“Mawu Auzimu” Kaamba ka Osautsidwa Mwamaganizo
MAVUTO a maganizo amakantha ngakhale atumiki ena okhulupirika a Mulungu. Ndipo pamene kuli kwakuti pa nthaŵi zina chingakhale chofunika ndi choyenera kwa osautsidwawo kufuna thandizo la akatswiri, iwo angapindulenso kuchokera ku chithandizo ndi chilimbikitso cha mpingo Wachikristu. Mwachitsanzo, pamene Mkristu wokhulupirika Epafrodito anakhala wopsyinjika mokulira, akhulupiriri anzake mu Filipi anasonkhezeredwa kusanyalanyaza kusautsidwa kwake koma “kumulandira mwa Ambuye ndi chimwemwe chonse; [ndi kupitiriza kusunga amuna oterowo okondeka, NW].”—Afilipi 2:25-29.
Mboni za Yehova lerolino mofananamo ziri pansi pa thayo la “kumangirirana wina ndi mnzake” ndi “kuchirikiza ofooka.” (1 Atesalonika 5:11, 14) Akulu Achikristu, ayenera kutenga chitsogozo m’nkhaniyi.—Yesaya 32:2.
Ndithudi, akulu kaŵirikaŵiri sali oyeneretsedwa kuchita monga asing’anga kapena kugwiritsira ntchito malingaliro ndi mawu a matenda a maganizo. Kuchita tero kukakhala kusadzichepetsa ndipo mwinamwake kowopsya. (Miyambo 11:2) Mofanana ndi mtumwi Paulo, iwo ayenera “kulankhula, si ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma opohunzitsidwa ndi mzimu, [pamene, NW] [iwo] akulinganiza za mzimu ndi [mawu auzimu, NW].” (1 Akorinto 2:13) “Mawu auzimu” amenewa amaphatikiza lingaliro ndi maprinsipulo opezedwa m’Baibulo. Atagwiritsiridwa ntchito molondola, awa angachite zambiri kutonthoza ndi kumangirira anthu osautsidwa.—2 Timoteo 3:16.
“Otchera Khutu”
Choyamba, ngakhale ndi tero, akulu ayenera kukhala “otchera khutu, odekha polankhula.” (Yakobo 1:19) ‘Kuyankha ku nkhani musanaimve iyo’ mopepuka kungatulukemo kupereka uphungu wosayenerera. (Miyambo 18:13) Mwa kulephera kugwira nsonga ya mtundu wa kusokonezeka kopsyinja kwa mbale wina, gulu limodzi la akulu linamunyalanyaza iye monga wofooka mwauzimu. “Pemphera mowonjezereka,” iwo anamuuza iye—langizo lomwe analipeza kukhala lovuta kuligwiritsira ntchito chifukwa cha mkhalidwe wake wopsyinjidwa wa maganizo.
Chotero, asanapereke uphungu, akulu ayenera kumva zonse zimene wovutikayo ayenera kunena. Mwinamwake, chimene iye amafunikira chiri mvetseri wabwino. Kupyolera m’kuleza mtima ndi kuzindikira, ‘kokani’ chomwe chiri mumtima mwake. (Miyambo 20:5) Ngati munthu wosautsidwayo ali ndi vuto m’kukamba malingaliro ake, kumbukirani mmene Elikana anafunsira mafunso achifundo koma achindunji ponena za mkhalidwe wopsyinjika wa mkazi wake. “Hana,” iye anafunsa, “umaliriranji, ndipo umakaniranji kudya, ndipo mtima wako uwawa ninji?” (1 Samueli 1:8) Mafunso ochenjera, ofunsidwa mofatsa, kaŵirikaŵiri angathandize mbale wopsyinjikayo kuloza mwachindunji magwero a “nkhawa zake.” (Miyambo 12:25) Mwachitsanzo, m’nkhani imodzi mavuto a mu ukwati anatsimikizira kukhala chochititsa kupsyinjika kwa mbale.
