Yendani Monga Olangizidwa ndi Mulungu
“Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, . . . kuti iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake.”—MIKA 4:2.
1. Malinga ndi Mika, kodi nchiyani chimene Mulungu akachitira anthu ake m’masiku otsiriza?
MNENERI wa Mulungu Mika analosera kuti ‘m’masiku otsiriza,’ m’nthaŵi yathu, anthu ambiri adzafunafuna Mulungu mokangalika, kuti amlambire. Iwowa akalimbikitsana wina ndi mnzake, akumati: “Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, . . . kuti iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake.”—Mika 4:1, 2.
2, 3. Kodi kulosera kwa Paulo ponena za anthu okonda ndalama kukukwaniritsidwa motani lerolino?
2 Kuphunzira kwathu 2 Timoteo 3:1-5 kungatithandize kuona zotulukapo za kulangizidwa ndi Mulungu ‘m’masiku otsiriza.’ M’nkhani yapitayo, tinayamba mwa kuona mapindu obwera kwa awo amene amalabadira chenjezo la Paulo la kusakhala “odzikonda okha.” Paulo anawonjezera kuti m’nthaŵi yathu anthu akakhalanso “okonda ndalama.”
3 Munthu satofunikira kukhala ndi madigiri akukoleji m’mbiri yamakono kuti azindikire mmene mawuwo akuyenererana ndendende ndi nthaŵi zathu. Kodi simunaŵerenge za eni malonda ndi akuluakulu a makampani amene ali osakhutiritsidwa ndi kupeza ndalama mamiliyoni ambirimbiri chaka chilichonse? Okonda ndalama ameneŵa akufunabe zowonjezereka, ndipo ngakhale mwa njira zoswa lamulo. Mawu a Paulo akuyenereranso ambiri lerolino amene, ngakhale kuti sali olemera, ali osirira mofananamo, osakhutira konse. Mungakhale mukudziŵa ambiri otero m’dera lanulo.
4-6. Kodi ndimotani mmene Baibulo limathandizira Akristu kupeŵa kukhala okonda ndalama?
4 Kodi zimene Paulo anatchula zangokhala mkhalidwe wosapeŵeka wa chibadwa cha munthu? Osati malinga ndi kunena kwa Mlembi Wamkulu wa Baibulo, amene kalekalelo ananena chowonadi ichi: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” Onani kuti, Mulungu sananene kuti, ‘Ndalama ndizo muzu wa zoipa zonse.’ Iye anati chili “chikondi cha pa ndalama.”—1 Timoteo 6:10.
5 Mokondweretsa, nkhani yozungulira mawu a Paulo imavomereza kuti Akristu ena abwino m’zaka za zana loyamba anali olemera m’dongosolo la zinthu lilipoli, kaya chuma chawo chinali cha choloŵa kapena chodzipezera. (1 Timoteo 6:17) Motero, kuyenera kukhala koonekeratu kuti mosasamala kanthu kuti mkhalidwe wathu wachuma uli wotani, Baibulo limachenjeza za ngozi ya kukhala wokonda ndalama. Kodi Baibulo limapereka chilangizo chowonjezereka ponena za kupeŵa chifooko chatsoka ndi chofala chimenechi? Ndithudi limatero, monga ngati mu Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu. Nzeru yake njotchuka padziko lonse. Mwachitsanzo, onani zimene Yesu ananena pa Mateyu 6:26-33.
6 Monga kwalembedwa pa Luka 12:15-21, Yesu analankhula za mwamuna wachuma amene anapitirizabe kukundika chuma chochuluka koma anataya moyo wake mwadzidzidzi. Kodi mfundo ya Yesu inali yotani? Iye anati: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” Limodzi ndi uphungu umenewu, Baibulo limatsutsa ulesi ndipo limagogomezera phindu la ntchito yowona mtima. (1 Atesalonika 4:11, 12) Eya, ena angatsutse kuti ziphunzitso zimenezi sizigwira ntchito m’nthaŵi zathu—koma izo zimatero, ndipo zimapambanadi.
Analangizidwa Napindula
7. Kodi tili ndi chifukwa chotani chokhalira ndi chidaliro chakuti tikhoza kugwiritsira ntchito mwachipambano uphungu wa Baibulo wonena za chuma?
