Ufumu
Tanthauzo: Ufumu wa Mulungu ndiwo chisonyezero cha ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Yehova ku zolengedwa zake, kapena njira imene iye amagwiritsira ntchito kusonyeza ufumuwo. Kwakukulukulu liwuli limagwiritsiridwa ntchito kutanthauza kusonyezedwa kwa ulamuliro wa Mulungu kupyolera mwa boma la ufumu lotsogozedwa ndi Mwana wake, Yesu Kristu. “Ufumu” ungasonye ku ulamuliro wa wodzozedwa kukhala Mfumu kapena kugawo la dziko lapansi lolamulidwa ndi boma lakumwamba limenelo.
Kodi Ufumu wa Mulungu ndiwo boma lenileni?
Kapena kodi mmalo mwake, ndiwo, mkhalidwe m’mitima ya anthu?
Luka 17:21, KJ: “Ndipo sadzanena, Tawonani uwu, kapena uwo! Pakuti, tawonani, Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu [ndiponso TEV, Dy; koma “pakati panu,” KJ mawu a m’mphepete, NE, JB; “pakati panu,” RS; “pakati panu,” NW].” (Tawonani kuti, monga momwe kwasonyezedwera ndi vesi 20, Yesu anali kulankhula kwa Afarisi, amenenso anawatsutsa kukhala onyenga, chotero iye sakanatanthauza kuti Ufumuwo unali m’mitima yawo. Koma Ufumuwo monga momwe unaimiridwa ndi Kristu unali pakati pawo. Motero The Emphatic Diaglott imati: “Ukulu wa ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”)
Kodi Baibulo limanenadi za Ufumu wa Mulungu kukhala boma?
Yes. 9:6, 7: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro [“boma” RS, KJ, AT, Dy; “kulamulira,” JB, NE; “kulamulira kwa kalonga,” NW] udzakhala papheŵa lake, ndipo adzatchedwa dzina lake ‘Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.’ Za kuenjezera ulamuliro wake ndi za mtendere sizidzatha.”
Kodi ndani amene ali olamulira mu Ufumuwo?
Chiv. 15:3: “Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyose; njira zanu nzolungama ndi zowona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha.”
Dan. 7:13, 14: “Anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu [Yesu Kristu; wonani Marko 14:61, 62], nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe [Yehova Mulungu]; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. Ndipo anampatsa [Yesu Kristu] ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse ndi mitundu yonse ya anthu, ndi manenedwe onse, amtumikire.”
Chiv. 5:9, 10: “Mwaphedwa [Yesu Kristu], ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu amafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.” (Pa Chivumbulutso 14:1-3 “ogulidwa kuchokera kudziko lapansi” ameneŵa kukakhala olamulira limodzi ndi Mwanawankhosa pa Phiri la Ziyoni lakumwamba akunenedwa kufikira chiŵerengero cha 144 000.)
Kodi nchiyambukiro chotani chimene Ufumuwo udzakhala nacho pamaboma a anthu?
Dan. 2:44: “Masiku a mafumu aja Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse nudzakhala chikhalire.”
Sal. 2:8, 9: “Undifunse, ndipo ndidzakupatsa a mitundu akhale choloŵa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako. Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.”
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachitanji?
Udzayeretsa dzina la Yehova ndi kuchirikiza ufumu wake
Mat. 6:9, 10: “Pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze.” (Panopa kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu kuli kogwirizanitsidwa kwambiri ndi kudza kwa Ufumu wake.)
Ezek. 38:23: “Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.” (Dzina la Mulungu lidzachotseredwa chitonzo chonse; lidzachitiridwa monga lopatulika ndi loyenerera ulemu, ndipo amoyo onse adzakhala anthu amene mofunitsitsa amachirikiza ufumu wa Yehova, okondwera kuchita chifuniro chake. Mtendere ndi ubwino wa chilengedwe chonse zimadalira pa kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova.)
Udzathetsa ulamuliro wololedwa wa Satana padziko
Chiv. 20:2, 3: “[Mfumu yakumwambayo, Yesu Kristu] anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi, patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthaŵi.” (Motero anthu adzamasulidwa pachisonkhezero chauchiŵanda chimene chinapangitsa moyo kukhala wovuta kwambiri kwa anthu amene amafuna kuchita cholungama. Chisonkhezero chauchiŵanda chimene chachititsa zochitika zankhalwe zopambanitsa ndi chisonkhezero chauchiŵanda chimene chadzaza miyoyo ya anthu ochuluka ndi mantha chidzatha.)
