NYIMBO 101
Tizichita Zinthu Mogwirizana
Losindikizidwa
1. M’dziko logawikanali,
Tili m’gulu la Mulungu.
Timakhala mwamtendere,
Timasangalala.
Timaunyadira
Mgwirizanowu.
Tili ndi ntchito yambiri.
Yesu akutsogolera.
Tiyeni tizimumvera
N’kumagwirizana.
2. Popempherera umodzi
Tizikondana kwambiri.
Chikondi chimabweretsa
Chimwemwe, mtendere.
Mgwirizano wathu
Ndi wabwinodi.
Pamene tikukondana,
M’lungu adzatithandiza
Kukhala ogwirizana,
Pomutumikira.
(Onaninso Mika 2:12; Zef. 3:9; 1 Akor. 1:10.)