Kodi Ndinu “Wolemera kwa Mulungu”?
“Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”—LUKA 12:21.
1, 2. (a) Kodi anthu amachita chilichonse chomwe chingafunike n’cholinga choti apeze chiyani? (b) Kodi Akhristu ayenera kulimbana ndi vuto komanso kupewa ngozi yotani?
KUYAMBIRA kale kwambiri, anthu a m’madera osiyanasiyana akhala akuyesetsa kugwira ntchito mwakhama n’cholinga choti alemere. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1800, anthu m’mayiko osiyanasiyana anatengeka ndi golide amene anapezeka ku Australia, South Africa, Canada, ndi ku United States. Anthuwo anali okonzeka kuchoka kwawo ndiponso kusiya mabanja awo kuti akapeze chuma kumayiko achilendo ndiponso komwe nthawi zina ankakhala movutikira. Inde, anthu ambiri n’ngokonzeka kuchita chilichonse chimene chingafunike n’cholinga choti apeze chuma.
2 Ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano sakuchita kuyenda maulendo aatali n’cholinga chofufuza chuma, koma amayenera kugwira ntchito mwakhama kuti apeze zofunika pamoyo. Komatu kuchita zimenezi kungakhale kovuta, mwinanso kofunika kugwira ntchito mwakalavulagaga. N’zosavuta kuti munthu adere nkhawa kwambiri za chakudya, zovala, ndiponso pogona, mpaka kufika ponyalanyaza zinthu zofunika kwambiri kapena mwinanso kuziiwala kumene. (Aroma 14:17) Yesu anapereka fanizo lomwe limasonyeza bwino kwambiri mtima woterewu. Fanizoli timalipeza pa Luka 12:16-21.
3. Fotokozani mwachidule fanizo la Yesu lomwe lili pa Luka 12:16-21.
3 Yesu anapereka fanizo lakeli nthawi imene ananena za kufunika kochenjera ndi kusirira kwa nsanje, zomwe takambirana m’nkhani yapitayi. Atachenjeza anthu za kusirira kwa nsanje, Yesu analankhula za munthu wina wachuma amene sanakhutitsidwe ndi nkhokwe zomwe zinali zodzaza ndi zinthu zabwino zimene anali nazo kale. Iye anazipasula n’kumanga zina zazikulu n’cholinga choti asungiremo zinthu zina zambiri zabwino. Atangoyamba kuganiza zoti nthawi yoti asangalale ndi kukhala moyo wapamwamba yakwana, Mulungu anamuuza kuti watsala pang’ono kufa ndipo munthu wina adzatenga zinthu zonse zabwino zimene iye anasungazo. Ndiyeno Yesu anatsiriza fanizoli ndi mawu akuti: “Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.” (Luka 12:21) Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera m’fanizoli? Kodi phunziro limenelo tingaligwiritsire ntchito motani m’moyo wathu?
Munthu Amene Anathedwa Nzeru
4. Kodi tinganene kuti munthu wa m’fanizo la Yesu anali wotani?
4 Fanizo limene Yesu anaperekali si lachilendo. Yesu anangoyamba ndi mawu akuti: “Munda wa munthu wina wachuma unabereka bwino.” Yesu sananene kuti munthuyu anapeza chuma chakechi mwachinyengo. M’mawu ena, munthuyu sanatchulidwe monga munthu woipa. Ndipo, malinga ndi zimene Yesu ananena, sikulakwa kunena kuti munthu wam’fanizoli anali wolimbikira ntchito. Tingathe kuona kuti iye anakonzekera bwino mwa kusunga zinthu zodzagwiritsira ntchito m’tsogolo, mwina poganizira za banja lake. Choncho, kuona nkhaniyi mosaganizira zinthu zauzimu, iye angaimire munthu wogwira ntchito mwakhama amene sanyalanyaza udindo wake.