7 M’mitundu yambiri, mungapeze zitsanzo zenizeni za amuna ndi akazi a pamalo aliwonse m’chitaganya ndi m’zachuma amene agwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe aumulungu ameneŵa onena za ndalama. Iwo apindula okha limodzi ndi mabanja awo, monga momwe ngakhale akunjanso angaonere. Mwachitsanzo, m’buku lakuti Religious Movements in Contemporary America, lolembedwa ndi wofalitsa wa Yunivesite ya Princeton, katswiri wa mafuko a anthu analemba kuti: “M’zofalitsidwa [za Mboni] ndi m’nkhani za mu mpingo izo zimakumbutsidwa kuti sizimadalira pa galimoto zatsopano, zovala zamtengo, kapena moyo wolemerera kuti zizindikiridwe. Panthaŵi imodzimodziyo Mboni iyenera kupereka ntchito yokwanira ya tsiku kwa woilemba ntchito [ndipo iyenera] kukhala yowona mtima kotheratu . . . Mikhalidwe yoteroyo imapangitsa ngakhale munthu wopanda maluso ambiri kukhala wantchito wofunika, ndipo Mboni zina ku North Philadelphia [U.S.A.] zakwezedwa pantchito zawo.” Mwachionekere, anthu amene amvera chilangizo chochokera kwa Mulungu kudzera m’Mawu ake achenjezedwa ponena za mikhalidwe yamaganizo imene imakuchititsa kukhala kovuta kwambiri kulimbana ndi mikhalidwe yamakono. Zimene zachitika kwa iwo zimatsimikizira kuti chilangizo cha Baibulo chimatsogolera ku moyo wabwinopo ndi wachimwemwe chokulirapo.
8. Kodi nchifukwa ninji “odzitamandira,” “odzikuza,” ndi “amwano” angagwirizanitsidwe, ndipo kodi mawu atatuŵa amatanthauzanji?
8 Tikhoza kugwirizanitsa pamodzi zinthu zitatu zotsatira zimene Paulo akundandalika. M’masiku otsiriza, anthu adzakhala “odzitamandira, odzikuza, amwano.” Mikhalidwe itatu imeneyi siyofanana, koma yonse imakhudza kunyada. Woyamba ndiwo ‘kudzitamandira.’ Dikishonale limatiuza kuti liwu loyambirira Lachigiriki panopo limatanthauza: “‘Munthu amene amadzikweza kupitirira pamalo pake,’ kapena ‘amene amalonjeza zoposa zimene angathe kuchita.’” Mukhoza kuzindikira chifukwa chake Mabaibulo ena amagwiritsira ntchito liwu lakuti “kudzitukumula.” Wotsatira ndiwo ‘kudzikuza,’ kapena kumasulira mwachindunji “maonekedwe apamwamba.” Womalizira, “mwano.” Ena angalingalire amwano kukhala awo amene amalankhula motonza Mulungu, koma liwu lake lenileni limaphatikizapo mawu opweteka, onyoza, kapena otukwana oneneza anthu ena. Chotero Paulo akunena za mwano wochitidwa kwa Mulungu ndi munthu yemwe.
9. Mosiyana ndi mikhalidwe yamaganizo yofala yovulaza, kodi ndi mikhalaidwe yamaganizo yotani imene Baibulo limalimbikitsa anthu kukulitsa?
9 Kodi mumamva bwanji ngati muli pakati pa anthu oyenerera malongosoledwe a Paulo, kaya akhale ogwira nawo ntchito, anzanu akusukulu, kapena achibale anu? Kodi kumachititsa moyo wanu kukhala wabwinopo? Kapena kodi anthu oterowo amavutitsa moyo wanu, akumachititsa kukhala kovuta kwa inu kulimbana ndi nthaŵi zathuzi? Komabe, Mawu a Mulungu amatiphunzitsa kupeŵa mikhalidwe yamaganizo yotero, akumapereka chilangizo chopezeka pa 1 Akorinto 4:7; Akolose 3:12, 13; ndi Aefeso 4:29.
