-
Kodi Kugonana Tili Pachibwenzi Kungachititse Kuti Tizikondana Kwambiri?Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
-
-
Mutu 24
Kodi Kugonana Tili Pachibwenzi Kungachititse Kuti Tizikondana Kwambiri?
Pangodutsa miyezi iwiri kuchokera pamene Heather anadziwana ndi Mike koma zimangokhala ngati anadziwana kalekale. Amatumizirana mameseji pafupipafupi, amacheza pa foni kwa nthawi yaitali moti eniakewo amangoona kuti zonse zili bwino. Koma tsiku lina usiku akucheza m’galimoto yomwe inangoima, Mike anayamba kusonyeza kuti akufuna kucheza kwawo kutafika pena.
Pa miyezi iwiri imene yapitayi, Mike ndi Heather samachita zambiri, amangogwirana manja kapena kukisana pang’ono. Heather sakufuna kuchita zimene Mike akufunazo koma akuopa kuti akakana chibwenzi chawo chitha. Iye amamukonda kwambiri Mike chifukwa zimene amamuchitira zimamupangitsa kudziona kuti ndi wokongola komanso wofunika. Mumtima mwake amadziuza kuti, ‘Ine ndi Mike timakondana kwambiri ndiye . . .’
MWINA mwadziwiratu kumene nkhaniyi ikulowera. Koma mwina simungadziwe kuti ngati Mike ndi Heather atagonana chibwenzi chawo komanso moyo wawo zikhoza kusokonekera. Taganizirani izi:
Munthu akapanda kutsatira lamulo linalake amakumana ndi mavuto. N’zimenenso zingachitike ngati mutapanda kutsatira lamulo lakuti: ‘Muzipewa dama.’ (1 Atesalonika 4:3) Koma kodi munthu amene sangatsatire lamulo limeneli angakumane ndi mavuto otani? Baibulo limanena kuti: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.” (1 Akorinto 6:18) Kodi zimenezi ndi zoona? Yesani kulemba mavuto atatu amene wachinyamata angakumane nawo ngati atagonana ndi munthu wina asanalowe m’banja.
1 ․․․․․
2 ․․․․․
3 ․․․․․
Mukayang’ana zimene mwalemba pamwambapa, kodi mwatchula zinthu ngati kutenga matenda opatsirana pogonana, kutenga mimba yosakonzekera kapena kukhumudwitsa Mulungu? Zinthu zimenezi ndi zimene zingachitikiredi munthu aliyense amene sanatsatire lamulo la Mulungu loletsa dama.
Komabe mukhoza kupusitsika n’kumaganiza kuti, ‘Palibe chimene chingandichitikire.’ Ndipo m’mesa aliyense akuchita zomwezi? Mwina anzanu akusukulu amakusirizani kuti anagonana ndi winawake ndipo zimaoneka kuti palibe chilichonse chimene chawachitikira. Ndipotu mwina nanunso muli ndi maganizo ofanana ndi a Heather oti kugonana ndi chibwenzi chanu kungachititse kuti muzikondana kwambiri. Ndipo ndani angafune kuti azisekedwa ndi anzake kuti sanagonanepo ndi munthu wina? Mwina mungamaone kuti ndi bwino kungochita zimene aliyense akuchita.
Koma ayi. Choyamba, dziwani kuti si kuti aliyense akuchitadi zimenezo. N’kutheka kuti munawerengapo nkhani zosonyeza kuti achinyamata ambiri amagonana. Mwachitsanzo, kafukufuku wina anasonyeza kuti achinyamata awiri pa atatu alionse a ku United States amayamba zogonana asanamalize sukulu. Koma kafukufuku ameneyu akutsimikiziranso kuti pa achinyamata atatu aliwonse, wachinyamata mmodzi amakhala kuti sanayambe zogonana. Koma kodi amene amachitadi zimenezi zimawathera bwanji? Kafukufuku amasonyeza kuti achinyamata ambiri amene amachita zimenezi amakumana ndi mavuto amene ali m’munsiwa.
VUTO LOYAMBA KUVUTIKA MAGANIZO. Achinyamata ambiri amene anagonanapo asanalowe m’banja amadandaula moti amanena kuti amalakalaka akanapanda kuchita zimenezo.
