-
Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?Nsanja ya Olonda—1995 | October 15
-
-
Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?
“Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake.”—MATEYU 25:31.
1-3. Kodi tili ndi chifukwa chotani chokhalira ndi chiyembekezo chabwino ponena za chilungamo?
‘KODI ALI NDI MLANDU KAPENA ALIBE MLANDU?’ Ambiri amadzifunsa motero akamva za mlandu wa m’khoti. Oweruza ndi ogamula mlandu amayesa kukhala oona mtima, koma kodi chilungamo chimakhalapo nthaŵi zonse? Kodi simunamvepo za chisalungamo ndi kukondera poweruza mlandu? Chisalungamo chotero si chalero ayi, monga momwe tikuonera m’fanizo la Yesu lopezeka pa Luka 18:1-8.
2 Mulimonse mmene mwachidziŵira chilungamo chaumunthu, tamverani mawu omalizira a Yesu: “Kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku . . . ? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa munthu pakudza iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?”
3 Inde, Yehova adzatsimikiza kuti atumiki ake potsirizira pake achitidwa molungama. Nayenso Yesu alimo ndi mbali, makamaka tsopano popeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo loipa lilipoli. Posachedwa Yehova adzagwiritsira ntchito Mwana wake wamphamvuyo kusesa kuipa pa dziko lapansi. (2 Timoteo 3:1; 2 Atesalonika 1:7, 8; Chivumbulutso 19:11-16) Tingadziŵe bwino za mbali ya Yesu mwa kupenda limodzi la mafanizo omalizira amene iye anapereka, limene kambiri limatchedwa fanizo la nkhosa ndi mbuzi.
4. Kodi takhala ndi kamvedwe kotani ponena za nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa fanizo la nkhosa ndi mbuzi, koma nchifukwa ninji tidzasumika maganizo pa fanizolo tsopano? (Miyambo 4:18)
4 Nthaŵi yaitali tadziŵa kuti fanizolo limatanthauza kukhala kwa Yesu pa mpando monga Mfumu mu 1914 ndi kuti chiyambire nthaŵiyo wakhala akuweruza—moyo wosatha kwa anthu onga nkhosa, imfa yachikhalire kwa mbuzi. Koma kupendanso fanizolo kumasonyeza kusintha kwa kamvedwe kathu ponena za nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwake ndi zimene limaimira. Kamvedwe kowongoleredwa kameneka kamasonyeza kufunika kwake kwa ntchito yathu yolalikira ndi kuti anthu ayenera kuchitapo kanthu. Kuti tipeze maziko a kamvedwe kakuya kwambiri kameneka ka fanizolo, tiyeni tipende zimene Baibulo limasonyeza ponena za Yehova ndi Yesu, onse aŵiri monga Mafumu ndi Oweruza.
Yehova Monga Woweruza Wamkulu
5, 6. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuona Yehova monga Mfumu ndiponso Woweruza?
5 Yehova akulamulira chilengedwe chonse ndi mphamvu pa zonse. Pokhala wopanda chiyambi ndi mapeto, iye ndi “Mfumu yosatha.” (1 Timoteo 1:17; Salmo 90:2, 4; Chivumbulutso 15:3) Ali ndi ulamuliro wa kupanga malamulo ndi kuwasungitsa. Koma ulamuliro wake umaphatikizapo kukhala kwake Woweruza. Yesaya 33:22 amati: “Yehova ndiye Woweruza wathu, Yehova ndiye Wotipatsa malamulo, Yehova ndiye Mfumu yathu; iye adzatipulumutsa.”
6 Kwa nthaŵi yaitali atumiki a Mulungu azindikira kuti Yehova ndiye Woweruza milandu ndi nkhani. Mwachitsanzo, “Woweruza wa dziko lonse lapansi” atapenda umboni wonena za kuipa kwa Sodomu ndi Gomora, anaweruza kuti nzika zake ziwonongedwe ndiponso anapereka chiweruzo cholungama chimenecho. (Genesis 18:20-33; Yobu 34:10-12) Zimatilimbikitsa chotani nanga kudziŵa kuti Yehova ali Woweruza wolungama amene amachita ziweruzo zake nthaŵi zonse!
7. Kodi Yehova anachita motani monga Woweruza pochita ndi Israyeli?
7 Mu Israyeli wakale, Yehova nthaŵi zina anapereka chiweruzo mwachindunji. Kodi sizikanakukondweretsani kalelo kudziŵa kuti Woweruza wangwiro ndiye anali kuweruza milandu? (Levitiko 24:10-16; Numeri 15:32-36; 27:1-11) Mulungu anaperekanso “maweruzo” omwe anali abwino onse monga miyezo yoweruzira. (Levitiko 25:18, 19; Nehemiya 9:13; Salmo 19:9, 10; 119:7, 75, 164; 147:19, 20) Ndiye “Woweruza wa [dziko lonse lapansi, NW],” choncho tonsefe tikukhudzidwa.—Ahebri 12:23.
8. Kodi ndi masomphenya otani oyenera amene Danieli anaona?
8 Tili ndi umboni woperekedwa ndi “mboni yoona ndi maso” pankhaniyi. Mneneri Danieli anasonyezedwa masomphenya a zilombo zolusa zomwe zinaimira maboma kapena maufumu. (Danieli 7:1-8, 17) Anawonjezera kuti: “Anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya Kale Lomwe, zovala zake zinali za mbu ngati chipale chofeŵa.” (Danieli 7:9) Onani kuti Danieli anaona mipando yachifumu “nikhalapo Nkhalamba ya Kale Lomwe [Yehova].” Tsono dzifunseni, ‘Kodi Danieli panopa anali kuona Mulungu akukhala Mfumu?’
