Maulosi Amene Anakwaniritsidwa
M’nkhani yoyambirira tinaona kuti Kolosase anapusitsidwa ndi wansembe wina wa ku Delphi ndipo zimenezi zinachititsa kuti agonjetsedwe ndi mfumu ya ku Perisiya. Koma mosiyana ndi zimenezi, m’Baibulo muli ulosi wochititsa chidwi womwe unakwaniritsidwa ndendende wonena za mfumu ya ku Perisiyayo.
Kutatsala zaka pafupifupi 200 kuti Koresi abadwe, mneneri Yesaya ananeneratu kuti Koresiyo ndi amene adzagonjetse mzinda wa Babulo komanso ananena mmene adzaugonjetsere.
Yesaya 44:24, 27, 28: “Yehova, . . . wanena kuti, . . . ‘ndine amene ndikuuza madzi akuya kuti, “Iphwa ndipo mitsinje yako yonse ndidzaiumitsa.” Ndine amene ndikunena za Koresi kuti, “Iye ndi m’busa wanga ndipo adzakwaniritsa bwinobwino zonse zimene ndikufuna,” ngakhale zimene ndanena zokhudza Yerusalemu zakuti, “Adzamangidwanso,” ndi zokhudza kachisi zakuti, “Maziko ako adzamangidwa.”’”
Malinga ndi zimene ananena wolemba mbiri wina wachigiriki dzina lake Herodotus, asilikali a Koresi anapatutsa madzi a mumtsinje wa Firate womwe unkadutsa mozungulira mzinda wa Babulo. Zimenezi zinathandiza kuti asilikaliwo awoloke mosavuta n’kukalowa mumzindamo. Atalanda mzindawo, Koresi anamasula Ayuda omwe anali akapolo n’kuwalola kupita kwawo kuti akamange mzinda wa Yerusalemu womwe unawonongedwa zaka 70 zapitazo.
Yesaya 45:1: “Ine Yehova ndalankhula kwa wodzozedwa wanga. Ndalankhula kwa Koresi amene ndamugwira dzanja lake lamanja kuti ndigonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, kuti ndimasule m’chiuno mwa mafumu, kuti ndimutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri, moti ngakhale zipata sizidzatsekedwa.”
Asilikali a Koresi analowa kudzera pageti lalikulu la mzindawu, lomwe pazifukwa zosadziwika bwino linasiyidwa losatseka. Akanakhala kuti Ababulo ankadziwa zomwe Koresi ndi asilikali ake ankafuna kuchita, akanaonetsetsa kuti geti lililonse lomwe linali m’mbali mwa mtsinje latsekedwa. Koma iwo sankadziwa moti pa nthawiyi mzindawu unali wosatetezeka.
Umenewu ndi ulosi umodzi wokha mwa maulosi ambiri omwe amapezeka m’Baibulo ndipo anakwaniritsidwa ndendende.a Mosiyana ndi maulosi a anthu omwe amati amachokera kwa milungu yawo yomwe ndi yonyenga, maulosi a m’Baibulo amachokera kwa Mulungu yemwe ananena kuti: “Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.”—Yesaya 46:10.
Mulungu woona yekha, yemwe dzina lake ndi Yehova ndi amene angachite zimenezi. Dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Amachititsa Zinthu Kuchitika.” Tanthauzoli likusonyeza kuti iye ali ndi mphamvu yotha kudziwa komanso kukonza kuti zinthu zichitike mogwirizana ndi chifuniro chake. Ndipo izi zimatitsimikizira kuti zonse zimene walonjeza kuti adzachita m’tsogolomu, zidzachitikadi.
MAULOSI AMENE AKUKWANIRITSIDWA MASIKU ANO
Kodi mukufuna mutadziwa ena mwa maulosi amene akukwaniritsidwa m’masiku athu ano? Zaka zoposa 2,000 zapitazo Baibulo linaneneratu kuti “masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.” Awatu si masiku otsiriza a dziko lapansili kapenanso mtundu wa anthu, koma ndi mapeto a nkhondo, nkhanza, komanso mavuto omwe akhala akuvutitsa anthu kwa zaka zambiri. Tiyeni tione maulosi angapo omwe akusonyeza kuti tili ‘m’masiku otsiriza.’
2 Timoteyo 3:1-5: ‘M’masiku otsiriza . . . anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.’
Kodi simukuvomereza kuti makhalidwe amenewa ndi omwe anthu ambiri akusonyezadi masiku ano? Kodi inunso mumaona kuti anthu ambiri ndi odzikonda, okonda ndalama komanso onyada? Kodi mumaona kuti anthu ambiri amangomva zawo zokha ndipo amafuna kuti anthu azingoyendera maganizo awo basi? N’zosachita kufunsa kuti mumaonanso ana ambiri omwe samvera makolo awo komanso anthu ambiri amene amakonda zosangalatsa kuposa Mulungu. Ndipotu zinthu zikuipiraipira tsiku ndi tsiku.
Mateyu 24:6, 7: “Mudzamva phokoso la nkhondo ndi mbiri za nkhondo. . . . Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.”
Kafukufuku amasonyeza kuti chiwerengero cha anthu amene anafa pa nkhondo komanso zachiwawa kuchokera mu 1914 ndi choposa 100 miliyoni. Chiwerengerochi n’choposa cha anthu omwe ali m’mayiko ambiri. Ndiye taganizirani mavuto, chisoni, ndi misozi yomwe inabwera chifukwa cha imfa ya anthu ochuluka chonchi. Kodi mayiko aphunzirapo kanthu n’kuthetsa nkhondo?
Mateyu 24:7: “Kudzakhala njala.”
Nthambi ya World Food Programme inanena kuti: “Dzikoli limatulutsa chakudya chomwe chikhoza kukwanira anthu onse padzikoli, koma anthu 815 miliyoni, kapena kuti munthu mmodzi pa 9 alionse padziko lonse, amagona ndi njala. Kuonjezera apo munthu mmodzi pa atatu alionse amadwala matenda osowa zakudya m’thupi.” Kafukufuku akusonyeza kuti ana pafupifupi 3 miliyoni amamwalira chaka chilichonse chifukwa cha njala.
Luka 21:11: “Kudzachitika zivomezi zamphamvu.”
Chaka chilichonse, padzikoli pamachitika zivomezi pafupifupi 50,000. Zivomezi 100 mwa zivomezi zimenezi zimakhala zowononga kwambiri moti zimatha kugwetsa nyumba ndipo chaka chilichonse pamachitika chivomezi chimodzi champhamvu kwambiri. Malinga ndi kafukufuku wina, kuchokera mu 1975 kudzafika mu 2000, zivomezi zinapha anthu 471,000.
Mateyu 24:14: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”
A Mboni za Yehova, omwe alipo oposa 8 miliyoni, akhala akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse m’mayiko pafupifupi 240. Iwo amalalikira uthenga wabwino m’mizinda ikuluikulu, m’midzi yakutali kwambiri komanso m’madera ena ovuta kufikako. Mulungu akadzaona kuti uthengawu walalikidwa mokwanira, ulosiwu umanena kuti: “Kenako mapeto adzafika.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti maboma onse a anthu adzathetsedwa ndipo Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira. Kodi ndi malonjezo ati omwe adzakwaniritsidwe Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira? Werengani nkhani yotsatira kuti mumve yankho la funso limeneli.
a Werengani nkhani yakuti “Chipilala Chomwe Chimasonyeza Kuti Maulosi a M’Baibulo Ndi Olondola.”