Udzagwirizanitsa chilengedwe chonse m’kulambiridwa kwa Mulungu mmodzi wowona
Chiv. 5:13; 15:3, 4: “Ndipo cholengedwa chirichonse chiri m’mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m’nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndinazimva ziri kunena, Kwa iye wakukhala pa mpando wachifumu [Yehova Mulungu], ndi kwa Mwana wa nkhosa [Yesu Kristu] zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthaŵi za nthaŵi.” “Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zowona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalamekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidawonetsedwa.”
Udzabwezeretsa anthu ku unansi wa kumvana ndi Mulungu
Aroma 8:19-21, NW: “Pakuti chiyembekezo chaphamphu cha chilengedwe [anthu] chikuyembekezera kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu [umboni wakuti oukitsidwira kumoyo wakumwamba limodzi ndi Yesu Kristu ayamba kugwira ntchito monga olamulira]. Pakuti chilengedwe chinagonjetseredwa kuutsiru, osati mwanjira ya chifuniro chake koma kupyolera mwa iye amene anachigonjetsa, pamaziko a chiyembekezo chakuti chilengedwe chenichenicho [anthu onse] chidzamasulidwanso ku ukapolo wa chivundi ndi kukhala ndi ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”
Udzamasula anthu ku chiwopsezo chonse cha nkhondo
Sal. 46:8, 9: “Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa padziko lapansi. Aletsa nkhondo kumalekekezero adziko lapansi.”
Yes. 2:4: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”
Udzachotsera dziko lapansi olamulira oipa ndi chitsenderezo
Sal. 110:5: “Yehova padzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku lamkwiyo wake.”
Sal. 72:12-14: ‘[Mfumu Yaumesiya ya Yehova] idzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzaombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wamtengo pamaso pake.’
Udzagaŵira chakudya chochuluka kwa anthu onse
Sal. 72:16: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri.”
Yes. 25:6: “M’phiri limeneli [m’Phiri la Ziyoni wakumwamba, malo a mpando wachifumu a Ufumu wa Mulungu, mudzapangidwa makonzedwe a nzika zake za padziko lapansi], Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.”
Udzachotsa matenda ndi kulemala konse
Luka 7:22; 9:11: “Mukani, muuze Yohane zimene mwaziwona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuwona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphaŵi ulalikidwa Uthenga Wabwino.” “Iye [Yesu Kristu] anaŵalandira, nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasoŵa kuchiritsidwa.” (Chotero Yesu anasonyeza zimene iye monga Mfumu yakumwamba adzachitira anthu.)
Udzagaŵira nyumba zoyenerera kaamba ka aliyense
Yes. 65:21, 22: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya.”
Udzapereka ntchito yokhutiritsa kwa onse
Yes. 65:23: “Sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.”
Udzatsimikizira chisungiko, ufulu pangozi kwa munthu kapena chuma chake
Mika 4:4: “Adzakhala munthu yense patsinde pampesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”
Sal. 37:10, 11: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”
Udzachititsa chilungamo ndi chiweruzo cholungama kufunga
2 Pet. 3:13, NW: “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuziyembekezera monga mwa lonjezano lake, ndipo m’zimenezi mudzakhala chilungamo.”
Yes. 11:3-5: “[Mfumu Yaumesiya] sidzaweruza monga apenya maso, sidzadzudzula mwamphekesera: koma ndi chilungamo idzaweruza aumphaŵi, nidzadzudzulira ofatsa a m’dziko mowongoka; . . . ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa mchuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpsyo zake.”
Udzatetezera anthu ku chivulazo chirichonse chochititsidwa ndi mphamvu za chilengedwe
Marko 4:37-41: “Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira m’ngalaŵa, motero kuti ngalaŵa inayamba kudzala. . . . Ndipo anauka [Yesu], nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu. . . . Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera iye? (Motero Kristu anasonyeza mphamvu imene iye monga Mfumu yakumwamba adzagwiritsira ntchito pa zinthu zachilengedwe zotero.)
Udzaukitsa akufa
Yoh. 5:28, 29: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali mmanda adzamva mawu ake, [mawu a Kristu Mfumuyo], nadzatulukira.”
Chiv. 20:12: “Ndinawona akufa, akulu ndi ang’ono alinkuima ku mpando wachifumu; ndipo mabukhu anatsegulidwa; ndipo bukhu lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabukhu, monga mwa ntchito zawo [zochitika pambuyo pa chiukiriro chawo; yerekezerani ndi Aroma 6:7].”
Udzachotsa imfa yonse yochititsidwa ndi choloŵa cha uchimo wa Adamu
Yes. 25:8: “Iye wameza imfa kunthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pankhope zonse.”
Chiv. 21:4, NW: “Adzapukuta msozi uliwonse mmaso mwawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale kufuula ngakhale kupweteka sizidzakhalakonso. Zinthu zoyambazo zapita.”
