Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Ena a Mboni za Yehova apatsidwa mwayi wolembedwa ntchito yokhudzana ndi nyumba kapena zinthu zachipembedzo. Kodi Malemba amati bwanji ponena za ntchito ngati zimenezo?
Akristu ofunitsitsa kutsatira lemba la 1 Timoteo 5:8, limene limagogomezera kufunika kwa kuchirikiza apabanja lako mwakuthupi angayang’anizane ndi nkhani imeneyi. Pamene Akristu ayeneradi kutsatira uphungu umenewo, zimenezo sizikuwapatsa chilolezo cholandira ntchito yolembedwa iliyonse ndipo ya mtundu uliwonse, kaya ikhale yotani. Akristu amadziŵa kufunika kwa kutsatira bwino zitsogozo zina za chifuniro cha Mulungu. Mwachitsanzo, kufunitsitsa kwa mwamuna kuti achirikize banja lake sikungam’patse chilolezo choswa malamulo a Baibulo okhudza khalidwe loipa kapena kupha. (Yerekezani ndi Genesis 39:4-9; Yesaya 2:4; Yohane 17:14, 16.) N’kofunikanso kuti Akristu atsatire lamulo la kutuluka m’Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonama.—Chivumbulutso 18:4, 5.
Padziko lonse lapansi, atumiki a Mulungu amakumana ndi mikhalidwe yosiyanasiyana yokhudza ntchito. Kungakhale kopanda phindu ndipo si ulamuliro wathu kuyesa kundandalika mikhalidwe yonse ndi kupanga malamulo oyenera kuwatsatira. (2 Akorinto 1:24) Komano, tiyeni tingotchulapo mfundo zina zimene Akristu ayenera kuganizira posankha ntchito. Mfundo zimenezi zinalongosoledwa mwachidule mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 15, 1982, m’nkhani yonena za kupindula ndi chikumbumtima chathu chopatsidwa ndi Mulungu. Bokosi linafunsa mafunso aŵiri aakulu ndi kundandalika mfundo zina zothandiza.
Funso loyamba lalikulu ndi lakuti: Kodi ntchito yolembedwayo ndi yoletsedwa m’Baibulo? Ponena za zimenezi, Nsanja ya Olonda imeneyo inanena kuti Baibulo limaletsa kuba, kugwiritsa ntchito magazi molakwa, ndi kulambira mafano. Mkristu ayenera kupeŵa ntchito yolembedwa imene mwachindunji imachirikiza zimene Mulungu amatsutsa, monga zotchulidwa pamwambazo.
Funso lachiŵiri ndi lakuti: Kodi kugwira ntchito imeneyo kungapangitse munthu kukhala wotengamo mbali mumchitidwe woletsedwawo? Ndithudi, munthu wolembedwa ntchito m’nyumba yotchovera juga, m’chipatala chothandiza kuchotsa mimba, kapena m’nyumba ya mahule angakhale akutengamo mbali mumchitidwe wosemphana ndi Malemba. Ngakhale ntchito yake yatsiku ndi tsiku kumeneko itangokhala yosesa m’nyumbamo kapena kulandira mafoni, iye angakhale akuchirikiza mkhalidwe umene Mawu a Mulungu amaletsa.
Akristu ambiri ofuna kusankha ntchito apeza kuti kusinkhasinkha pamafunso aŵiri amenewo kumawathandiza kusankha chimene ayenera kuchita.
Mwachitsanzo, pamafunso aŵiriwo, munthu atha kuona chifukwa chimene wolambira woona sangaloŵere ntchito mwachindunji m’gulu lachipembedzo chonama, kugwirira ntchito tchalitchi ndiponso m’tchalitchi. Chivumbulutso 18:4 chikupereka lamulo lakuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake.” Munthu angayanjane ndi ntchito ndi machimo a Babulo Wamkulu ngati iye walembedwa ntchito yachikhalire ndi chipembedzo chophunzitsa kulambira konama. Kaya wantchitoyo akhale wosamalira munda wa maluŵa, woyeretsa, wokonza zinthu zowonongeka, kapena woŵerengera ndalama, ntchito yake ingamachirikize kulambira kotsutsana ndi chipembedzo choona. Ndiponso, anthu amene angamaone wantchitoyu akukongoletsa tchalitchi, kuikonza bwino, kapena kuchita zolinga zake zachipembedzo angamuyesedi kuti ndi wachipembedzo chomwecho.
Komano, bwanji za munthu amene sali wantchito wachikhalire watchalitchi kapena gulu lachipembedzo? Mwina wangoitanidwa kudzakonza mpope wamadzi umene waphulika mwadzidzidzi m’tchalitchi. Kodi zimenezo sizingakhale zosiyana ndi kudzipereka kuti achite ntchitoyo, monga yokakonza denga la tchalitchi?
