu lowona mtima la ophunzira Baibulo—kubwezeretsa zowonadi zenizeni za Baibulo ndi kuvumbula ziphunzitso zonyenga za Chibabulo. (Malaki 3:1a) Gulu la “mthenga” limeneli linagwirizana ndi mawu a ulosi wa pa Chibvumbulutso 4:11: “Muyenera inu, [Yehova, NW] ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” “Mthengayo” anakhalanso mlengezi woyambirira wa nsembe ya dipo ya Yesu, mphatso ya Mulungu kaamba ka kuwombola mtundu wa anthu. Mtundu wa anthu owomboledwa ukaphatikizapo, choyamba, “kagulu ka nkhosa” komwe kadzafunikira kulamulira ndi Yesu mu Ufumu wake wa kumwamba ndipo, pambuyo pake, mamiliyoni mazana angapo omwe adzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi—ambiri a omwe adzawukitsidwa kuchokera kwa akufa. (Luka 12:32; 1 Yohane 2:2; Machitidwe 24:15) Inde, Ophunzira Baibulo amenewo anabwezeretsa zowonadi zofunika zimenezi, ndipo m’njira yophiphiritsira, iwo anakhoza ngakhale ‘kutembenuzira paipi ya madzi pa helo ndi kuzima moto’ wa chiphunzitso choikidwiratu Chachibabulo cha kuzunzidwa kosatha!a
8. (a) Ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko anagwiritsira ntchito Nkhondo ya Dziko ya I kuyesa kuwononga Ophunzira Baibulo? (b) Nchiyani chomwe chinachitika kwa woweruza yemwe anasunga akuluakulu asanu ndi atatu a Watch Tower Society m’ndende mwa kukana kuwamasula?
8 Kwa zaka 40 Ophunzira Baibulo analengeza molimba mtima kuti chaka cha 1914 chikazindikiritsa mapeto a Nthaŵi za Akunja. Monga momwe zinayembekezeredwa, chaka chimenecho chinabweretsa zochitika zogwedeza dziko, popanda chochepera chirichonse cha izi kukhala nkhondo yoyamba ya dziko. Eya, ndimotani nanga mmene atsogoleri a chipembedzo cha Chikristu cha Dziko—mbali yotchuka kwenikweni ya Babulo Wamkulu—anayesera kugwiritsira ntchito nsautso ya dziko kuwononga Ophunzira Baibulo opanda mantha amenewo! Potsirizira pake, mu 1918, iwo anapangitsa akuluakulu asanu ndi atatu a Watch Tower Society kuzengedwa mlandu ndi kuikidwa m’ndende kaamba ka kuweruzidwa mwachinyengo. Koma akuluakulu amenewa anamasulidwa pambuyo pa miyezi isanu ndi inayi ndipo pambuyo pake anatulutsidwa. Woweruza wamkulu wa ku U.S. Martin T. Manton, yemwe anasunga Ophunzira Baibulo amenewa m’ndende mwa kukana lamulo la kuwamasula kwa kanthaŵi kochepa, pambuyo pake anakometseredwa ndi Papa Pius XI, mwa kupangidwa “nduna ya chisilikali ya St. Gregory the Great.” Ngakhale kuli tero, ulemerero wake unali wosakhalitsa, popeza kuti mu 1939 iye anazengedwa mlandu wa zaka ziŵiri m’ndende ndi kulipiritsidwa kokulira. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti anapezedwa wa liwongo la kugulitsa zigamulo zisanu ndi chimodzi za bwalo lamilandu kaamba ka ndalama za chiphuphu za chiwonkhetso cha $186,000!
9. Ndimotani mmene ulosi wa Malaki umalongosolera chomwe chinkachitika kwa anthu a Yehova, ndipo chotero chiweruzo chinayamba ndi ndani?
9 Monga momwe tawonera, anthu a Yehova analoŵa m’nyengo ya kuyesa koipa mu 1918. Mawu owonjezereka a mneneriyo pa Malaki 3:1-3 akulongosola chomwe cinkachitika: “Ndipo Ambuye [Yehova] amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; [ndi, NW] mthenga wa chipangano cha [Abrahamu]”—Yesu. Inde, Yehova anabwera ndi Kristu wake kaamba ka chiweruzo. Yehova kenaka akufunsa kuti: “Ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? ndipo adzaima ndani powoneka Iye? pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka.” Mogwirizana ndi 1 Petro 4:17, chiweruzo chikayamba ndi awo odzinenera kukhala a “nyumba ya Mulungu.” Chotero, Akristu owona anayengedwa ndi kuyeretsedwa kaamba ka utumiki wa Yehova.