Kupereka Thandizo “Popanda Kutonza”
Anthu osautsidwa nthaŵi zonse samakhala ndi kulongosola komvekera bwino kwa mmene amadzimverera. analemba tero m’nkhole mmodzi wa matenda a maganizo: “Pamene ndinadwala, sindinachimvetsetse icho ndipo nthaŵi zina ndinapatsa mlandu Yehova.” Okanthidwa mwakutero angapange zodandaula zopanda maziko kuti iwo sakusamaliridwa bwino kapena kunyalanyazidwa ndi mpingo. Ndimotani mmene akulu ayenera kuvomerezera?
Yehova amakhazikitsa chitsanzo mwa ‘kupatsa kwa onse modzala manja ndi mosatonza.’ (Yakobo 1:5) Ovutika safunikira kupangidwa kudzimva kuti iwo ali opusa kapena opulukira kaamba ka kudzimva m’njira imene akuchitira. Malingaliro awo—ngakhale kuti angakhale opanda nzeru—alidi enieni kwa iwo. Iwo amafunikira “kuchitiridwa chifundo,” osati kusulizidwa. (1 Petro 3:8) Akulu ayeneranso kukhala osamala kusawonjezera ku malingaliro a wovutikayo mwa kumpatsa iye liwongo la kuchita cholakwa. Munthu wolungama Yobu anasautsidwa koposa kotero kuti iye analira kuti: “Mtima wanga ulema nawo moyo wanga.” (Yobu 10:1) Koma anzake atatu sanamutonthoze iye. Mmodzi wa iwo anafikira ngakhale pa kunena kuti: “Zoipa zako sizichuluka kodi, ndi mphulupulu zako sizikhala zosaŵerengeka?”—Yobu 22:5.
Nthaŵi zina, ngakhale kuli tero, mkhalidwe woipa uli choyambitsa cha kusinthika kwa malingaliro kapena chiri chothandizira ku kuipirako kwake. “Pamene ndinakhala chete [pa kuchita cholakwa] mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse,” anatero wamasalmo Davide. (Salmo 32:3) Mofananamo, mbale mmodzi anavutika ndi kudera nkhaŵa kosautsa koteroko kotero kuti iye sakanathanso kugwira ntchito. Choyambitsa cha nsautso yake? Kachitidwe ka chigololo kamene iye anakabisa. Chotero ngati pali chifukwa cha kukaikira kuti kachitidwe koipa kakuphatikizidwa, akulu angafufuze ichi monga chothekera. Koma iwo ayenera kuchita tero m’njira ya chifundo, osati motonza kupatsa munthuyo mlandu wa cholakwa.
Kuchiritsa Ndi Lilime la Nzeru
Pambuyo pakuti akulu achita zomwe iwo angathe kugamulapo mtundu wa vuto la munthuyo, iwo ayenera kuchita m’chigwirizano ndi Miyambo 12:18, imene imanena kuti: “Lilime la anzeru lilamitsa.” Ayi, akulu sangachiritse matendawo. Koma mwa kugwiritsira ntchito mawu osankhidwa mosamalitsa, iwo angakhale okhoza kuchepetsako mwa maganizo kudera nkhaŵa ndi kupsyinjika kosayenerera kwa munthu wosautsidwayo. Akuluwo angayambe mwa kusankha nkhani za Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zochita ndi mavuto a maganizo ndi malingaliro. Izi zingakambitsiridwe ndi osautsidwawo kotero kuti muwathandize iwo kumvetsetsa mkhalidwe wawo bwino. Kaŵirikaŵiri iwo amapatsidwa mpumulo kudziŵa kuti vuto lawo liri chotulukapo cha kupanda ungwiro kwa kuthupi, osati kusoweka kwa chiyanjo cha Yehova.
