Chaputala 6
Kudikira Mkati mwa “Mapeto a Dongosolo la Zinthu”
1. Kodi nchifukwa ninji tifunikira kukhala odikira?
TIRI mkati mwenimweni mwa “mapeto a dongosolo la zinthu,” koma ‘sitidziŵa tsiku ndi nthaŵi yake’ pamene nthaŵi ya kuunika kopulumutsa moyo idzatha. Ndicho chifukwa chake Yesu anati: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.”—Mateyu 24:3; 25:13.
2. Kodi ndichokumana nacho chomvetsa chisoni chotani chimene chiyenera kupeŵedwa?
2 Ndithudi kukakhala kotayitsa mtima kwa munthu ngati anafika mochedwa pamalo a phwando laukwati napeza khomo litatsekedwa. Chikhalirechobe ndizo zimene zaikidwiratu kugwera anthu ambiri odzinenera kukhala Akristu mtsogolo pafupi. “Kalonga wa Mtendere,” anafotokoza zimenezi mwafanizo mwa mawu aŵa: “Pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayanakha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziŵani.”—Mateyu 25:11, 12.
3. (a) Kodi chaka cha 1919 chinatsimikizira kukhala nthaŵi ya chiyani? (b) Kodi olambira a Dziko Lachikristu akhala okhoza kugaŵira mafuta auzimu ofunikawo?
3 Chiyambire 1919 kuunika kwauzimu koperekedwa ndi ochenjera mwa chithandizo cha “mafuta” a Mawu a Yehova ndi mzimu woyera zapezeka, koma opusa amayesa kugula mafuta auzimu kwa anthu a m’Dziko Lachikristu amene amanena kuti amawagulitsa. (Mateyu 25:9) Komabe, achipembedzo cha Dziko Lachikristu, alibe mtundu woyenerera wa mafuta. Iwo akhala osakhoza kupereka kuunika konena za kukhalapo kwa Yesu Kristu monga Mkwati wakumwamba. Iwo amayembekezera kuti pamene amwalira adzapita kumwamba nthaŵi yomweyo ndi kukakumana naye popanda kukhala atagaŵanamo m’ntchito yopereka kuunika mkati mwa ‘mapeto ameneŵa a dongosolo la zinthu.’
4. Kufikira tsopano, kodi ophiphiritsiridwa ndi anamwali opusa alephera kuchita chiyani, ndipo chifukwa ninji?
4 Kumbali ina, pakhala awo amene, mofanana ndi anamwali auzimu, atsimikizira kukhala ndi mafuta osungidwa a mzimu woyera ndi Mawu a Mulungu kaamba ka ntchito ya pambuyo pa nkhondo ya kuunikira kwa padziko lonse lapansi ponena za “ufumu.” (Mateyu 24:14) Ophiphiritsiridwa kukhala anamwali opusa m’fanizo la Yesu sakugaŵanamo mwa kulola kuunika kwawo kuŵalira pambiri yabwino imeneyi yofunika pamitundu yonse. Iwo analibe “mafuta” a Mawu a Mulungu ounikira ndi mzimu wake woyera, ndipo Woweruza amenenso ali Mkwati anazindikira kulephera kwawo kumeneku ali m’kachisi wauzimu. Mitima yawo siinatsimikizire kukhala pantchito imene inatengedwa kukhala yofulumira mu 1919 ndi anamwali Achikristu amene anali anzeru m’kuzindikira ponse paŵiri nthaŵi ndi ntchito.
5. Kodi anamwali opusa amalephera kukhala ndi mbali m’chiyani chimene chiri chofunika ku kukhala kwawo ogwirizanitsidwa ndi Mkwati Mfumuyo?
5 Mwa kudzilekanitsa kwa awo amene anali kuchirikiza gulu lowoneka la Yehova, opusawo anali kulephera kukhala ndi phande m’kuchitira umboni Ufumu kwa padziko lonse lapansi. Potsirizira pake iwo anapeza “mafuta” a kuunika kwa chipembedzo, koma iwo sanali mafuta a mtundu woyenera. Iwo sanapereke kuunika kaamba ka chochitika choyenerera panthaŵi yoyenerera. Motero iwo sakulalikira uthenga wa Ufumu ndi “tsiku la kubwezera la Mulungu wathu.” (Yesaya 61:1-3) Iwo sakutamanda Mfumuyo amenenso ali Mkwati monga momwe otsalira odzozedwa a kagulu ka anamwali akuchitira.