9. Kodi tanthauzo lina la ‘kukhala’ pa mpando wachifumu nlotani? Perekani zitsanzo.
9 Chabwino, pamene tiŵerenga kuti wina ‘anakhala’ pa mpando wachifumu, tingaganize za kukhala kwake mfumu, pakuti Baibulo nthaŵi zina limagwiritsira ntchito mawu amenewo. Mwachitsanzo: “Ataloŵa ufumu [Zimri] nakhala pa mpando wachifumu wake, . . . ” (1 Mafumu 16:11; 2 Mafumu 10:30; 15:12; Yeremiya 33:17) Ulosi wa Mesiya unati: “Adzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake.” Chotero, ‘kukhala pa mpando wachifumu’ kungatanthauzedi kukhala mfumu. (Zekariya 6:12, 13) Yehova akunenedwa kukhala Mfumu imene imakhala pa mpando wachifumu. (1 Mafumu 22:19; Yesaya 6:1; Chivumbulutso 4:1-3) Iye ndiye “Mfumu yosatha.” Komabe, pamene anayamba kuchita ulamuliro watsopano, ananenedwa kuti wakhala Mfumu, ngati kuti wakhalanso pa mpando wake wachifumu.—1 Mbiri 16:1, 31; Yesaya 52:7; Chivumbulutso 11:15-17; 15:3; 19:1, 2, 6.
10. Kodi ntchito yaikulu ya mafumu a Israyeli inali yotani? Perekani chitsanzo.
10 Koma nayi mfundo yofunika: Ntchito yaikulu ya mafumu akale inali ija ya kuzenga milandu ndi kugamula ziweruzo. (Miyambo 29:14) Kumbukirani chiweruzo cha nzeru cha Solomo pamene aliyense wa akazi aŵiriwo anati khanda limodzimodzilo ndi lake. (1 Mafumu 3:16-28; 2 Mbiri 9:8) Imodzi ya nyumba zake zaboma inali “Khumbi la Mpando Wachifumu loweruziramo iye,” lotchedwanso “khumbi la milandu.” (1 Mafumu 7:7) Yerusalemu anatchedwa malo kumene “anaika mipando ya chiweruzo.” (Salmo 122:5) Mwachionekere, ‘kukhala pa mpando wachifumu’ kungatanthauzenso kuweruza.—Eksodo 18:13; Miyambo 20:8.
11, 12. (a) Kodi kukhala pa mpando kwa Yehova, kotchulidwa m’Danieli chaputala 7 kunatanthauzanji? (b) Kodi malemba ena amatsimikiza motani kuti Yehova amakhala pa mpando kuweruza?
11 Tsopano tiyeni tibwerere kuja kumene Danieli anaona ‘Nkhalamba ya Kale Lomwe ikukhala.’ Danieli 7:10 amawonjezera kuti: “Woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.” Inde, Nkhalamba ya Kale Lomwe inali kukhala pansi kuti ipereke chiweruzo chokhudza kulamulira dziko ndi kuweruza Mwana wa munthu kukhala woyenera kulamulira. (Danieli 7:13, 14) Ndiyeno timaŵerenga kuti “inadza Nkhalamba ya Kale Lomwe; ndi mlandu unakomera opatulika,” aja oweruzidwa kukhala oyenera kulamulira ndi Mwana wa munthu. (Danieli 7:21, 22) Potsirizira pake ‘Woweruza mlandu anakhalako’ ndi kupereka chiweruzo chowopsa pa ulamuliro womaliza wa padziko lonse.—Danieli 7:26.a
12 Chotero, pamene Danieli anaona Mulungu ‘akukhala pa mpando wachifumu’ zinatanthauza kuti Iye anafika kudzapereka chiweruzo. Poyambirira Davide anaimba kuti: “[Yehova] mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama.” (Salmo 9:4, 7) Ndipo Yoweli analemba kuti: “Agalamuke amitundu, nakwerere ku chigwa cha Yosafati; pakuti [ine Yehova] ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse.” (Yoweli 3:12; yerekezerani ndi Yesaya 16:5.) Onse aŵiri Yesu ndi Paulo anakhalapo pamlandu umene munthu anakhala pansi akumazenga mlandu ndi kupereka chiweruzo.b—Yohane 19:12-16; Machitidwe 23:3; 25:6.
Malo a Yesu
13, 14. (a) Kodi ndi chitsimikizo chiti chimene anthu a Mulungu anali nacho chakuti Yesu adzakhala Mfumu? (b) Kodi Yesu anakhala liti pa mpando wake wachifumu, ndipo analamulira kuyambira mu 33 C.E. ndi mtsogolo mwake m’lingaliro lotani?
13 Yehova ali ponse paŵiri Mfumu ndi Woweruza. Bwanji nanga za Yesu? Mngelo wolengeza kubadwa kwake anati: “Ambuye Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: . . . ndipo ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:32, 33) Yesu adzakhala woloŵa nyumba wachikhalire wa ufumu wa Davide. (2 Samueli 7:12-16) Adzalamulira ali kumwamba, pakuti Davide anati: “Yehova ananena kwa Ambuye wanga [Yesu], Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu. Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu.”—Salmo 110:1-4.