VUTO LACHIWIRI KUSAKHULUPIRIRANA. Achinyamata amene ali pa chibwenzi akagonana, aliyense amayamba kudzifunsa kuti, ‘Ndiye kuti wachita zimenezi ndi anthu angati?’
VUTO LACHITATU KUKHUMUDWA. Ngakhale atsikana amene amavomera kugonana ndi anyamata, mumtima mwawo amafuna mwamuna amene angawateteze osati kungowapezerera. Ndipo anyamata ambiri amaonanso kuti mtsikana amene walolera kuti agone nawo sawasangalatsanso ngati poyamba.
Kuwonjezera pa zimenezi, anyamata ambiri amanena kuti sangakwatire mtsikana amene anagonanapo naye. Koma n’chifukwa chiyani amanena zimenezi? Chifukwa chakuti amafuna kukwatira mkazi wakhalidwe labwino.
Ngati ndinu mtsikana, kodi zimenezi zikukudabwitsani kapena kukukhumudwitsani? Ngati ndi choncho, dziwani kuti zimene zimachitika munthu akagonana ndi chibwenzi chake asanalowe m’banja n’zosiyana ndi zimene amasonyeza m’mafilimu kapena pa TV. Anthu opanga mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV amafuna kuti achinyamata aziona ngati kugonana asanalowe m’banja kulibe vuto lililonse, ndi kosangalatsa komanso kumasonyeza kuti mumakondana zenizeni. Koma musapusitsike. Anthu amene amakunyengererani kuti muzichita zimenezi amangofuna kupezerapo phindu. (1 Akorinto 13:4, 5) Komanso kodi munthu amene amakukondanidi angachite zinthu zimene zingakuvulazeni? (Miyambo 5:3, 4) Ndipo kodi munthu amene amakukondani angakunyengerereni kuti musokoneze ubwenzi wanu ndi Mulungu?—Aheberi 13:4.
Ngati ndinu mnyamata ndipo muli ndi chibwenzi, zimene takambirana m’mutuwu zikuthandizeni kuganizira mmene mukuchitira pa chibwenzi chanucho. Dzifunseni kuti, ‘Kodi mtsikanayu ndimamukondadi?’ Ngati mumamukonda, mungasonyeze zimenezi poyesetsa kutsatira malamulo a Mulungu, kuchita zinthu mwanzeru mwa kupewa kukhala pamalo amene mukhoza kuyesedwa n’kuchita zoipa komanso muyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti mumamuganizira. Mukamayesetsa kuchita zimenezi, mtsikanayo azidzakuonani ngati mmene Msulami ankaonera chibwenzi chake. Iye anati: “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.” (Nyimbo ya Solomo 2:16) Mwachidule tingati azidzakukondani kwambiri komanso kukudalirani.
Kaya ndinu mnyamata kapena mtsikana, ngati mutalolera kugonana ndi chibwenzi chanu mungadzichotsere ulemu. (Aroma 1:24) N’chifukwa chake anthu ambiri amakhumudwa komanso kudziona ngati achabechabe akachita zimenezi. Iwo amadziimba mlandu poona kuti alolera kuti munthu wina agwiritse ntchito thupi lawo mwa njira imeneyi ndipo amamva ngati kuti aberedwa chinthu chinachake chamtengo wapatali. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni. Ngati munthu wina atakunyengererani kuti mugone naye pokuuzani kuti, “Ngati umandikondadi, ulola,” muyankheni molimba mtima kuti, “Ukanakhala kuti iweyo umandikondadi sukanandiuza kuti tichite zimenezi.”
Thupi lanu ndi lamtengo wapatali kwambiri ndipo musalitchipitse. Muzisonyeza kuti muli ndi chikhulupiriro cholimba moti mumayesetsa kutsatira lamulo la Mulungu loti tizipewa dama. Ndipo ngati mudzakwatire muzidzasangalala kugonana ndi mkazi kapena mwamuna wanuyo. Ndipo simudzakhumudwa kapena kukhala ndi nkhawa imene anthu ambiri amakhala nayo akagonana ndi munthu asanalowe m’banja.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:3.
KUTI MUMVE ZAMBIRI PA NKHANIYI WERENGANI MUTU 4 NDI 5, M’BUKU LACHIWIRI
Kodi kuseweretsa maliseche n’koopsa bwanji?
