‘Tavalani Zida Zonse za Mulungu’
AKRISTU kuvala zida? Kodi ayenera kunyamuliranji zida zankhondo zimenezo? Kodi iwo sali okonda mtendere? (2 Timoteo 2:24) Inde, alidi otero. Komabe, Akristu owona onse akumenya nkhondo—imene akumenyera, osati kupha, koma kugonjetsa.
Akadapanda kupanduka Satana, nkhondo yoteroyo sikadakhala yofunikira. Koma iye anapanduka, ndipo anasokeretsa Adamu ndi Hava kugwirizana naye m’chipanduko chake. Chiyambire pamenepo dongosolo ladziko limene lakhalapo likugona m’manja mwa “woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Awo amene amagonjera kwa Mfumu yoyenera, Yehova, ayenera kukaniza chisonkhezero cha dziko ndi wolamulira wake. Ayenera kumenya nkhondo yotetezera miyoyo yawo yauzimu. Chifukwa chake, Akristu akuchenjezedwa kuti: ‘Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.’—Aefeso 6:11.
Zida
Onani kuti tifunikira “zida zonse za Mulungu” ngati titi titetezeredwe kotheratu. Pamenepo, tiyeni tsopano tipende chirichonse cha zida zimenezi monga momwe zalongosoledwera ndi mtumwi Paulo ndi kudzisanthula tokha mowona mtima kuwona ngati tiri okonzeka mokwanira kuimenya nkhondo yauzimu.—Aefeso 6:14-17.
‘Chifukwa chake chirimikani, mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi chowonadi.’ (Aefeso 6:14a) M’nthaŵi za Baibulo asirikali anavala lamba wachikopa waukulu wofika 15 sentimita. Chomangira chimenechi chinawathandiza kutetezera chuuno. Pamene msirikali anamanga lamba wake, zinatanthauza kuti anali wokonzeka kumenya nkhondo.
Pamenepo, nzoyenerera chotani nanga kuti chowonadi cha Mulungu chafaniziridwa ndi lamba wa msirikali! Izi zimafotokoza mwafanizo bwino lomwe kuti tiyenera kumamatira kwambiri ku Mawu a Mulungu a chowonadi, monga ngati nkudzimanga nawo. Tiyenera kusinkhasinkha mozama pamalingaliro okhala m’Mawu a Mulungu. Kutero kudzatitetezera kusasokeretsedwa ndi mabodza ndi zinyengo. Ndiponso, mawu otuluka pakamwa pa Yehova adzatichirikiza ndi kutilimbitsa mwauzimu ndi kukhwimitsa umphumphu wathu.
‘Mutavalanso chapachifuŵa cha chilungamo.’ (Aefeso 6:14b) Chapachifuŵa cha msirikali chinatetezera chiŵalo cha thupi chofunika kwambiri—mtima. Pamenepa, m’zida zathu zauzimu zopatsidwa ndi Mulungu, chilungamo chimatetezera mtima wathu. Malinga nkunena kwa Malemba, mtima ndiwo chizindikiro choyenerera cha amene tiri mkati mwathu—malingaliro athu, maganizo, ndi zikhumbo. Popeza kuti Baibulo limanenanso kuti mtima ngwokhoterera kuchita zoipa, nkofunika kukulitsa chifuno chakumamatira ku muyezo wa Yehova wa chilungamo. (Yeremiya 17:9) Kumvera Mulungu sikuyenera kukhala kwachiphamaso; kuyenera kuchokera mumtima. Kutero kumafuna kuti tikulitse chikondi chachikulu cha chilungamo ndi udani waukulu mofananamo wa kusayeruzika. (Salmo 45:7) Motero mtima wathu udzatetezeredwa.
‘Mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a uthenga wabwino wa mtendere.’ (Aefeso 6:15) Kodi mapazi anu ali ovekedwa motero? Kodi amakuperekani nthaŵi zonse muutumiki wakumunda kukalengeza mbiri yabwino? Kodi mukukalimira kuwongolera kalalikidwe kanu ndi kaphunzitsidwe? Zowona, magawo ena ali osatchera khutu. Anthu ena angakhale osakondwerera, amphwayi, kapena otsutsa. Nthaŵi zina kulalikira kwathu kungatigwetsere m’chizunzo. Koma mwakulimbika chilimbikire, Akristu amakulitsa chipiriro, mkhalidwe umene umatetezera ku ziukiro za Satana. Ngakhale kuti anazunzidwa, Paulo anali mlaliki wachangu, ndipo tikulimbikitsidwa ‘kukhala omtsanza iye, monga iyenso anatsanza Kristu.’—1 Akorinto 11:1.
