Mbiri ya Moyo Wanga
Moyo Wanga Wosangalatsa Ngakhale Ndakumana N’zachisoni
YOSIMBIDWA NDI AUDREY HYDE
Ndikaganizira zaka 63 zimene ndakhala ndikuchita utumiki wa nthaŵi zonse, 59 mwa izo ndikutumikira pa likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova, ndimaona kuti moyo wanga wakhala wosangalatsa. N’zoona kuti chisoni chinandigwira kwambiri poona mwamuna wanga woyamba akufa ndi matenda a kansa ndiponso kuona mwamuna wanga wachiŵiri akuzunzika ndi matenda osautsa a Alzheimer. Koma taimani ndikuuzeni mmene ndakhalirabe wosangalala ngakhale kuti ndakumana ndi zovuta zoterezi.
NDINAKULIRA pa famu ina, pafupi ndi katauni kotchedwa Haxtun m’chigwa chomwe chili kumpoto chakum’maŵa m’boma la Colorado, kufupi ndi malire a boma la Nebraska. Ndinali mwana wachisanu m’banja la ana asanu ndi mmodzi la Orille ndi Nina Mock. Russel, Wayne, Clara ndi Ardis anabadwa pakati pa 1913 ndi 1920, ndipo ineyo ndinabadwa chaka chotsatiracho. Curtis anabadwa mu 1925.
Mu 1913, mayi anga anakhala Wophunzira Baibulo, dzina limene Mboni za Yehova zinkadziŵika nalo panthaŵiyo. Kenaka, tonse m’banja mwathu tinakhala Mboni.
Ndinkasangalala ku Chigwa
Bambo anali munthu wochita zinthu motsogola. Motero, m’nyumba zathu zonse pa famupo munali magetsi, ngakhale kuti masiku amenewo zimenezi zinali zosoŵa kwabasi. Komanso tinkadyerera ntchito ya ulimi, moti tinkakhala ndi mazira kuchokera ku nkhuku zathu, ndipo ng’ombe zathu zinkatipatsa mkaka, mafuta ochokera ku mkaka komanso batala. Tinkagwiritsira ntchito mahatchi polima ndipo tinkalima mbewu zinazake zamtundu wa mabulosi (malubeni) komanso tinkalima mbatata, tirigu ndi chimanga.
Bambo ankafuna kuti ana awo tonsefe tiphunzire zintchito. Ngakhale ndisanayambe sukulu, anandiphunzitsa kulima. Ndikukumbukira kuti masiku ena m’chilimwe, kunja kukutentha kwambiri, ndinali kupalira mizere italiitali m’munda mwathu. Ndiye ndinkadzifunsa kuti, ‘Koma ndikafikadi kumapeto kwa mzerewu?’ Thupi lonse linali thukuta kamukamu, kwinakunso njuchi zikundiluma. Nthaŵi zina ndinkadzimvera chisoni poganizira kuti ana ena sankagwira ntchito zolimba ngati ifeyo. Komabe, ndikamakumbukira ubwana wanga, ndimayamikira kuti anatiphunzitsa kukhala azintchito.
Ana tonse anatigaŵira ntchito. Ardis ankadziŵa kukama mkaka kuposa ine, motero ntchito yanga inali yoyeretsa m’khola la mahatchi, kuchotsamo ndoŵe zonse. Komatu tinkachitanso zinthu zina zosangalatsa ndiponso tinkaseŵera. Ine ndi Ardis tinkaseŵera mpira m’timu inayake ya kumene tinkakhala. Tinkaseŵera malo osiyana m’timuyo.
