NKHANI 50
Akazi Awiri Olimba Mtima
POLOWA m’bvuto Aisrayeli, akupfuulira kwa Yehova. Yehova akuwayankha mwa kuwapatsa atsogoleri olimba mtima kuwathandiza. Baibulo limacha atsogoleri amene’wa Oweruza. Yoswa anali woweruza woyamba, ndipo oweruza ena om’tsatira anali Otiniyeli, Ehudi ndi Samagara. Koma anthu awiri amene anathandiza Israyeli ndiwo akazi Debora ndi Yaeli.
Debora ndiye mneneri wachikazi. Yehova akum’patsa chidziwitso cha za m’tsogolo, ndiyeno iye akuuza anthu zimene Yehova wanena. Debora ali’nso woweruza. Iye akukhala pansi pa mgwalangwa m’dziko la mapiri, ndipo anthu akudza kwa iye kudzathandizidwa zobvuta zao.
Pa nthawi’yi Yabini ndiye mfumu ya Kanani. Iye ali ndi magaleta ankhondo 900. Gulu lake lankhondo n’lamphamvu kwambiri kwakuti Aisrayeli ambiri akakamizika kukhala atumiki a Yabini. Mkulu wa gulu lankhondo la Mfumu Yabini ndiye Sisera.
Tsiku lina Debora akutumiza mthenga kwa Woweruza Baraki, namuuza kuti: ‘Yehova wati: “Tenga amuna 10,000 ndi kumka nawo ku Phiri la Tabori. Kumene’ko ndidzakupatsa Sisera. Ndipo ndidzakupatsani chipambano pa iye ndi ankhondo ake.”’
Baraki akuuza Debora kuti: ‘Ndidzapita ngati mumka nane.’ Debora akumka nawo, koma akuti kwa Baraki: ‘Usadzitamandira pa chipambano’chi, pakuti Yehova adzapereka Sisera m’dzanja la mkazi.’ Ndipo izi ndizo zimene zikuchitika.
Baraki akutsika ku Phiri la Tabori kukakumana ndi ankhondo a Sisera. Mwadzidzidzi Yehova akuchititsa liyambwe, ndipo ankhondo ambiri a mdani akumizidwa. Koma Sisera sakutsika pa gareta wake nathamanga.
Patapita kanthawi Sisera akufika pa hema wa Yaeli. Akum’lowetsa, nam’patsa mkaka. Uwo ukum’gonetsa tulo, ndipo m’kanthawi wagona tulo tatikulu. Ndiyeno Yaeli akutenga chikhomo cha hema n’kuchikhomera m’mutu wa munthu woipa’yu. Pambuyo pake, Baraki akudza, iye akum’sonyeza Sisera wakufa’yo! Chotero mungaone kuti zimene Debora ananena zinakwaniritsidwa.
Potsiriza naye’nso Mfumu Yabini akuphedwa, ndipo Aisrayeli ali ndi mtendere kwa kanthawi.