Kukhala otanganitsidwa m’ntchito yolalikira Ufumu kumalimbitsa chidaliro chathu m’mbiri yabwino. Ndiponso, kumalola mzimu wa Yehova kugwira ntchito kupyolera mwa ife kukwaniritsa chifuniro chake. Kwenikweni, ntchito yoteroyo imatikhalitsa antchito anzawo a angelo—ngakhale ndi Yehova Mulungu iye mwiniyo. (1 Akorinto 3:9; Chivumbulutso 14:6) Ndipo kukhala ‘akuchuluka m’ntchito ya Ambuye’ kumatikhalitsa “okhazikika, osasunthika.” (1 Akorinto 15:58) Ha, zimenezi zimapereka chitetezero chodabwitsa chotani nanga!
‘Mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro.’ (Aefeso 6:16) Ndi chikopa chachikulu, msirikali wa m’nthaŵi zakale anadzitetezera ku mikondo ndi mivi. Ngati analephera kugwiritsira ntchito chikopa, akavulazidwa kwambiri ngakhale kuphedwa. Akristu amayang’anizana ndi zida zowopsa koposapo—‘mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ Izi zimaphatikizapo zonse zimene Satana amagwiritsira ntchito kotero kuti afooketse chikhulupiriro chathu ndi kutipha kuuzimu. Zimaphatikizapo chizunzo, mabodza, nthanthi zadziko zonyenga, zinthu zakuthupi zokopa, ndi chiyeso chakudziloŵetsa m’makhalidwe oipa. Kuti tidzitetezere ku zimenezi, timafunikira chikopa chachikulu. Palibe mbali ya thupi lathu imene ingalasidwe.
Abrahamu ndi mkazi wake, Sara, anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ngakhale kuti anapyola pausinkhu wakubala, iwo anaika chikhulupiriro m’lonjezo la Mulungu lakuti mbewu ikabadwa kwa iwo. Pambuyo pake, Abrahamu anasonyeza chikhulupiriro chachikulu pamene anauzidwa kupereka nsembe Isake, mwana wake yekha mwa mkazi wake wokondedwa Sara. Yehova analetsa dzanja la Abrahamu ndi kumpatsa nsembe ina mmalo mwake. Koma Abrahamu anali wokonzekera kulabadira. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anakhulupirira kotheratu kuti Yehova akaukitsa mwana wake ndi kukwaniritsa lonjezo limene analipereka kwa iye.—Aroma 4:16-21; Ahebri 11:11, 12, 17-19.
Mose nayenso anali ndi chikhulupiriro chimene tiyenera kukhala nacho. Iye anakana chuma cha Igupto, nasankha kuvutika ndi anthu a Mulungu oponderezedwa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova aliko ndipo akapulumutsa Aisrayeli. Chikhulupiriro cha Mose chinali cholimba kotero kuti ‘anapirira molimbika, monga ngati kuwona wosawoneka.’—Ahebri 11:6, 24-27.
Kodi tiri nacho chikhulupiriro chotero mwa Yehova? Kodi unansi wathu ndi Yehova ngwathithithi moti nkuchita ngati tikumuwona? Kodi ndife ofunitsitsa kupereka nsembe kapena kupirira zovuta kuti tisungitse unansi wathu ndi Mulungu? Kodi tiri nacho chikhulupiriro chokwanira mwa Yehova? (Ahebri 11:1) Ngati nditero, mivi yoyaka moto ya Satana siidzapyola m’chikopa chathu cha chikhulupiriro.
‘Mutengenso chisoti cha chipulumutso.’ (Aefeso 6:17a) Chisoti cha msirikali chinatetezera mutu wake ndi ubongo—chiŵalo cha thupi chogwirizanitsa minyewa ndi malingaliro. Chiyembekezo Chachikristu cha chipulumutso chafaniziridwa ndi chisoti chifukwa chakuti chimatetezera maganizo. Maganizo a Mkristu akhalitsidwa atsopano mwa chidziŵitso cholongosoka, koma amakhalabe a munthu wofooka ndi wopanda ungwiro. (Aroma 7:18; 12:2) Ngati tilola maganizo kulingalira zinthu zodetsedwa zowononga chikhulupiriro zoperekedwa ndi mzimu wa dziko lino, chidaliro chathu m’chipulumutso chidzazilala ndipo chingaferetu pomalizira pake. Kumbali ina, ngati nthaŵi zonse tidyetsa maganizo athu ndi mawu olimbikitsa a Mulungu, chiyembekezo chathu chidzakhalabe choŵala ndi chotsimikizirika. Kodi mumavala zolimba chisoti chanu cha chipulumutso?
