Mboni za Yehova
Tanthauzo: Gulu Lachikristu la padziko lonse lapansi la anthu amene amachita umboni mokangalika ponena za Yehova Mulungu ndi zifuno zake zophatikizapo anthu. Amazika zikhulupiriro zawo pa Baibulo lokha.
Kodi ndizikhulupiriro ziti za Mboni za Yehova zimene zimazipangitsa kukhala zosiyana ndi zipembedzo zina?
(1) Baibulo: Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Baibulo lathunthu ndilo Mawu ouziridwa a Mulungu, ndipo mmalo mwa kumamatira ku chikhulupiriro chozikidwa pamwambo wa anthu, zimamamatira ku Baibulo monga muyezo wa zikhulupiriro zawo zonse.
(2) Mulungu: Zimalambira Yehova monga Mulungu wowona yekha ndipo zimalankhula momasuka kwa ena ponena za iye ndi zifuno zake zachikondi kulinga kwa anthu. Kaŵirikaŵiri munthu aliyense amene amachitira umboni poyera ponena za Yehova amadziŵikitsidwa kukhala wa kagulu kamodzi kameneko—“Mboni za Yehova.”
(3) Yesu Kristu: Zimakhulupirira, osati kuti Yesu Kristu ali mbali ya Utatu, koma kuti, monga momwe Baibulo limanenera, iye ali Mwana wa Mulungu, wachisamba wa zolengedwa za Mulungu; kuti iye anakhalako asanakhale munthu ndi kuti moyo wake unasamutsidwa kuchokera kumwamba kumka m’mimba ya namwali Mariya; kuti moyo wake waumunthu wangwiro woperekedwa nsembe umatheketsa chipulumutso kumka kumoyo wamuyaya kwa osonyeza chikhulupiriro; kuti Kristu akulamulira monga Mfumu, mwaulamuliro woperekedwa ndi Mulungu padziko lonse lapansi kuyambira 1914.
(4) Ufumu wa Mulungu: Zimakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu; kuti uwo uli boma lenileni; kuti posachedwa udzawononga dongosolo loipa liripoli la zinthu, kuphatikizapo maboma onse a anthu, ndi kuti udzadzetsa dongosolo latsopano mmene mudzakhala chilungamo chochuluka.
(5) Moyo wakumwamba: Zimakhulupirira kuti Akristu odzozedwa ndi mzimu 144 000 adzakhala ndi phande limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba, kulamulira monga mafumu limodzi naye. Izo sizimakhulupirira kuti kumwamba ndiko mphotho ya munthu aliyense “wabwino.”
(6) Dziko lapansi: Zimakhulupirira kuti chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi chidzakwaniritsidwa; kuti dziko lapansi lidzakhalidwa kotheratu ndi olambira Yehova ndi kuti amenewa adzakhoza kusangalala nawo moyo wamuyaya mu ungwiro waumunthu; kuti ngakhale akufa adzaukitsidwira mwaŵi wa kukhala ndi phande m’madalitso amenewa.
(7) Imfa: Zimakhulupirira kuti akufa sadziŵa kanthu bii; kuti iwo sakumva ululu kapena chikondwerero m’dziko la mizimu; kuti iwo kulibeko kusiyapo kuti ali m’chikumbukiro cha Mulungu, chotero chiyembekezo cha moyo wawo wamtsogolo chiri m’chiukiriro cha akufa.
(8) Masiku otsiriza: Zimakhulupirira kuti ife tsopano tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo loipa lino la zinthu, kuyambira 1914; kuti ena amene anawona zochitika za 1914 adzawonanso chiwonongeko chotheratu cha dziko loipa liripoli; kuti okonda chilungamo adzapulumuka kuloŵa m’dziko lapansi loyeretsedwa.
