NYIMBO 33
Umutulire Yehova Nkhawa Zako
Losindikizidwa
1. Chonde ndimveni Yehova
musandinyalanyaze.
Ndikuvutika mumtima
chonde mundithandize.
(KOLASI)
Tulira Yehova nkhawa,
Iye sangakusiye wekha.
Akuteteza chifukwa ndi
wokhulupirika.
2. N’kanakhala ndi mapiko
ndikanaulukatu,
Kuti ndibisale
kwa ondichitira zoipa.
(KOLASI)
Tulira Yehova nkhawa,
Iye sangakusiye wekha.
Akuteteza chifukwa ndi
wokhulupirika.
3. M’lungu akatitonthoza
timapeza mtendere.
Amatithandiza kuti
tipirire mavuto.
(KOLASI)
Tulira Yehova nkhawa,
Iye sangakusiye wekha.
Akuteteza chifukwa ndi
wokhulupirika.
(Onaninso Sal. 22:5; 31:1-24.)