5. Kodi munthu wa m’fanizo la Yesu uja anakumana ndi vuto lotani?
5 Yesu ananena kuti munthu wa m’fanizoli anali wachuma, kutanthauza kuti anali kale ndi zinthu zambiri zabwino. Komabe, malinga n’kunena kwa Yesu, munthu wachumayu anakumana ndi vuto. Munda wake unabereka bwino kwambiri kuposa mmene ankayembekezera, ndipo zokololazo zinali zoposa zimene ankafunikira kapena zimene akanatha kuzisamalira. Kodi akanachita chiyani?
6. Kodi atumiki a Mulungu masiku ano amafunika kusankha zochita pankhani ngati ziti?
6 Nawonso atumiki ambiri a Yehova masiku ano amakumana ndi zinthu zofanana kwambiri ndi zimene munthu wachumayu anakumana nazo. Akhristu oona amayesetsa kugwira ntchito mokhulupirika ndiponso mwakhama. (Akolose 3:22, 23) Kaya analembedwa ntchito kapena akuyendetsa bizinesi yawo, kawirikawiri zinthu zimawayendera bwino kwambiri. Akapatsidwa mwayi wokwezedwa pantchito kapena mwayi wotukula bizinesi zawo, amafunika kusankha zoti achite. Iwo amafunika kuona ngati ndi bwino kuvomera mwayi umenewo n’kumapanga ndalama zambiri kapena kuukana. N’chimodzimodzinso ndi achinyamata a Mboni. Ambiri mwa iwo amakhoza bwino kwambiri kusukulu. Chifukwa cha zimenezi, iwo angathe kupatsidwa mphoto kapena mwayi wolipiriridwa maphunziro kusukulu zapamwamba. Kodi ndi bwino kuti angovomera mwayi umenewo?
7. Kodi munthu wa m’fanizo la Yesu uja anathetsa bwanji vuto limene anakumana nalo?
7 Tikaonanso fanizo la Yesu lija, kodi munthu wachuma uja anatani munda wake utabereka bwino kwambiri mpaka kufika poti analibe malo osungiramo zokolola zake? Iye anaganiza zopasula nkhokwe zomwe anali nazo n’kumanga zina zazikulu. Mwachionekere maganizo akewo anam’thandiza kumva ngati kuti moyo wake ukhala wotetezeka ndiponso wabwino. Iye anayamba kuganiza kuti: “Ndidzauza moyo wanga kuti: ‘Moyo wangawe, uli ndi zinthu zambiri zabwino mwakuti zisungika kwa zaka zambiri; ungoti phee tsopano, udye, umwe, usangalale.’”—Luka 12:19.
N’chifukwa Chiyani Anatchedwa “Wopanda Nzeru”?
8. Kodi munthu wa m’fanizo la Yesu uja ananyalanyaza mfundo yofunika iti?
8 Koma, mogwirizana ndi zimene Yesu anafotokoza, zimene munthu wachuma uja anaganiza kuchita, zinali zosam’thandiza kukhala wotetezeka. N’kutheka kuti zinkaoneka ngati zanzeru, koma anaiwala mfundo yofunika kwambiri yomwe ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. Iye ankangoganizira za iye yekha basi. Ankaganizira za mmene angakhalire mosatekeseka, n’kumangodya, kumwa, ndi kusangalala. Iye ankaona kuti chifukwa chakuti ali ndi “zinthu zambiri zabwino,” angathenso kukhala “zaka zambiri.” Koma n’zomvetsa chisoni kuti zinthu sizinatero. Monga momwe Yesu ananenera, “ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Usiku womwewo, zinthu zonse zimene munthu wachuma uja anakundika zinakhala zopanda ntchito kwa iye, chifukwa Mulungu anati: “Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna. Nanga chuma chimene wakundikachi chidzakhala cha ndani?”—Luka 12:20.