(9) Kulekanitsidwa ndi dziko: Zimayesayesa kwambiri kusakhala mbali ya dziko, monga momwe Yesu ananenera kuti zikatero kwa otsatira ake owona. Zimasonyeza chikondi chenicheni Chachikristu kwa anansi awo, koma sizimakhala ndi phande m’ndale zadziko kapena nkhondo za dziko lirilonse. Zimagaŵira zosoŵa zakuthupi za mabanja awo koma zimakaniza kulondola mwaphamphu zinthu zakuthupi za dzikoli ndi mbiri ya iwo eni limodzi ndi kuphatikizidwa kwake kopambanitsa m’chikondwerero.
(10) Kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo: Zimakhulupirira kuti kuli kofunika kugwiritsira ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu m’moyo wa tsiku ndi tsiku tsopano—panyumba, m’sukulu, m’bizinesi, mumpingo wawo. Mosasamala kanthu za njira ya moyo ya papitapo ya munthuyo, angakhale mmodzi wa Mboni za Yehova ngati asiya zizoloŵezi zotsutsidwa ndi Mawu a Mulungu nagwiritsira ntchito uphungu wake waumulungu. Koma ngati pambuyo pake aliyense akhala ndi chizoloŵezi cha kuchita chigololo, dama lachigololo, kugonana kwa aziŵalo zofanana, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa maganizo, uchidakwa, kunama, kapena kuba, iye adzachotsedwa m’gulu.
(Ndandanda yapamwambapayi imafotokoza mwachidule zina za zikhulupiriro zapadera za Mboni za Yehova koma mwanjira iriyonse siziri mfundo zonse pa zimene zikhulupiriro zawo zimasiyana ndi za magulu ena. Maziko Amalemba a zikhulupiriro zapamwambapazi angapezedwe mwa Zosonyezera za bukhu lino.)
Kodi Mboni za Yehova nchipembedzo cha ku Amereka?
Ndizo ochirikiza Ufumu wa Mulungu, osati wa dongosolo la ndale za dziko, la zachuma kapena la makhalidwe a anthu a mtundu uliwonse wa dziko lino lakale.
Nzowona kuti chiyambi cha Mboni za Yehova zamakono chinali mu United States. Kukhala kwawo ndi malikulu a dziko lonse kumeneko kwathandizira kupangitsa kukhala kotheka kusindikiza ndi kutumiza mabukhu a Baibulo m’mbali zambiri za dziko lapansi. Koma Mboni sizimayanja mtundu umodzi kuposa wina; zimapezedwa pafupifupi mu mtundu uli wonse, ndipo ziri ndi maofesi m’mbali zochuluka za dziko lapansi kuyang’anira ntchito yawo m’zigawo zimenezo.
Talingalirani: Yesu monga Myuda anabadwira m’Palestina, koma Chikristu sichiri chipembedzo cha ku Palestina, eti? Malo obadwirako Yesu monga munthu sali chinthu chamtengo wapatali koposa chochilingalira. Magwero a zimene Yesu anaphunzitsa zinachokera kwa Atate ŵake, Yehova Mulungu, amene alibe tsankhu ndi anthu a mitundu yonse.—Yoh. 14:10; Mac. 10:34, 35.
Kodi ndimotani mmene ntchito ya Mboni za Yehova imalipiridwira?
Mwazopereka zodzifunira, monga momwe zinaliri kwa Akristu oyambirira. (2 Akor. 8:12; 9:7) Mbale za zopereka sizimayendetsedwa konse pamisonkhano yawo; sizipempha ndalama kwa anthu. Zopereka zaufulu zilizonse zochokera kwa anthu amene akufuna zimagwiritsidwa ntchito kuthandiza pantchito ya padziko lonse ya maphunziro a Baibulo imene Mbonizo zimachita.
Mboni sizimalipidwa kuti zipite kunyumba ndi nyumba kapena kugaŵira mabukhu a Baibulo m’makwalala. Kukonda kwawo Mulungu ndi mnansi kumawasonkhezera kulankhula za makonzedwe achikondi a Mulungu kwa anthu.
Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, gulu la chipembedzo la lamulo limene limagwiritsiridwa ntchito ndi Mboni za Yehova, linapangidwa mu 1884 mogwirizana ndi lotchedwa Nonprofit Corporation Law of the Commonwealth of Pennsylvania, U.S.A. Chotero, mwalamulo silingakhoze kukhala, ndipo siliri, gulu lopanga phindu, ndiponso anthu ali onse paokha samapanga phindu kupyolera mwa Sosaite imeneyi. Tchata cha Sosaite chimafotokoza kuti: “Iyo [Sosaite] siimalinganiza kupeza geni kapena phindu la ndalama, mwa mwaŵi kapena mwa njira ina, kumamembala ake kapena atsogoleri kapena adindo.”
Kodi Mboni za Yehova ndizo kagulu ka mpatuko kapena kagulu kopanda mwambo?
Ena amatanthauzira mpatuko kukhala kagulu kamene kakhadzuka m’chipembedzo chokhazikitsidwa. Ena amagwiritsira ntchito liwulo ku kagulu kamene kamatsatira mtsogoleri wina waumunthu kapena mphunzitsi. Kaŵirikaŵiri liwulo limagwiritsiridwa ntchito monyoza. Mboni za Yehova siziri mphukira ya tchalitchi chirichonse koma zaphatikizapo anthu ochokera kumbali zonse za moyo ndi mikhalidwe ya zipembedzo zambiri. Izo sizimayang’ana kwa munthu aliyense, monga mtsogoleri wawo, mmalo mwake zimayang’ana kwa Yesu Kristu.
Kagulu kopanda mwambo ndiko chipembedzo chimene chimanenedwa kukhala mwambo kapena chimene chimagogomezera kudzipereka kogwirizana ndi dzoma lofotokozedwa. Zipembedzo zambiri zopanda mwambo zimatsatira mtsogoleri waumuthu wamoyo, ndipo kaŵirikaŵiri mamembala awo amakhala m’timagulu tolekanitsidwa ndi anthu onse. Komabe, muyeso wa chimene chiri kusunga mwambo, uyenera kukhala Mawu a Mulungu, ndipo Mboni za Yehova zimamamatira kotheratu ku Baibulo. Kulambira kwawo ndiko njira ya moyo, osati kudzipereka kwadzoma. Izo sizimatsatira munthu ndiponso sizimadzilekanitsa ndi anthu onse. Zimakhala ndi kugwira ntchito pakati pa anthu ena.
Kodi chipembedzo cha Mboni za Yehova nchakale motani?
Mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, mzera wa Mboni za Yehova umabwerera mmbuyo kwa Abele wokhulupirika. Ahebri 11:4–12:1 amati: “Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini . . . Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha . . . Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kumka kumalo amene adzalandira ngati choloŵa . . . Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao; nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi . . . Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni titaye cholemetsa chiri chonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo amene adatiikira.”
Ponena za Yesu, Baibulo limafotokoza kuti: “Izi anena Amenyo, mboni yokhulupirika ndi yowona, woyamba wa chilengo cha Mulungu.” Kodi iye anali mboni ya yani? Iye mwiniyo ananena kuti anadziŵikitsa dzina la Atate ŵake. Iye anali mboni ya Yehova yaikulu koposa.—Chiv. 3:14; Yoh. 17:6.
Mokondweretsa, ena a Ayuda anafunsa ngati ntchito ya Yesu Kristu inaimira “chiphunzitso chatsopano.” (Marko 1:27) Pambuyo pake, Agiriki ena analingalira kuti mtumwi Paulo anali kuyambitsa “chiphunzitso chatsopano.” (Mac. 17:19, 20) Chinali chatsopano m’makutu mwa awo amene anali kuchimva, koma chinthu chofunika chinali chakuti icho chinali chowonadi, chogwirizana ndi Mawu a Mulungu.
