Baibulo Limasintha Anthu
KODI n’chiyani chinachititsa kuti munthu wina yemwe anakwatira mitala komanso ankadana kwambiri ndi Mboni za Yehova akhale wa Mboni? Nanga zinatheka bwanji kuti m’busa wina wa tchalitchi cha Pentekosite asiye chipembedzo chake? Komanso kodi n’chiyani chinathandiza mayi amene sanaleredwe bwino kuthana ndi vuto lake lodziona kuti ndi wosafunika, n’kukhala bwenzi la Mulungu? Nanga n’chiyani chinachititsa munthu wina wokonda kumvera nyimbo zaphokoso komanso zachiwawa kusintha n’kukhala wa Mboni za Yehova? Werengani nkhani zotsatirazi kuti mumve mayankho a mafunso amenewa.
“Panopa ndine mwamuna wabwino kusiyana ndi kale.”—RIGOBERT HOUETO
CHAKA CHOBADWA: 1941
DZIKO: BENIN
POYAMBA: NDINAKWATIRA MITALA KOMANSO NDINKADANA KWAMBIRI NDI MBONI ZA YEHOVA
KALE LANGA:
Kwathu ndi ku Cotonou, mzinda waukulu womwe uli m’dziko la Benin. Ndinakulira m’banja lachikatolika koma nthawi zambiri sindinkapita kutchalitchi. Akatolika ambiri akudera limene tinkakhala, ankakwatira akazi ambiri popeza pa nthawiyo zinali zololeka kukwatira mitala. Choncho inenso nditakula ndinakwatira akazi anayi.
M’ma 1970, pamene anthu anaukira boma n’cholinga chofuna kusintha zinthu, ndinaganiza kuti zimenezi zithandiza dziko lathu. Choncho ndinayamba ndale ndipo ndinathandiza anthu oukirawo ndi mtima wonse. Anthu amene ankafuna kusintha zinthuwo ankadana ndi a Mboni za Yehova chifukwa a Mboniwo sankasapota gulu lililonse landale. Ineyo ndinali mmodzi mwa anthu amene ankazunza a Mboni. M’chaka cha 1976 pamene amishonale a Mboni anathamangitsidwa m’dziko la Benin, ndinkakhulupirira kuti anthu amenewa sadzabweranso m’dzikoli.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:
Mavuto azandale atatha m’chaka cha 1990, ndinadabwa kwambiri kuona kuti nthawi yomweyo amishonale a Mboni abweranso m’dzikoli. Moti ndinayamba kuganiza kuti mwina anthu amenewa akutsogoleredwadi ndi Mulungu. Cha nthawi yomweyi, ndinasintha malo amene ndinkagwirira ntchito. Mmodzi mwa anthu amene ndinkagwira nawo ntchito anali wa Mboni ndipo ankatiuza zimene amakhulupirira. Anandisonyeza mavesi a m’Baibulo amene amafotokoza kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi ndiponso wachilungamo. (Deuteronomo 32:4; 1 Yohane 4:8) Ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti Mulungu ali ndi makhalidwe amenewa. Ndinkafuna kudziwa zambiri za Yehova choncho ndinavomera kuphunzira Baibulo.
Pasanapite nthawi ndinayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Ndinagoma kuona kuti anthu amenewa amasonyezana chikondi chenicheni ndipo sasankhana chifukwa chosiyana mitundu kapena chifukwa chakuti wina ndi wolemera kapenanso wosauka. Kupitiriza kusonkhana ndi a Mboni kunandithandiza kuzindikira kuti anthu amenewa ndi otsatira enieni a Yesu.—Yohane 13:35.
Ndinaona kuti ngati ndikufuna kutumikira Yehova, ndiyenera kusiya tchalitchi cha Katolika. Koma kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri chifukwa ndinkaopa kuti anthu aganiza chiyani akaona kuti ndasiya Chikatolika. Komabe patapita nthawi yaitali, komanso ndi thandizo la Yehova, ndinalimba mtima ndipo ndinatsanzika ku tchalitchi cha Katolika.
Koma panalinso chinthu china chachikulu chimene ndinafunika kusintha pa moyo wanga. Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kuzindikira kuti Mulungu salola mitala. (Genesis 2:18-24; Mateyu 19:4-6) Ndinazindikira kuti kwa Mulungu, mkazi wanga weniweni anali amene ndinayamba kumukwatira. Choncho, ndinalembetsa ukwati ndi mkazi wamkuluyo, ndipo enawo ndinawasiya koma ndinakonza njira yoti azipeza zinthu zofunika pa moyo. Patapita nthawi, awiri mwa azimayi amene anali akazi anga aja anakhala a Mboni za Yehova.