14 Kodi zimenezo zinali kudzachitika liti? Yesu sanalamulire monga Mfumu pamene anali munthu. (Yohane 18:33-37) Mu 33 C.E., iye anamwalira, anaukitsidwa, nakwera kumwamba. Ahebri 10:12 amati: “Adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.” Kodi Yesu anali ndi ulamuliro wotani? “[Mulungu] namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m’zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu . . . nampatsa iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Eklesia.” (Aefeso 1:20-23) Chifukwa chakuti Yesu nthaŵiyo anali ndi ulamuliro waufumu pa Akristu, Paulo anakhoza kulemba kuti Yehova “anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutiloŵetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake.”—Akolose 1:13; 3:1.
15, 16. (a) Kodi nchifukwa ninji tikuti Yesu sanakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 33 C.E.? (b) Kodi Yesu anayamba liti kulamulira mu Ufumu wa Mulungu?
15 Komabe, nthaŵiyo Yesu sanakhale Mfumu ndi Woweruza pa amitundu. Anakhala pafupi ndi Mulungu, akumayembekezera nthaŵi ya kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Paulo analemba ponena za iye kuti: “Za mngelo uti anati nthaŵi iliyonse, Khala pa dzanja lamanja langa, kufikira ndikaika adani ako mpando wa ku mapazi ako?”—Ahebri 1:13.
16 Mboni za Yehova zafalitsa umboni wochuluka wakuti nyengo ya kuyembekeza kwa Yesu inatha mu 1914, pamene iye anakhala wolamulira wa Ufumu wa Mulungu m’miyamba yosaoneka. Chivumbulutso 11:15, 18 chimati: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” “Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu.” Inde, amitundu anakwiyirana pa Nkhondo Yadziko I. (Luka 21:24) Nkhondo, zivomezi, miliri, njala, ndi zina zotero, zimene taona chiyambire 1914 zimatsimikiza kuti Yesu tsopano akulamulira mu Ufumu wa Mulungu, ndi kuti mapeto a dzikoli ali pafupi.—Mateyu 24:3-14.
17. Kodi ndi mfundo zofunika ziti zimene tapeza kufikira pano?
17 Nawa malongosoledwe achidule: Mulungu anganenedwe kuti wakhala pa mpando wachifumu monga Mfumu, koma m’lingaliro lina iye angakhale pa mpando wake wachifumu kuweruza. Mu 33 C.E., Yesu anakhala kudzanja lamanja la Mulungu, ndipo tsopano ndi Mfumu ya Ufumuwo. Koma kodi Yesu, amene akulamulira monga Mfumu tsopano, alinso Woweruza? Ndipo nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika kwa ife, makamaka nthaŵi inoyi?
18. Kodi pali umboni wotani wakuti Yesu adzakhalanso Woweruza?
18 Yehova, amene ali ndi mphamvu ya kuika oweruza, anasankha Yesu monga Woweruza wokwaniritsa miyezo Yake. Yesu anasonyeza zimenezi polankhula zakuti anthu adzakhala amoyo mwauzimu: “Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana.” (Yohane 5:22) Komabe, mbali ya Yesu ya kuweruza imaposa pamenepo, pakuti alinso woweruza wa amoyo ndi akufa. (Machitidwe 10:42; 2 Timoteo 4:1) Nthaŵi ina Paulo anati: “[Mulungu] anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu [Yesu] amene anamuikiratu, napatsa anthu chitsimikizo, pamene anamuukitsa iye.”—Machitidwe 17:31; Salmo 72:2-7.
19. Kodi nchifukwa ninji kuli kolondola kunena kuti Yesu amakhala pa mpando monga Woweruza?
19 Kodi tili ndi chifukwa chomveka chonenera kuti Yesu amakhala pa chimpando cha ulemerero wake pantchito yeniyeni ya Woweruza? Inde. Yesu anauza atumwi kuti: “Inu amene munanditsata ine, m’kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iŵiri, kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Mateyu 19:28) Ngakhale kuti Yesu tsopano ndi Mfumu ya Ufumuwo, ntchito yake ina yotchulidwa pa Mateyu 19:28 idzaphatikizapo kukhala pa mpando wachifumu kuweruza mkati mwa Zaka Chikwi. Panthaŵiyo adzaweruza anthu onse, olungama ndi osalungama. (Machitidwe 24:15) Kuli kothandiza kukumbukira zimenezi pamene tisumika maganizo athu pa limodzi la mafanizo a Yesu limene limakhudza nthaŵi yathu ndi miyoyo yathu.
Kodi Fanizolo Limati Chiyani?
20, 21. Kodi atumwi a Yesu anafunsa za chiyani chimene chimakhudza nthaŵi yathu, chikumabutsa funso lotani?
20 Imfa ya Yesu itayandikira, atumwi ake anamfunsa kuti: “Zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha [kukhalapo, NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Yesu analosera zochitika zazikulu zimene zidzakhalako pa dziko lapansi ‘mathedwe asanadze.’ Mapetowo atakhala pafupi, mitundu ‘idzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.’—Mateyu 24:14, 29, 30.
21 Koma kodi anthu a mitunduwo zinthu zidzawakhalira bwanji pamene Mwana wa munthu adza ndi ulemerero wake? Tiyeni tipeze yankho lake m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, limene limayamba ndi mawu aŵa: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 25:31, 32.