Chotulukapo cha Kuunika kwa Nyali Pakati pa Usiku
6, 7. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika cha pakati pa ma 1930, chimene chinapereka lingaliro lakuti panali anamwali okwanira kumaliza mamembala a kagulu kamkwatibwi? (b) Kodi chisamaliro chinalunjikitsidwa pa kagulu kati tsopano kamene kanafunikira kusonkhanitsidwa?
6 Pakati pa ma 1930, chinthu china chapadera chinachitika. Chimene chinachitika chinapereka lingaliro lakuti mamembala a mkwati wauzimu wa Kristu anakwana, kuti padziko lapansi panali ophunzira obadwa ndi mzimu okwanira a Mkwati kupanga chiŵerengero chokwanira cha mkwatibwi wake wakumwamba.
7 Panthaŵi imeneyo, mu 1935, chisamaliro chinayamba kusumikidwa pa kagulu kena ka ophunzira onga nkhosa a Yesu. Kameneka kanali kagulu kamene kanasonyezedwa kwa anthu onse mkati mwa nkhondo yoyamba ya dziko. Panali pa February 24, 1918, pamene nkhani yokhala ndi mutu wakuti “Mamiliyoni Amoyo Tsopano Sangamwalire Konse” inakambidwa kwa omvetsera achidwi, ndipo mwinamwake okaikira. Pamsonkhano wa Mboni za Yehova wa mu 1935 m’Washington, D.C., kanthu kena kotsimikizirika kanayambitsidwa ponena za kusonkhanitsidwa kwa mamiliyoni ameneŵa a “nkhosa zina” za Kristu kukhala ‘m’gulu’ logwirizanitsidwa mwa Yesu Kristu monga “mbusa mmodzi.” (Yohane 10:16) Kulongosoledwa kwa gulu la “nkhosa zina” monga momwe kudanenedweratu m’Chivumbulutso 7:9-17 kunaululidwa.
8. Kodi ndithayo losayembekezeredwa kwa iwo lotani, limene anamwali ochenjera anakhala nalo mu 1935?
8 Tsopano otsalira a “kagulu ka nkhosa” anakhala ndi thayo la kuyamba kusonkhanitsidwa kwa “khamu lalikulu” limeneli la “nkhosa zina.” (Luka 12:32) Zimenezi zinali chifukwa chakuti chiŵerengero cha anamwali ochenjera chofunika kumalizira mkwatibwi wa Yesu tsopano chinakwaniritsidwa. Koma anamwali amenewo sanatengeredwe mwadzidzidzi kumwamba. Iwo afunikira kuloŵetsedwa m’chipinda chochitira phwando kumwamba pamene amaliza njira yawo ya padziko lapansi monga mboni zosunga umphumphu za Mulungu wawo, Yehova. Chifukwa cha ntchito yawo yokhulupirika ya kuunikira kufikira 1935, iwo analoŵetsedwa m’mwaŵi wapadera umene sanayembekezerepo ndi kale lonse zisanafike zaka za pakati pa ma 1930.
9. Kodi ndiangati lerolino amene ali otsala a anamwali ochenjera?
9 Papita zaka zoposa makumi asanu chiyambire 1935, ndipo mkati mwa zaka zimenezi chiŵerengero cha kagulu ka anamwali ochenjera chakhala chikuchepa. Kumbali ina, ntchito yochitira umboni yawonjezereka kufikira milingo ya dziko lonse, inde, kuphatikizapo maiko enieni oposa 200. Pakali pano, kagulu ka anamwali kachepa kukhala chiŵerengero cha pafupifupi 9 000.