PHINDU LIMENE NDAPEZA:
Ngakhale kuti mkazi wanga adakali m’tchalitchi cha Katolika, amalemekeza chipembedzo changa. Panopa tonse timaona kuti tsopano ndine mwamuna wabwino.
Poyamba ndinkaganiza kuti ndingathe kusintha dera lathu pogwiritsa ntchito ndale koma ndinaona kuti zonse zimene ndinachita sizinaphule kanthu. Panopa ndikudziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto onse a anthu. (Mateyu 6:9, 10) Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chondiphunzitsa zoyenera kuchita kuti ndikhale ndi moyo wabwino komanso wosangalala.
“Zinali zovuta kuti ndisinthe.”—ALEX LEMOS SILVA
CHAKA CHOBADWA: 1977
DZIKO: BRAZIL
POYAMBA: NDINALI M’BUSA WA TCHALITCHI CHA PENTEKOSITE
KALE LANGA:
Ndinakulira m’tauni ina yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Itu, womwe uli m’chigawo cha São Paulo. Kudera limeneli kunkachitika zinthu zambiri zophwanya malamulo.
Ndinali wachiwawa kwambiri komanso ndinkachita chiwerewere. Ndinkachitanso malonda ozembetsa mankhwala osokoneza bongo. Koma patapita nthawi ndinazindikira kuti khalidwe limeneli likandifikitsa kundende kapena kumanda, choncho ndinasiya. Kenako ndinalowa tchalitchi cha Pentekosite ndipo patapita nthawi ndinakhala m’busa.
Ndinkaganiza kuti ndingathe kumathandiza anthu kudzera mu utumiki umene ndinkachita m’tchalitchichi. Ndinayambanso kumaulutsa mapologalamu achipembedzo pa wailesi ya kuderali ndipo zimenezi zinachititsa kuti nditchuke kwambiri. Koma patapita nthawi ndinazindikira kuti anthu a m’tchalitchichi sankasamala za anzawo komanso sankalemekeza Mulungu kwenikweni. Ndinayamba kuona kuti cholinga chachikulu cha tchalitchichi chinali kupeza ndalama basi choncho ndinaganiza zotuluka m’tchalitchi chimenechi.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:
Nditangoyamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova, nthawi yomweyo ndinaona kuti chipembedzo chawo ndi chosiyana ndi zipembedzo zina. Pali zinthu ziwiri zimene zinandichititsa chidwi. Choyamba, ndinaona kuti a Mboni za Yehova samangolankhula za chikondi koma amasonyezadi chikondicho kwa ena. Chachiwiri, iwo sachita nawo ndale kapena nkhondo. (Yesaya 2:4) Mfundo ziwiri zimenezi zinandichititsa kukhulupirira kuti ndapeza chipembedzo choona kapena kuti msewu wopanikiza wopita ku moyo wosatha.—Mateyu 7:13, 14.
Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kusangalatsa Mulungu, ndiyenera kusintha kwambiri zinthu pa moyo wanga. Ndinafunika kumasamalira kwambiri banja langa komanso kukhala wodzichepetsa. Kusintha zinthu ngati zimenezi pa moyo wanga kunali kovuta kwambiri koma Yehova anandithandiza mpaka ndinasinthadi. Mkazi wanga anadabwa kwambiri ataona kuti ndasintha. M’mbuyomo ine ndisanayambe kuphunzira Baibulo, iye anali atayamba kale kuphunzira. Koma ataona kuti ndasintha chonchi, anayamba kuphunzira moikirapo mtima. Pasanapite nthawi tonse tinaganiza zokhala a Mboni za Yehova ndipo tinabatizidwa tsiku limodzi.
PHINDU LIMENE NDAPEZA:
Ine ndi mkazi wanga tathandiza ana athu atatu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Panopa banja lathu ndi losangalala kwambiri. Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chondikoka kuti ndidziwe choonadi chopezeka m’Mawu ake, Baibulo. Baibulo limasinthadi anthu ndipo umboni wa zimenezi ndi ineyo.