22, 23. Kodi ndi mfundo ziti zimene zikusonyeza kuti fanizo la nkhosa ndi mbuzi silinayambe kukwaniritsidwa mu 1914?
22 Kodi fanizo limeneli limanena za nthaŵi pamene Yesu anakhala pa mpando m’mphamvu yachifumu mu 1914, malinga ndi zimene tadziŵa nthaŵi yaitali? Eya, Mateyu 25:34 amanenadi kuti iye ndi Mfumu, choncho fanizolo moyenerera liyamba kugwira ntchito Yesu atakhala Mfumu mu 1914. Koma kodi ndi kuweruza kotani kumene anachita mwamsanga pambuyo pake? Sikunali kuweruza “mitundu yonse.” M’malo mwake, anasumika maganizo ake pa aja omwe amati ndiwo “nyumba ya Mulungu.” (1 Petro 4:17) Mogwirizana ndi Malaki 3:1-3, Yesu, monga mthenga wa Yehova, anayang’anira mwa chiweruzo Akristu odzozedwa otsala pa dziko lapansi. Inalinso nthaŵi ya kupereka chiweruzo pa Dziko Lachikristu, limene monama linati ndilo “nyumba ya Mulungu.”c (Chivumbulutso 17:1, 2; 18:4-8) Komabe palibe chimene chikusonyeza kuti panthaŵiyo, kapena chiyambire nthaŵiyo, Yesu anakhala pa mpando kuweruza anthu a mitundu yonse komaliza monga nkhosa kapena mbuzi.
23 Tikapenda zochita za Yesu m’fanizolo, tikumuona iye akuweruza mitundu yonse komaliza. Fanizolo silikusonyeza kuti kuweruzako kudzapitiriza kwa nyengo ya zaka zambiri, ngati kuti anthu onse amene afa zaka zakumbuyoku aweruzidwira ku imfa yosatha kapena ku moyo wosatha. Zikuoneka kuti unyinji wa awo amene amwalira zaka zaposachedwapa apita kumanda a anthu onse. (Chivumbulutso 6:8; 20:13) Koma, fanizolo likusonyeza nthaŵi pamene Yesu akuweruza anthu a “mitundu yonse” amene ali amoyo panthaŵiyo ndipo akuyang’anizana ndi chilango cha chiweruzo chake.
24. Kodi fanizo la nkhosa ndi mbuzi lidzakwaniritsidwa liti?
24 M’mawu ena, fanizolo likusonya mtsogolo pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake. Adzakhala pa mpando kuweruza anthu amoyo panthaŵiyo. Chiweruzo chake chidzazikidwa pa umunthu wawo umene asonyeza. Nthaŵiyo “wolungama ndi woipa” adzakhala atazindikiridwa bwino. (Malaki 3:18) Kupereka chiweruzocho ndi chilango chake kudzachitika panthaŵi yaifupi. Yesu adzapereka ziweruzo zolungama zozikidwa pa mkhalidwe umene munthu yense adzakhala atasonyeza.—Onaninso 2 Akorinto 5:10.
25. Kodi Mateyu 25:31 akusonyezanji mwa kunena kuti Mwana wa munthu wakhala pa chimpando choŵala?
25 Chotero, zimenezi zikutanthauza kuti ‘kukhala kwa Yesu pa chimpando cha kuŵala kwake’ kwa chiweruzo, kotchulidwa pa Mateyu 25:31, kumanena za nthaŵi ya mtsogolo pamene Mfumu yamphamvu imeneyi idzakhala pa mpando kupereka chiweruzo ndi chilango pa mitundu. Inde, nkhani ya chiweruzo imene ikunena za Yesu pa Mateyu 25:31-33, 46 njofanana ndi nkhani ya pa Danieli chaputala 7, pamene Mfumu yolamulira, Nkhalamba ya Kale Lomwe, inakhala pa mpando kuchita ntchito yake ya Woweruza.
26. Kodi ndi kafotokozedwe kotani katsopano kamene kakhalapo?
26 Kulimva mwa njira imeneyi fanizo la nkhosa ndi mbuzi kumasonyeza kuti chiweruzo pa nkhosa ndi mbuzi chidzaperekedwa mtsogolo. Chidzachitika “masauko” [“chisautso,” NW] otchulidwa pa Mateyu 24:29, 30 atayamba ndipo Mwana wa munthu ‘adza ndi ulemerero.’ (Yerekezerani ndi Marko 13:24-26.) Ndiyeno, pokhala dongosolo lonse loipa lidzakhala litafika pamapeto ake, Yesu adzakhala pabwalo la milandu ndi kupereka chiweruzo ndi chilango.—Yohane 5:30; 2 Atesalonika 1:7-10.
27. Kodi tiyenera kufuna kudziŵa chiyani ponena za fanizo la Yesu lomaliza?
27 Zimenezi zikuwongolera kamvedwe kathu ka nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa fanizo la Yesu, kamene kakusonyeza pamene nkhosa ndi mbuzi zidzaweruzidwa. Koma kodi zimatikhudza motani ife amene tikulalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu? (Mateyu 24:14) Kodi zikuchititsa ntchito yathu kukhala yosafunika kwenikweni, kapena kodi zikutipatsa thayo lolemera kwambiri? Tiyeni tione m’nkhani yotsatira mmene zikutikhudzira.
-
-
Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?Nsanja ya Olonda—1995 | October 15
-
-
Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?
“Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.”—MATEYU 25:32.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita chidwi ndi fanizo la nkhosa ndi mbuzi?