Pamenepanso pali mikhalidwe yambiri yosiyanasiyana imene tingaganizire. Choncho tiyeni tipende mfundo zina zisanu zimene Nsanja ya Olonda imeneyo inafotokoza:
1. Kodi ntchitoyo yangokhala ntchito yothandiza anthu imene payokha siyoletsedwa m’Malemba? Titenge chitsanzo cha woperekera makalata. Kupereka kwake makalata m’deralo sikungatanthauze kuti akuchirikiza mchitidwe woletsedwa ngati imodzi mwa nyumba zimene amaperekako makalata ndi tchalitchi kapena chipatala chothandiza kuchotsa mimba. Mulungu amapereka kuwala kumene kumaloŵa m’nyumba zonse, kuphatikizapo m’tchalitchi kapena m’chipatala choterocho. (Machitidwe 14:16, 17) Mkristu amene amaperekera makalata atha kuona kuti akuchita ntchito yothandiza anthu onse, tsiku ndi tsiku. Zingakhalenso chimodzimodzi ndi Mkristu amene walola kukathandiza kumene kwabuka vuto mwadzidzidzi—wokonza mipope amene waitanidwa kudzatseka madzi amene akutayikira m’tchalitchi kapena wantchito wa mu ambulasi amene wapemphedwa kuthandiza wina amene wakomokera m’mapemphero m’tchalitchi. Atha kuona ntchitoyi monga thandizo wamba kwa ena.
2. Kodi munthuyo ali ndi ulamuliro wotani pa chochitikacho? Mkristu amene ali ndi sitolo sangalole kuoda ndi kugulitsa mafano, njirisi, fodya, kapena masoseji opangidwa ndi magazi. Pokhala mwini ndiye, ulamuliro ndi wake. Anthu angamulimbikitse kugulitsa fodya kapena mafano kuti apeze ndalama zambiri, koma iye adzatsatira zikhulupiriro zake za m’Malemba. Komano, Mkristu wolembedwa ntchito m’sitolo yaikulu yogulitsa zakudya angapatsidwe ntchito yolandira ndalama, kukolopa, kapena kuŵerengera ndi kulemba ndalama m’mabuku. Iye alibe ulamuliro pa zinthu zoodedwa ndi kugulitsidwa, ngakhale ngati zina mwa zimenezi n’zoletsedwa, monga fodya kapena zinthu zokhudzana ndi maholide achipembedzo.a (Yerekezani ndi Luka 7:8; 17:7, 8.) Zimenezi n’zogwirizana ndi mfundo yotsatira.
3. Kodi munthuyo akuloŵetsedwamo kwambiri motani? Tiyeni tibwerere ku chitsanzo cha sitolo. Wantchito wolandira ndalama kapena kuika zinthu m’mashelufu mwinamwake amagwira fodya kapena zinthu zachipembedzo mwakamodzikamodzi; imeneyo ndi mbali yaing’ono ya ntchito yake yonse. Komano n’zosiyana kwambiri ndi wantchito wa m’sitolo yomweyo amene akugwira ntchito pogulitsira fodya! Ntchito yake yonse, masiku onse, ndi yochita ndi chinthu chosemphana ndi zikhulupiriro zachikristu. (2 Akorinto 7:1) Zimenezi zikusonyeza chifukwa chimene mlingo wa kuloŵetsedwamo uyenera kupendedwa pofuna kuyankha mafunso okhudza ntchito.
4. Kodi malipiro amachokera kuti kapena kodi ntchitoyo ichitikira kuti? Talingalirani za mikhalidwe iŵiri. Pofuna kukopa anthu, chipatala chothandiza kuchotsa mimba chisankha kulemba ntchito munthu woti azisesa misewu yodutsa pafupi. Iye akulipiridwa ndi chipatala chothandiza kuchotsa mimba, koma si kumene akugwira ntchito, ndipo palibe amene amamuona m’chipatalacho tsiku lonse. M’malo mwake, amamuona akugwira ntchito yopindulitsa anthu onse imene mwa iyo yokha siyosemphana ndi Malemba, mosasamala kanthu za amene akumulipira. Tsopano mkhalidwe wina ndi uwu. M’dziko mmene lamulo limalola uhule, azachipatala alemba ntchito nesi woti azigwira ntchito m’nyumba za mahule, kuwapima kuti matenda opatsirana mwa njira yachiwerewere asafalikire. Ngakhale kuti akulipidwa ndi azachipatala, ntchito yake yonse amaichitira m’nyumba za mahule, kupangitsa chiwerewere kukhala chosaopsa, kuti chikhale cholandirika kwambiri. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza chifukwa chimene gwero lamalipiro a munthu ndi malo ogwirirako ntchitoyo zili mbali zofunika kuziganizira.