“Ndikuona kuti ndine woyera komanso ndili ndi moyo waphindu.”—VICTORIA TONG
CHAKA CHOBADWA: 1957
DZIKO: AUSTRALIA
POYAMBA: NDINAKULA MOVUTIKA KWAMBIRI
KALE LANGA:
Ndinakulira mumzinda wa Newcastle ku New South Wales, m’banja la ana 7 ndipo ndine woyamba kubadwa. Bambo athu anali achiwawa komanso chidakwa. Mayi anga nawonso anali achiwawa ndipo ankakonda kundimenya komanso kundilankhula mawu oipa. Nthawi zambiri ankandiuza kuti ndine woipa ndipo ndidzakapsa kumoto. Zimenezi zinkandichititsa mantha kwambiri.
Nthawi zambiri mayi ankandivulaza moti mpaka ndinkalephera kupita kusukulu. Ndili ndi zaka 11, bungwe lina la boma linanditenga kuchoka m’manja mwa makolo anga n’kuyamba kundisunga pamalo ena ndipo kenako ndinayamba kusungidwa kunyumba ya masisitere. Koma nditakwanitsa zaka 14 ndinathawa pamalopa. Sindinkafuna kubwereranso kwathu, choncho ndinayamba kukhala m’misewu ya m’tauni ya Kings Cross, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Sydney.
Pa nthawi imeneyi ndinayamba kumwa mankhwala osokoneza bongo, mowa, kuonera zolaula komanso kuchita uhule. Koma zimene ndinakumana nazo tsiku lina zinandichititsa mantha kwambiri. Pa nthawiyi ndinkakhala kunyumba ya munthu wina yemwe anali ndi malo omwera mowa. Ndiyeno tsiku lina usiku azibambo awiri anabwera kudzaonana ndi munthuyu. Iye anandiuza kuti ndikakhale kuchipinda komabe ndinkamva chapansipansi zimene ankakambirana. Iye ankakonza zoti andigulitse kwa azibambo awiriwo. Ankafuna kuti andibise musitima yonyamula katundu ndipo apite nane ku Japan kuti ndizikagwira ntchito m’bala. Ndinachita mantha kwambiri ndipo ngakhale kuti ndinali m’chipinda chosanja, ndinatulukira pawindo n’kudumphira pansi n’kuthawa.
Ndinakumana ndi bambo wina amene anabwera mumzinda wa Sydney kudzacheza ndipo ndinamufotokozera mavuto anga poganiza kuti mwina andipatsa ndalama. Koma iye ananditengera kumalo amene ankakhala ndipo anandipatsa madzi osamba komanso chakudya. Ndinapitirizabe kukhala ndi bambo ameneyu ndipo patatha chaka chimodzi tinakwatirana.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:
Nditayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinkakhala ndi maganizo osiyanasiyana, ondisowetsa mtendere ndiponso ena ondilimbitsa mtima. Ndinakwiya kwambiri nditadziwa kuti Satana ndi amene amachititsa kuti padzikoli pazichitika zinthu zoipa. Poyamba ndinaphunzitsidwa kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti anthufe tizivutika. Komanso ndinasangalala nditaphunzira kuti Mulungu salanga anthu oipa mwa kuwaotcha pamoto. Chiphunzitso chimenechi chinkandichititsa mantha kuyambira kalekale.
Ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti a Mboni za Yehova akafuna kusankha zochita pa nkhani iliyonse, amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. Komanso iwo amachitadi zimene amakhulupirira. Ineyo ndinali munthu wovuta kwambiri, komabe kaya ndilankhule kapena kuchita zotani, a Mboni za Yehova ankachita nane zinthu mwachikondi komanso mwaulemu.
Vuto lalikulu limene ndinkalimbana nalo linali kudziona kuti ndine munthu wosafunika. Ndinkadziona kuti ndine munthu wachabechabe ndipo nditabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova, ndinapitirizabe kukhala ndi maganizo amenewa kwa nthawi yaitali. Ndinkadziwa kuti ndimakonda Yehova koma ndinkakhulupirira kuti n’zosatheka kuti iyeyo akonde munthu wa ngati ine.
Koma patatha zaka 15 kuchokera pamene ndinabatizidwa, zinthu zinasintha. Tsiku lina, m’bale wina akukamba nkhani m’Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, anawerenga lemba la Yakobo 1:23, 24. Lembali linayerekezera Mawu a Mulungu ndi galasi limene tingadziyang’anire n’kudziona mmene Yehova amationera. Ndinayamba kuganiza kuti mwina mmene ndinkadzionera si mmene Yehova ankandionera. Poyamba sindinavomereze mfundo imeneyi chifukwa ndinkaganizabe kuti n’zosatheka kuti mpaka Yehova andikonde.