YESU KRISTU analidi Mphunzitsi wamkulu woposa onse pa dziko lapansi. (Yohane 7:46) Imodzi ya njira zake zophunzitsira inali kugwiritsira ntchito miyambi, kapena mafanizo. (Mateyu 13:34, 35) Ameneŵa anali osavuta koma amphamvu posonyeza choonadi chakuya chauzimu ndi chaulosi.
2 M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu anasonyeza nthaŵi pamene iye adzakhala ndi malo apadera: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi . . . ” (Mateyu 25:31) Fanizo limeneli tiyenera kuchita nalo chidwi chifukwa ndilo limene Yesu akumaliza nalo yankho lake pa funsolo: “Chizindikiro cha [kukhalapo, NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Koma kodi zimenezi zikutanthauzanji kwa ife?
3. Poyambirira m’nkhani yake, kodi Yesu anati nchiyani chidzachitika chitangoyamba chisautso chachikulu?
3 Yesu ananeneratu za zochitika zodabwitsa zimene zidzachitika “pomwepo” chitaulika chisautso chachikulu, zochitika zomwe tikuziyembekezera. Anati pomwepo padzaoneka “chizindikiro cha Mwana wa munthu.” Chimenechi chidzakhudza kwambiri “mitundu yonse ya pa dziko lapansi” imene “idzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” Mwana wa munthu adzatsagana ndi “angelo ake.” (Mateyu 24:21, 29-31)a Bwanji nanga za fanizo la nkhosa ndi mbuzi? Mabaibulo amakono amaliika m’chaputala 25, koma lili mbali ya yankho la Yesu, lomafotokoza zowonjezera ponena za kudza kwake ndi ulemerero ndipo lomasumika pa kuweruza kwake “mitundu yonse.”—Mateyu 25:32.
Anthu a m’Fanizolo
4. Kodi fanizo la nkhosa ndi mbuzi likuyamba ndi mawu otani ponena za Yesu, ndipo ndaninso amene akutchulidwa?
4 Yesu akuyamba fanizo lake mwakuti: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza.” Mwachionekere mukumdziŵa “Mwana wa munthu.” Kaŵirikaŵiri olemba Mauthenga Abwino anagwiritsira ntchito mawuwo kunena Yesu. Ngakhale Yesu mwiniyo anatero, mosakayika akumakumbuka masomphenya a Danieli a “wina ngati mwana wa munthu” akuyandikira kwa Nkhalamba ya Kale Lomwe kulandira “ulamuliro ndi ulemerero, ndi ufumu.” (Danieli 7:13, 14; Mateyu 26:63, 64; Marko 14:61, 62) Pamene Yesu ndiye munthu wamkulu m’fanizoli, iye saali yekha. Poyambirira m’nkhaniyo, monga momwe pakufotokozera pa Mateyu 24:30, 31, iye anati pamene Mwana wa munthu ‘alinkudza ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu,’ angelo ake adzachita mbali yofunika kwambiri. Mofanana ndi zimenezo, fanizo la nkhosa ndi mbuzi likusonyeza angelo pamodzi ndi Yesu pamene iye ‘akukhala pa chimpando cha kuŵala kwake’ kuweruza. (Yerekezerani ndi Mateyu 16:27.) Koma Woweruzayo ndi angelo ake ali kumwamba, choncho kodi fanizolo likufotoza za anthu?
5. Kodi “abale” a Yesu tingawadziŵe motani?
5 Kupenda fanizolo kumasonyeza magulu atatu amene tiyenera kuwazindikira. Pa nkhosa ndi mbuzi, Mwana wa munthu akuwonjezapo gulu lina lachitatu limene kudziŵika kwake nkofunika kwambiri pa kuzindikira nkhosa ndi mbuzi. Yesu akutcha gulu lachitatulo abale ake auzimu. (Mateyu 25:40, 45) Iwo ayenera kukhala alambiri oona, pakuti Yesu anati: “Aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga . . . , yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.” (Mateyu 12:50; Yohane 20:17) Moyenerera kwambiri, Paulo analemba za Akristu omwe ali mbali ya “mbewu ya Abrahamu” ndi amenenso ali ana a Mulungu. Anatcha ameneŵa “abale” a Yesu ndi “olandirana nawo maitanidwe akumwamba.”—Ahebri 2:9–3:1; Agalatiya 3:26, 29.
6. Kodi “aang’onong’ono” a abale a Yesu ndani?
6 Kodi nchifukwa ninji Yesu anatchula “aang’onong’ono” a abale ake? Mawuwo amakumbutsa zimene atumwi anamumva akunena poyambirira. Posiyanitsa Yohane Mbatizi, yemwe anafa Yesu asanafe, motero nakhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi, ndi aja opeza moyo wakumwamba, Yesu anati: “Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu ufumu wakumwamba amkulira iye.” (Mateyu 11:11) Ena opita kumwamba angakhale anali omveka mumpingo, monga atumwi, ndi ena osamveka kwenikweni, koma onsewo ndi abale auzimu a Yesu. (Luka 16:10; 1 Akorinto 15:9; Aefeso 3:8; Ahebri 8:11) Chotero, ngakhale ngati ena anaoneka ochepa pa dziko lapansi, anali abale ake ndipo anayenera kuchitidwa monga otero.
Kodi Nkhosa ndi Mbuzi Ndani?
7, 8. Kodi Yesu anati bwanji ponena za nkhosa, choncho nchiyani chomwe tinganene za iwo?