Usiku wopanda mitambo, kumwamba kunkaoneka bwino kwambiri m’chigwachi. Nyenyezi zambirimbiri zimene ndinkatha kuziona zinkandikumbutsa za Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Ngakhale ndili mwana, ndinkaganizira lemba la Salmo 147:4, lomwe limati: “[Yehova] aŵerenga nyenyezi momwe zili; azitcha mayina zonsezi.” Nthaŵi zambiri, usiku kukakhala kulibe mitambo chonchi, sindinkasungulumwa chifukwa ndinkakhala ndi galu wathu, dzina lake Judge, amene ankagoneka mutu wake pamwendo panga. Nthaŵi zambiri masana, ndinkakhala pakhonde n’kumayang’ana mwachidwi minda ya tirigu wosacha kwinaku mphepo ikukupiza m’mindayo, n’kumachititsa kuti izichita nyezinyezi chifukwa cha kuwala kwa dzuŵa.
Chitsanzo Chabwino Chimene Amayi Anatipatsa
Mayi anga anali munthu wodzipereka kwambiri ku banja lake. Nthaŵi zonse iwo ankaona kuti bambo ndiwo anali mutu panyumbapo ndipo anatiphunzitsa kuti tiziwalemekeza. Mu 1939 bambo nawo anakhala a Mboni za Yehova. Tinkadziŵa kuti bambo ankatikonda ngakhale kuti ankatigwiritsa ntchito zolimba ndipo sankatisasatitsa. Nthaŵi zambiri, m’nyengo yachisanu iwo ankatikweza m’kangolo kopanda matayala kokokedwa ndi mahatchi aŵiri. Ndiye ife si kusangalala kwake tikamaona chipale chofeŵa chili waliwali!
Komano mayi ndi amene anatiphunzitsa kukonda Mulungu ndiponso kulemekeza Baibulo. Anatiphunzitsa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova ndiponso kuti iyeyu ndiye Chitsime cha moyo. (Salmo 36:9; 83:18) Anatiphunzitsanso kuti iye anatipatsa malamulo, osati n’cholinga choti tisamasangalale, koma n’cholinga choti tipindule nawo. (Yesaya 48:17) Mayi ankakonda kugogomezera kwambiri kuti tili ndi ntchito yapadera yoyenera kuichita. Anatiphunzitsa kuti Yesu anauza otsatira ake kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
M’masiku amenewo ndikanali mwana, ndikangobwera kusukulu n’kupeza kuti mayi mulibe m’nyumba, ndinkapita kukawafunafuna. Tsiku lina ndili ndi zaka sikisi kapena mwina seveni, ndinawapeza m’khola. Kenaka kunayamba kugwa chimvula chadzaoneni. Tinali m’chinyumba chosungiramo zakudya za ziŵeto, ndipo ndinawafunsa amayiwo ngati chimvulacho chinali Chigumula china cha Mulungu. Anandilimbikitsa pondiuza kuti Mulungu analonjeza kuti sadzawononganso dzikoli ndi chigumula. Ndikukumbukiranso kuti nthaŵi zambiri ndinali kuthamangira m’chipinda chapansi pa nyumba yathu, chifukwa kaŵirikaŵiri kunkawomba chimphepo chamkuntho.
Mayi anali atayamba kale kuchita nawo ntchito yolalikira ngakhale ineyo ndisanabadwe. Kagulu kakang’ono ka anthu kankakumana kunyumba kwathu, ndipo onsewo anali ndi chiyembekezo chokakhala ndi Kristu kumwamba. Ngakhale kuti amayi zinkawavuta kulalikira nyumba ndi nyumba, iwo anagonjetsa mantha awo chifukwa chokonda kwambiri Mulungu. Anali wokhulupirika mpaka pa tsiku limene anamwalira pa November 24, 1969, ali ndi zaka 84. Ndinawauza mawu aŵa mowanong’oneza m’khutu: “Mayi, mukupita kumwamba, ndipo mukakhala ndi anthu amene akukudziŵani.” Ndinasangalala kwambiri kuti ndinali nawo limodzi mayi anga panthaŵiyi ndiponso kuti ndinakambirana nawo za mmene ineyo ndimakhulupiririra chiyembekezo chimenecho! Iwo ananena chapansipansi kuti, “Zikomo wandilimbikitsa.”