10. Kodi nchiyani chimasonyeza kuti anthu a Yehova apindula mwa kuvomereza chilangizo cha Baibulo?
10 Ngakhale kuti Akristu ali opanda ungwiro, kugwiritsira ntchito kwawo chilangizo chabwino chimenechi kumawathandiza kwambiri m’nthaŵi zino zoŵaŵitsa. Magazini Achitaliyana akuti La Civiltà Cattolica ananena kuti chimodzi cha zifukwa zimene Mboni za Yehova zikupitirizira kuwonjezereka “nchakuti gululo limapangitsa ziŵalo zake kukhala ndi chizindikiro choyenera ndi champhamvu.” Komabe, kodi mwa kunena kuti “chizindikiro champhamvu,” wolembayo anatanthauza kuti iwo ali “odzitamandira, odzikuza, amwano”? Mosiyana ndi zimenezo, magazini Achijesuit akunena kuti gululo “limapangitsa ziŵalo zake kukhala ndi chizindikiro choyenera ndi champhamvu, ndipo ndicho malo awo kumene amalandirana ndi manja aŵiri ndi mzimu waubale ndi chigwirizano.” Kodi sizoonekeratu kuti zinthu zimene Mboni zaphunzitsidwa zikuzithandiza?
Chilangizo Chipindulitsa Ziŵalo za Banja
11, 12. Kodi Paulo anasonyeza molondola kuti mkhalidwe m’mabanja ambiri ukakhala wotani?
11 Tingaphatikize pamodzi zinthu zinayi zotsatira, zimene zili zogwirizana mwanjira ina. Paulo ananeneratu kuti mkati mwa masiku otsiriza, ambiri akakhala “osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe.” Mumadziŵa kuti ziŵiri za zifooko zimenezi—kukhala wosayamika ndi wosayera mtima—nzofala kwambiri. Chikhalirechobe, tikhoza kuona mosavuta chifukwa chake Paulo anaziika pakati pa kukhala “osamvera akuwabala” ndi “opanda chikondi chachibadwidwe.” Zinayizi zimaloŵerana.
12 Kwenikweni munthu aliyense woona bwino zinthu, wachichepere kapena wachikulire, ayenera kuvomereza kuti kusamvera makolo nkwakukulu, ndipo kukukulirakulira. Makolo ambiri amadandaula kuti achichepere akuonekera kukhala osayamikira pa zonse zimene amawachitira. Achichepere ambiri amakana kuti makolo awo sali okhulupirika kwenikweni kwa iwo (kapena kwa banja lonselo) koma amangosamala za ntchito zawo, zokondweretsa, kapena iwo okha basi. M’malo moyesa kuloza chala amene angakhale wolakwa, tiyeni tiyang’ane pa zotulukapo zake. Kusamvana pakati pa achikulire ndi achichepere kaŵirikaŵiri kumapangitsa achichepere kudzipangira muyezo wawo wa makhalidwe abwino, kapena oipa. Kodi chotulukapo chimakhala chiyani? Kukwera kochititsa mantha kwa mimba za atsikana, kutaya mimba, ndi matenda opatsirana mwa kugonana. Kaŵirikaŵiri, kusoŵeka kwa chikondi chachibadwidwe panyumba kumachititsa chiwawa. Mwinamwake inuyo mukhoza kusimba zitsanzo za m’dera lanu, umboni wakuti chikondi chachibadwidwe chikuzimiririka.
13, 14. (a) Poona kunyonyotsoka kwa mabanja ambiri, kodi nchifukwa ninji tiyenera kulabadira Baibulo? (b) Kodi ndichilangizo chanzeru chotani chimene Mulungu amapereka ponena za moyo wa banja?
13 Zimenezi zingasonyeze chifukwa chake anthu owonjezerekawonjezereka amaukira ena amene kale anali achibale awo, a fuko lawo, mtundu, kapena gulu. Komabe, kumbukirani kuti sitikutchula zimenezi ndi cholinga chogogomezera zoipa zokhazokha za moyo wa lerolino. Mfundo zathu zazikulu ziŵiri nzakuti: Kodi ziphunzitso za Baibulo zingatithandize kupeŵa kuvutika kochititsidwa ndi zifooko zimene Paulo anandandalika, ndipo kodi tidzapindula mwa kugwiritsira ntchito ziphunzitso za Baibulo m’miyoyo yathu? Mayankho angakhale akuti inde, monga momwe zikuonedwera ponena za mfundo zinayizo m’ndandanda ya Paulo.