Atsamwali Othandiza a Onyamula Kuunika
10. Chifukwa cha kukula kwa ntchito, kodi otsalira a anamwali ochenjera ngwokhoza kukwaniritsa zofunika za antchito?
10 Otsalira odzozedwa a anamwali ophiphiritsira achititsidwa kuwonekera poyera kwambiri ndi ofalitsa a Ufumu oposa mamiliyoni atatu m’mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 49 000 kuzungulira padziko lapansi. Kodi ndimotani mmene chiŵerengero chaching’ono cha otsalira odzozedwa chingasamalirire ntchito yochitira umboni m’maiko oposa 200 kumene mipingo zikwi zambiri imeneyo iri? Iwo sakanatha.
11. (a) Kodi kusonyezedwa kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kunachititsa kuchitika kwa chiyani mkati mwa odzinenera kukhala anamwali? (b) Kodi nchiyani chimene a kagulu ka “kapolo woipa” ali osakhoza kuzindikira chifukwa cha kusoŵa kuunika kwauzimu?
11 Ndithudi, mogwirizana ndi Malemba amatumikira m’malo antchito onenedweratuwo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene Mbuye ndi Mkwati anampeza kukhala wokhulupirika pakudza kwake ku kachisi kudzapereka chiweruzo. Panali panthaŵi imeneyo pamene kulekana kunayamba kuchitika pakati pa anamwali ochenjera ndi anamwali opusa a kagulu ka anamwali ophiphiritsira. Owonongedwa kukhala kagulu ka “kapolo woipa” alibe mafuta a Mawu ounikira a Mulungu ndi mzimu wake woyera m’nsupa zawo kuti aunikire nyali zawo. Motero iwo analibe kuunika kokwanira kwauzimu kuti azindikire “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” limene liri kusonkhanitsidwa kale chiyambire 1935 monga mbali ya “gulu limodzi.”—Mateyu 24:45-51.
12. Kodi ndani amene akhala atsamwali a ponda apa mpondepo a otsalira a kagulu ka mkwatibwi?
12 Chiyambire Nkhondo Yadziko II, kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wa “mapeto a dongosolo la zinthu,” kwakukulukulu kukuchitika chifukwa cha mbali imene “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” likuchita. Kuunika kochokera kunyali zounikidwa za otsalira kwaŵalitsira m’maso a mitima yawo, ndipo athandizidwa kusonyeza kuunikako kwa ena amene akali chikhalirebe mu mdima wa dziko lino. (Yerekezerani ndi Aefeso 1:18.) Iwo athandiza mamiliyoni ambiri a nzika za dziko lino lapansi kuzindikira kukhalapo kwa Mkwati Mfumuyo pamene tsiku la ukwati wake ndi kagulu kamkwatibwi kokwanira liyandikira. Iwo afikira kukhala atsamwali a ponda apa mpondepo a otsalira a kagulu ka mkwatibwi.
13, 14. (a) Kodi ndimkhalidwe wokondweretsa wotani ponena za atsamwali a otsalira umene walongosoledwa mwafanizo m’Chivumbulutso 7:9, 10? (b) Kodi nchiyani chimene chinali kulabadira kwa mwamsanga kwa malongosoledwe a ulosi umenewo?
13 Chiyambire 1935 mkhalidwe wa atsamwali a otsalira a kagulu ka mkwatibwi wakhala wachisangalalo. Iwo amasangalala osati kokha chifukwa cha mwaŵi waukulu umene otsalira aloŵamo kale komanso chifukwa cha mwaŵi wodalitsidwa mu umene iwo eni aloŵetsedwamo kupyolera mwa kagulu ka mkwatibwi ka otsalira.
14 Pamsonkhano wa 1935 ku Washington, D.C., anthu a Yehova anathandizidwa kuzindikira lemba lokondweretsa kwambiri limene lidaneneratu za mkhalidwe wosangalatsa wa ‘khamu lalikulu,’ atsamwali a odzozedwa. Tawawonani, “akuimirira kumpando wachifumu [wa Yehova Mulungu] ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, [ali] ndi makhwatha akanjedza m’manja mwawo”! Mvetserani zimene akunena mofuula kuti anthu onse amve: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wa kukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa”! (Chivumbulutso 7:9, 10) Iwo asonyeza kale chikhulupiriro mwa “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa uchimo wa dziko,” ndipo kupyolera mwa iye iwo adzipatulira kwa Yehova Mulungu ndi kubatizidwa kusonyeza kudzipatulira kumeneko. (Yohane 1:29) Mwawona nanga, okwanira 840 a iwo anabatizidwa mmaŵa mwa tsiku limene anamva kutanthauziridwa kwa Chivumbulutso 7:9-17 pa Lachisanu, May 31, 1935.