LEMBA
“Thawani dama. . . . amene amachita dama amachimwira thupi lake.”—1 Akorinto 6:18.
MFUNDO YOTHANDIZA
Mukamachita zinthu ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanu, mungachite bwino kumatsatira mfundo iyi: Ngati zimene mukufuna kuchitazo simungazichite pamaso pa makolo anu, ndi bwino osazichita n’komwe.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Nthawi zambiri mnyamata akagonana ndi mtsikana amene ali naye pa chibwenzi amathetsa chibwenzicho n’kuyamba chibwenzi ndi mtsikana wina.
ZOTI NDICHITE
Ndikamacheza ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanga ndiyenera kupewa zinthu izi: ․․․․․
Ngati munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanga atandiuza kuti tikakumane kwa awiri, ndingamuuze kuti: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● Ngakhale kuti mwachibadwa timalakalaka kugonana ndi munthu tisanalowe m’banja, n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuchita zimenezi?
● Kodi inuyo mungatani ngati munthu winawake atakuuzani kuti mukagonane?
[Mawu Otsindika patsamba 176]
“Monga Akhristu muli ndi makhalidwe amene angachititse anthu ena kukopeka nanu. Choncho muyenera kukhala osamala ndipo muzipewa anthu amene angakunyengerereni kuti muchite zinthu zolakwika. Muziona kuti makhalidwe amene muli nawowo ndi amtengo wapatali ndipo muziwatetezera.”—Anatero Joshua
[Chithunzi patsamba 176, 177]
Kugonana ndi munthu musanalowe m’banja kuli ngati kutenga chithunzi chokongola n’kuchiika pakhomo kuti muzipukutira kuphazi polowa m’nyumba
-
-
Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Chizolowezi Choseweretsa Maliseche?Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
-
-
Mutu 25
Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Chizolowezi Choseweretsa Maliseche?
“Ndinayamba zoseweretsa maliseche ndili ndi zaka 8. Patapita nthawi ndinadziwa kuti Mulungu amadana ndi khalidwe limeneli. Ndinkadziimba mlandu nthawi iliyonse ndikachita zimenezi moti ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu angakonde munthu wochita khalidwe limeneli?’”—Anatero Luiz.
WACHINYAMATA akamakula, amafika msinkhu winawake pamene amakhala ndi chilakolako cha mphamvu chofuna kugonana. Zimenezi zimachititsa kuti achinyamata ena ayambe kuseweretsa maliseche.a Ambiri anganene kuti kuchita zimenezi kulibe vuto lililonse chifukwa palibe amene ukumulakwira. Komabe, pali zifukwa zomveka zomwe ziyenera kutichititsa kupewa khalidwe limeneli. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chititsani ziwalo za thupi lanu . . . kukhala zakufa ku . . . chilakolako cha kugonana.” (Akolose 3:5) Kuseweretsa maliseche sikumathetsa chilakolako chofuna kugonana koma kumangochiwonjezera. Komanso ganizirani mfundo zotsatirazi:
● Kuseweretsa maliseche kumalimbikitsa maganizo odzikonda. Mwachitsanzo, munthu akamaseweretsa maliseche amakhala kuti akungoganizira zokhutiritsa zimene thupi lake likufuna.
● Akakhala mwamuna, kuseweretsa maliseche kumam’pangitsa kuona akazi ngati ofunika pogonana pokha. Akazinso amene ali ndi khalidwe limeneli amawaona choncho amuna.
● Kudzikonda kumene munthu amayamba chifukwa choseweretsa maliseche kumam’pangitsa kuti asamadzakhutitsidwe pogonana ndi mwamuna kapena mkazi wake.
M’malo moseweretsa maliseche pofuna kuthetsa chilakolako champhamvu chimene mungakhale nacho, yesetsani kukhala wodziletsa. (1 Atesalonika 4:4, 5) Pofuna kukuthandizani kuchita zimenezi, Baibulo limakulimbikitsani kupewa kuchita zinthu kapena kukhala pamalo amene angakuchititseni kuti mukhale ndi chilakolako chofuna kugonana. (Miyambo 5:8, 9) Koma kodi mungatani ngati munazolowera khalidwe limeneli moti zikukuvutani kusiya? Ngati munayesa kuti musiye khalidwe limeneli n’kulephera, n’zotheka kuyamba kuganiza kuti simungasinthe n’kuyamba kutsatira mfundo zimene Mulungu amafuna. Mnyamata wina, dzina lake Pedro, ankadzionanso choncho. Iye anati: “Ndikayambiranso khalidweli, ndinkavutika kwambiri mumtima mwanga. Ndinkaona kuti Mulungu sangandikhululukirenso moti ndinkakanika kupemphera.”