“Tulukani Mwa . . . Iye, Anthu Anga”!
10. Ndi chiweruzo chaumulungu chotani chomwe chinadza pa Chikristu cha Dziko ndi chipembedzo chonse chonyenga podzafika mu 1919, chikumatulukapo m’nchiyani kaamba ka Babulo Wamkulu?
10 Monga mbali yosalapa ya Babulo Wamkulu, atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko sakakhoza kuima pa chiweruzo cha Yehova. Iwo anaipitsa zovala zawo moipa monga otengamo mbali mu kusakaza kwa nkhondo ya dziko ndipo monga ozunza a Akristu owona. (Yeremiya 2:34) M’malo molengeza kudza kwa Ufumu wa kumwamba wa Kristu, iwo anachirikiza Chigwirizano cha Mitundu chopangidwa ndi anthu, chomwe anadzachilongosola monga “chisonyezero cha ndale zadziko cha Ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi.” Podzafika mu 1919 chinakhala chowonekera kuti Yehova anapereka chiweruzo pa Chikristu cha Dziko—ndipo ndithudi pa chipembedzo chonse chonyenga. Babulo Wamkulu anali atagwa, kutsutsidwa ku imfa! Inali nthaŵi yovuta kaamba ka okonda chowonadi onse ndi olungama kuchitapo kanthu pa lamulo la ulosi la pa Yeremiya 51:45: “Anthu anga, tulukani pakati pake, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo wa ukali wa Yehova.”
11, 12. (a) Nchiyani chomwe mngelo akunena pa Chibvumbulutso 17:1, 2 m’chigwirizano ndi chiweruzo cha Babulo Wamkulu? (b) Nchiyani chomwe chiri “madzi ambiri” amene mkazi wachigololo akukhalapo, ndipo ndimotani mmene iye akupangitsira okhala pa dziko “kuledzera ndi vinyo wa chigololo chake”?
11 Babulo Wamkulu wagwa! Koma sanawonongedwebe. Monga ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga, iye adzakhalapo kwa utali wa nyengo yochepera monga chiwiya chopambana cha Satana cha chinyengo. Kodi nchiyani chomwe chiri chiweruzo chotsirizira cha Mulungu pa iye? Sitikusiidwa m’chikaikiro! Tiyeni titembenukire ku Mabaibulo athu pa Chibvumbulutso 17:1, 2. Pano mngelo akulongosola kwa mtumwi Yohane ndipo, kupyolera mwa iye, ophunzira a ulosi lerolino, akumanena kuti: “Idza kuno, ndidzakuwonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri, amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.” Mawu akuti “madzi ambiri” amalozera ku unyinji wosakhazikika wa mtundu wa anthu, wotsenderezedwa motalikira chotero ndi mkazi wachigololo wamkulu. Ndipo ulosiwo ukulongosola kuti “akukhala padziko” aledzera ndi vinyo wake. Iwo amamwerekera ziphunzitso zonyenga ndi zakudziko, njira za chisembwere za Babulo Wamkulu ndipo akudzandiradzandira, monga ngati kuti afooketsedwa ndi vinyo wotsika mtengo, woipa.
12 Pa Yakobo 4:4 timaŵerenga kuti: “Akazi achigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu?” Chipembedzo cha m’zana la makumi aŵiri chonse chiri chokonzekeratu kukometsa ziyanjo ndi dziko, ndipo chimenecho chiri makamaka chowona ndi Chikristu cha Dziko. Osati kokha kuti atsogoleri ake a chipembedzo alephera kulengeza mbiri yabwino ya kudza kwa Ufumu wa Yehova koma amanyalanyaza ziphunzitso za makhalidwe abwino za Baibulo, kulekerera kulolera kwa dziko pakati pa ziŵalo za tchalitchi. Ngakhale atsogoleri a chipembedzo sali opanda liwongo chotero ponena za dama lakuthupi, lomwe linatsutsidwa mwakuya chotero ndi mtumwi Paulo pamene iye ananena kuti: “Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsya ndi amuna . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa.”—1 Akorinto 6:9-11.