Mbiri yamakono ya Mboni za Yehova inayamba mwa kupangidwa kwa kagulu kophunzira Baibulo m’Allegheny, Pennsylvania, U.S.A., kuchiyambiyambi kwa ma 1870. Poyamba anadziŵika kokha monga Ophunzira Baibulo, koma mu 1931 analandira dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Zikhulupiriro zawo ndi ntchito siziri zatsopano koma ndizo kubwezeretsedwa kwa Chikristu cha zaka za zana loyamba.
Kodi Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti chipembedzo chawo ndicho chokha cholondola?
Baibulo silimavomerezana ndi lingaliro lamakono lakuti pali njira zambiri zovomerezeka m’kulambira Mulungu. Aefeso 4:5 imati pali ‘Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi.’ Yesu anafotokoza kuti: “Chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo ya kumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka. . . . Siyense wa kunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.”—Mat. 7:13, 14, 21; wonaninso 1 Akorinto 1:10.
Malemba amasonya mobwerezabwereza kuchiungwe cha ziphunzitso Zachikristu chowona kukhala “chowonadi,” ndipo Chikristu chimalankhulidwa kukhala “njira ya chowonadi.” (1 Tim. 3:15; 2 Yoh. 1; 2 Pet. 2:2) Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zimazika zikhulupiriro zawo zonse, miyezo yawo ya kudzisungira, ndi machitidwe a gulu pa Baibulo, chikhulupiriro chawo m’Baibulo lenilenilo monga Mawu a Mulungu chimazipatsa chikhutiro chakuti zimene izo ziri nacho chiridi chowonadi. Chotero mkhalidwe wawo suli kudzitamandira koma umasonyeza kuti chidaliro chawo chakuti Baibulo ndilo muyeso wolungama umene chipembedzo cha munthu chiyenera kupimidwa nawo. Izo siziri zadyera koma ziri zofunitsitsa kugaŵana zikhulupiriro zawo ndi ena.
Kodi zipembedzo zina nazonso sizimatsatira Baibulo?
Zambiri zimaligwiritsira ntchito kumlingo wakutiwakuti. Koma kodi izo zimaphunzitsadi ndi kugwiritsira ntchito zolembedwamo? Talingalirani: (1) Izo zachotsa dzina la Mulungu wowona lolembedwa nthaŵi zikwi zambiri m’matembenuzidwe awo ambiri a Baibulo. (2) Chiphunzitso cha Utatu, lingaliro lawo la Mulungu mwiniyo, chabwerekedwa kumagwero achikunja ndipo chinakula kukhala mpangidwe wake wamakono pambuyo pa zaka mazana ambiri Baibulo litatha kulembedwa. (3) Kukhulupirira kwawo kusakhoza kufa kwa moyo wa munthu monga maziko a kupitirizabe kwa moyo sikunatengedwe m’Baibulo; maziko ake ali m’Babulo wakale. (4) Mutu wankhani wa ulaliki wa Yesu unali Ufumu wa Mulungu, ndipo anatumiza ophunzira ake kukalankhula za uwo mwachindunji kwa ena; koma matchalitchi lerolino amatchula mwakamodzikamodzi Ufumu umenewo ndipo mamembala awo sakuchita ntchito yolalikira “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mat. 24:14) (5) Yesu ananena kuti otsatira ake owona akadziŵika mosavuta mwa chikondi chawo chodzipereka kwa wina ndi mnzake. Kodi zimenezo ziri choncho ponena za zipembedzo za Dziko Lachikristu pamene mitundu ipita kunkhondo? (6) Baibulo limanena kuti ophunzira a Kristu sakakhala mbali ya dziko, ndipo limachenjeza kuti yense wofuna kukhala bwenzi la dziko akudzipangitsa kukhala mdani wa Mulungu; koma matchalitchi a Dziko Lachikristu ndi mamembala awo ngophatikizidwa kwambiri m’zochitika zandale zadziko za mitundu. (Yak. 4:4) Chifukwa cha mbiri yotero, kodi kunganenedwe mowona mtima kuti iwo akumamatiradi ku Baibulo?