Patapita masiku ochepa ndinawerenga lemba linanso limene linasintha moyo wanga. Lemba lake linali Yesaya 1:18, pamene pali mawu a Yehova akuti: “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine. Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.” Ndinamva ngati kuti Yehova akulankhula ndi ineyo kuti: “Tabwera Vicky, tiye tikambirane ndipo ndikuthandiza kuti ukhale pa ubwenzi wabwino ndi ine. Ndikukudziwa, ndikudziwa machimo ako, ndipo ndikudziwanso mtima wako. Komabe ndimakukonda.”
Usiku wa tsiku limeneli sindinagone. Ndinkakaikirabe zoti Yehova angandikonde koma ndinayamba kuganiza za nsembe ya dipo ya Yesu. Kenako ndinayamba kuganiza kuti Yehova wandilezera mtima kwa nthawi yaitali ndiponso wandisonyeza m’njira zambiri kuti amandikonda. Choncho ndinayamba kuona kuti zimene ndinkachitazo zinali ngati kumuuza Yehova kuti: “Chikondi chanu si chachikulu moti mpaka chingafike pa ine komanso nsembe ya Mwana wanu siingathe kugwira ntchito pa ine.” Zinali ngati Yehova wandipatsa dipo koma ineyo ndikulibwenzanso kwa iye chifukwa sindikulifuna. Koma kenako chifukwa choganizira mozama za mphatso ya dipo, ndinayamba kuona kuti Yehova amandikonda.
PHINDU LIMENE NDAPEZA:
Panopa ndikuona kuti ndine woyera komanso ndili ndi moyo waphindu. Ukwati wanga ukuyenda bwino ndipo ndikusangalala kuti ndikuthandiza ena pogwiritsa ntchito zimene ndakumana nazo pa moyo wanga. Panopa chikondi changa pa Yehova chikukula komanso ndikuona kuti amandikonda.
“Pemphero langa linayankhidwa.”—SERGEY BOTANKIN
CHAKA CHOBADWA: 1974
DZIKO: RUSSIA
POYAMBA: NDINKAKONDA NYIMBO ZAPHOKOSO KWAMBIRI KOMANSO ZACHIWAWA
KALE LANGA:
Ndinabadwira mumzinda wa Votkinsk komwenso ndi kwawo kwa woimba wina wotchuka dzina lake Pyotr Ilich Tchaikovsky. Banja lathu linali losauka. Bambo anga anali ndi makhalidwe abwino ambiri kungoti anali chidakwa ndipo zimenezi zinkabweretsa mavuto ambiri panyumba pathu.
Kusukulu sindinkakhoza bwino kwenikweni ndipo patapita nthawi ndinayamba kumadziona kuti ndine wolephera basi moti sindingachite zinthu bwino ngati mmene anthu ena amachitira. Ndinayamba kudzipatula ndipo sindinkakhulupirira munthu aliyense. Komanso sukulu ndinayamba kuiona ngati chintchito. Mwachitsanzo, akandiuza kuti ndifotokoze lipoti linalake, nthawi zambiri ndinkalephera kulongosola ngakhale zinthu zodziwika bwino zomwe ndinkatha kuzilongosola bwinobwino ndikakhala kuti sindili kusukulu. Pasukulu lipoti langa la giledi 8 anandilembera kuti: “Sadziwa mawu ambiri ndiponso satha kufotokoza mfundo momveka bwino.” Mawu amenewa anandifooketsa kwambiri ndipo anandiwonjezera kudziona kuti ndine wosafunika. Ndinayamba kukaikira kuti mwina moyo wanga ulibe phindu lililonse.
Ndili wachinyamata ndinayamba kumwa mowa. Pa nthawiyi ndinkamvako bwino ndikamwa mowa. Komabe ndikamwa kwambiri chikumbumtima changa chinkandivutitsa. Ndinayamba kuona kuti moyo wanga ndi wopanda phindu ndipo ndinkavutika maganizo moti nthawi zina ndinkatha masiku angapo ndikungokhala pakhomo. Kenako ndinayamba kuganiza zodzipha.
Nditakwanitsa zaka 20 ndinayamba kuona kuti zinthu zayambako kuyenda bwino koma zimenezi zinali zakanthawi. Ndinayamba kumamvetsera nyimbo zaphokoso kwambiri komanso zachiwawa. Ndinkaona kuti nyimbo zimenezi zikundithandiza kukhala wosangalala ndipo ndinayamba kufufuza anthu ena okonda nyimbo zimenezi. Ndinayamba kuweta tsitsi, ndinaboola makutu komanso ndinkavala ngati oimba amene ndinkawakonda. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuchita zinthu motayirira, ndinali wamwano ndipo sindinkati ndakangana liti ndi azibale anga.