Tinayamba Kulalikira
Mu 1939, Russel anakhala mpainiya, dzina limene timatchula Mboni za Yehova zimene zimafalitsa uthenga wabwino nthaŵi zonse. Iye ankachita upainiya ku Oklahoma ndi ku Nebraska mpaka mu 1944 pamene anamuitana kuti akatumikire pa likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova (lotchedwa Beteli), ku Brooklyn, ku New York. Ndinayamba kuchita upainiya pa September 20, 1941, ndipo ndinatumikira m’madera osiyanasiyana ku Colorado, Kansas, ndi Nebraska. Ndinali wosangalala kwambiri zaka zimene ndinkachita upainiyazi chifukwa chakuti ndinkatha kuthandiza ena kudziŵa Yehova komanso ndinaphunzira kudalira Yehova ndi mtima wanga wonse.
Panthaŵi imene Russel anayamba kuchita upainiya, Wayne anali ku yunivesite m’chigawo cha kumpoto chakum’maŵa kwa dziko la United States ndipo apa n’kuti atagwirako ntchito yolembedwa kwa kanthaŵi kochepa. Kenaka, anamuitana ku Beteli. Kwa kanthaŵi ndithu, iye anatumikira ku famu yotchedwa Kingdom Farm, pafupi ndi Ithaca, ku New York. Kumeneko, ankalimako chakudya chodyetsa anthu ochepa ogwira ntchito pa famupo komanso anthu pafupifupi 200 ogwira ntchito ku Beteli ya ku Brooklyn. Wayne anatumikira Yehova pogwiritsira ntchito luso lake ndiponso zimene anaphunzira, mpaka pamene anamwalira mu 1988.
Mkulu wanga Ardis anakwatiwa ndi James Kern, ndipo anabereka naye ana asanu. Iye anamwalira mu 1997. Mkulu wanga wina, Clara, adakali wokhulupirika kwa Yehova mpaka panopo, ndipo ndikakhala patchuthi, ndimapitabe kunyumba kwake ku Colorado. Curtis, yemwe ali chitsirizira m’banja mwathu, anabwera ku Beteli ya ku Brooklyn chakumapeto kwa m’ma 1940. Ntchito yake inali yoyendetsa chigalimoto chachikulu chotenga katundu ndiponso zakudya kuchoka nazo ku Kingdom Farm kapena kupita nazo kumeneko. Iye sanakwatire, ndipo anamwalira mu 1971.
Cholinga Changa Chinali Kukatumikira pa Beteli
Azichimwene anga aakulu ndiwo anayamba kupita ku Beteli, ndipo ineyo ndinkafunanso kukatumikira kumeneko. Sindikukayika kuti ndinaitanidwa ku Beteli chifukwa cha chitsanzo chawo chabwino. Kumvetsera amayi akukamba mbiri ya gulu la Mulungu ndiponso kudzionera ndekha kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo okhudza masiku otsiriza kunachititsa kuti chikhumbo changa chofuna kukhala pa Beteli chikule. Ndinalonjeza Yehova m’pemphero kuti ngati atandilola kukhala pa Beteli, sindidzachokapo pokhapokha ngati nditapezeka ndi maudindo ena amene Baibulo limalamula kuti ndiyenera kuwakwaniritsa.
Ndinafika ku Beteli pa June 20, 1945, ndipo ndinapatsidwa ntchito yokonza m’nyumba kuti muzikhala mwaukhondo. Ndinali ndi zipinda 13 zoti ndizikonza, ndipo tsiku lililonse ndinkayala mabedi 26, kuphatikizapo kukonza m’njira zam’kati mwa nyumba, m’masitepe, ndiponso kupukuta mawindo. Inali ntchito yotopetsa kwambiri. Tsiku lililonse ndikamagwira ntchito, ndinkadziuza kuti, ‘N’zoona kuti watopa, komatu uli pa Beteli, panyumba ya Mulungu!’