5. Kodi chotsatirapo cha kugwira ntchitoyo n’chotani; kodi chidzapweteka chikumbumtima chake kapena kukhumudwitsa ena? Chikumbumtima chathu ndiponso cha anthu ena chiyenera kuganiziridwa. Ngakhale kuti ntchito yakutiyakuti (kuphatikizapo kumene ikuchitikira ndi gwero la malipiro ake) ikuoneka kukhala yololeka kwa Akristu ambiri, munthu angaone kuti ingavutitse chikumbumtima chake. Mtumwi Paulo, amene anapereka chitsanzo chabwino, anati: “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino.” (Ahebri 13:18) Tiyenera kupeŵa kugwira ntchito imene idzatisautsa mtima; komatunso sitiyenera kutsutsa ena a chikumbumtima chosiyana. Komanso, mwina Mkristu sangaone kuchita ntchito yakutiyakuti kukhala kosemphana ndi Baibulo, koma akuona kuti zingakhumudwitse ambiri mu mpingo ndi kumene akukhala. Paulo anasonyeza malingaliro abwino m’mawu ake akuti: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.”—2 Akorinto 6:3, 4.
Tsopano tiyeni tibwerere ku funso lalikulu lija la kugwira ntchito panyumba ya tchalitchi, monga kuika mawindo atsopano, kuyeretsa makapeti, kapena kukonza poyatsira moto. Kodi mfundo zapamwambazo tingazigwiritse ntchito motani?
Kumbukirani mbali ya ulamuliro. Kodi Mkristuyo ndiye mwini kapena mkulu wantchito amene angasankhe kuvomera kapena kukana ntchito ya patchalitchi? Kodi Mkristu wokhala ndi ulamuliro umenewo angafune kuyanjana ndi Babulo Wamkulu mwa kudzipereka kuti achite ntchito yothandiza chipembedzo chinachake kupititsa patsogolo kulambira konama? Kodi zimenezo sizingafanane ndi kusankha kumagulitsa fodya kapena mafano m’sitolo yake?—2 Akorinto 6:14-16.
Ngati Mkristuyo ndi wolembedwa ntchito amene alibe ulamuliro wosankha ntchito zoti zichitidwe, mbali zina ziyenera kuganiziridwa, monga malo antchitoyo ndi utali wa nthaŵi yomwe adzakhala akugwira ntchitoyo. Kodi wolembedwa ntchitoyo wauzidwa kungopereka kapena kuika mipando yatsopano pachochitika china kapena kuchita utumiki wachifundo, monga wantchito yozimitsa moto kuti azimitse moto m’tchalitchi usanakule? Ambiri angaone kuti zimenezi zikusiyana ndi wolembedwa ntchito wa m’kampani ina yemwe akuthera nthaŵi yaitali kupaka utoto tchalitchi kapena kusamalira maluŵa nthaŵi zonse kuti tchalitchiyo izikongola. Kugwira ntchito yachikhalire kapena kwa nthaŵi yaitali patchalitchi kumeneku kungapangitse kuti ambiri aone Mkristuyo monga wa chipembedzo chomwe iyeyo amati sakugwirizana nacho, zimene zitha kuwakhumudwitsa.—Mateyu 13:41; 18:6, 7.
Tafotokoza mfundo zingapo zofunika zokhudza ntchito yolembedwa. Zimenezi zafotokozedwa m’nkhani yokhudzana kwenikweni ndi chipembedzo chonama. Komabe, zingagwiritsidwenso ntchito mofananamo pa mitundu ina ya ntchito zolembedwa. Pantchito iliyonse, pendani zinthu mwapemphero, mukumalingalira mbali zakutizakuti—ndiponso mwina zosafanana ndi zina zilizonse—za mkhalidwewo. Mfundo zimene zatchulidwa pamwambazo zathandiza kale Akristu ambiri oona mtima kuti apange zosankha zogwirizana ndi chikumbumtima chawo zosonyeza kuti akufuna kuyenda molunjika ndi moongoka pamaso pa Yehova.—Miyambo 3:5, 6; Yesaya 2:3; Ahebri 12:12-14.
[Mawu a M’munsi]
a Akristu ena ogwira ntchito m’chipatala afika polingalira mfundo imeneyi yaulamuliro. Dokotala angakhale ndi ulamuliro wolamula mankhwala kapena chinthu choyenera kuchitidwa pa wodwala. Ngakhale kuti wodwalayo sangakane, kodi dokotala wachikristu wokhala ndi ulamulirowo angalamule bwanji kuti aikidwe magazi kapena kuchotsa mimba, akudziŵa zimene Baibulo limanena pa nkhani zimenezi? Mosiyana ndi zimenezo, nesi wolembedwa ntchito m’chipatala angakhale alibe ulamuliro umenewo. Pochita ntchito zake za masiku onse, dokotala angamuuze kuti ayese magazi a wodwala pa zolinga zina kapena kuti asamalire wodwala amene wabwera kudzachotsa mimba. Mogwirizana ndi chitsanzo cholembedwa pa 2 Mafumu 5:17-19, atha kuona kuti popeza iye alibe ulamuliro umenewo ndipo sindiye walamula kuti wodwala aikidwe magazi kapena kuchotsa mimba, iye angapereke thandizo wamba kwa wodwalayo. Zoonadi, adzayenerabe kuganizira chikumbumtima chake, kuti ‘akhale pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma.’—Machitidwe 23:1.