Kodi Mboni za Yehova zimafika motani pamalongosoledwe awo a Baibulo?
Mfundo yaikulu njakuti Mboni zimakhulupiriradi kuti Baibulo ndiro Mawu a Mulungu ndi kuti zolembedwamo zalinganizidwira kutilangiza. (2 Tim. 3:16, 17; Aroma 15:4; 1 Akor. 10:11) Chotero sizimatembenukira kumikangano ya nthanthi kuti zizembe mawu ake omvekera bwino a chowonadi kapena kulungamitsa njira ya moyo ya anthu amene asiya miyezo yake ya makhalidwe abwino.
Potchula tanthauzo la chinenero chophiphiritsira m’Baibulo, zimalola Baibulo kupereka malongosoledwe akeake, mmalo mwa kupereka ziganizo zawo ponena za tanthauzo lake. (1 Akor. 2:13) Zisonyezero zonena za tanthauzo la mawu ophiphiritsira kaŵirikaŵiri zimapezedwa mmbali zina za Baibulo. (Mwachitsanzo, wonani Chivumbulutso 21:1; ndiyeno, ponena za tanthauzo la “nyanja,” ŵerengani Yesaya 57:20. Kuti mudziŵe “Mwanawankhosa” wotchulidwa pa Chivumbulutso 14:1, wonani Yohane 1:29 ndi 1 Petro 1:19.)
Ponena za kukwaniritsidwa kwa ulosi, izo zimagwiritsira ntchito zimene Yesu adanena ponena za kukhala maso ku zochitika zimene zimayenderana ndi zimene zinanenedweratu. (Luka 21:29-31; yerekezerani ndi 2 Petro 1:16-19.) Zimasonya mowona mtima ku zochitika zimenezo ndi kusonyeza chimene Baibulo limanena kuti zimatanthauza.
Yesu adanena kuti padziko lapansi akakhala ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” (otsatira ake odzozedwa atawonedwa monga kagulu), gulu mwa limene akagaŵira chakudya chauzimu kwa ziŵalo za banja la chikhulupiriro. (Mat. 24:45-47) Mboni za Yehova zimavomereza kakonzedwe kameneko. Monga momwe zinaliri ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba, zimayang’ana ku bungwe lolamulira la kagulu ka “kapolo” kameneko kuthetsa mafunso ovuta—osati pamaziko a nzeru yaumunthu, koma mwa kugwiritsira ntchito chidziŵitso chawo cha Mawu a Mulungu ndi zochita zake ndi atumiki ake, ndipo mwachithandizo cha mzimu wa Mulungu, umene amapempherera mwaphamphu.—Mac. 15:1-29; 16:4, 5.
Kodi nchifukwa ninji pakhala masinthidwe m’kupita kwa zaka m’ziphunzitso za Mboni za Yehova?
Baibulo limasonyeza kuti Yehova amakhozetsa atumiki ake kuzindikira chifuno chake mwanjira yopita patsogolo. (Miy. 4:18; Yoh. 16:12) Chotero, aneneri amene anauzidwa ndi Mulungu kulemba zigawo za Baibulo sanazindikire tanthauzo la zinthu zonse zimene adalemba. (Dan. 12:8, 9; 1 Pet. 1:10-12) Atumwi a Yesu Kristu anazindikira kuti panali zambiri zimene sanazindikire m’nthaŵi yawo. (Mac. 1:6, 7; 1 Akor. 13:9-12) Baibulo limasonyeza kuti pakakhala kuwonjezereka kwa chidziŵitso cha chowonadi mkati mwa “nthaŵi ya chimaliziro.” (Dan. 12:4) Kaŵirikaŵiri chidziŵitso chowonjezereka chimachititsa masinthidwe m’kuganiza kwa munthu. Mboni za Yehova ziri zofunitsitsa kupanga masinthidwe otero modzichepetsa.
Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimalalikira kunyumba ndi nyumba?