Ngati nanunso mumamva choncho musataye mtima, n’zotheka kusintha. Achinyamata ambiri, ngakhalenso achikulire, anakwanitsa kusiya chizolowezi choseweretsa maliseche. Nanunso mukhoza kusiya.
Zimene Mungachite Ngati Mumangodziimba Mlandu
Zimene zafotokozedwa m’mbuyomu zikusonyeza kuti nthawi zambiri anthu amene ali ndi chizolowezi choseweretsa maliseche amadziimba mlandu. Kukhala ndi “chisoni chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu” kungakuthandizeni kuti muyesetse kusiya khalidwe limeneli. (2 Akorinto 7:11) Komabe si bwino kumangokhalira kudziimba mlandu chifukwa zingakuchititseni kugwa ulesi n’kusiya kulimbana ndi vutolo.—Miyambo 24:10.
Choncho, yesetsani kumaiona nkhaniyi moyenera. Kuseweretsa maliseche kuli m’gulu la zinthu zonyansa zimene Mulungu amadana nazo. Kukhoza kukuchititsani kukhala “akapolo a zilakolako ndi zosangalatsa zosiyanasiyana,” ndiponso kungakuchititseni kukhala ndi maganizo olakwika. (Tito 3:3) Ngakhale zili choncho, kuseweretsa maliseche sikuli m’gulu la dama loipitsitsa. (Yuda 7) Choncho, ngati muli ndi chizolowezi choseweretsa maliseche musafulumire kuganiza kuti mwachita tchimo limene simungakhululukidwe. Chofunika ndi kuyesetsa kulamulira mtima wanu komanso kupitirizabe kulimbana ndi vutolo.
N’zosavuta kukhumudwa ngati mutayambiranso khalidweli. Zimenezi zikachitika, kumbukirani mawu a pa Miyambo 24:16 omwe amati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso. Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa.” Kulephera kutsatira mfundo inayake kamodzi kokha sikungakupangitseni kukhala m’gulu la anthu oipa. Choncho musafooke. Ganizirani chimene chachititsa kuti muyambirenso khalidwelo ndipo muyesetse kuchipewa kuti musadzachitenso.
Muzipeza nthawi yoganizira mofatsa za chikondi cha Mulungu ndiponso za chifundo chake. Davide, yemwe analemba buku la masalimo, ankalakwitsa zinthu kawirikawiri koma ananena kuti: “Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake, Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa. Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:13, 14) Yehova amaganizira zoti anthufe ndi ochimwa n’kale ndipo ndi ‘wokonzeka kutikhululukira.’ (Salimo 86:5) Komabe amafuna kuti patokha tiziyesetsa kukonza vutolo. Ndiye kodi mungachite chiyani kuti musiye chizolowezi choseweretsa maliseche?
Ganizirani zinthu zosangalatsa zimene mumakonda. Kodi mumaonera mafilimu, mapulogalamu a pa TV kapena kutsegula zinthu za pa intaneti zomwe zimakuchititsani kuti mukhale ndi chilakolako chogonana? Wamasalimo anapemphera kwa Mulungu kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”b—Salimo 119:37.
Muzidzikakamiza kuganiza zinthu zabwino. Mkhristu wina, dzina lake William, ananena kuti: “Musanagone muziwerenga kaye zinthu zauzimu. Ndi bwino kuti muzigona m’maganizo mwanu muli mfundo za m’Malemba.”—Afilipi 4:8.
Kambiranani ndi munthu wina za vuto lanulo. Manyazi akhoza kukuchititsani kuti muziopa kumuuza munthu wina za vutoli. Komabe kufotokozera munthu wina kungakuthandizeni kusiya chizolowezi chimenechi. Izi ndi zimene Mkhristu wina, dzina lake David anachita. Iye anati: “Ndinafotokozera bambo anga tili awiri ndipo sindidzaiwala zimene ananena. Anandiuza mawu olimbikitsa akuti: ‘Zimene umachita zimandipangitsa kuti ndizikukonda kwambiri.’ Ndipo ananena mawu amenewa kwinaku akumwetulira. Ankadziwa kuti zinali zovuta kuti ndilimbe mtima kuwafotokozera zimenezi. Zimene anandiuzazi zinandilimbikitsa kwambiri kuti ndiziyesetsa kulimbana ndi vutoli.
