Kodi Mudzakhulupirika Monga Eliya?
“Ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.” —MALAKI 4:5.
1. Kodi pakuoneka tsoka lotani Israyeli atakhala m’Dziko Lolonjezedwa zaka ngati 500?
‘DZIKO loyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.’ (Eksodo 3:7, 8) Ndilo limene Yehova Mulungu anapatsa Aisrayeli atawamasula mu undende ku Igupto m’zaka za zana la 16 B.C.E. Koma taonani! Zaka mazana asanu zapita, ndipo tsopano mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi muli njala yadzaoneni. Udzu wobiriŵira kulibe. Nyama zikufa, ndipo mvula siinagwe zaka zitatu ndi theka. (1 Mafumu 18:5; Luka 4:25) Kodi chachititsa tsokali nchiyani?
2. Kodi nchiyani chachititsa vuto la dziko lonse la Israyeli?
2 Mpatuko ndiwo wachititsa mavutowa. Moswa Chilamulo cha Mulungu, Mfumu Ahabu wakwatira mfumukazi yachikanani Yezebeli ndipo wamlola kuyambitsa kulambira Baala m’Israyeli. Komanso, wamangira mulungu wonyengayu kachisi m’Samariya, likulu la ufumuwo. Kalanga ine! Aisrayeli anyengedwa nakhulupirira kuti kulambira Baala kudzawadzetsera mbewu zochuluka! Komabe, monga momwe Yehova wachenjezera, iwo tsopano ali pangozi ya ‘kuwonongeka msanga m’dziko lawo lokomalo.’—Deuteronomo 7:3, 4; 11:16, 17; 1 Mafumu 16:30-33.
Mayeso Aakulu a Umulungu
3. Kodi mneneri Eliya akusumika motani maganizo pa vuto lenileni la Israyeli?
3 Njalayo itayamba, mneneri wokhulupirika wa Mulungu Eliya akuuza Mfumu Ahabu kuti: “Pali Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.” (1 Mafumu 17:1) Choonadi choŵaŵa cha chilengezochi chitakwaniritsidwa, mfumuyo ikuimba mlandu Eliya kuti ndiye wadzetsa mavuto pa Israyeli. Koma Eliya ayankha kuti Ahabu ndi anyumba yake ndiwo ali ndi mlandu chifukwa cha mpatuko wawo pokhala olambira Baala. Kuti athetse nkhaniyo, mneneri wa Yehova alimbikitsa Mfumu Ahabu kuti asonkhanitse Israyeli yense ku Phiri la Karimeli limodzi ndi aneneri 450 a Baala ndi aneneri 400 a mlongoti wopatulika. Ahabu ndi anthu ake asonkhana komweko, mwinamwake ali ndi chiyembekezo chakuti chochitikacho chidzathetsa chiralacho. Koma Eliya asumika maganizo pankhani yofunika kwambiri. “Mukayikakayika kufikira liti?” Afunsa motero. “Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo.” Aisrayeli alibe mawu.—1 Mafumu 18:18-21.
4. Kuti athetse nkhani ya Umulungu, kodi Eliya akuti achitenji?
4 Kwa zaka zambiri Aisrayeli ayesa kusanganiza kulambira Yehova ndi kulambira Baala. Kuti athetse nkhani ya Umulungu, Eliya tsopano akuti pakhale mpikisano. Iye adzakonza ng’ombe yopereka nsembe, ndipo inayo, aneneri a Baala adzaikonza. Kenako Eliya akuti: “Muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu.” (1 Mafumu 18:23, 24) Tangolingalirani moto kuchokera kumwamba poyankha pemphero!
5. Kodi kupanda pake kwa kulambira Baala kukuvumbulidwa motani?
5 Eliya apempha aneneri a Baala kuti ayambe ndiwo. Iwo akonza ng’ombe yopereka nsembe naiika paguwa. Ndiyeno avinavina mozungulira guwalo, akupemphera kuti: “Baala, timvereni ife.” Zimenezi zipitiriza “kuyambira m’maŵa kufikira pausana.” “Kwezani mawu,” awatonyola Eliya. Baala ayenera kuti watanganidwa ndi nkhani ina yofulumira, “kaya agona, adzagalamuka.” Posapita nthaŵi aneneri a Baala ataya mtima nachita ngati amsala. Taonani! Akudzitematema ndi mipeni, ndipo mwazi uli chuu pamabala awo. Ndipotu pali phokoso lalikulu chotani nanga pamene onse 450 alira mofuula kwambiri! Koma kulibe yankho.—1 Mafumu 18:26-29.
