KODI MUKUKUMBUKIRA?
Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
Kodi Akhristu ayenera kupemphera kwa Yesu Khristu?
Ayi. Yesu analimbikitsa anthu kuti azipemphera kwa Yehova, ndipo nayenso ankapemphera kwa Atate ake. (Mat. 6:6-9; Yoh. 11:41; 16:23) Akhristu oyambirira ankapempheranso kwa Mulungu osati kwa Yesu. (Mac. 4:24, 30; Akol. 1:3)—1/1, tsamba 14.
Fotokozani zinthu zina zimene tingachite pokonzekera Chikumbutso chaka chilichonse.
Tizitsatira ndandanda ya kuwerenga Baibulo pokonzekera Chikumbutso. Kuwonjezera nthawi yolalikira kungatithandizenso. Tiyeneranso kupemphera ndiponso kuganizira mofatsa chiyembekezo chathu.—1/15, tsamba 14-16.
Kodi maloto odabwitsa amene akaidi ena anauza Yosefe ankatanthauza chiyani?
Yosefe anauza woperekera chikho kwa Farao kuti maloto ake akutanthauza kuti adzabwezeretsedwa pa ntchito yake. Koma wophika mikate anamuuza kuti maloto ake akutanthauza kuti Farao adzauza anthu kuti amuphe n’kumupachika pamtengo. Zimene Yosefe ananenazi zinachitikadi. (Gen. 40:1-22)—2/1, tsamba 12-14.
Kodi abale a ku Japan analandira mphatso iti?
Analandira kabuku ka Uthenga wa Mateyu umene unatengedwa mu Baibulo la Dziko Latsopano. Kabukuka amakagawira mu utumiki ndipo anthu amene sadziwa zambiri zokhudza Baibulo akukakonda.—2/15, tsamba 3.
N’chiyani chinathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wabwino m’nthawi ya atumwi?
M’madera a ufumu wa Aroma munali mtendere. Akhristu ankagwiritsa ntchito misewu yabwino imene Aroma anamanga. Akhristu ankalalikira mosavuta chifukwa anthu ambiri m’madera a ufumu wa Aroma, ngakhale Ayuda, ankalankhula Chigiriki. Akhristu ankagwiritsa ntchito malamulo a Aroma kuti akhale ndi ufulu wolalikira.—2/15, tsamba 20-23.
N’chifukwa chiyani Akhristu enieni sakondwerera Isitala?
Yesu anauza otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake osati kuuka kwake. (Luka 22:19, 20)—3/1, tsamba 8.
N’chifukwa chiyani masiku ano mabuku athu safotokoza kwambiri kuti zinthu zosiyanasiyana zotchulidwa m’Baibulo zimaphiphiritsira zinazake?
Baibulo limanena kuti anthu ena ankaphiphiritsira anthu enaake kapena zinthu zinazake. Pali chitsanzo cha zimenezi pa Agalatiya 4:21-31. Koma si bwino kunena kuti zinthu zina zikuphiphiritsira zinazake ngati Baibulo silifotokoza. M’malomwake tingachite bwino kuona zimene tingaphunzire kwa anthu kapena zinthu zina za m’Baibulo. (Aroma 15:4)—3/15, tsamba 17-18.
Kodi chidutswa cha mpukutu chomwe anachipeza pamulu wa zinyalala ku Egypt ndi chofunika bwanji?
Pa zaka 100 zapitazi, akatswiri ena anapeza chidutswa cha mpukutu wa Uthenga Wabwino wa Yohane. N’kutheka kuti mpukutuwu unalembedwa zaka zochepa pambuyo poti Yohane analemba buku lake. Zimene zinalembedwa pa chidutswachi n’zofanana ndi zimene zili m’Baibulo lathu masiku ano ndipo zikutithandiza kukhulupirira kuti uthenga wa m’Baibulo sunasinthe.—4/1, tsamba 10-11.
Kodi kuchotsa munthu wosalapa kumasonyeza bwanji chikondi?
Baibulo limasonyeza kuti kuchotsa munthu wosalapa n’kofunika komanso kothandiza. (1 Akor. 5:11-13) Kumathandiza kuti dzina la Yehova lilemekezedwe, mpingo utetezedwe ndi kuyeretsedwa komanso kuti wolakwayo asinthe maganizo.—4/15, tsamba 29-30