Nditangobwera kumene pa Beteli, ndinachita zinazake zochititsa manyazi. Poti ndinakulira kumidzi, sindinkadziŵa kuti kachikepe konyamulira katundu pokwera naye m’mwamba kapena potsika naye pansi m’zipinda za m’nyumba yosanja ankangokatcha kuti choperekera. Ndiyeno tsiku lina ndili pantchito yanga ndinalandira telefoni ndipo uthenga wake unali wakuti, “Choperekeracho chibwere kuno!” Woimba foniyo anaidula atangonena mawuŵa, moti sindinadziŵe kuti ndichite chiyani makamaka. Koma kenaka ndinakumbukira kuti mbale wina amene ankakhala m’chipinda china mwa zipinda zimene ndinkasamalirazo anali woperekera zakudya m’chipinda chodyeramo. Motero ndinagogoda pachitseko cha chipinda chake n’kumuuza kuti, “Akuti akukufunani kukhitchini.”
Kukwatiwa ndi Nathan Knorr
Kuyambira m’ma 1920, otumikira pa Beteli amene ankafuna kukwatira kapena kukwatiwa ankayenera kuchoka pa Beteli n’kukachita ntchito zina za Ufumu. Koma kumayambiriro kwa m’ma 1950, anthu angapo amene anali atatumikira pa Beteli kwa nthaŵi yaitali ndithu, analoledwa kukwatirana n’kukhalabe pa Beteli. Ndiyeno Nathan H. Knorr, yemwe panthaŵiyo ankayang’anira ntchito ya Ufumu padziko lonse, atasonyeza kuti akundifuna, ndinaganiza kuti, ‘Ameneyu akhala basi!’
Nathan anali ndi maudindo ambiri okhudza kuyang’anira ntchito ya padziko lonse yolalikira ya Mboni za Yehova. Motero sanandibisire ayi, anandiuza zifukwa zambirimbiri zakuti ndiganizire mofatsa ndisanalole kumanga naye banja. Panthaŵiyo, iye sankakhazikika chifukwa ankayendera maofesi a nthambi a Mboni za Yehova padziko lonse ndipo nthaŵi zambiri ankatha milungu yambirimbiri akachokapo. Motero analongosola kuti tizidzasiyana kwa nthaŵi yaitali.
Ndili mwana ndinkaganiza zodzakwatiwa m’nyengo yoti kwayamba kufunda ndiyeno n’kupita kaye pa zilumba za m’nyanja ya Pacific zotchedwa Hawaii kukasangalala. Koma m’malo mwake tinakwatirana m’nyengo yozizira, pa January 31, 1953, ndipo madzulo Loŵeruka limenelo ndiponso Lamlungu lake tinakasangalalira ku New Jersey. Lolemba tinayamba ntchito. Komano patatha mlungu umodzi m’pamene tinapitadi kokasangalala kwa mlungu wathunthu.
Mwamuna Wolimbikira Ntchito
Nathan anabwera pa Beteli mu 1923, ali ndi zaka 18. Anaphunzitsidwa ndi anthu odziŵa ntchito monga Joseph F. Rutherford, amene anali kutsogolera ntchito ya Mboni, ndiponso Robert J. Martin, yemwe anali woyang’anira zosindikiza mabuku. Mbale Martin atamwalira mu September 1932, Nathan anakhala woyang’anira zosindikiza mabuku. Chaka chotsatira, mbale Rutherford anatenga Nathan paulendo wake woyendera nthambi za Mboni za Yehova ku Ulaya. Mu January 1942 Mbale Rutherford atamwalira, Nathan anapatsidwa udindo woyang’anira ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova.