6. Kodi Eliya akukonzekera motani kuti ayese Umulungu?
6 Ndi nthaŵi ya Eliya tsopano. Iye amanganso guwa la nsembe la Yehova, kukumba mchera molizungulira, ndi kuikapo nsembe yake. Kenako awauza kuthira madzi pankhuni ndi pansembeyo. Athira madzi mbiya zinayi zazikulu paguwapo mpaka mchera kudzaza. Tangolingalirani kugunda kwa mitima pamene Eliya apemphera kuti: “Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isake ndi Israyeli, lero kudziŵike kuti inu ndinu Mulungu wa Israyeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mawu anu ndachita zonsezi. Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziŵe kuti inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti inu mwabwezanso mitima yawo.”—1 Mafumu 18:30-37.
7, 8. (a) Kodi Yehova akuliyankha motani pemphero la Eliya? (b) Kodi zochitika za pa Phiri la Karimeli zikukwaniritsanji?
7 Poyankha pemphero la Eliya, ‘moto wa Yehova ukugwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mumchera.’ Anthu agwetsa nkhope zawo ndi kunena: “Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.” (1 Mafumu 18:38, 39) Eliya tsopano akuchitapo kanthu motsimikiza. Alamula kuti: “Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense.” Atawapha m’chigwa cha Kisoni, mitambo yakuda iphimba kumwamba. Pomalizira pake, mvula yaikulu ithetsa chirala!—1 Mafumu 18:40-45; yerekezerani ndi Deuteronomo 13:1-5.
8 Ndi tsiku lalikulu chotani nanga! Yehova wapambana pamayeso aakulu ameneŵa a Umulungu. Ndiponso, zochitika zimenezi zibweza mitima ya Aisrayeli ambiri kwa Mulungu. Mwa njira imeneyi ndi njira zina, Eliya asonyeza kukhulupirika monga mneneri, ndipo iyeyo amachita mbali yaulosi.
Kodi “Eliya Mneneri” Adzabweranso?
9. Kodi nchiyani chinaloseredwa pa Malaki 4:5, 6?
9 Pambuyo pake, kudzera mwa Malaki, Mulungu analosera kuti: “Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate awo; kuti ndisafike ndi kukantha dziko liwonongeke konse.” (Malaki 4:5, 6) Eliya anakhalako zaka ngati 500 mawu amenewo asananenedwe. Popeza umenewu unali ulosi, Ayuda a m’zaka za zana loyamba C.E. anayembekezera kuti Eliya adze kudzaukwaniritsa.—Mateyu 17:10.
10. Kodi Eliya wonenedweratuyo anali yani, ndipo tikudziŵa motani?
10 Tsono, kodi Eliya wakudzayo anali yani? Iye anadziŵika pamene Yesu Kristu anati: “Kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu. Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.” Inde, Yohane Mbatizi ndiye anali Eliya wonenedweratuyo. (Mateyu 11:12-14; Marko 9:11-13) Mngelo anali atauza atate wa Yohane, Zekariya, kuti Yohane adzakhala ndi “mzimu ndi mphamvu ya Eliya” ndipo ‘adzakonzeratu Ambuye anthu okonzeka.’ (Luka 1:17) Ubatizo wochitidwa ndi Yohane unali chisonyezero chapoyera chakuti munthuyo walapa machimo ake ochimwira Chilamulo, chimene chinali kutsogoza Ayuda kwa Kristu. (Luka 3:3-6; Agalatiya 3:24) Choncho ntchito ya Yohane ‘inakonzeratu Yehova anthu okonzeka.’
11. Pa Pentekoste, kodi Petro ananenanji za “tsiku la Yehova,” ndipo linachitika liti?
11 Ntchito ya Yohane Mbatizi monga “Eliya” inasonyeza kuti “tsiku la Ambuye [“Yehova,” NW]” linali pafupi. Mtumwi Petro nayenso anasonyeza kuyandikira kwa tsikulo pamene Mulungu adzachitapo kanthu motsutsana ndi adani ake ndi kupulumutsa anthu ake. Iye anafotokoza kuti zochitika zozizwitsa zimene zinachitika pa Pentekoste wa 33 C.E. zinali kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yoweli wonena za kutsanulidwa kwa mzimu wa Mulungu. Petro anasonyeza kuti zimenezi zinali kudzachitika “tsiku la Yehova lalikulu ndi loonekera” lisanachitike. (Machitidwe 2:16-21, NW; Yoweli 2:28-32) Yehova anakwaniritsa Mawu ake mu 70 C.E. mwa kuchititsa magulu ankhondo achiroma kupereka chiweruzo chaumulungu pamtundu umene unakana Mwana wake.—Danieli 9:24-27; Yohane 19:15.