14 Chifukwa nchomvekera bwino chonenera kuti: Palibe chiphunzitso china chilichonse chimene chingapambane cha Baibulo m’kupangitsa moyo wa banja kukhala wosangalatsa mtima ndi wachipambano chabwino. Zimenezi zimatsimikiziridwa ndi chitsanzo cha uphungu wake umene ungathandize ziwalo za banja kusapeŵa chabe mbuna komanso kukhala ndi chipambano. Lemba la Akolose 3:18-21 limasonyeza zimenezo bwino lomwe, ngakhale kuti palinso ndime zambiri zabwino ndi zogwira ntchito zonena za amuna, akazi, ndi ana. Chilangizo chimenechi chimagwiradi ntchito m’tsiku lathu. Zowona, ngakhale m’mabanja a Akristu owona, mumakhala zovuta ndi zitokoso. Komabe, zotulukapo zazikulu zimasonyeza kuti Baibulo limapereka chiphunzitso chothandiza kwambiri ku mabanja.
15, 16. Kodi ndimkhalidwe wotani umene wofufuza wina anapeza pofufuza za Mboni za Yehova m’Zambia?
15 Kwa chaka chimodzi ndi theka, wofufuza wina wamkazi wochokera ku Yunivesite ya Lethbridge, ku Canada, anafufuza moyo wa anthu m’Zambia. Iye anati: “Mboni za Yehova zimakhala ndi chipambano chachikulu kuposa ziŵalo za zipembedzo zina m’kusunga maukwati awo. . . . Chipambano chawo chimasonyeza unansi wowongoleredwa pakati pa mwamuna ndi mkazi, amene, m’zochita zawo zatsopano, popanda mantha, ndipo mogwirizana, amakhala oŵerengeredwa mlandu mmene amachitira kwa wina ndi mnzake kwa mutu watsopano, Mulungu. . . . Mwamuna amene ali Mboni ya Yehova amaphunzitsidwa kudziŵa kuchita thayo lake la kusamalira bwino mkazi wake ndi ana ake. . . . Mwamuna ndi mkazi amalimbikitsidwa kukhala ndi umphumphu . . . Kufunika kwakukulu kwa umphumphu kumeneku kumalimbitsa ukwati.”
16 Kupenda kumeneko kunazikidwa pa zochitika zenizeni zambiri. Mwachitsanzo, wofufuza ameneyu ananena kuti mosiyana ndi mkhalidwe wofala, “amuna amene ali Mboni za Yehova amapezedwa kaŵirikaŵiri akuthandiza akazi awo m’minda, osati panthaŵi yakupha mphanje yokha, komanso polima ndi pobzala.” Chotero, kuli koonekeratu kuti zokumana nazo zambiri kuzungulira dziko lonse zimasonyeza kuti chilangizo cha Baibulo chimaumba miyoyo.
17, 18. Kodi nzotulukapo zodabwitsa zotani zimene zinaoneka m’kufufuza mkhalidwe wa chipembedzo ndi kugonana kwa osakwatira?
17 Nkhani yapitayo inatchula zopeza za m’magazini ya Journal for the Scientific Study of Religion. Mu 1991 iyo inali ndi nkhani ya mutu wakuti “Mwambo wa Chipembedzo ndi Kugonana Usanakwatire: Umboni Wochokera kwa Achinyamata Okhwima a Mtundu Wonse.” Muyenera kuti mukudziŵa mmene kugonana usanakwatire kwakhalira kowanda kwambiri. Pausinkhu waung’ono ambiri amagonjera ku chilakolako chakugonana, ndipo achinyamata ambiri ali ndi ogonana nawo oposa mmodzi. Kodi ziphunzitso za Baibulo zingathe kusintha zimenezi?