‘Lupanga la mzimu, ndilo mawu a Mulungu.’ (Aefeso 6:17b) Kunena kwakuti kudzichinjiriza choyamba ndiko kulimbana kwabwino kumagwira ntchito m’nkhondo Yachikristu. Pamene mapazi athu, ovekedwa mbiri yabwino ya mtendere, atipereka pakati pa osakhulupirira, sitimakhala opanda chida. Mawu a Mulungu, Baibulo, amakhala lupanga lamphamvu lokanthira mabodza auzimu ndi malingaliro olakwa ndi kuthandizira anthu owongoka mtima kupeza ufulu wauzimu.—Yohane 8:31, 32.
Yesu anasonyeza mphamvu ya chida chimenechi pamene analimbana zenizeni ndi Satana Mdyerekezi. Pamene anayesedwa m’chipululu, Yesu anadzitetezera ku ziukiro zitatu za Satana mwakugwiritsira ntchito bwino Mawu a Mulungu ndi kunena kuti: “Kwalembedwa.” (Mateyu 4:1-11) Ngati tiphunzira kugwiritsira ntchito lupanga limeneli mwaluso, tikhoza kuthandiza ofatsa kumasuka ku mphamvu ya Satana. Ndiyenonso, akulu a mpingo amagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kutetezera nkhosa kwa anthu amene amayesa kululuza chikhulupiriro cha osalimba.—Machitidwe 20:28-30.
Luso la msirikali lakugwiritsira ntchito lupanga silimabwera mosavuta. Pamafunikira kuphunzira, ndi kuyeseza kwanthaŵi yaitali kuti adziŵe kuligwiritsira ntchito mochenjera. Mofananamo, m’nkhondo yauzimu, pamafunikira kuyesayesa zolimba kuphunzira ndi kuyeseza muuminisitala kuti tikhale ogwiritsira ntchito Mawu a Mulungu mwaluso. Ndithudi, tiyeni tiyeseyese mwamphamvu kotero kuti tikhale olimbana ndi lupanga auzimu aluso, okhoza ‘kulunjika nawo bwino mawu a chowonadi.’—2 Timoteo 2:15.
Limbikani m’Kupemphera, Chirimikani
Zida zonse zauzimu nzofunika kuti tisunge umphumphu kwa Mulungu. Koma kodi ndimotani mmene tingasungire zida zimenezi? Kuphunzira Baibulo mokhazikika, kukonzekera misonkhano Yachikristu pasadakhale, ndiyeno kumvetsera mosamalitsa ndi kukhalamo ndi phande mwachangu kudzatithandiza kuvalabe zida zathu. (2 Timoteo 3:16; Ahebri 10:24, 25) Uminisitala wakumunda wokangalika ndi mayanjano abwino Achikristu zidzatithandizanso kusunga zida zathu zauzimu zolimbanira ndi zodzitetezerera kukhalabe zolimba.—Miyambo 13:20; Aroma 15:15, 16; 1 Akorinto 15:33.
Kukulitsa kaimidwe kamaganizo kabwino nkofunikanso. Sitiyenera kulola zokopa za dziko lino kuticheukitsa. Mmalomwake, tiyeni tikulitse ‘diso lakumodzi.’ (Mateyu 6:19-24) Potsanzira Yesu Kristu, tiyeneranso kuphunzira kukonda chilungamo ndi kuda kusayeruzika. (Ahebri 1:9) Zonsezi zimatithandiza kuvala chivalire zida zathu zauzimu zopatsidwa ndi Mulungu.
Pambuyo pofotokoza chirichonse cha zida zauzimu, Paulo akumaliza mwakunena kuti: ‘Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthaŵi yonse mwa mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse.’ (Aefeso 6:18) Asirikali okhulupirika amalankhulana ndi malikulu ndi kulabadira malangizo. Monga asirikali Achikristu, tiyenera kumalankhulana nthaŵi zonse ndi Mfumu yathu, Yehova Mulungu, kupyolera mwa “wotsogolera ndi wolamulira anthu” wamkulu, Yesu Kristu. (Yesaya 55:4) Izi zikhoza kuchitidwa, osati mwapemphero lachiphamaso, koma mwakupembedzera kochokera mumtima kumene kumasonyeza kuyandikana ndi kudzipereka kwathu kwakuya kwa Yehova. Mwakulankhulana mokhazikika ndi Yehova, timalandira nyonga tsiku ndi tsiku kotero kuti tikhalebe olimba m’nkhondoyo.
Yesu anati: “Ndalilaka dziko lapansi Ine.” (Yohane 16:33) Yehova amafunanso kuti tikhale olakika. Pamene imfa ya mtumwi Paulo inayandikira, iye anati: ‘Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro.’ (2 Timoteo 4:7) Tiyeni tikhaletu okhoza kunena zofananazo ponena za mbali yathu m’kulimbanako. Ngati tifunadi zimenezi, tiyeni ‘tichirimike pokana machenjerero a Mdyerekezi’ mwakuvala chivalire zida zonse za Mulungu.—Aefeso 6:11.