12. (a) Kodi Paulo ndi Petro ananenanji za “tsiku la Yehova” lomwe likudza? (b) Kodi nchifukwa ninji panali kudzaonekeradi chinachake choimiridwa ndi ntchito ya Eliya?
12 Komabe, panali kudzachitikanso zina 70 C.E. itapita. Mtumwi Paulo anagwirizanitsa “tsiku la Yehova” lomwe likudza ndi kukhalapo kwa Yesu Kristu. Ndiponso, mtumwi Petro analankhula za tsiku limenelo moligwirizanitsa ndi “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” zamtsogolomu. (2 Atesalonika 2:1, 2; 2 Petro 3:10-13) Kumbukirani kuti Yohane Mbatizi anachita ntchito yonga ya Eliya “tsiku la Yehova” lisanadze mu 70 C.E. Zonsezi pamodzi zinasonyeza bwino lomwe kuti padzachitika zinanso zoimiridwa ndi ntchito imene Eliya anachita. Kodi ndizo chiyani?
Ali ndi Mzimu wa Eliya
13, 14. (a) Kodi pali kufanana kotani pakati pa zochita za Eliya ndi za Akristu odzozedwa amakono? (b) Kodi ampatuko a m’Dziko Lachikristu achita chiyani?
13 Ntchito ya Eliya siinafanane ndi zochita za Yohane Mbatizi zokha koma yafanananso ndi zochita za Akristu odzozedwa m’nyengo ino yoŵaŵitsa imene idzadzetsa “tsiku la Yehova” likudzalo. (2 Timoteo 3:1-5) Pokhala ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, iwo ali achirikizi okhulupirika a kulambira koona. Ndipotu zimenezi zakhala zofunika chotani nanga! Atumwi a Kristu atamwalira, kunali mpatuko pa Chikristu choona, monga momwenso kulambira Baala kunafalira m’Israyeli m’tsiku la Eliya. (2 Petro 2:1) Odzitcha Akristu anayamba kusanganiza Chikristu ndi ziphunzitso ndi machitachita onyenga achipembedzo. Mwachitsanzo, anatengako chiphunzitso chachikunja ndi chosakhala cha m’Malemba chakuti munthu ali ndi sou yosafa. (Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Ampatuko a m’Dziko Lachikristu asiya kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu yekha woona, Yehova. M’malo mwake, iwo akulambira Utatu. Atengakonso kachitidwe kofanana ndi kulambira Baala ka kugwadira mafano a Yesu ndi amayi wake, Mariya. (Aroma 1:23; 1 Yohane 5:21) Koma sizinalekezere pompo.
14 Kuyambira m’zaka za zana la 19 kumka mtsogolo, atsogoleri a matchalitchi a Dziko Lachikristu anayamba kukayikira mbali zambiri za Baibulo. Mwachitsanzo, anakana mbiri ya kulenga ya Genesis nagwadira nthanthi ya chisinthiko, namati ndi “yasayansi.” Zimenezi zinatsutsana kotheratu ndi ziphunzitso za Yesu Kristu ndi atumwi ake. (Mateyu 19:4, 5; 1 Akorinto 15:47) Komabe, monga Yesu ndi otsatira ake oyambirira, Akristu odzozedwa ndi mzimu lerolino amachirikiza mbiri ya kulenga ya Baibulo.—Genesis 1:27.
15, 16. Mosiyana ndi Dziko Lachikristu, kodi ndani akhala ndi chakudya chauzimu nthaŵi zonse, ndipo motani?
15 Pamene dziko linali kuloŵa “nthaŵi ya chimariziro,” njala yauzimu inagwira Dziko Lachikristu. (Danieli 12:4; Amosi 8:11, 12) Koma gulu laling’ono la Akristu odzozedwa nthaŵi zonse linali ndi chakudya chauzimu choperekedwa ndi Mulungu “panthaŵi yake,” monga momwenso Yehova anatsimikizira kuti Eliya akudyetsedwa pamene kunali njala m’tsiku lake. (Mateyu 24:45; 1 Mafumu 17:6, 13-16) Amene nthaŵi ina ankadziŵika kuti Ophunzira Baibulo a Padziko Lonse, atumiki okhulupirika ameneŵa a Mulungu pambuyo pake analandira dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova.—Yesaya 43:10.