Movomereza, anthu ovutitsidwa angakhale ovuta kuchita nawo, ena akumakhala okwiyitsidwa. Komabe, mkulu wanzeru amakumbukira kuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Kutsimikizira kuti mawu ake ali nthaŵi zonse achisomo kumamuchinjiriza iye kukulitsa mkhalidwewo mosayenerera. (Akolose 4:6) Mwachitsanzo, mbale wovutika ndi kusokonezeka kwa maganizo angawumirire kuti iye amamva mawu.a Wawona tero, Dr. E. Fuller Torrey: ‘Chiri chosaphula kanthu kuyesera kukangana ndi osokonezeka maganizo kuchoka ku zikhulupiriro zawo zosokonezeka. Zoyesayesa za kuchita tero kaŵirikaŵiri zimatulukapo m’kusamvana ndi mkwiyo. M’malo mokangana, tangopangani kokha ndemanga ya kusagwirizana.’ M’mawu ena, akulu angalongosole moleza mtima kuti ngakhale kuti mawu amenewo angawoneke kukhala enieni, mwachidziŵikire maganizo ake akungochita chiphwete ndi iye.
Kugwiritsira ntchito kokhutiritsa kwa Baibulo kungatulutsenso zotulukapo zabwino. (Ahebri 4:12) Mwachitsanzo, ngati munthu wodwalayo alongosola mantha osalingalirika akuti Mulungu wamulekelera iye, mwachifundo sonyezani kudera nkhaŵa kaamba ka mantha ake. Pa nthaŵi imodzimodziyo, ngakhale kuli tero, moleza mtima mukumbutseni iye mphamvu ya dipo, kugwiritsira ntchito malemba onga ngati Salmo 103:8-14 ndi 1 Yohane 2:1, 2. Petro Woyamba 5:6, 7 ndi Aroma 8:26, 27 angamuthandize iye kuyamikira kuti Mulungu ‘amasamalira kaamba ka iye’ ndipo amamva mapemphero ake, ngakhale ngati iye ali ndi vuto m’kuika malingaliro ake m’mawu. Akumatsatira prinsipulo la pa Yakobo 5:14, akulu kenaka angapemphere ndi munthu wosautsidwayo.
Bwanji ngati wovutikayo akhoterera kukhala wosangalatsidwa ndi zinthu zazing’ono? Iye angakumbutsidwe za uphungu wa Baibulo wa kusakhala “wolungama pa zambiri.” (Mlaliki 7:16) Wina angapindule kuchokera ku chilimbikitso chopezeka pa Afilipi 4:8, chomwe chingamuthandize kulimbana ndi malingaliro a mkhalidwe woipa. Komabe wina angalephere kulandira malire ake ndipo angakhumudwitsidwe chifukwa chakuti matenda ake amaika malire ku ntchito yake Yachikristu. Malemba oterowo onga ngati Mateyu 13:23 ndi Luka 21:1-4 angagwiritsiridwe ntchito kumuthandiza iye kuyamikira kuti ngakhale kuti mikhalidwe yathu ingaike malire ku zimene tingachite, Yehova mozama amayamikira zoyesayesa zathu.
Inde, okonzekeretsedwa ndi lilime lophunzitsidwa ndi Baibulo, akulu angachite zambiri kuthandiza ndi kutonthoza akhulupiriri anzawo osautsidwa. Akutero mlongo wina yemwe anavutika ndi mavuto a maganizo: “Ndimayamikiradi zimene Yesaya 32:2 amanena ponena za akulu mu mpingo.Iwo nthaŵi zonse anali pamenepo ndi uphungu wokhoza kugwira ntchito pamene ndinawufuna iwo.”
Misonkhano ndi Utumiki wa M’munda
Munthu wosautsidwa mwa maganizo adakali ndi zosowa zauzimu. (Mateyu 5:3) Ndithudi, kukhala wolimba mwauzimu kwatanthauza kusiyana pakati pa moyo ndi imfa kwa ena. Irene, yemwe anavutika chifukwa cha kudwala maganizo kwa zaka 30, akukumbukira kuti: “Pa nthaŵi zina, ndinali wosokonezeka koposa. Koma chowonadi nthaŵi zonse chinali m’maganizo mwanga—cholimba monga simenti. Chinandipulumutsa ine ku kutenga moyo wanga!”