18 Maprofesa atatu amene anafufuza nkhaniyo anayembekezera kupeza kuti ‘achichepere omasinkhuka ndi achinyamata okhwima okulira m’mwambo Wachikristu wosalekerera kwambiri ayenera kukhala asanachitepo kugonana asanakwatire.’ Koma kodi maumboni anasonyezanji? Onse pamodzi, pakati pa 70 peresenti ndi 82 peresenti anachitapo kugonana asanakwatire. Kwa ena “kusunga mwambo [kunachepetsapo] kuthekera kwa kugonana asanakwatire, koma osati ponena za ‘kugonana kwa achichepere osakwatira.’” Ofufuzawo anapereka ndemanga zonena za achichepere amene anachokera m’mabanja oyenera kukhala achipembedzo “amene anaonetsa kuthekera kwakukulu kwa kugonana asanakwatire powayerekezera ndi Aprotestanti enieni.”—Kanyenye ngwathu.
19, 20. Kodi ndimotani mmene chilangizo cha Mulungu chathandizira ndi kutetezera achichepere ambiri pakati pa Mboni za Yehova?
19 Maprofesawo anapeza zosiyana pakati pa achichepere a Mboni za Yehova, amene anali pakati pa “gulu losiyana koposa ndi ena.” Chifukwa ninji? “Ukulu wa kudzipereka ndi kutengera makhalidwe abwino mwa kuchita zinthu, mwa kukhala ndi ziyembekezo, ndi kudziloŵetsa m’zochitika zachipembedzo . . . zingakulitse kwambiri kumamatira ku malamulo a mkhalidwe a chikhulupiriro.” Iwo anawonjezera kuti: “Mboni zimayembekezeredwa kukwaniritsa mathayo akulalikira monga achichepere omasinkhuka ndi achinyamata okhwima.”
20 Chotero, chilangizo cha Baibulo chinayambukira Mboni za Yehova mozipindulitsa mwa kuzithandiza kupeŵa makhalidwe achisembwere. Zimenezo zimawatetezera ku matenda opatsirana mwa kugonana, ena amene ali osachiritsika ndipo ena akupha. Kumatanthauza kupeŵa kutaya mimba, kumene Baibulo limaphunzitsa kuti kuli kolingana ndi kupha kwenikweniko. Kumatanthauzanso kukhala ndi achinyamata okhwima amene amaloŵa ukwati ndi chikumbumtima choyera. Zimenezo zimatanthauzanso kukhala ndi maukwati omangidwa pa maziko olimba. Zili ziphunzitso zotero zimene zingatithandize kulimbana nazo, kukhala athanzi labwinopo, ndi achimwemwe chokulirapo.
Chilangizo Chopindulitsa
21. Kodi ndizinthu zotani zimene Paulo ananeneratu molondola ponena za nthaŵi yathu?
21 Tsopano bwererani pa 2 Timoteo 3:3, 4, ndi kuona zina zimene Paulo anati zikapangitsa nthaŵi zathu kukhala zovuta kuchita nazo kwa ambiri—koma osati kwa onse: “[Anthu akakhala] osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima [ndi] okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” Ha, nzowona chotani nanga zimenezo! Komabe, chilangizo chochokera m’Baibulo chikhoza kutitetezera ndi kutikonzekeretsa kulimbana nazo ndi kupambana.
22, 23. Paulo anamaliza ndandanda yake ndi chilangizo chopindulitsa chotani, ndipo kodi nchofunika motani?
22 Mtumwi Paulo akumaliza ndandanda yakeyo ndi mfundo yopindulitsa. Iye akusintha mbali yotsirizirayo kukhala lamulo laumulungu limene lingatipatsenso phindu losayerekezereka. Paulo akutchula awo “akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.” Kumbukirani kuti achichepere m’matchalitchi ena ali m’ziŵerengero za kugonana asanakwatire zapamwamba kwambiri. Eya, ngakhale ngati chisembwere cha opita ku tchalitchiwo chikanakhala pamlingo wocheperapo, kodi zimenezo sizikanakhalabe umboni wakuti kulambira kwawo nkopanda mphamvu? Ndiponso, kodi ziphunzitso za chipembedzo zimasintha mmene anthu amachitira m’malonda, mmene amachitira kwa amene amawalamulira, mmene amachitira ndi achibale awo?
23 Mawu a Paulo amasonyeza kuti tiyenera kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu, tikumakhala ndi njira yakulambira imene imasonyeza mphamvu yeniyeni ya Chikristu. Ponena za awo amene kulambira kwawo kuli kopanda mphamvu, Paulo akutiuza kuti: “Kwa iwonso udzipatule.” Limenelo ndilamulo lomvekera bwino, limene lidzatidzetsera mapindu otsimikizirika.