15. Kuyambira pamenepo, kodi ndiangati amene abatizidwa, ndipo kodi iwo achitiridwa chithunzi motani m’Chivumbulutso 7:14-17?
15 Oposa mamiliyoni atatu achita mofananamo kuyambira pamsonkhano umenewo wa ku Washington mu 1935. Motero iwo akuchitiridwa chinthunzi kukhala atavala miinjiro yoyera chifukwa cha kukhala ataitsuka m’mwazi woyeretsa wa Mwanawankhosa. Ndipo ali ndi chiyembekezo cha kutuluka m’chisautso chachikulu chimene chiri kutsogolo kwa anthu onse, pokhala ndi chitetezo cha Mulungu cha kupulumuka chisautso chimenecho. (Mateyu 24:21, 22) Chifukwa chake, iwo asonyezedwa kukhala m’kachisi wauzimu wa Yehova ndipo mmenemo akumlambira iye limodzi ndi otsalira a kagulu ka anamwali.—Chivumbulutso 7:14-17.
16. Pamenepa, kodi nkwayani kumene zithokozo zazikulu zimaperekedwa kaamba ka mbali yawo mogwirizana ndi kukwaniritsidwa kwa Mateyu 24:14?
16 Chifukwa chake, tikuyamika kwambiri, “khamu lalikulu” lochokera m’mitundu yonse, m’zilankhulidwe zonse, chifukwa cha mbali yaikulu imene iwo akhala nayo m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Mkwatibwi pa Mateyu 24:14!
“Ndipo Anatseka Pakhomo”
17. (a) Kodi ndiliti pamene khomo loloŵera kumadyerero a ukwati lidzatsekedwa? (b) Kodi nchiyani chimene chiri chofunika kwa otsalira a kagulu ka anamwali ndi “khamu lalikulu” la atsamwali awo kuti achite tsopano?
17 Kuti ndiliti kwenikweni pamene otsalira a kagulu ka anamwali adzakhala ataloŵa m’phwando la madyerero aukwati, ndiyeno kutseka pakhomo, sikukudziŵika. Koma mosakaikira kwayandikira kwambiri koposa nthaŵi ina iriyonse kalero, ndipo nthaŵi ikutha! Pamenepa, moyenerera, Yesu anamaliza fanizo la anamwali ndi mawu ochenjeza akuti: “Dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.”—Mateyu 25:13.
18. (a) Kodi anamwali opusa tsopano akudzigwirizanitsa ndiyani? (b) Kodi ndimbali iti ya fanizo la Yesu imene ali pafupi kukomana nayo mwamsanga?
18 Chifukwa cha chimenechi anamwali opusa adzadzidzimutsidwa. Chifukwa cha kudzilekanitsa kwawo ndi anamwali ochenjera, iwo afikira kukhala mbali ya dziko loweruzidwira ku chiwonongeko ndipo akudziŵerengera limodzi ndi zipembedzo zina zonse kunjako zimene ziri mumdima wa ndiwe yani padziko lonse lapansi. Motero iwo aikidwiratu kudzakomana ndi chimene Yesu Kristu Mkwatiyo analongosola m’mawu aŵa a fanizolo: “Anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziŵani.”—Mateyu 25:10-12.
19. Chifukwa chake kodi anamwali opusa amaphiphiritsira yani, ndipo nchifukwa ninji iwo adzaŵerengeredwa limodzi ndi Babulo Wamkulu?