7 Timaŵerenga zotere ponena za chiweruzo cha nkhosa: “[Yesu] [a]dzanena kwa iwo akudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza ine; wamaliseche ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi ine; ndinali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa ine. Pomwepo olungama adzamyankha iye kuti, Ambuye, tinakuonani inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuonani inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tinadza kwa inu? Ndipo mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale aang’onong’ono aŵa, munandichitira ichi ine.”—Mateyu 25:34-40.
8 Ndithudi, nkhosa zoweruzidwa kukhala kulamanja kwa Yesu kolemekezeka ndi kwachiyanjo zimaimira kagulu ka anthu. (Aefeso 1:20; Ahebri 1:3) Kodi anachitanji ndipo liti? Yesu akuti iwo mokoma mtima, mwaulemu, ndi mowoloŵa manja anampatsa chakudya, madzi, ndi zovala, kumthandiza pamene anadwala kapena pamene anali m’ndende. Pamene nkhosazo zikuti sizinachite zimenezo kwa Yesu mwachindunji, iye akuti zinachirikizadi abale ake auzimu, otsalira a Akristu odzozedwa, choncho m’lingaliro limenelo anamchitira iye zimenezo.
9. Kodi nchifukwa ninji fanizolo silikunena za mu Zaka Chikwi?
9 Fanizolo silikunena za mu Zaka Chikwi, pakuti nthaŵiyo odzozedwa sadzakhala anthu omavutika ndi njala, ludzu, kudwala, kapena sadzakhala m’ndende. Komabe, ambiri a iwo zinthu zotero zawachitikira m’nthaŵi ino ya chimaliziro cha dongosolo ili la zinthu. Chiyambire pamene Satana anagwetseredwa pa dziko lapansi, walunjikitsa mkwiyo wake pa otsalira monga chandamale chake chapadera, akumawatonzetsa, kuwazunza, ndi kuwapha.—Chivumbulutso 12:17.
10, 11. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kosayenera kulingalira kuti nkhosazo zikuphatikizapo aliyense wokomera mtima abale a Yesu? (b) Moyenerera, kodi nkhosa zimaimira yani?
10 Kodi Yesu akunena kuti yense wosonyeza kukoma mtima pang’ono kwa abale ake, monga mwa kuwapatsa buledi kapena madzi akumwa, amakhala mmodzi wa nkhosazo? Zoona, kuchita mokoma mtimako kungasonyeze kukoma mtima kwa munthu, komatu, zikuoneka kuti pali zochuluka zimene zikufunika kwa nkhosa za m’fanizoli. Mwachitsanzo, Yesu sanali konse kunena za okana Mulungu kapena atsogoleri achipembedzo amene angakomere mtima mmodzi wa abale akeŵa. Mosiyana ndi zimenezo, Yesu kaŵiri anatcha nkhosazo “olungama.” (Mateyu 25:37, 46) Chotero nkhosazo ziyenera kukhala aja omwe nthaŵi yaitali athandiza—kuchirikiza mwachangu—abale a Kristu ndipo asonyeza chikhulupiriro kufikira pa kukhala ndi kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu.
11 M’zaka mazanamazana, anthu ambiri monga Abrahamu akhala ndi kaimidwe kolungama. (Yakobo 2:21-23) Nowa, Abrahamu, ndi okhulupirika ena akuphatikizidwa pa “nkhosa zina” amene adzalandira moyo m’Paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. Posachedwapa enanso mamiliyoni ambiri alandira kulambira koona monga nkhosa zina ndipo akhala “gulu limodzi” ndi odzozedwa. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9) Aŵa oyembekezera kukhala pa dziko lapansi amazindikira kuti abale a Yesu ndiwo akazembe a Ufumu choncho awathandiza—kuthupi ndi mwauzimu. Zimene nkhosa zina zimachitira abale ake pa dziko lapansi Yesu amaona kuti zimachitira iye. Anthu otero amene adzakhala ndi moyo pamene iye adzadza kudzaweruza mitundu adzaweruzidwa monga nkhosa.
12. Kodi nkhosa zingafunsirenji mmene zinamkomera mtima Yesu?
12 Ngati nkhosa zina tsopano zikulalikira uthenga wabwino limodzi ndi odzozedwa ndipo zikuwathandiza, chifukwa ninji akufunsa kuti: “Ambuye, tinakuonani inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani?” (Mateyu 25:37) Pangakhale zifukwa zingapo. Limeneli ndi fanizo. Mwa ilo, Yesu akusonyeza kudera nkhaŵa kwambiri abale ake auzimu; amalingalira za iwo, amavutika nawo. Poyamba Yesu anati: “Iye wakulandira inu, andilandira ine, ndi wakulandira ine, amlandira iye amene ananditumiza ine.” (Mateyu 10:40) M’fanizo limeneli, Yesu akupitiriza ndi mfundo imeneyo, kusonyeza kuti (zabwino kapena zoipa) zochitidwa kwa abale ake zimafika ndi kumwamba komwe; zili monga ngati zimachitidwa kwa iye kumwamba. Ndiponso, Yesu panopa akugogomezera muyezo wa Yehova woweruzira, kumveketsa bwino kuti chiweruzo cha Mulungu kaya choyanja kapena chotsutsa, nchoyenera ndi cholungama. Mbuzizo sizingapereke chodzikhululukira chakuti, ‘Koma tikanakuonani inu mwini.’