9. Kodi n’chifukwa chiyani munthu wa m’fanizo uja anatchedwa kuti wopanda nzeru?
9 Apa tafika pa mfundo yaikulu ya fanizoli. Mulungu anatchula munthu uja kuti wopanda nzeru. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo (Exegetical Dictionary of the New Testament), limafotokoza kuti mawu a Chigiriki omwe anamasuliridwa kuti “wopanda nzeru,” “nthawi zonse amasonyeza kulephera kuzindikira zinthu.” Bukuli limanena kuti m’fanizoli, Mulungu akufotokozedwa kuti anagwiritsira ntchito mawu amenewo posonyeza kuti “zoganiza za m’tsogolo za anthu olemera n’zopanda ntchito.” Mawu a Chigirikiwo satanthauza munthu wopusa, koma amatanthauza “munthu amene amakana kudalira Mulungu.” Mmene Yesu anafotokozera za munthu wachuma uja zikutipangitsa kuganizira zimene anadzanena panthawi ina kwa Akhristu a mumpingo wa m’nthawi ya atumwi ku Laodikaya, ku Asia Minor kuti: “Ukunena kuti: ‘Ndine wolemera, ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu,’ koma sukudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, wosauka, wakhungu, ndi wa maliseche.”—Chivumbulutso 3:17.
10. N’chifukwa chiyani kukhala ndi “zinthu zambiri zabwino” sikutsimikizira kuti munthu akhala “zaka zambiri”?
10 Tingachite bwino kuganizira kwambiri phunziro la mfundoyi. Kodi ifeyo tikufanana ndi munthu wa m’fanizoli, pogwira ntchito mwakhama n’cholinga choti tikhale ndi “zinthu zambiri zabwino,” koma n’kumalephera kuchita zinthu zofunikira kuti tikhale ndi chiyembekezo chodzakhala “zaka zambiri”? (Yohane 3:16; 17:3) Baibulo limati: “Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo,” ndipo “wokhulupirira chuma chake adzagwa.” (Miyambo 11:4, 28) Motero, Yesu anamaliza fanizoli ndi malangizo awa: “Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”—Luka 12:21.
11. Kodi n’chifukwa chiyani kudalira chuma n’kosathandiza?
11 Ponena kuti “umu ndi mmene zimakhalira,” Yesu ankatanthauza kuti zimene zinachitikira munthu wachuma wa m’fanizoli zingachitikirenso anthu amene amangodalira chuma basi. Kwenikweni vuto sikuti lili pa ‘kudziunjikira chuma,’ koma lili pa kulephera kukhala “wolemera kwa Mulungu.” Nayenso wophunzira Yakobe anapereka chenjezo lofanana ndi limeneli. Iye analemba kuti: “Tamverani tsopano inu amene mumati: ‘Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti ndipo tikatha chaka kumeneko, ndi kuchita malonda ndi kupeza phindu.’ Mumatero pamene simudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa. . . . M’malo mwake muyenera kunena kuti: ‘Yehova akalola, tidzakhala ndi moyo, ndi kuchita zakutizakuti.’” (Yakobe 4:13-15) Zilibe kanthu kuti munthu ali ndi chuma chochuluka motani, chonsecho chingakhale chosathandiza ngati munthuyo sali wolemera kwa Mulungu. Ndiye, kodi kukhala wolemera kwa Mulungu n’kutani?
Kukhala Wolemera kwa Mulungu
12. Kodi tingakhale olemera kwa Mulungu mwa kuchita chiyani?
12 Yesu anasiyanitsa kukhala wolemera kwa Mulungu ndi kudzikundikira chuma chakuthupi. Choncho, Yesu ankatanthauza kuti cholinga chathu chachikulu pamoyo chisakhale kudzikundikira chuma chakuthupi n’kumasangalala nacho. M’malo mwake, tiyenera kugwiritsira ntchito chuma chathucho polimbikitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kukhala olemera kwa Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iye amatidalitsa kwambiri tikamatero. Baibulo limati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.