Poyamba ndinkaganiza kuti kumvera nyimbo zimenezi kundithandiza kuti ndizikhala wosangalala, koma kunangowonjezera mavuto anga ndipo ndinali munthu wosasangalala. Komanso nditazindikira zinthu zoipa zimene oimba amene ndinkawakonda aja amachita, ndinaona kuti andigwiritsa mwala.
Apa maganizo ofuna kudzipha aja anandibwereranso ndipo pa nthawiyi ndinatsimikiza zodzipha. Koma ndinasintha maganizo nditaganizira mmene kuchita zimenezi kukanakhudzira mayi anga. Mayi anga ankandikonda kwambiri ndipo anali atandichitira zinthu zambiri. Mumtima mwanga ndinkavutika kwambiri, sindinkafuna kukhala ndi moyo komabe ndinkaonanso kuti sibwino kuti ndidziphe.
Pofuna kuti ndisamaganize kwambiri zodzipha, ndinayamba kuwerenga mabuku otchuka a ku Russia. Nkhani ina imene ndinawerenga inali yonena za munthu wina wotchuka amene ankatumikira patchalitchi. Zimenezi zinandichititsa kuyamba kulakalaka kuti ndizichita zinazake potumikira Mulungu ndiponso anthu. Ndinapemphera kwa Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo aka kanali koyamba kuti ndipemphere. Ndinamupempha Mulungu kuti andithandize kudziwa zimene ndingachite kuti moyo wanga ukhale waphindu ndiponso wosangalala. Pa nthawi imene ndinkapempherayo ndinamva bwino mumtima mwanga ndipo zimenezi zinandidabwitsa. Koma zimene zinachitika pambuyo pake ndi zimene zinandidabwitsa kwambiri. Patangotha maola awiri kuchokera nthawi imene ndinapempherayi, munthu wina wa Mboni za Yehova anagogoda pakhomo pathu ndipo anandipempha kuti ndiziphunzira naye Baibulo. Apa ndinangoona kuti pemphero langa lija layankhidwa. Tsiku limeneli ndi limene zinthu zinayamba kusintha pa moyo wanga kuti ndiyambe kukhala munthu wosangalala.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:
Ndinataya zinthu zonse zimene ndinali nazo zokhudza nyimbo zomwe ndinkakonda kumvera zija ngakhale kuti kuchita zimenezi sikunali kophweka. Komabe nyimbo zimenezi zinali zitakhazikika m’maganizo mwanga moti kwa nthawi yaitali ndinkazikumbukirabe. Ndinkati ndikamadutsa pamalo aliwonse pamene pankaimbidwa nyimbozi, ndinkakumbukira za moyo wanga wakale. Sindinafune kuti maganizo amenewa asokoneze zinthu zabwino zimene ndinkaphunzira pa nthawiyi. Choncho ndinkapewa kudutsa pamalo oterewa. Komanso ndikayamba kuganizira moyo wanga wakale, ndinkapemphera kuchokera pansi pa mtima kuti maganizo amenewa andichokere. Kuchita zimenezi kunkandithandiza kukhala ndi “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afilipi 4:7.
Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kudziwa kuti Akhristu ayenera kuuza ena zimene amakhulupirira. (Mateyu 28:19, 20) Koma ineyo ndinkaona kuti sindingathe kuchita zimenezo. Komabe zinthu zimene ndinkaphunzira zinkandithandiza kukhala wosangalala komanso kukhala ndi mtendere wamumtima. Ndinkaona kuti anthu ena afunikanso kuphunzira zinthu zimenezi. Choncho ngakhale kuti ndinali ndi mantha, ndinayamba kuuza ena zimene ndinkaphunzira. Ndinadabwa kuona kuti kuuza ena zimene Baibulo limaphunzitsa kunandithandiza kuyamba kudziona kuti ndine wofunika. Kuchita zimenezi kunkalimbitsanso chikhulupiriro changa.
PHINDU LIMENE NDAPEZA:
Panopa ndili ndi banja losangalala komanso ndathandiza anthu angapo kuphunzira Baibulo. Ena mwa anthu amenewa ndi mchemwali wanga komanso mayi anga. Kutumikira Mulungu komanso kuthandiza ena kuphunzira za iye kwachititsa kuti moyo wanga ukhale waphindu komanso wosangalala.