Nyimbo 125
Tizigonjera Mokhulupirika Dongosolo la Mulungu Loyendetsera Zinthu
Losindikizidwa
1. Tikamalengeza padziko lonse
Ufumu wa M’lungu ndi ntchito zake
N’kofunika kuti tizitsatira
Dongosolo lomwe linaikidwa.
(KOLASI)
Tigonjeretu Mulungu wathu
Mokhulupirika.
Tate Yehova amatikonda,
Iye atiteteza.
2. M’lungu watipatsa mzimu woyera
Ndi kapolo azititsogolera.
Choncho tiyenitu tiziyesetsa
Mfundo zake za nzeru kulengeza.
(KOLASI)
Tigonjeretu Mulungu wathu
Mokhulupirika.
Tate Yehova amatikonda,
Iye atiteteza.
(Onaninso Luka 12:42; Aheb. 13:7, 17.)