“Kukunkhulika m’Thope”
13, 14. (a) Ndi zitsanzo zotani zomwe zimasonyeza kuti atsogoleri a chipembedzo amakono “sanayeretsedwe”? (b) Ndi mkhalidwe wotani umene msonkhano wa Tchalitchi cha England unatenga kulinga ku kachitidwe ka kugonana kwa ofanana ziŵalo, ndipo ndimotani mmene wolemba nkhani analingalira kuti tchalitchi chiyenera kutchedwanso? (c) Atsogoleri a chipembedzo opatuka amalingana ndi mawu otani a mtumwi Petro?
13 Kodi atsogoleri a chipembedzo amakono “ayeretsedwa”? Chabwino, monga chitsanzo, onani mkhalidwe mu Britain, yomwe pa nthaŵi imodzi inali maziko a Chiprotesitanti. Mu November 1987, pamene nduna yaikulu ya Britain inakumbutsa atsogoleri a chipembedzo kupereka chitsogozo mu makhalidwe abwino, nduna ya tchalitchi cha Anglican inkanena kuti: “Ogonana ofanana ziŵalo ali ndi kuyenera kochulukira ku kusonyeza kwa kugonana mofanana ndi wina aliyense; tiyenera kuyang’ana kaamba ka ubwino mu icho ndi kulimbikitsa chikhulupiriro [pakati pa ogonana ofanana ziŵalo].” Nyuzipepala ya ku London inasimba kuti: “Kachitidwe ka kugonana kwa ofanana ziŵalo kanakhala kofala kwenikweni pa koleji imodzi ya zaumulungu ya Anglican kotero kuti ophunzira kuchokera ku koleji ina anayenera kuletsedwa ndi ogwira ntchito kuchezera iyo.” Phunziro limodzi linaŵerengera kuti “mu boma limodzi la London, chiŵerengero cha atsogoleri a chipembedzo okhala ndi chikhoterero cha kugonana kwa ofanana ziŵalo chingakhale choposa theka la chiŵerengero chonse.” Ndipo pa msonkhano wa tchalitchi, 95 peresenti ya atsogoleri a chipembedzo a Tchalitchi cha England anachirikiza kachitidwe komwe kanazindikiritsa dama ndi chigololo kukhala machimo, koma osati kachitidwe ka kugonana kwa ofanana ziŵalo; kachitidwe ka kugonana kwa ofanana ziŵalo koteroko kananenedwa kokha kukhala kuphonya kwa chenicheni. Akumachitira ndemanga pa zonsezi, wolemba nkhani mmodzi analingalira kuti Tchalitchi cha England chingatchedwe bwino lomwe kukhala Sodomu ndi Gomora. Nyuzipepala ina ya ku London inalengeza kuti: “Anthu a ku Britain akuwopsyezedwa pamene akuwona zotulukapo za mbadwo wa kulekerera.”
14 Ndi moyenerera chotani nanga mmene atsogoleri a chipembedzo a mpatuko mkati mwa zaka agwirizanirana ndi mawu a mtumwi Petro: “Chidawayenera iwo cha nthanthi yowona, Galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulika m’thope”!—2 Petro 2:22.
15. (a) Ndi kunyonyotsoka kotani m’mapindu a mkhalidwe komwe kwachitika m’Chikristu cha Dziko chonse? (b) Ndani yemwe ayenera kugawana thayo kaamba ka kututa kwatsoka kumeneku?