Yesu adaneneratu za nchito imeneyi kaamba ka tsiku lathu: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” Iye adalangizanso otsatira ake kuti: “Mukani . . . ndi kupanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse.”—Mat. 24:14, NW; 28:19, NW.
Pamene Yesu anatuma ophunzira ake oyambirira, anawalangiza kupita kunyumba za anthu. (Mat. 10:7, 11-13) Mtumwi Paulo anati ponena za uminisitala wake: “Sindinaleka kukuuzani chirichonse cha zinthu zimene zinali zopindulitsa ngakhale kukuphunzitsani poyera ndi kunyumba ndi nyumba.”—Mac. 20:20, 21, NW; wonaninso Machitidwe 5:42.
Uthenga umene Mboni zimalengeza umaphatikizapo miyoyo ya anthu; zimafuna kusamala kuti zisaphonye aliyense. (Zef. 2:2, 3) Kucheza kwawo kumasonkhezeredwa ndi chikondi—choyamba kukonda Mulungu, ndiponso kukonda mnansi wawo.
Msonkhano wa atsogoleri achipembedzo m’Spanya unanena kuti: “Mwinamwake [matchalitchi] amanyalanyaza mopambanitsa imene kwenikweni iri ntchito yaikulu koposa ya Mboni—kucheza kunyumba, kumene kuli kofanana ndi mchitidwe wa atumwi m’tchalitchi choyambirira. Pamene kuli kwakuti kaŵirikaŵiri matchalitchi, amalekezera pa kumanga akachisi awo, kuimba mabelo awo okopa anthu ndi kulalikilira mkati mwa malo awo olambirira, [Mboni] zimatsatira njira yochitira ya atumwi ya kupita kunyumba ndi nyumba ndi kugwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse wa kuchitira umboni.”—El Catolicismo, Bogotá, Colombia, September 14, 1975, p. 14.
Koma kodi nchifukwa ninji Mboni zimafika mobwerezabwereza ngakhale panyumba za anthu amene saali achipembedzo chawo?
Izo sizimakakamizira uthenga wawo pa ena. Koma zimadziŵa kuti anthu amasamukira kumalo okhala atsopano ndi kuti mikhalidwe ya anthu imasintha. Lero munthu angakhale wotanganitsidwa kwambiri kosakhoza kumvetsera; nthaŵi ina angakhale wokondwera kupeza nthaŵi. Chiŵalo chimodzi cha banja chingakhale chosakondwera, koma ena angakhale. Anthu enieniwo amasintha; mavuto aakulu mmoyo angachititse kuzindikira chosoŵa chauzimu.—Wonaninso Yesaya 6:8, 11, 12.
Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimazunzidwa ndi kunenezedwa?
Yesu anati: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likanakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.” (Yoh. 15:18, 19; wonaninso 1 Petro 4:3, 4.) Baibulo limasonyeza kuti dziko lonse ligona mu ulamuliro wa Satana; iye alinso wosonkhezera wamkulu wa chizunzo.—1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:17.
Yesu anauzanso ophunzira ake kuti: “Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa.” (Marko 13:13) Panopa liwu lakuti “dzina” limatanthauza chimene Yesu ali mwa ukumu, Mfumu Yaumesiya. Chizunzo chimadza chifukwa chakuti Mboni za Yehova zimaika malamulo ake patsogolo pa a wolamulira aliyense wa padziko lapansi.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Kodi nchifukwa ninji anthunu simumaphatikizidwa m’kuchita zinthu zothandizira kuti dziko (chitaganya) likhale malo abwinopo kukhalamo?