13. Kodi nchiyani chimene onga mbuzi angatchere Yesu “Ambuye”?
13 Titangomvetsa pamene chiweruzo chosonyezedwa m’fanizoli chidzaperekedwa, timakhala ndi chithunzi chabwino cha amene ali mbuzi. Lidzakwaniritsidwa pamene “padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza . . . ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:29, 30) Opulumuka chisautso cha Baibulo Wamkulu amene anyozera abale a Mfumu mwina tsopano adzatcha Woweruzayo “Ambuye,” pokhulupirira kuti adzapulumutsa miyoyo yawo.—Mateyu 7:22, 23; yerekezerani ndi Chivumbulutso 6:15-17.
14. Kodi Yesu adzaweruza nkhosa ndi mbuzi pazifukwa zotani?
14 Komabe, chiweruzo cha Yesu sichidzazikidwa pa kuyesayesa kudzilungamitsa kwa omwe kale anali atchalitchi, okana Mulungu, ndi ena. (2 Atesalonika 1:8) M’malo mwake, woweruzayo adzapenda mitima yawo ndi zochita zakale za anthuwo kulinga kwa “aang’onong’ono aŵa [a abale ake].” Zoona, Akristu odzozedwa otsalira pa dziko lapansi chiŵerengero chawo chikuchepa. Komabe, malinga ngati odzozedwa, opanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” apitiriza kugaŵira chakudya chauzimu ndi chitsogozo, oyembekeza kukhala nkhosa ali ndi mwaŵi wakuchitira chabwino kagulu ka kapolo, monga momwedi lachitira ‘khamu lalikulu ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu.’—Chivumbulutso 7:9, 14.
15. (a) Kodi ambiri asonyeza motani kuti ali ngati mbuzi? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kunena kuti kaya wina ndi nkhosa kapena mbuzi?
15 Kodi abale a Kristu ndi mamiliyoni a nkhosa zina ogwirizana nawo kukhala gulu limodzi achitiridwa motani? Anthu ambiri angakhale sanaukire oimira Kristu, komanso sanachitire anthu ake mwachikondi. Pokonda dziko loipa, onga mbuzi amakana uthenga wa Ufumu, kaya adzimverere iwo eni kaya aumve mwa njira ina. (1 Yohane 2:15-17) Ndithudi, Yesu makamaka ndiye waikidwa kupereka chiweruzo. Sizili kwa ife kunena amene ali nkhosa ndi amene ali mbuzi.—Marko 2:8; Luka 5:22; Yohane 2:24, 25; Aroma 14:10-12; 1 Akorinto 4:5.
Kodi Gulu Lililonse Lili ndi Mtsogolo Motani?
16, 17. Kodi nkhosa zidzakhala ndi mtsogolo motani?
16 Yesu anapereka chiweruzo chake pa nkhosa kuti: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Ndi chiitano chabwino chotani nanga chimenecho—“Idzani”! Kuti? Ku moyo wosatha, malinga ndi zimene anafotokoza mwachidule kuti: “Olungama [adzaloŵa] ku moyo wa nthaŵi zonse.”—Mateyu 25:34, 46.
17 M’fanizo la matalente, Yesu anasonyeza zofunika kwa aja amene adzalamulira naye kumwamba, koma m’fanizo ili akusonyeza zofunika kwa nzika za Ufumuwo. (Mateyu 25:14-23) Mosapita m’mbali, chifukwa cha kuthandiza kwawo abale a Yesu ndi mtima wonse, nkhosazo zilandira malo m’chigawo cha pa dziko lapansi cha Ufumu wake. Adzasangalala ndi moyo m’paradaiso pa dziko lapansi—mtsogolo mmene Mulungu anawakonzera “pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi” la anthu oomboleka.—Luka 11:50, 51.
18, 19. (a) Kodi Yesu adzapereka chiweruzo chotani pa mbuzi? (b) Kodi titsimikiza bwanji kuti mbuzi sizidzazunzika kwa muyaya?
18 Ha, chiweruzo choperekedwa pa mbuzi nchosiyana chotani nanga ndi zimenezo! “Pomwepo iye adzanena kwa iwo akudzanja lamanzere, Chokani kwa ine otembereredwa inu, kumoto wa nthaŵi zonse wokolezedwera Mdyerekezi ndi amithenga ake: pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa ine: ndinali mlendo, ndipo simunandilandira ine; wamaliseche ndipo simunandiveka ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona ine. Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m’nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani inu? Pomwepo iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa aŵa aang’onong’ono, munalibe kundichitira ichi ine.”—Mateyu 25:41-45.
19 Ophunzira Baibulo akudziŵa kuti zimenezi sizikutanthauza kuti miyoyo yosafa ya onga mbuzi idzazunzika m’moto wamuyaya ayi. Pakuti anthu ndiwo miyoyo; alibe moyo wosafa. (Genesis 2:7; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Mwa kuweruzira mbuzi ku “moto wa nthaŵi zonse,” Woweruzayo akutanthauza chiwonongeko chopanda chiyembekezo cha mtsogolo, chimenenso chidzakhala mapeto achikhalire a Mdyerekezi ndi ziŵanda zake. (Chivumbulutso 20:10, 14) Chotero, Woweruza wa Yehova akupereka ziweruzo zosiyana. Akuuza nkhosa kuti, “Idzani”; mbuzi, “Chokani kwa ine.” Nkhosazo zidzalandira “moyo wa nthaŵi zonse.” Mbuzi zidzalandira “chilango cha nthaŵi zonse.”—Mateyu 25:46.b
Kodi Zikutanthauzanji kwa Ife?