Nathan ankachita zinthu moganizira za m’tsogolo, motero nthaŵi zonse ankakonzekereratu za kuwonjezeka kwa m’tsogolo. Ena ankaganiza kuti akulakwa, chifukwa zinkaoneka kuti mapeto a dzikoli ayandikira kwambiri. Munthu wina amene anaona zimene Nathan ankakonza kaamba ka m’tsogolo anamufunsa kuti: “Kodi Mbale Knorr zimenezi n’zantchito yanji makamaka? Kodi mulibe chikhulupiriro?” Iye anayankha kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho, koma ngati chimaliziro chitapanda kubwera mwamsanga monga mmene tikuganizira, ndiye kuti tidzakhala tili okonzeka.”
Chinthu chimodzi chimene Nathan ankafunitsitsa chitachitika ndicho kukhazikitsa sukulu ya amishonale. Motero pa February 1, 1943, sukulu ya amishonale inayamba pa famu yaikulu imene mchimwene wanga Wayne ankagwirako ntchito. Ngakhale kuti sukuluyo inali kosi yophunzira Baibulo yolira nthaŵi yochuluka yomwe inkachitika kwa miyezi pafupifupi isanu, Nathan ankaonetsetsa kuti ophunzirawo akupumako n’kumasangalala. M’makalasi oyambirira a sukuluyi, iye ankachita nawo maseŵera a mpira, koma kenaka anasiya kuseŵera poopa kuti akavulala zingamusokoneze kukapezeka pamisonkhano yachigawo. M’malo mwake anaganiza zoti azingokhala woimbira mpirawo. Ophunzirawo zinkawaseketsa kuona iyeyu akupotoza dala malamulo pokondera ophunzira ochokera mayiko akunja.
Maulendo Amene Ndinayenda ndi Nathan
M’kupita kwa nthaŵi, ndinayamba kupita nawo kumayiko akunja ndi Nathan. Ndinkasangalala pocheza ndi anthu ogwira ntchito m’maofesi a nthambi ndiponso amishonale n’kumakambirana nawo zimene ifeyo ndiponso iwowo anakumana nazo. Ndinaona ndekha chikondi chawo ndiponso kudzipereka kwawo, ndipo ndinaona mmene ntchito yawo ndiponso moyo wawo umakhalira m’mayiko amene anatumizidwa. Kwa zaka zambiri, ndakhala ndikulandira makalata othokoza chifukwa cha maulendo ameneŵa.
Ndimakumbukira zinthu zambiri zimene zinachitika m’maulendo ameneŵa. Mwachitsanzo, titapita ku Poland, alongo aŵiri ankanong’onezana ine ndili pomwepo. Ndiye ndinawafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani mukulankhula monong’ona?” Iwo anapepesa, n’kundilongosolera kuti anazoloŵera zonong’onezana, chifukwa chakuti ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Poland ndipo m’nyumba zawo, aboma ankabisamo mamaikolofoni kuti azimvetsera zimene akulankhula.
Mlongo Adach anali mmodzi wa anthu amene anatumikira ku Poland pamene ntchito yathu inali yoletsedwa. Iwo anali ndi tsitsi lopotanapotana ndipo ankakonda kulipesa moligwetsera pamphumi. Tsiku lina anatukula tsitsilo pamphumipo n’kundisonyeza chipsera chachikulu chimene anakhala nacho chifukwa chomenyedwa ndi munthu panthaŵi ya chizunzo. Zinandikhudza kwambiri kuona ndekha nkhanza zimene abale ndi alongo athu anakumana nazo.
Kupatulapo pa Beteli, malo amene amandisangalatsa kwambiri ndi ku Hawaii. Ndimakumbukira msonkhano umene unachitikira kumeneku mumzinda wa Hilo mu 1957. Unali msonkhano waukulu kwambiri, ndipo panabwera anthu ambiri kuposa Mboni za Yehova zonse kumeneko. Meya wa mzindawu mpaka anapatsa Nathan ufulu wapadera wopita malo alionse amene angakonde kupitako mumzindawo. Anthu ambiri anabwera kudzatipatsa moni n’kumativeka maluŵa.
