Nyimbo 152
Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani
O, Yehova mwatiphunzitsa
za moyo wosatha.
Zimatikhudzadi mtima
n’kuphunzitsa ena.
Nthawi zina timada nkhawa
chifukwa cha mavuto.
Chiyembekezo chathunso
chimatha kuchepa.
(KOLASI)
Inu Mulungu ndinu
mphamvu yathu,
inde mumatithandiza.
Mwalimbitsa
chiyembekezo chathu,
timadaliratu inu.
Yehova muzitikumbutsa
tisamaiwale,
zoti mumatithandiza
kutumikirabe.
Tikakumbukira mfundoyi
sitimaopa kanthu.
Koma timalimba mtima
pophunzitsa anthu.
(KOLASI)
Inu Mulungu ndinu
mphamvu yathu,
inde mumatithandiza.
Mwalimbitsa
chiyembekezo chathu,
timadaliratu inu.
(Onaninso Sal. 72:13, 14; Miy. 3:5, 6, 26; Yer. 17:7.)