“Kenako anandisonyeza malemba angapo amene anandithandiza kudziwa kuti ndikhoza kusintha, komanso ena ondithandiza kudziwa kuipa kwa zomwe ndimachitazo. Atachita zimenezi, anandiuza kuti tidzakambirananso nkhaniyo nthawi ina. Anandiuza kuti ndisadzakhumudwe kwambiri ngati nthawi ina nditakanika kupirira n’kuchitanso khalidweli. Ndidzangoyesetsa kuti papite nthawi yaitali zimenezi zisanachitikenso.” Kodi zimenezi zinamuthandiza bwanji David? Iye anati: “Kuzindikira kuti pali munthu wina amene akudziwa za vuto langa ndipo akundithandiza kunandilimbikitsa kwambiri.”c
Anthu ena amagonana n’cholinga choti angothandizana basi. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake kuchita zimenezi kuli kulakwa.
[Mawu a M’munsi]
a Tikamanena za kuseweretsa maliseche sitikutanthauza kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana kumene kumatha kuchitika mwachibadwa komanso mosayembekezereka. Mwachitsanzo, nthawi zina mnyamata akhoza kudzuka m’mawa zitamusokonekera polota. Atsikana enanso chilakolako chikhoza kuwapeza mosayembekezereka, makamaka akatsala pang’ono kuyamba kusamba kapena akangomaliza kumene. Tikamanena za kuseweretsa maliseche tikutanthauza kuchita zinthu mwadala zomwe zingakupangitse kumva ngati ukugonana ndi munthu.
b Kuti mumve zambiri, werengani Mutu 33, m’Buku Lachiwiri.
c Kuti mudziwe zambiri, werengani Buku Lachiwiri tsamba 239-241.
LEMBA
“Thawa zilakolako zaunyamata, koma tsatira chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, ndi mtendere limodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyera.”—2 Timoteyo 2:22.
MFUNDO YOTHANDIZA
Muzipemphera chilakolako chisanafike poipa. Muzipempha Yehova Mulungu kuti akupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa” imene ingakuthandizeni kupirira mayesero.—2 Akorinto 4:7.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Munthu amene amalephera kupirira akakhala ndi chilakolako si mwamuna kapena mkazi weniweni. Mwamuna kapena mkazi weniweni amatha kudziletsa, ngakhale akakhala kwa yekha.
ZOTI NDICHITE
Kuti ndisamaganizire zinthu zoipa ndizichita izi: ․․․․․
Kuti ndisagonje pamene chilakolako chikundivutitsa ndizichita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani muyenera kukumbukira kuti Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka”?—Salimo 86:5.
● Ngati Mulungu, yemwe analenga anthu ndi zilakolako zogonana, amanena kuti tiziyesetsa kudziletsa, ndiye kuti amatikhulupirira kuti tikhoza kuchita chiyani?
[Mawu Otsindika patsamba 182]
“Kuchokera pamene ndinathana ndi vutoli ndimadzimva kuti ndili ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Yehova ndipo sindingalole kuti chilichonse chisokoneze zimenezi.”—Anatero Sarah
[Chithunzi patsamba 180]
Munthu ukagwa pothamanga sizitanthauza kuti ukufunika kubwerera n’kukayambiranso. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene waseweretsanso maliseche pambuyo poti anasiya khalidwe limeneli. Sizitanthauza kuti zonse zimene wakhala akuyesetsa kuchita m’mbuyomu n’zopanda phindu
-
-
Kodi Kugonana Pongofuna Kuthandizana Kuli Ndi Vuto?Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
-
-
Mutu 26
Kodi Kugonana Pongofuna Kuthandizana Kuli Ndi Vuto?
“Achinyamata amagwirizana zoti azigonana ngakhale asali pa chibwenzi pongofuna kuona kuti angagonane ndi anthu angati.”—Anatero Penny.