24. Kodi ndimotani mmene chenjezo la m’Chivumbulutso chaputala 18 limagwirizanira ndi uphungu wa Paulo?
24 Kodi lidzatipindulitsa motani? Eya, buku lomalizira la Baibulo limasonyeza mkazi wophiphiritsira, mkazi wachigololo, wotchedwa Babulo Wamkulu. Umboni umasonyeza kuti Babulo Wamkulu amaimira ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, umene Yehova Mulungu waupenda ndi kuukana. Komabe, ife sitiyenera kuphatikizidwa mmenemo. Lemba la Chivumbulutso 18:4 limachenjeza kuti: “Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.” Kodi umenewo sindiwo uthenga umodzimodzi umene Paulo anapereka, “kwa iwonso udzipatule”? Kulabadira kwathu kuli njira ina imene ingatipangitse kupindula ndi chilangizo cha Mulungu.
25, 26. Kodi awo amene amavomereza ndi kugwiritsira ntchito chilangizo cha Yehova Mulungu tsopano ali ndi mtsogolo motani?
25 Posachedwapa Mulungu adzaloŵerera mwachindunji m’nkhani za anthu. Iye adzafafaniza chipembedzo chonyenga chonse ndipo dongosolo la zinthu loipa lonseli. Chimenecho chidzakhaladi chifukwa chosangalalira, monga momwe lemba la Chivumbulutso 19:1, 2 limasonyezera. Padziko lapansi, awo amene amavomereza ndi kulondola chilangizo cha Mulungu adzaloledwa kupitirizabe kulondola ziphunzitso zake pamene zopinga za nthaŵi zoŵaŵitsa zino zidzakhala zitachoka.—Chivumbulutso 21:3, 4.
26 Kukhala ndi moyo m’Paradaiso wobwezeretsedwa wa padziko lapansi ameneyo kudzakhala kokondweretsa moti sititha kukuyerekezera. Mulungu akulonjeza kuti kuli kotheka kwa ife, ndipo tikhoza kumdalira iye kotheratu. Motero iye akutipatsa zifukwa zochuluka zolandirira ndi kutsatira chiphunzitso chake chothandiza. Liti? Tiyeni titsatire malangizo ake tsopano m’nthaŵi zathu zino zoŵaŵitsa mpaka kuloŵa m’Paradaiso amene iye walonjeza.—Mika 4:3, 4.
Mfundo Zosinkhasinkhapo
◻ Kodi anthu a Yehova apindula motani ndi uphungu wake wonena za chuma?
◻ Kodi magazini a Chijesuit anapereka umboni wa zotulukapo zabwino zotani zochokera kwa atumiki a Mulungu mwa kugwiritsira ntchito Mawu ake?
◻ Kodi kufufuza kochitidwa m’Zambia kunavumbula mapindu otani pa mabanja omwe amagwiritsira ntchito chilangizo chaumulungu?
◻ Kodi ndichitetezo chotani chimene chilangizo chaumulungu chimapereka kwa achichepere?
[Bokosi patsamba 15]
NDI MPHOTHO YATSOKA CHOTANI NANGA!
“Azaka za 13 mpaka 19 ali pangozi yaikulu yotenga AIDS chifukwa chokonda kugonana ndi mankhwala oledzeretsa, akumayesa mwaŵi ndi kukhalira moyo chisangalalo cha panthaŵiyo, ndi chifukwanso chakuti amaona ngati kuti sangafe namanyalanyaza lamulo,” likutero lipoti loperekedwa pamsonkhano wonena za AIDS ndi azaka za 13 mpaka 19.—New York Daily News, Sunday, March 7, 1993.
“Atsikana azaka za 13 mpaka 19 omwerekera m’zakugonana akuonekera kukhala gulu lachiŵiri ‘potsogolera’ ndi mliri wa AIDS, kwapezedwa motero ndi kufufuza kwa Mitundu Yogwirizana kochitidwa mu Ulaya, Africa ndi Kummwera koma Chakummaŵa kwa Asia.”—The New York Times, Friday, July 30, 1993.
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Chilangizo cha Baibulo chimapindulitsa Mboni za Yehova mumpingo ndi panyumba