Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Onse?
KODI MUNGAYANKHE KUTI . . .
Amayankha mapemphero onse
Amayankha mapemphero ena
Sayankha
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Yehova ali pafupi ndi onse . . . amene amamuitana m’choonadi.”—Salimo 145:18.
MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO
Mulungu samvetsera mapemphero a anthu amene samumvera. (Yesaya 1:15) Komabe anthu oterewa akhoza kusintha zochita zawo n’kukhala “pa ubwenzi wabwino” ndi Mulungu.—Yesaya 1:18.
Kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kupemphera mogwirizana ndi mfundo zimene amatiuza m’Baibulo.—1 Yohane 5:14.
Kodi tiyenera kukhala mwanjira inayake popemphera?
ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti ayenera kupemphera atagwada, atazyolika kapena ataika manja awo pamodzi. Nanga inuyo mukuganiza bwanji?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Mulungu anamvetserapo mapemphero a anthu omwe ankapemphera ‘atakhala pansi,’ ‘ataimirira’, ‘atagona’ kapenanso ‘atagwada.’ (1 Mbiri 17:16; 2 Mbiri 30:27; Ezara 10:1; Machitidwe 9:40) Choncho Mulungu safuna kuti anthu azichita kukhala mwanjira inayake akamapemphera.
MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO
Mulungu amamvetsera mapemphero a anthu odzichepetsa.—Salimo 138:6.
Mukhoza kupemphera kwa Mulungu chamumtima komanso m’chinenero chilichonse.—2 Mbiri 6:32, 33; Nehemiya 2:1-6.