“Anyamata amakambirana momasuka nkhani imeneyi pagulu. Amadzichemerera kuti amagonana ndi atsikana ambirimbiri ngakhale kuti ali ndi chibwenzi.”—Anatero Edward.
ACHINYAMATA ambiri masiku ano amawawalira anzawo kuti amagonana ngakhale kuti sali pa chibwenzi. Ndipo ena ali ndi azinzawo amene amagonana nawo nthawi ndi nthawi ngakhale kuti sali pa chibwenzi.
Choncho musamadabwe ngati mutayamba kulakalaka kuchita zimenezi kapena ngati winawake atakunyengererani kuti mugone naye ngakhale kuti simuli naye pa chibwenzi. (Yeremiya 17:9) Edward, yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Atsikana ambiri ankandinyengerera kuti ndikagone nawo ndipo kukana zimenezi kunali kovuta kwambiri kuposa zina zonse. Kunena kuti sukufuna si chinthu chophweka.” Koma kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni ngati munthu wina atakunyengererani kuti mugone naye?
Dziwani Chifukwa Chake Kuchita Zimenezi Kuli Kulakwa
Dama ndi tchimo lalikulu moti anthu amene amachita dama “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Ndipotu mfundo imeneyi imagwira ntchito pa aliyense wochita dama, kaya ali pa chibwenzi kapena akungofuna kuthandizana. Choncho, kuti mupewe kugonana ndi munthu, kaya amene muli naye pa chibwenzi kapena wina aliyense, muyenera kuona dama ngati mmene Yehova amalionera.
“Ndimakhulupirira zoti kuti zinthu zikuyendere bwino pa moyo wako uyenera kumachita zinthu motsatira zimene Yehova amafuna.”—Anatero Karen, wa ku Canada.
“Nthawi zonse muzikumbukira kuti ndinu mwana wa enaake, muli ndi anzanu a ku mpingo komanso anzanu ena ambirimbiri omwe amakukondani. Anthu amenewa akhoza kukhumudwa kwambiri ngati mutakopeka n’kugonana ndi munthu amene akukunyengereraniyo.”—Anatero Peter, wa ku Britain.
Mukamaona dama ngati mmene Yehova amalionera, mudzatha ‘kudana nacho choipa’ ngakhale thupi lanu litakhala kuti likulakalaka kuchita zoipazo.—Salimo 97:10.
Mavesi amene mungawerenge: Genesis 39:7-9. Onani mmene Yosefe anasonyezera kulimba mtima pokana atanyengereredwa kuti agonane ndi mkazi wa mbuye wake. Onaninso zimene zinamuthandiza kuchita zimenezi.
Muzinyadira Zimene Mumakhulupirira
Nthawi zambiri zimakhala zophweka kwa achinyamata kuchita zinazake molimba mtima komanso monyadira akakhala kuti zinthuzo amazikhulupirira. Muli ndi mwayi wapadera wochita zinthu zosonyeza kuti mumatsatira mfundo za Mulungu. Choncho musamachite manyazi kufotokozera anzanu mmene mumaonera nkhani yogonana musanalowe m’banja.
“Muziwauziratu anzanu pasadakhale kuti muli ndi mfundo zimene mumatsatira pa nkhani zosiyanasiyana.”—Anatero Allen, wa ku Germany.
“Anyamata amene ndinaphunzira nawo ankandidziwa bwino moti ankadziwiratu kuti kulimbana ndi kundinyengerera kunali kungotaya nthawi.”—Anatero Vicky, wa ku United States.
Kuyesetsa kutsatira zimene mumakhulupirira ndi umboni wakuti mukukula mwauzimu.—1 Akorinto 14:20.
Mavesi amene mungawerenge: Miyambo 27:11. Onani mmene kuchita zinthu zoyenera kungasangalatsire Yehova.
Muzichita Zinthu Motsimikiza
Kunena kuti simukufuna n’kofunika kwambiri koma anthu ena akhoza kuona ngati mukuyankha zimenezi pongofuna kuti winayo aoneke ngati wachita kuvutikira kuti mulole.
“Chilichonse chimene mumachita, kaya ndi mmene mumavalira, mmene mumalankhulira, anthu amene mumalankhula nawo, mmene mumachitira zinthu ndi anthu ena, ziyenera kusonyeza kuti simukufuna kuchita dama.”—Anatero Joy, wa ku Nigeria.
