NYIMBO 7
Yehova Ndi Mphamvu Yathu
1. Yehova inu ndi mphamvu yathu.
Inu ndinu Mpulumutsi wathu.
Ndife Mboni za uthenga wanu,
Anthu amve kapena akane.
(KOLASI)
Yehova ndinu mphamvudi yathu.
Tilengezabe dzina lanu.
Yehova ndinu wamphamvuyonse,
M’lungu wathu ndinu thanthwe lathu.
2. Yehova mumatiwunikira
Ndipo taphunzira choonadi.
Malamulo anu tawadziwa.
Ife tasankha Ufumu wanu.
(KOLASI)
Yehova ndinu mphamvudi yathu.
Tilengezabe dzina lanu.
Yehova ndinu wamphamvuyonse,
M’lungu wathu ndinu thanthwe lathu.
3. Tizichita chifuniro chanu
Ngakhale Satana atizunze.
Tisafooke tithandizeni
Kukhala kumbali yanu M’lungu.
(KOLASI)
Yehova ndinu mphamvudi yathu.
Tilengezabe dzina lanu.
Yehova ndinu wamphamvuyonse,
M’lungu wathu ndinu thanthwe lathu.
(Onaninso 2 Sam. 22:3; Sal. 18:2; Yes. 43:12.)