13. Kodi madalitso a Yehova ‘amalemeretsa’ bwanji?
13 Yehova akamadalitsa anthu ake, nthawi zonse madalitsowo amakhala osayerekezeka. (Yakobe 1:17) Mwachitsanzo, dziko limene Yehova anapatsa Aisiraeli, linali ‘dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ngakhale kuti dziko la Iguputo analifotokozanso choncho, koma panali chinthu chimodzi chofunika kwambiri chimene chinkalisiyanitsa ndi dziko limene Yehova anapereka kwa Aisiraeli. Pofotokozera Aisiraeli za dzikolo, Mose ananena kuti ndi ‘dziko loti Yehova Mulungu wanu akulisamalira.’ Zimenezi zinatanthauza kuti iwo adzasangalala ndi dzikolo chifukwa chakuti Yehova azikawasamalira. Aisiraeliwo akakhala okhulupirika kwa Yehova, iye ankawadalitsa kwambiri ndipo ankasangalala ndi moyo kuposa mitundu ina yonse yowazungulira. Zoonadi, madalitso a Yehova ndi amene ‘amalemeretsa.’—Numeri 16:13; Deuteronomo 4:5-8; 11:8-15.
14. Kodi ndi madalitso otani amene anthu olemera pamaso pa Mulungu amakhala nazo?
14 Mawu oti “wolemera kwa Mulungu” amamasuliridwanso kuti ‘wolemera pamaso pa Mulungu.’ (Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Anthu olemera mwakuthupi amaganizira kwambiri mmene ena angawaonere. Kawirikawiri zimenezi zimaonekera ndi mmene akukhalira pamoyo wawo. Iwo amangofuna kukopa chidwi cha anthu ndi zimene Baibulo limati “kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake.” (1 Yohane 2:16) Anthu amenewa amasiyana kwambiri ndi anthu olemera pamaso pa Mulungu, omwe Mulungu amawayanja, amawakomera mtima, ndiponso amakhala naye paubwenzi wolimba. Iwo amakhala mosangalala ndiponso motetezeka kwambiri chifukwa cha zimenezi, zomwe sizingatheke chifukwa chodalira chuma. (Yesaya 40:11) Komabe funso n’lakuti, Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale olemera pamaso pa Mulungu?
Olemera Pamaso pa Mulungu
15. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale olemera kwa Mulungu?
15 M’fanizo la Yesu lija, munthu uja anaganizira ndiponso anagwira ntchito mwakhama n’cholinga choti alemere basi, ndipo n’chifukwa chake anatchedwa wopanda nzeru. Motero kuti tikhale olemera kwa Mulungu tiyenera kuchita khama ndi kugwira nawo mokwanira ntchito zimene n’zofunika kwambiri pamaso pa Mulungu. Imodzi mwa ntchito zimenezi ndi imene Yesu analamula kuti: “Choncho pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyo 28:19) Tikagwiritsira ntchito nthawi, mphamvu, ndi luso lathu, osati n’cholinga chofuna kudzilemeretsa, koma pantchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira, timakhala ngati tikusunga chuma. Anthu amene achita zimenezi apindula kwambiri mwauzimu, monga momwe zitsanzo zotsatirazi zikusonyezera.—Miyambo 19:17.
16, 17. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene mungafotokoze zosonyeza moyo umene umachititsa munthu kukhala wolemera pamaso pa Mulungu?