Msonkhano winanso wosangalatsa unali wa ku Nuremberg, Germany, mu 1955, womwe unachitikira m’bwalo limene Hitler ankaligwiritsira ntchito monga pogubira asilikali. N’zodziŵika kwambiri kuti Hitler analumbira kuti adzamaliza anthu onse a Yehova ku Germany, komano ingoganizirani kuti panthaŵiyi bwaloli linadzaza thothotho ndi Mboni za Yehova! Ndinalephera kudziletsa kuti ndisalire. Pulatifomu yake inali yaikulu kwambiri ndipo kupulatifomuko kunali mizati yokongoletsera yokwana 144. Ineyo ndinakhala kupulatifomuko ndipo ndinkatha kuona chikhwimbi cha anthu oposa 107,000 opezeka pamsonkhanopo. Mzere womalizira unali kutali kwambiri moti zinali zovuta kuti ndione bwinobwino kumeneko.
Tinkatha kuona kukhulupirika kwa abale athu a ku Germany ndiponso mmene Yehova anawalimbikitsira panthaŵi ya chizunzo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi. Zinatilimbikitsa kuti nafenso tipitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova. Nathan anakamba nkhani yotsiriza, ndipo pamapeto pake anakweza manja potsanzika anthu onse pamsonkhanopo. Nthaŵi yomweyo iwonso anakweza manja awo m’mwamba n’kumakupiza tinsalu topukutira thukuta potifunira ulendo wabwino. Zimangooneka ngati munda wokongola wa maluŵa.
Ulendo umene tinapita ku Portugal m’mwezi wa December, mu 1974 unalinso wosaiwalika. Tinapezeka pamsonkhano woyamba wa Mboni mumzinda wa Lisbon ntchito yathu yolalikira itavomerezedwa mwalamulo m’dzikoli. Inali italetsedwa kwa zaka zokwana 50! Ngakhale kuti panthaŵiyi m’dzikomo munali ofalitsa Ufumu 14,000 okha, pamisonkhano iŵiri imene inachitika kumeneko panapezeka anthu opitirira 46,000. Ndinatuluka misozi abale atanena kuti: “Palibenso chifukwa chobisalira. Tsopano ndife omasuka.”
Kuchokera panthaŵi imene ndinali kuyenda ndi Nathan mpaka kufika panopo, ndakhala ndikusangalala pochita ulaliki wamwamwayi m’ndege, m’malesitilanti ndiponso polalikira m’misewu. Nthaŵi zonse ndimatenga mabuku kuti ndizikhala wokonzeka kulalikira. Tsiku lina tikudikirira ndege imene inali itachedwa, mayi wina anandifunsa kuti ndimuuze kumene ndimagwira ntchito. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kucheza naye ndiponso kucheza ndi anthu ena amene ankamvetsera. Utumiki wa pa Beteli ndiponso ntchito yolalikira zandichititsa kuti ndisamasoŵe chochita nthaŵi zonse ndiponso kuti ndizisangalala.
Kudwala Kwake Ndiponso Mawu Ake Olimbikitsa Onditsanzikira
Mu 1976, Nathan anadwala matenda a kansa, ndipo ineyo, pamodzi ndi anthu ogwira ntchito pa Beteli, tinamuthandiza pa matendawo. Ngakhale kuti sankapeza bwino, tinkaitana anthu osiyanasiyana ochokera m’maofesi a nthambi padziko lonse omwe anali kudzaphunzira ku Brooklyn kuti abwere adzacheze nafe kuchipinda kwathu. Ndikukumbukira kuti tinaitanapo Don ndi Earline Steele, Lloyd ndi Melba Barry, Douglas ndi Mary Guest, Martin ndi Gertrud Poetzinger, Price Hughes, ndi enanso ambiri. Nthaŵi zambiri iwo ankatiuza nkhani zina zochokera m’mayiko awo. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri ndi nkhani zokhudza kusagonja kwa abale athu ngakhale panthaŵi imene ankaletsedwa.
