NYIMBO 32
Khalani Kumbali ya Yehova
1. Kalekale tinali mumdima,
Pokhala m’chipembedzo chabodza.
Koma pano tikusangalala
Tadziwa choonadi.
(KOLASI)
Khala kumbali ya Yehova M’lungu.
Ukamamumvera, sangakusiye.
Lengeza uthenga wamtenderewu.
Ulamuliro wa M’lungu sudzatha.
2. Timakhala ku mbali ya M’lungu
Polalikira kwa anthu onse
Kuti nawo azisankha okha
Kumvera M’lungu wathu.
(KOLASI)
Khala kumbali ya Yehova M’lungu.
Ukamamumvera, sangakusiye.
Lengeza uthenga wamtenderewu.
Ulamuliro wa M’lungu sudzatha.
3. Sitidzamuopa Mdyerekezi.
Tidzakhulupirira Yehova.
Kaya adani angachuluke,
M’lungu ndi mphamvu yathu.
(KOLASI)
Khala kumbali ya Yehova M’lungu.
Ukamamumvera, sangakusiye.
Lengeza uthenga wamtenderewu.
Ulamuliro wa M’lungu sudzatha.
(Onaninso Sal. 94:14; Miy. 3:5, 6; Aheb. 13:5.)