16 Mwamuna wina wachikhristu m’dziko lina la kum’mawa kwa Asia ankagwira ntchito yokonza makompyuta, yomwe inali ya malipiro ambiri. Komatu iye ankagwira ntchitoyo kwa nthawi yaitali kwambiri ndipo anakhala wofooka mwauzimu. Kenaka, iye anasiya ntchitoyo n’kuyamba kupanga ayisikilimu n’kumagulitsa m’misewu. Anachita zimenezi n’cholinga choti akhale ndi nthawi yambiri yochita zinthu zauzimu. Anzake amene ankagwira nawo ntchito anayamba kumuseka, koma kodi zinthu zinamuyendera bwanji? Iye anati: “Kunena zoona, panthawi imeneyi ndinkapeza ndalama zambiri kusiyana ndi pamene ndinkagwira ntchito yokonza makompyuta.” Ndiyeno anapitiriza kuti: “Panopa ndikusangalala kwambiri chifukwa ndilibenso nkhawa zimene ndinkakhala nazo pantchito yoyamba ija. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti tsopano ndili paubwenzi wolimba ndi Yehova.” Chifukwa cha kusintha kumeneku Mkhristu ameneyu anayamba utumiki wa nthawi zonse, ndipo tsopano akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko la kwawo. Zoonadi, madalitso a Yehova ‘amalemeretsa.’
17 Chitsanzo china ndi cha mayi wina yemwe anakulira m’banja limene linkaona kuti maphunziro n’ngofunika kwambiri. Iye anakaphunzira ku mayunivesite a ku France, Mexico, ndi ku Switzerland, ndipo ankaona kuti adzapeza ntchito yabwino kwambiri. Mayiyu anati: “Zinthu zinkandiyendera bwino kwambiri. Ndinapeza ntchito yapamwamba ndipo anthu ankandilemekeza kwambiri, koma mumtima mwangamu ndinkaona kuti ndikusoweka chinachake.” Kenaka, iye anaphunzira za Yehova ndipo anati: “Pamene ndinkadziwa zinthu zambiri zauzimu, ndinayamba kukhala ndi cholinga choti ndim’sangalatse Yehova ndiponso ndim’bwezere kenakake pa zimene wandichitira. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti ndiyenera kum’tumikira nthawi zonse.” Iye anasiya ntchito yake ndipo posapita nthawi anabatizidwa. Kwa zaka 20 zapitazi, iye wakhala akuchita utumiki wa nthawi zonse mosangalala. Ndiyeno, iye anati: “Ena amaganiza kuti ndawononga luso langa, koma amaonanso okha kuti ndine wosangalala, ndipo amasirira mfundo zimene ndimayendera pa moyo wanga. Tsiku lililonse ndimapemphera kwa Yehova kuti andithandize kukhala wodzichepetsa n’cholinga choti azindiyanja.”
18. Mofanana ndi Paulo, kodi tingatani kuti tikhale olemera kwa Mulungu?
18 Saulo, yemwe anadzakhala mtumwi Paulo, anali wophunzira kwambiri, moti akanatha kukhala wolemera mwakuthupi. Koma iye analemba kuti: “Zoonadi, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa cha kudziwa Khristu Yesu Ambuye wanga.” (Afilipi 3:7, 8) Paulo anaona kuti chuma chimene anachipeza chifukwa cha Khristu chinaposa chuma chilichonse chimene akanapeza m’dzikoli. Nafenso, ngati titasiya zolinga zonse zadyera n’kuyamba moyo wodzipereka kwa Mulungu, tingakhale ndi moyo wolemera pamaso pake. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Mphoto ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”—Miyambo 22:4.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi munthu wa m’fanizo la Yesu anakumana ndi vuto lotani?
• N’chifukwa chiyani munthu wa m’fanizoli anatchedwa wopanda nzeru?
• Kodi kukhala wolemera kwa Mulungu kumatanthauza chiyani?
• Tingatani kuti tikhale olemera kwa Mulungu?
[Chithunzi patsamba 26]
N’chifukwa chiyani munthu wachuma uja anatchedwa kuti wopanda nzeru?
[Chithunzi patsamba 27]
Kodi mwayi woti titukule moyo wathu ungakhale bwanji chiyeso?
[Chithunzi pamasamba 28, 29]
“Madalitso a Yehova alemeretsa”