16 Eliya anakhala monga mwa dzina lake, limene limatanthauza “Mulungu Wanga Ndi Yehova.” Nsanja ya Olonda, monga magazini imene atumiki a padziko lapansi a Yehova amagwiritsira ntchito, yagwiritsira ntchito dzina la Mulungu mosaleka. Kwenikweni, kope lake lachiŵiri (August 1879) linafotokoza chidaliro chakuti Yehova ndiye mchirikizi wa magaziniyo. Magazini imeneyi ndi zofalitsa zina za Watch Tower Society zimavumbula ziphunzitso zosakhala za m’Malemba za Dziko Lachikristu ndi Babulo Wamkulu yense, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, kwinaku zikumachirikiza kuona kwa Mawu a Mulungu, Baibulo.—2 Timoteo 3:16, 17; Chivumbulutso 18:1-5.
Okhulupirika Poyesedwa
17, 18. Kodi aneneri a Baala ataphedwa Yezebeli anatani, koma kodi Eliya anathandizidwa motani?
17 Zomwe atsogoleri achipembedzo anachita atavumbulidwa zinafanana ndi zomwe Yezebeli anachita atamva kuti Eliya wapha aneneri a Baala. Anatumiza uthenga kwa mneneri wokhulupirika wa Yehova, nalumbira kuti adzaphedwa. Chiopsezo chimenechi sichinali nkhambakamwa chabe, popeza kuti Yezebeli anali atapha kale aneneri ambiri a Mulungu. Atachita mantha, Eliya anathaŵira kummwera chakumadzulo ku Beereseba. Atasiya mnyamata wake kumeneko, anapitiriza ulendowo, m’chipululu, napempherera kufa. Koma Yehova sanamsiye mneneri wake. Mngelo anaonekera kwa Eliya kumkonzekeretsa ulendo wautali wopita ku Phiri la Horebu. Choncho analandira chichirikizo kaamba ka ulendo wamasiku 40 wamakilomita oposa 300. Pa Horebu, Mulungu analankhula naye atasonyeza mphamvu yake yochititsa mantha m’mphepo yaikulu, chivomezi, ndi moto. Yehova sanali m’zochitikazi. Zinali zochita za mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito. Kenako Yehova analankhula kwa mneneri wake. Tangolingalirani mmene zimenezi zinalimbikitsira Eliya. (1 Mafumu 19:1-12) Bwanji ngati ife, monga Eliya, mwina tachita mantha ndi chiopsezo cha adani a kulambira koona? Chokumana nacho chake chiyenera kutithandiza kuona kuti Yehova sasiya anthu ake.—1 Samueli 12:22.
18 Mulungu ananena momveka kuti Eliya anali ndi ntchito yoti achitebe monga mneneri. Ndiponso, ngakhale Eliya anaganiza kuti ndiye yekha anali wolambira Mulungu woona m’Israyeli, Yehova anamsonyeza kuti anthu 7,000 sanagwadire Baala. Ndiyeno Mulungu anamtumizanso Eliya kuntchito yake. (1 Mafumu 19:13-18) Monga Eliya, adani a kulambira koona angatilondelonde. Tingazunzidwe koopsa, monga momwe Yesu ananeneratu. (Yohane 15:17-20) Nthaŵi zina, tingachite mantha. Komabe, tiyenera kukhala monga Eliya, amene analandira chitsimikizo cha Mulungu nalimbikira mokhulupirika mu utumiki wa Yehova.
19. Kodi Akristu odzozedwa anakumana ndi chiyani panthaŵi ya Nkhondo Yadziko I?
19 Chifukwa cha kuzunzidwa kwambiri m’Nkhondo Yadziko I, Akristu ena odzozedwa anachita mantha naleka kulalikira. Analakwitsa poganizira kuti ntchito yawo padziko lapansi yatha. Koma Mulungu sanawasiye. M’malo mwake, anawachirikiza mwachifundo, mongatu anapatsira Eliya chakudya. Monga Eliya, odzozedwa okhulupirika anamva kuwongolera kwa Mulungu nayambanso kugwira ntchito. Anawazindikiritsa mwaŵi waukulu wolalikira uthenga wa Ufumu.
20. Kodi awo amene ali okhulupirika ngati Eliya amapatsidwa mwaŵi wotani lerolino?
20 Mu ulosi wake wa kukhalapo kwake, Yesu analongosola za ntchito ya padziko lonse imene idzamalizidwa mapeto a dongosolo loipali la zinthu asanafike. (Mateyu 24:14) Lero, ntchito imeneyi ikuchitidwa ndi Akristu odzozedwa ndi mamiliyoni a atsamwali awo amene akuyembekeza kudzakhala ndi moyo padziko lapansi la paradaiso. Kuchita ntchito yolalikira za Ufumu mpaka itamalizidwa ndi mwaŵi wopatsidwa kwa okhawo okhulupirika ngati Eliya.
