NYIMBO 140
Tidzakhala Ndi Moyo Wosatha
Losindikizidwa
1. Onani m’maganizo,
Mtendere uli konse,
Chisoni nacho chatha,
Kulira kwathanso.
(KOLASI)
Tiimbire M’lungu
Mosangalaladi.
Patsikulo tidzati,
‘Zakale zapita.’
2. Sitidzakalambanso,
Tidzakhala ndi mphamvu.
Mavutowa adzatha,
Sitidzaliranso.
(KOLASI)
Tiimbire M’lungu
Mosangalaladi.
Patsikulo tidzati,
‘Zakale zapita.’
3. Tizidzasangalala
Poimbira Mulungu.
Tidzamulemekeza
Mpaka kale kale.
(KOLASI)
Tiimbire M’lungu
Mosangalaladi.
Patsikulo tidzati,
‘Zakale zapita.’
(Onaninso Yobu 33:25; Sal. 72:7; Chiv. 21:4.)