15 Kupyola mu Chikristu cha Dziko chonse, ndipo ndithudi dziko lonse, pali kunyonyotsoka kowopsya m’mapindu a makhalidwe abwino. M’zitaganya zina, ukwati tsopano ukuwonedwa kukhala wosayenera, ndipo awo omwe ali okwatira amaganizira kuti kukhulupirika kwa mu ukwati kuli kwachikale. Ochepera akukhalitsa kwalamulo kugwirizana kwawo, ndipo chiŵerengero cha kusudzulana chakula pakati pa omwe amachita tero. Mu United States, kusudzulana kwawirikiza kuposa katatu mkati mwa zaka 25 zapitazo kufika ku mlingo woposa wa miliyoni imodzi chaka chirichonse. Mkati mwa nyengo ya zaka 20 kuchokera mu 1965, zisudzulo mu Britain zinawirikiza kanayi, kuchokera pa 41,000 kufikira pa 175,000. Mbeta zimakhumba kugwirizana ndi mbeta za chiŵalo chirichonse, ndipo ambiri amayenda kuchokera kwa uyu kupita kwa uyo. Iwo amachitira chisoni matenda opatsirana mwa kugonana, moposerapo AIDS, yomwe imafalikira monga chotulukapo cha kakhalidwe kawo ka chisembwere koma amapitirizabe kuwumirira pa kachitidwe kawo konyonyotsoka ka kugonana. Atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko sanalange ziŵalo za tchalitchi zochimwa. Ku utali umene iwo amwetulira pa chisembwere, iwo afunikiranso kugawana thayo kaamba ka kututa kwa tsoka kumeneko.—Yeremiya 5:29-31.
16. (a) Nchiyani chomwe chimawunikira chenicheni chakuti Babulo Wamkulu wagwa, ndipo ndi kufuula kotani kwa mngelo pa Chibvumbulutso 18:2 komwe kuli koyenerera? (b) Onse amene amafuna kupulumuka mathedwe a dziko ayenera kuchita chiyani?
16 Mkhalidwe womvetsa chisoni wa makhalidwe mu ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga umawunikiranso chenicheni chakuti Babulo Wamkulu wagwa. Mulungu wamuweruza iye ndipo wazindikiritsa iye kaamba ka chiwonongeko. Ndi koyenerera chotani nanga, kenaka, mmene kuliri kufuula kwa mawu amphamvu a mngelo pa Chibvumbulutso 18:2: “Wagwa, wagwa, Babulo Wamkulu, nasandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.” Ndipo ndi chofunika chotani nanga kuti onse omwe amafuna kupulumuka mapeto a dziko achitepo kanthu tsopano m’kuyankha ku chiitano mu versi 4, (NW): “Tulukani mwa iye, anthu anga, ngati simufuna kugawana naye machimo ake, ndipo kuti ngati simufuna kulandira mbali ya miliri yake”! Kutuluka m’chipembedzo chonyenga liri sitepi lofunika koposa kulinga ku kupulumuka “chisautso chachikulu” chomwe chiri patsogolopa. (Chibvumbulutso 7:14) Koma zambiri zimafunikira, monga momwe tidzawonera!
[Mawu a M’munsi]
a Pa November 1, 1903, kutsatira chotsirizira cha mpambo wa kukambitsirana pa Carnegie Hall, Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A., pakati pa Charles T. Russell ndi Dr. E. L. Eaton, mmodzi wa atsogoleri ansembe opezekapo anavomereza chilakiko cha Mbale Russell, akumanena kuti: “Ndiri wosangalala kukuwonani mukusinthira paipi ya madzi pa helo ndi kuzima motowo.”
[Bokosi patsamba 8]
MAKHALIDWE A ATSOGOLERI A CHIPEMBEDZO
“Ana mazana angapo omwe aipitsidwa ndi ansembe a Chikatolika mu United States mkati mwa zaka zisanu zapitazo avutika ndi matenda owopsya a maganizo, akutero makolo, akatswiri a zamaganizo, nduna za apolisi ndi maloya ophatikizidwa m’milanduyo.”—Akron Beacon Journal, January 3, 1988.
“Tchalitchi cha Roma Katolika mu United States chakakamizidwa kulipira mamiliyoni angapo a madola m’kuvulaza ku mabanja omwe amawumirira kuti ana awo aipsyidwa mwakugonana ndi ansembe. Mosasamala kanthu za chimenecho, mavuto akula moipitsitsa kotero kuti maloya ambiri ndi minkhole amanena kuti tchalitchi chimanyalanyaza ndi kuphimba milandu yoteroyo.”—The Miami Herald, January 3, 1988.
[Zithunzi patsamba 6]
Mafano a milungu itatu—kuchokera ku Igupto wakale ndi Chikristu cha Dziko
[Mawu a Chithunzi]
Saint-Remi Museum collection, Reims, photo by J. Terrisse
Louvre Museum, Paris
[Chithunzi patsamba 9]
Baibulo limafananitsa atsogoleri a chipembedzo a chisembwere ku nkhumba yosamba yomwe imabwerera kukunkhulika m’thope