Mungayankhe kuti: ‘Mwachiwonekere mikhalidwe ya m’chitaganya njofunika kwa inu, ndipo irinso yotero kwa ine. Ntakufunsani, Kodi ndi vuto liti limene muganiza kuti liyenera kukhala pakati pa oyamba kuthetsedwa?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji mukulingalira kuti limeneli lafikira kukhala chofunika chachikulu kwambiri motero? . . . Mwachiwonekere, kuchitapo kanthu mofulumira pankhaniyo kungakhale kopindulitsa, koma ndiri wotsimikiza kuti mudzavomereza kuti tingafune kuwona kuwongokera pamlingo wa nthaŵi yaitali. Ndiyo njira imene ife monga Mboni za Yehova timatenga pankhaniyo. (Fotokozani zimene timachita kuthandiza anthu kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo m’miyoyo yawo kuchitira kuti afikire maziko a nkhaniyo pamlingo waumwini; ndiponso, zimene Ufumu wa Mulungu udzachita, ndi chifukwa chake uwo udzathetsa vuto la anthu kosatha.)’
Kapena munganene kuti: ‘(Pambuyo pakufotokoza mfundo zina m’yankho lapitali . . . ) Anthu ena amathandizira kuwongolera chitaganya mwa kupereka ndalama; ena amatero mwa kupereka modzifunira mautumiki awo. Mboni za Yehova zimachita zonse ziŵiri. Tandilolani ndifotokoze.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, munthuyo ayenera kukhoma misonkho yake mowona mtima; umenewo umapatsa ndalama boma, zoperekera mautumiki ofunika.’ (2) ‘Timachita zoposa zimenezo, timapita kunyumba za anthu, kupempha kuphunzira nawo Baibulo kwaulere. Pamene azoloŵerana ndi zimene Baibulo limanena, amaphunzira kugwiritsira ntchito malamulo a Baibulo amakhalidwe abwino ndipo chotero amalaka mavuto awo.’
Kuthekera kwina: ‘Ndiri wokondwera kuti mwadzutsa nkhaniyo. Anthu ambiri sanafufuze konse kuti adziŵe zimene Mboni kwenikweni zimachita m’nkhani za chitaganya. Mwachiwonekere pali njira yoposa imodzi yoperekera chithandizo.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Ena amatero mwakupanga magulu—zipatala, nyumba zokhala nkhalamba, malo okonzerako mikhole ya anamgoneka, ndi zina zotero. Ena angadzipereke kupita kunyumba za anthu kwenikweniko ndi kukapereka chithandizo choyenerera chimene iwo ali okhoza. Ndizo zimene Mboni za Yehova zimachita.’ (2) ‘Tawona kuti pali kanthu kena kamene kangasinthe lingaliro lathunthu la munthu ponena za moyo, ndipo kameneko ndiko chidziŵitso cha zimene Baibulo limasonyeza kukhala chifuno chenicheni cha moyo ndi chimene mtsogolo muli namo.’
Lingaliro lowonjezereka: ‘Ndikuyamikira kuti mwadzutsa funso limeneli. Tikakonda kuwona mikhalidwe ikuwongokera, kodi sichoncho? Ntakufunsani, Mulingalira bwanji za zimene Yesu Kristu mwiniyo anachita? Kodi mukanati njira imene anagwiritsira ntchito kuthandiza anthu inali yopindulitsa? . . . Timayesa kutsatira chitsanzo chake.’
‘Akristu amayembekezeredwa kukhala Mboni za Yesu, osati za Yehova’
Mungayankhe kuti: ‘Imeneyo iri mfundo yokondweretsa imene mwadzutsa. Ndipo mwalondola kuti tiri ndi thayo la kukhala mboni za Yesu. Ndicho chifukwa chake ntchito ya Yesu m’chifuno cha Mulungu yagogomezeredwa m’mabukhu athu. (Mungafune kugwiritsira ntchito bukhu latsopano kapena magazine kuchitira chitsanzo zimenezi.) Koma nachi chinthu china chimene chingakhale lingaliro latsopano kwa inu. (Chiv. 1:5) . . . Kodi Yesu anali “Mboni Yokhulupirika” ya yani? (Yoh. 5:43; 17:6) . . . Yesu anapereka chitsanzo chimene tiyenera kutsatira, kodi sanatero? . . . Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kudziŵa onse aŵiri Yesu ndi Atate wake? (Yoh. 17:3)’