Udzagaŵira dziko m’limene anthu adzakondana mowona mtima
Yoh. 13:35: “Mwaichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga [chotero, akhala mu mzera wakukhala anzake a Yesu mu Ufumu wakumwamba kapena nzika za dziko lapansi za Ufumu umenewo], ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”
Udzachititsa zinyama ndi anthu kuloŵa mu unansi wogwirizana wina ndi mnzake
Yes. 11:6-9: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chirombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo ang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzaseŵera pauna wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera.” (Ndiponso Yesaya 65:25)
Hos. 2:18: “Tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwaŵa pansi; . . . ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.”
Udzapangitsa dziko lapansi kukhala paradaiso
Luka 23:43, NW: “Indetu, ndinena ndi iwe lerolino, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”
Sal. 98:7-9: “Nyanja ifuule ndi kudzala kwake; dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo; mitsinje iombe manja; mapiri afuule pamodzi mokondwera; pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo.”
Yerekezerani ndi Genesis 1:28; 2:15; Yesaya 55:11.
Kodi ndiliti pamene Ufumu wa Mulungu unayenera kuyamba kulamulira?
Kodi munali m’zaka za zana loyamba?
Akol. 1:1, 2, 13: “Paulo, mtumwi wa Kristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa oyera mtima [awo amene anali oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba] . . . amene [Mulungu] anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa [oyera mtimawo, ziŵalo za mpingo Wachikristu] kutiloŵetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake.” (Chotero ndithudi, Kristu anali atayamba kulamulira pampingo Wachikristu zaka za zana loyamba, zimenezi zisanalembedwe, koma kukhazikitsidwa kwa Ufumuwo kulamulira padziko lonse lapansi kunali mtsogolobe.)
1 Akor. 4:8: “Mwadzala kale, mwalemera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.” (Kuli kwachiwonekere kuti mtumwi Paulo anali kuwadzudzula chifukwa cha kukhala ndi lingaliro lolakwa.)
Chiv. 12:10, 12, NW: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakunenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku. Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Panopa kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu kukugwirizanitsidwa ndi kuponyedwa kwa Satana kuchokera kumwamba. Zimenezi sizinachitike panthaŵi yachipanduko m’Edene, monga momwe kwasonyezedwera m’Yobu mutu 1, 2. Chivumbulutso chinalembedwa mu 96 C.E., ndipo Chivumbulutso 1:1 chimasonyeza kuti chikusimba zochitika zimene panthaŵiyo zinali mtsogolo.)
Kodi kudza kwa ulamuliro wa Mulungu kuyenera kuyembekezera kutembenuzidwa kwa dziko lonse?
Sal. 110:1, 2: “Yehova ananena kwa Ambuye wanga [Yesu Kristu], Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu. Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu.” (Chotero pakakhala adani akuti iye agonjetse; sionse akagonjera ku ulamuliro wake.)
Mat. 25:31-46: “Pamene Mwana wa munthu [Yesu Kristu] adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pachimpando cha kuŵala kwake; ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; . . . Ndipo ameneŵa [amene sanasonyeze chikondi kwa abale ake odzozedwa] adzachoka kumka kuchilango cha nthaŵi zonse; koma olungama kumoyo wa nthaŵi zonse.” (Mwachiwonekere, sikukayembekezeredwa kuti anthu onse akatembenuka Kristu asanakhale pampando wake wachifumu; sionse amene akatsimikizira kukhala olungama.)
Kodi Baibulo limasonyeza kuti ndiliti pamene Ufumuwo ukayamba ulamuliro wake?
Wonani tsamba 231-233, pamutu waukulu wakuti “Madeti,” ndi tsamba 261-266, pa wakuti “Masiku Otsiriza.”
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Sudzadza m’nthaŵi ya moyo wanga’
Mungayankhe kuti: ‘Komatu udzadza m’nthaŵi ya moyo wa munthu wina, kodi sichoncho? . . . Kodi pali munthu amene akakhoza kudziŵa kuti mbadwo wake ndiwo umene ukawuwona? Atumwi a Yesu mwiniyo anafuna kudziŵa zimenezo, ndipo yankho limene anawapatsa nlofunika kwambiri kwa ife lerolino. (Mat. 24:3-14; Luka 21:29-32)’
Kapena munganene kuti: ‘Lingaliro limenelo liri lofala kwambiri. Koma pamaziko a Baibulo, Mboni za Yehova zimakhulupirira mwamphamvu kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira kale kumwamba ndi kuti ziri kwa ife kusonyeza kuti kaya tifuna kupitirizabe kukhala ndi moyo padziko lapansi molamulidwa ndi boma lolungama la Mulungu kapena ayi. Ndicho chifukwa chake ndafika pakhomo panu lerolino. Tamverani zimene zafotokozedwa pano pa Mateyo 25:31-33.’