“Muzichita zinthu zosonyezeratu kuti olo atachita zotani simungalole. Musamalandire mphatso kuchokera kwa anyamata amene akungofuna kupeza njira yokunyengererani. Akhoza kukukakamizani kuti mugone nawo apo ayi mubweze zimene anakupatsanizo.”—Anatero Lara, wa ku Britain.
Mukamachita zinthu motsimikiza, Yehova adzakuthandizani. Poganizira zimene zinamuchitikira pa moyo wake, Davide ananena kuti: “Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.”—Salimo 18:25.
Mavesi amene mungawerenge: 2 Mbiri 16:9. Onani kuti Yehova ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu amene akufuna kumachita zinthu zolondola pa moyo wawo.
Muziona Patali
Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mukutsatira mfundo ya pa lembali? Muzichita zinthu zosonyeza kuti mukuona patali.
“Yesetsani kupewa anthu amene amakonda kukamba nkhani zimenezi.”—Anatero Naomi, wa ku Japan.
“Musamangouza anthu mwachisawawa zinthu ngati kumene mumakhala kapena nambala yanu ya foni.”—Anatero Diana, wa ku Britain.
Ganizirani mofatsa za zinthu zimene mumalankhula, khalidwe lanu, anzanu komanso malo amene mumakonda kupita. Kenako dzifunseni kuti, ‘Kodi zimene ndimachitazi sizingapangitse anthu kukhala ndi maganizo oti andinyengerere kuti ndigone nawo?’
Mavesi amene mungawerenge: Genesis 34:1, 2. Onani mmene kupezeka pamalo olakwika kunachititsira mtsikana wina dzina lake Dina kuti akumane ndi mavuto.
Kumbukirani kuti Yehova Mulungu samaona nkhani imeneyi ngati yaing’ono, choncho nanunso musamaone kugonana ngati masewera chabe. Mukamayesetsa kuchita zinthu zoyenera mungakhale ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndiponso mungadzisungire ulemu. Mtsikana wina, dzina lake Carly, ananena kuti: “Musalole kuti wina angokugwiritsani ntchito pa zimene thupi lake likufuna. Muzikumbukira kuti panapita nthawi kuti mukwanitse kukhala ndi makhalidwe oyera pamaso pa Yehova. Choncho, yesetsani kuteteza makhalidwe amenewa.”
Kodi anyamata amanena kuti amafuna atsikana otani? Mukawerenga nkhaniyi mudabwa kudziwa zimene mnyamata amafuna mwa mtsikana.
LEMBA
“Chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.”—2 Petulo 3:14.
MFUNDO YOTHANDIZA
Yesetsani kuti mukhale ndi makhalidwe abwino. (1 Petulo 3:3, 4) Mukakhala ndi makhalidwe abwino, zidzakuthandizani kuti munthu winanso wamakhalidwe abwino akopeke nanu.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Yehova amafuna kuti mudzasangalale pogonana ndi mwamuna kapena mkazi wanu mogwirizana ndi mmene iyeyo ankafunira. Kugonana muli m’banja kudzathandiza kuti muzidzasangalala ndiponso kuti musadzavutike ndi nkhawa komanso kunong’oneza bondo, zomwe anthu amene amachita dama amavutika nazo.
ZOTI NDICHITE
Nthawi zonse ndizichita zotsatirazi kuti ndikhale woyera pamaso pa Mulungu ngati mmene analili Yosefe: ․․․․․
Kuti ndisakumane ndi zimene Dina anakumana nazo ndizichita zotsatirazi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● Ngakhale kuti mtima ungafune kuti mugonane ndi munthu pongofuna kuthandizana, n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi sikoyenera?
● Kodi mungatani ngati munthu atakuuzani kuti mukagonane?
[Mawu Otsindika patsamba 185]
“Muziyankha ndi mphamvu. Mnyamata wina ataoneka kuti wayamba kuganiza zopusa ndinamuuza kuti, ‘Iwe, chotsa msanga dzanja lakolo paphewa langa!’ Kenako ndinangochokapo nditakwiya.”—Anatero Ellen
[Chithunzi patsamba 187]
Ngati mungagonane ndi munthu wina mongothandizana ndiye kuti mukudzitchipitsa
-