NYIMBO 151
Iye Adzaitana
Losindikizidwa
1. Moyo wathu sumachedwa kutha,
Timafadi mwamsanga.
Mukanthawi kochepa kwambiri
Timayamba kulira.
Kodi akufa angadzauke?
M’lungu akulonjeza:
(KOLASI)
Iye adzawaitana,
Akufa adzayankha.
Akulakalakatu
Ntchito ya manja ake.
Mulungu adzatidzutsa
Chonde musakaike.
Tidzakhala kosatha
Mongadi anthu ake.
2. Anthu a M’lungu akamwalira
Iye sawaiwala.
Akuwakumbukira onsewo,
Iye adzawadzutsa
Ndipo tonsefe tidzakhaladi
Ndi moyo mpaka kale.
(KOLASI)
Iye adzawaitana,
Akufa adzayankha.
Akulakalakatu
Ntchito ya manja ake.
Mulungu adzatidzutsa
Chonde musakaike.
Tidzakhala kosatha
Mongadi anthu ake.
(Onaninso Yoh. 6:40; 11:11, 43; Yak. 4:14.)