Nathan atazindikira kuti watsala pang’ono kumwalira, anandipatsa malangizo abwino ondithandiza kuti ndisavutike kwambiri ndi umasiye. Iye anati: “Banja lathu linali losangalatsa. Anthu ambiri sakhala ndi mabanja otere.” Chinthu chimodzi chimene chinachititsa kuti banja lathu likhale losangalatsa chinali chakuti Nathan anali munthu wondiganizira. Mwachitsanzo, tikamakumana ndi anthu osiyanasiyana pamaulendo athuwo, iye ankandiuza kuti: “Audrey, nthaŵi zina ndikapanda kukudziŵitsa anthu enaake amene takumana nawo, uzingodziŵa kuti ndaiwala dzina lawo.” Ndipotu ankachita bwino kundiuziratu zimenezi.
Nathan anandiuza kuti: “Tikamwalira, chiyembekezo chathu sichikhalanso chokayikitsa, ndipo zikatere ndiye kuti sitidzamvanso ululu ayi.” Kenaka anandilimbikitsa kuti: “Uziganizira za m’tsogolo chifukwa mphoto yako ili m’tsogolo. Usamangoganizira za m’mbuyo ngakhale kuti sungalephere kuzikumbukira. M’kupita kwa nthaŵi udzaziiwala. Osamaipidwa nazo ndiponso osadzimvera chisoni. Uzingosangalala kuti unapeza chimwemwe ndiponso madalitso onseŵa. M’kupita kwa nthaŵi udzaona kuti ukamakumbukira za m’mbuyo uzidzasangalala nazo. Kukumbukira za m’mbuyo ndi mphatso yathu yochokera kwa Mulungu.” Ndiye anawonjezera kuti: “Uzionetsetsa kuti uli ndi chochita nthaŵi zonse, uziyesetsa kugwiritsira ntchito moyo wako kuthandiza anthu ena. Zimenezi zidzakuthandiza kusangalala ndi moyo.” M’kupita kwa nthaŵi, pa June 8, 1977, Nathan anasiyana nalo dziko lapansi lino.
Kukwatiwa ndi Glenn Hyde
Nathan anandiuza kuti ngati ndikufuna, ndingathe kumangoganizira za m’mbuyo kapena ndingathe kuyamba kukhala moyo wina watsopano. Motero, mu 1978, nditasamukira ku Watchtower Farms ku Wallkill, m’boma la New York, ndinakwatiwa ndi Glenn Hyde, mwamuna wooneka bwino kwambiri, wofatsa ndiponso wamtima wabwino. Asanakhale wa Mboni, anali m’gulu la asilikali a nkhondo ya pamadzi panthaŵi imene dziko la United States limamenyana ndi dziko la Japan.
Glenn ankagwira ntchito mu boti loponya mabomba ndipo ankakhala mmene munali injini. Chifukwa cha phokoso la injiniyo iye anakhala ndi vuto la kusamva bwinobwino. Nkhondoyo itatha, anayamba ntchito yozimitsa moto. Kwa zaka zambiri, ankadzidzimukadzidzimuka kutulo chifukwa cha zimene anaona kunkhondo kuja. Iye anadziŵa choonadi cha m’Baibulo kuchokera kwa mlembi wake kuntchito, yemwe ankamulalikira mwamwayi.
Pambuyo pake, mu 1968, Glenn anaitanidwa ku Beteli kuti azikaona zozimitsa moto ku Brooklyn. Kenaka ku Watchtower Farms atagula galimoto zozimitsira moto, iye anamutumiza kumeneko mu 1975. Patapita nthaŵi, anadwala matenda a Alzheimer. Glenn anamwalira titakwatirana kwa zaka teni.