20, 21. (a) Kodi ndi ntchito iti yofunika imene Akristu ayenera kuchita? (b) Kodi ndi kugaŵanika kotani kumene kukuchitika tsopano? (c) Kodi anthu adzakhala mumkhalidwe wotani pamene fanizo la nkhosa ndi mbuzi liyamba kukwaniritsidwa?
20 Atumwi anayi amene anamva yankho la Yesu lonena za chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha chimaliziro cha dongosololi anali ndi zochuluka zozilingalira. Anafunika kukhala ogalamuka ndi odikira. (Mateyu 24:42) Anafunikanso kuchita ntchito ya umboni yotchulidwa pa Marko 13:10. Lerolino Mboni za Yehova zikuchita ntchitoyo mwachangu.
21 Koma, kodi kamvedwe katsopano kameneka ka fanizo la nkhosa ndi mbuzi kamatanthauzanji kwa ife? Eya, anthu ayamba kale kusankha mbali yoimako. Ena ali ‘panjira yaikulu yakumuka nayo kukuonongeka,’ pamenenso ena akuyesa kukhalabe ‘panjirayo yochepetsa yakumuka nayo kumoyo.’ (Mateyu 7:13, 14) Koma nthaŵi imene Yesu adzapereka chiweruzo chomaliza pa nkhosa ndi mbuzi zosonyezedwa m’fanizoli ikali kutsogolo. Pamene Mwana wa munthu adzadza monga Woweruza, adzatsimikiza kuti Akristu oona ambiri—kwenikweni “khamu lalikulu” la nkhosa zodzipatulira—ayeneretsedwa kupyola mbali yomaliza ya “chisautso chachikulu” kuloŵa m’dziko latsopano. Chiyembekezocho chiyenera kutipatsa chimwemwe tsopano. (Chivumbulutso 7:9, 14) Komabe, unyinji wa “mitundu yonse” adzakhala atasonyeza kuti ali ngati mbuzi zouma khosi. “Adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse.” Dziko lapansi lidzakhala pampumulo wotani nanga!
22, 23. Popeza kukwaniritsidwa kwa fanizolo kukali mtsogolo, kodi nchifukwa ninji ntchito yathu yolalikira ili yofunika kwambiri lerolino?
22 Pamene chiweruzo chofotokozedwa m’fanizolo chili patsogolopa, ngakhale tsopano kanthu kena kofunika kwambiri kakuchitika. Ife Akristu tikuchita ntchito yopulumutsa miyoyo ya kulengeza uthenga wogaŵanitsa anthu. (Mateyu 10:32-39) Paulo analemba kuti: “Pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la [Yehova, NW] adzapulumuka. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:13, 14) Utumiki wathu wapoyera ukufika anthu m’maiko oposa 230 ndi dzina la Mulungu ndi uthenga wake wa chipulumutso. Abale odzozedwa a Kristu akali kutsogolera ntchitoyi. Pafupifupi mamiliyoni asanu a nkhosa zina agwirizana nawo tsopano. Ndipo anthu padziko lonse akulabadira uthenga wolengezedwa ndi abale a Yesu.
23 Ambiri amafikidwa ndi uthenga wathu pamene tilalikira kunyumba ndi nyumba kapena mwamwaŵi. Ena angamve za Mboni za Yehova ndi zimene timaimira mwa njira zosadziŵika kwa ife. Nthaŵi ya chiweruzo ikafika, kodi Yesu adzalingalira za thayo la anthu monga gulu ndi mikhalidwe ya banja kufika pamlingo wotani? Sititha kunena, ndipo kuyesa kulotera nkosathandiza. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:14.) Ambiri tsopano amanyalanyaza dala anthu a Mulungu, kuwatonza, kapena kutengamo mbali kuwazunza. Nchifukwa chake, nthaŵi ino njowopsa; oterowo angakhale akusanduka aja amene Yesu adzawaweruza monga mbuzi.—Mateyu 10:22; Yohane 15:20; 16:2, 3; Aroma 2:5, 6.
24. (a) Kodi nchifukwa ninji munthu yense afunika kuchitapo kanthu pa ulaliki wathu? (b) Kodi phunziroli lakuthandizani kuona motani utumiki wanu?
24 Koma chosangalatsa nchakuti ambiri amamva, amaphunzira Mawu a Mulungu, nakhala Mboni za Yehova. Ena amene tsopano akuoneka ngati mbuzi angasinthe ndi kukhala ngati nkhosa. Mfundo yake njakuti aja amene akumva ndi kuchirikiza mwachangu otsalira a abale a Kristu akupereka umboni tsopano mwa njira imeneyo umene udzapereka chifukwa chowaikira kudzanja lamanja la Yesu pamene iye, patsogolopa, adzakhala pa mpando wake wachifumu kuweruza. Ameneŵa akudalitsidwa ndipo adzadalitsidwabe. Chotero, fanizo limeneli liyenera kutisonkhezera kugwira ntchito ndi changu chonse mu utumiki Wachikristu. Tisanachedwe, tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu ndipo mwa njirayo kupatsa ena mwaŵi wa kuchitapo kanthu. Ndiyeno zili kwa Yesu kupereka chiweruzo, chotsutsa kapena choyanja.—Mateyu 25:46.
-