Ku ukulu wokhoza kugwirirapo ntchito, chotero, munthu wodwalayo ayenera kulimbikitsidwa kugawana mu ntchito yolalikira ndi kupezeka pa misonkhano, ndipo osati “kupanduka.” (Miyambo 18:1) Chifukwa cha matenda a maganizo, umu ndi mmene mlongo wina anadzimverera: ‘Ndinali wokhutiritsidwa kuti ndinachimwa mosakhululukidwa molakwira Mulungu wathu, Yehova. Monga chotulukapo, ndinachotsa chirichonse chomwe ndinamva pa misonkhano mu lingaliro lake lonse. Chirichonse chotsutsidwa, ndinachigwiritsira ntchito kwa inemwini.’ Koma iye anawumirira kupezeka pa misonkhano ndipo kenaka anamva nkhani yomwe inamuthandiza iye kulaka kulingalira kwake kwa kukhala wokanidwa ndi Mulungu.
Bwanji, ngakhale ndi tero, ngati munthu wodwala kwambiri akhala wokwiyitsidwa ndi kusokoneza msonkhano wa mpingo kapena utumiki wa m’munda? Mwachidziŵikire, wovutikayo sakukhala wankhalwe koma ali kokha wokwiyitsidwa chifukwa cha kulingalira kosokonezeka. Ngakhale kuli tero, ichi chingakhale choyesa kwa onse oyambukiridwa. Ngati kusokonezako kuli kochepera kapena kosabwerezabwereza, mwachidziŵikire mpingo udzasonyeza kupirira. (Akolose 3:12, 13) Kupanda apo, chingakhale choyenera kulingalira kuti wovutikayo akhale kumene kusokoneza kothekera kungapangitse kucheutsa kochepera. Makonzedwe achikondi angapangidwenso kusunga munthu woteroyo kukangalira mu ntchito yolalikira, mwinamwake kuwona ku icho kuti iye nthaŵi zonse amatsagana ndi wofalitsa wachikulire, wozindikira, kapena kuti amakhala pa maphunziro apanyumba a Baibulo pamene mkhalidwe wake umamvetsetsedwa ndi kuloledwa.
Nthaŵi zina, ngakhale ndi tero, mkhalidwe wa munthuyo umakhala wochititsa mantha, wotonza, kapena mowopsya mosalamulirika. Mwinamwake munthuyo waleka kutenga mankhwala ake olembedwa ndipo afunikira chilimbikitso champhamvu kuti abwerere ku ndandanda yake ya kumwa mankhwala. Koma ngati palibe yankho kapena machitidwe osokonezeka a munthuyo apitiriza, chingakhale choyenera kumuletsa iye kupita ku misonkhano ndi mu utumiki wa m’munda kotero kuti asungirire mtendere. (1 Akorinto 14:40) Mwa njira ya chifundo, akulu ayenera kuwuza munthu wodwalayo kuti iye sakuŵeruzidwa kukhala wosakhulupirika koma kuti matenda ake akungoika malire ku zimene iye angachite. ‘Mulungu sali wosalungama kuti aiwale ntchito yake’ ndipo Iye amamvetsetsa kukhala ndi polekezera kwake. (Ahebri 6:10) Maulendo obwerezabwereza a ubusa adzathandiza munthuyo kusungirira uzimu wake kufikira mkhalidwe wake utawongokera.
Kuthandiza Mabanja Awo
Matenda a maganizo amabweretsa tsoka lalikulu pa mabanja. “Chakhaladi chosakaza,” akutero mbale amene mwana wake wamwamuna wamkulu akudwala mowopsya mwa maganizo. “Tsiku ndi tsiku simupeza mpumulo,” akuwonjezera tero mkazi wake. “Zayambukira ukwati wathu, popeza kuti nthaŵi zina timadzipeza ife eni tikukalipirana wina ndi mnzake.” Tangolingalirani, kachiŵirinso, kupweteka kwa kuwona mnzanu wa mu ukwati akugwera m’matenda a maganizo. Anatero mbale wina: “Mkazi wanga anaikidwa chizindikiro kukhala ‘wodwala maganizo ozunza.’ Iye amamva mawu ndi kukana mankhwala chifukwa chakuti amakhulupirira kuti adzamupatsa iye ‘ululu.’ Iye samakhulupirira kuti ndine mwamuna wake ndipo amakana kupita mu utumiki kapena ku misonkhano.” Ndimotani mmene tingathandizire mabanja a okanthidwa oterowo?