19 Chotero khomo loloŵera kuphwando silidzatsegukira anamwali opusa amenewo. Iwo anaphiphiritsira bwino lomwe awo amene mkati mwa “mapeto a dongosolo la zinthu” alephera kuloŵa mu “ufumu wakumwamba.” (Mateyu 24:3; 25:1) Chifukwa cha kuumirira kumpangidwe wawo wodzisankhira wa chipembedzo, monga momwe wasonyezedwera mwa kupita kwawo kumsika kukagula mafuta ena, iwo akugwirizanitsidwa ndi Babulo Wamkulu.
20. (a) Pamene anamwali opusa awona “nyanga khumi” za “chirombo” ziyamba kutembenukira Babulo Wamkulu, kodi ndikwayani kumene iwo adzachonderera ndipo adzanena chiyani? (b) Komabe kodi nchifukwa ninji iwo adzawonongeka?
20 Chifukwa chake, pamene “chirombo,” chophiphiritsira chimene hule lachipembedzo lakwera, chimtembenukira ndi ‘nyanga zake khumi,’ iwo adzafunikira kufera pamodzi naye. (Chivumbulutso 17:16) Pamene achipembedzo otero, ophiphiritsiridwa ndi anamwali asanu opusa, awona kuyamba kumeneku kwa kukanidwa kwa chipembedzo Chachibabulo ndi magulu amphamvu a andale zadziko, adzatembenukira kwa Mfumu Mkwatiyo, akumanena kuti iwo ali a kagulu ka “ufumu wakumwamba” ndipo ngoyenera kuloŵa m’madyerero a ukwati wauzimu limodzi ndi anamwali ochenjera. Mwachisoni, iye amene akumutcha “Ambuye,” Mkwatiyo Yesu Kristu, adzakana kuwavomereza kuti ngoyenera kuloŵa mu Ufumu wakumwamba. Ndipo iwo sanakhale ndi chiyembekezo chirichonse cha moyo wamuyaya padziko lapansi limodzi ndi “khamu lalikulu.” Chotero achipembedzo opusa ameneŵa adzawonongedwa limodzi ndi ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga, Babulo Wamkulu!
21. (a) Chifukwa cha chiyembekezo chochititsa mantha chimenecho, kodi ndinjira yotani imene anamwali ochenjera ndi atsamwali awo akuilondola? (b) Kodi ndimwaŵi wa utumiki wotani umene mamembala a “khamu lalikulu” akuyembekeza kukhala nawo?
21 Ha nchiyembekezo chochititsa mantha chotani nanga chimene anali nacho! Pokhala ozindikira zimenezi, otsalira ndi atsamwali awo ambiriwo adzalabadira mosalekeza uphungu wa Yesu wa “kudikira.” Iwo nthaŵi zonse adzakhala odzala ndi mzimu wa Mulungu ndi kulola kuunika kuŵala mopanda mantha ku ulemerero wa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Motsimikizirika iwo adzafupidwa mwa kulandira chisangalalo! Ndipo mamembala a “khamu lalikulu” akuyembekezera malo antchito aukalonga ‘m’dziko lapansi latsopano’ monga momwe adzasankhidwira ndi Mkwatiyo Mfumu yokwatirayo.—Yesaya 32:1; yerekezerani ndi Salmo 45:16.
22. (a) Kodi kukwaniritsidwa kwa fanizo la anamwali kumatumikira kukhala chitsimikiziro cha chenicheni chotani? (b) Kodi ndani amene adzakondwera ndi ukwati umenewu wa Mkwati Mfumu ndi mkwatibwi wake namwaliyo?
22 Motero kukwaniritsidwa kwakukulu kwa fanizo la anamwali khumi kumeneku kumatumikira monga chitsimikiziro cha chenicheni chakuti tikukhala ndi moyo ‘m’mapeto a dongosolo la zinthu.’ Ha tingakhale oyamikira chotani nanga kuti taunikiridwa kuwona umboni umenewu wa kuyandikira kwa ukwati wa Yesu Kristu ndi kagulu ka mkwatibwi kokwanira! Ponse paŵiri kumwamba ndi “dziko lapansi latsopano” zidzasangalala ndi chisangalalo chosaneneka chifukwa cha ukwati umenewu wakumwamba.—Chivumbulutso 19:6-9.