Khalani Wokhulupirika Monga Eliya
21, 22. (a) Kodi Akristu odzozedwa akutsogoza ntchito yotani lerolino? (b) Kodi ntchito yolalikira ikukwaniritsidwa mothandizidwa ndi chiyani, ndipo nchifukwa ninji thandizolo likufunika?
21 Mwa changu monga Eliya, otsalira ochepawo a Akristu odzozedwa moona achita ntchito yawo yosamalira zinthu za padziko lapansi za Mfumu yoikidwayo, Yesu Kristu. (Mateyu 24:47) Ndipo kwa zaka zoposa 60 tsopano, Mulungu wagwiritsira ntchito odzozedwa ameneŵa kutsogoza ntchito yopanga ophunzira amene wapatsa chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Mateyu 28:19, 20) Mamiliyoni ameneŵa ngoyamikira chotani nanga kuti otsalira odzozedwa angapowo akuchita ntchito yawo mwachangu ndi mokhulupirika!
22 Ntchito yolalikira Ufumu imeneyi yakwaniritsidwa ndi anthu opanda ungwiro ndipotu mwamphamvu imene Yehova amapatsa aja amene amamdalira mwapemphero. “Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife,” anatero wophunzira Yakobo potchula chitsanzo cha mneneriyo cha kupemphera kuti asonyeze mphamvu ya pemphero la munthu wolungama. (Yakobo 5:16-18) Sikuti nthaŵi zonse Eliya anali kulosera ndi kuchita zozizwitsa ayi. Anali ndi malingaliro ndi zofooka zaumunthu zomwezi tili nazozi, koma anatumikira Mulungu mokhulupirika. Popeza ifenso tili ndi thandizo la Mulungu ndipo amatilimbitsa, tiyenera kukhala okhulupirika monga Eliya.
23. Kodi nchifukwa ninji tili ndi chifukwa chabwino chokhalira okhulupirika ndi oyembekezera zabwino zonse mtsogolo?
23 Tili ndi chifukwa chabwino chokhalira okhulupirika ndi oyembekeza zabwino zonse mtsogolo. Kumbukirani kuti Yohane Mbatizi anachita ntchito yonga ya Eliya lisanakanthe “tsiku la Yehova” mu 70 C.E. Akristu odzozedwa achita ntchito yopatsidwa ndi Mulungu yofananayo padziko lonse lapansi ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Zimenezi zikutsimikizadi kuti “tsiku [lalikulu] la Yehova” lili pafupi.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Umulungu wa Yehova unatsimikizidwa motani pa Phiri la Karimeli?
◻ Kodi ‘Eliya wakudzayo’ anali yani, ndipo anachitanji?
◻ Kodi Akristu odzozedwa amakono asonyeza motani kuti ali ndi mzimu wa Eliya?
◻ Kodi nchifukwa ninji nkotheka kuti ifenso tikhale okhulupirika monga Eliya?
[Bokosi patsamba 15]
Kodi Kumwamba Kwake Nkuti Kumene Eliya Anakwera?
“KUNACHITIKA, [Eliya ndi Elisa] akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa aŵiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kavumvulu.”—2 Mafumu 2:11.
Kodi panopa liwu lakuti “kumwamba” likutanthauzanji? Liwuli nthaŵi zina limatanthauza malo auzimu kumene Mulungu ndi ana ake aungelo amakhala. (Mateyu 6:9; 18:10) “Kumwamba” kungakhalenso thambo lenilenili. (Deuteronomo 4:19) Ndipo Baibulo limagwiritsira ntchito liwuli kunena za mlengalenga wa pamwamba pa dzikowu, mmene mbalame zimauluka ndi mmene mphepo imaomba.—Salmo 78:26; Mateyu 6:26.
Tsono kumwamba kwake nkuti kumene mneneri Eliya anakwera? Mwachionekere, anasamutsidwa kudzera mumlengalenga wa dziko ndi kuikidwa kumbali ina ya dziko. Zaka zambiri pambuyo pake, Eliya anakhalabe padziko, chifukwa chakuti analembera kalata Mfumu Yehoramu ya Yuda. (2 Mbiri 21:1, 12-15) Zoti Eliya sanakwere kumalo auzimu kumene Yehova Mulungu amakhala zinatsimikiziridwa ndi Yesu Kristu, amene anati: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m’Mwambayo,” ndiye, Yesu yemweyo. (Yohane 3:13) Njira yomkera ku moyo wakumwamba inatsegukira anthu opanda ungwiro nthaŵi yoyamba pambuyo pa imfa, kuukitsidwa, ndi kukwera kumwamba kwa Yesu Kristu.—Yohane 14:2, 3; Ahebri 9:24; 10:19, 20.