Kodi ndikanatani kuti ndilimbe mtima? Nzeru zimene Nathan anandipatsa pamene ankamwalira zinandilimbikitsanso pamenepa. Ndinapitirizabe kuŵerenga zimene anandilembera zokhudza mmene ndingalimbire mtima paumasiye. Mpaka pano zimenezi ndimauzako anthu ena amene mwamuna kapena mkazi wawo wamwalira, ndipo nawonso alimbikitsidwa ndi malangizo a Nathan. Inde, ndi bwino kuganizira za m’tsogolo monga mmene anandilimbikitsira.
Ubale Wamtengo Wapatali
Chimene chandithandiza kwambiri kuti ndikhale wosangalala ndiponso wokhutitsidwa ndicho anzanga okondedwa a m’banja la Beteli. Mmodzi wa iwoŵa ndi Esther Lopez, amene anali m’kalasi yachitatu ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo yomwe inamaliza maphunziro ake mu 1944. Iyeyu anabwerera ku Brooklyn mu February 1950 kudzagwira ntchito yomasulira mabuku ophunzitsa Baibulo m’chinenero cha Chisipanya. Nthaŵi zambiri Nathan akachokapo, Esther ndiye ndinkacheza naye kwambiri. Nayenso akugwira ntchito ku Watchtower Farms. Panopo ali ndi zaka zopitirira 90, ndipo ndi wodwaladwala motero akumusamalira m’chipatala cha kunoko.
Pa anthu onse a m’banja mwathu, amene adakali moyo ndi Russel ndi Clara basi. Russel ali ndi zaka zopitirira 90 ndipo akutumikirabe mokhulupirika pa Beteli ya ku Brooklyn. Anali m’gulu la anthu oyamba kuloledwa kukhalabe pa Beteli atakwatira. Mu 1952, anakwatira mnzake wotumikira pa Beteli dzina lake Jean Larson. Mlongo wake wa Jean, dzina lake Max anabwera ku Beteli mu 1939 ndipo mu 1942 analoŵa m’malo mwa Nathan pa ntchito yoyang’anira zosindikiza mabuku. Max adakali ndi maudindo ambirimbiri pa Beteli, kuphatikiza pa udindo wosamalira mkazi wake wokondedwa, Helen, amene amadwala matenda opha ziwalo otchedwa multiple sclerosis.
Kunena zoona, ndikaganizira zaka zopitirira 63 zimene ndakhala ndikutumikira Yehova kwa nthaŵi zonse, ndimaona kuti moyo wanga wakhala wosangalatsa kwambiri. Ku Beteli kunasanduka kwathu, ndipo ndikutumikirabe kunoko mosangalala. Ndikuthokoza makolo anga pondiphunzitsa kukhala munthu wazintchito ndiponso kukhala wofunitsitsa kutumikira Yehova. Koma chimene chimapangitsa moyo kukhala wosangalatsadi ndicho ubale wathu wachikondi ndiponso chiyembekezo chodzakhala ndi abale komanso alongo athu m’dziko lapansi la paradaiso, n’kumatumikira kosatha Mlengi wathu Wamkulu, yemwe ali Mulungu woona yekha, Yehova.
[Chithunzi patsamba 24]
Tsiku limene makolo anga anakwatirana mu June 1912
[Chithunzi patsamba 24]
Kuchokera kumanzere kupita kumanja: Russell, Wayne, Clara, Ardis, ineyo, ndi Curtis mu 1927
[Chithunzi patsamba 25]
Ndaima pakati pa Frances ndi Barbara McNaught, ndili mpainiya mu 1944
[Chithunzi patsamba 25]
Ndili ku Beteli mu 1951. Kuchokera kumanzere kupita kumanja: Ineyo, Esther Lopez, ndi mulamu wanga, Jean
[Chithunzi patsamba 26]
Ndili ndi Nathan pamodzi ndi makolo ake
[Chithunzi patsamba 26]
Ndili ndi Nathan mu 1955
[Chithunzi patsamba 27]
Ndili ndi Nathan ku Hawaii
[Chithunzi patsamba 29]
Ndili ndi mwamuna wanga wachiŵiri, Glenn