Paulo ananena kuti: “Lankhulani motonthoza ku mitima yopsyinjika.” (1 Atesalonika 5:14) Chikakhala cha nkhalwe kupewa kapena kunyalanyaza Akristu anzathu omwe akugwira ntchito kusamalira kaamba ka chiwalo cha banja chodwala mwa maganizo. “Mulandilane wina ndi mnzake,” anatero Paulo. (Aroma 15:7) Misonkhano Yachikristu imatipatsa ife mwaŵi wa kuchita tero motentha ndi kusonyeza chikondi ndi chiyamikiro kaamba ka awo amene ‘akuchita kudzipereka kwa umulungu m’mabanja mwawo.’—1 Timoteo 5:4.
Pa maulendo a ubusa, akulu angalimbikitse mowonjezereka anthu oterowo kusungirira phunziro la banja, kupezeka pa misonkhano, ndi kukhala okangalika monga alaliki a Ufumu. Pamene chibwera ku zosowa zawo za kuthupi ndi zogwira ntchito, ngakhale kuli tero, mpingo uyenera kuchita zoposa kunena kuti, “Mukafunde ndi kukhuta.” (Yakobo 2:16) Mwinamwake banjalo limafunikira thandizo m’kupita ku misonkhano. Anthu ena angakhale m’malo a kuthandiza iwo ndi kuwonjezereka kwa ndalama zolipirira mankhwala. (1 Yohane 3:17, 18) Ndimotani nanga mmene kudera nkhaŵa kwachikondi kumeneku kumayamikiridwira! Akutero mwamuna wa mlongo wodwala mwa maganizo: “Mpingo umadziŵa ponena za vuto lathu, ndipo iwo mwachikondi kwambiri amasonyeza kuti amasamalira.”
Kusunga Umphumphu
“Cholengedwa chonse chibuula ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano,” anatero Paulo. (Aroma 8:22) Ndipo nsautso ya maganizo iri kokha imodzi ya zowawa za kupanda ungwiro. adokotala angapereke muyezo wa mpumulo. Koma ambiri amene afuna thandizo lawo akhala ndi chokumana nacho chonga chija cha mkazi m’tsiku la Yesu yemwe “anamva zowawa zambiri ndi asing’anga ambiri nalipira zonse anali nazo osachira mpang’ono ponse koma, makamaka, nthenda yake idakula.”—Marko 5:26.
Ambiri, chotero, ayenera kuphunzira kukhala ndi mavuto awo, kuyang’ana ku mpumulo weniweni m’dziko latsopano la Mulungu. (Chivumbulutso 21:3, 4) “Lemekeza Yehova, . . . amene achiritsa nthenda zako zonse,” anafuula tero wamasalmo. (Salmo 103:2, 3) Pa nthaŵi ino, chodera nkhaŵa chathu chachikulu chiyenera kukhala, osati kukhala ndi umoyo wangwiro wa maganizo kapena wakuthupi, koma kutsimikizira umphumphu wathu. (Salmo 26:11; yerekezani ndi 1 Akorinto 7:29-31.) Kuvutika ndi kusokonezeka kwa maganizo kungachipange ichi kukhala chovuta. Koma atumiki ambiri a Mulungu, monga Paulo, atumikira mokhulupirika ndi “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7) “Ndaphunzira kuti palibe dokotala, kapena ngakhale abale, amene angandichiritse,” akutero m’nkhole mmodzi wa matenda a maganizo. “Koma ndaphunzira kudalira pa Yehova.” Anthu osautsidwa mwa maganizo angadalirenso pa abale ndi alongo achikondi omwe moleza mtima amalankhula “mawu auzimu” kaamba ka chitonthozo chawo ndi chichirikizo.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani yakuti “Nsautso ya Maganizo—Pamene Yakantha Mkristu” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1988, inapereka zitsogozo za kuchita ndi mikhalidwe kumene chisonkhezero cha uchiwanda chikukaikiridwa.
[Chithunzi patsamba 21]
“Mawu auzimu” kuchokera kwa akulu achikondi angachite zambiri kuthandiza anthu osautsidwa