Masiku Otsiriza
Tanthauzo: Baibulo limagwiritsira ntchito liwu lakuti “masiku otsiriza” kusonya kunyengo yomalizira yotsogolera kunthaŵi ya kuwononga yoikidwiratu ndi Mulungu imene idzatanthauza mapeto a dongosolo la zinthu. Dongosolo Lachiyuda limodzi ndi kulambira kwake kogwirizanitsidwa ndi kachisi m’Yerusalemu linaloŵa m’masiku ake otsiriza kuyambira 33 kufikira 70 C.E. Zimene zinachitika panthaŵiyo zinali chithunzi cha zimene zikachitika mwa njira yokulirapo kwambiri ndi pamlingo wapadziko lonse panthaŵi imene mitundu yonse ikayang’anizana ndi kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu. Dongosolo liripoli loipa la zinthu, limene likuphatikizapo dziko lonse, linaloŵa m’masiku ake otsiriza mu 1914, ndipo ena a mbadwo umene unalipo panthaŵiyo adzakhalaponso kuti awone mapeto ake otheratu mu “chisautso chachikulu.”
Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti tikukhala “m’masiku otsiriza”?
Baibulo limafotokoza zochitika ndi mikhalidwe zimene zimasonyeza nthaŵi yapadera imeneyi. “Chizindikiro” chiri cha chiwungwe chopangidwa ndi maumboni ochuluka; chotero kukwaniritsidwa kwake kumafunikiritsa kuti mbali zonse za chizindikirocho ziwonekere bwino lomwe mkati mwa mbadwo umodzi. Mbali zosiyanasiyana za chizindikiro zalembedwa pa Mateyu chaputala 24, 25, Marko 13, ndi Luka 21; maumboni ena ali pa 2 Timoteo 3:1-5, 2 Petro 3:3, 4 ndi Chivumbulutso 6:1-8. Kuti tifotokoze mwa fanizo, tidzapenda mbali zochepa zapadera za chizindikirocho.
“Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina ndi ufumu ndi ufumu wina” (Mat. 24:7)
Nkhondo yadodometsa moyo padziko lapansi kwazaka mazana ambiri. Nkhondo zamitundu yonse ndi nkhondo za mkati mwa mitundu zamenyedwa. Koma kuyambira 1914 nkhondo yoyamba yadziko inamenyedwa. Imeneyi siinali nkhondo wamba pakati pamagulu ankhondo aŵiri pabwalo lankhondo. Kwa nthaŵi yoyamba, maulamuliro onse aakulu anali pankhondo. Mitundu yathunthu—kuphatikizapo alaiya—anasonkhanitsidwa kuchirikiza zochitika za nkhondo. Kukuyerekezeredwa kuti podzafika mapeto a nkhondoyo 93 peresenti ya nzika za dziko lapansi inali italoŵetsedwamo. (Ponena za tanthauzo la m’mbiri la 1914, wonani tsamba 266, 267.)
Monga momwe kunanenedweratu pa Chivumbulutso 6:4, ‘mtendere unachotsedwa padziko lapansi.’ Chotero dziko lapitirizabe kukhala mu mkhalidwe wachipwirikiti chiyambire 1914. Nkhondo Yadziko II inameyedwa kuyambira 1939 mpaka 1945. Mogwirizana ndi kunena kwa Kazembe Wankhondo wotula udindo Gene La Rocque, podzafika mu 1982 panali patachitika nkhondo zina 270 chiyambire 1945. Anthu oposa mamiliyoni 100 aphedwa m’nkhondo mkati mwa zaka za zana lino. Ndiponso, mogwirizana ndi kunena kwa kope la 1982 la World Military and Social Expenditures, panali anthu 100 miliyoni m’chakacho amene anaphatikizidwa mwachindunji kapena kosakhala mwachindunji m’machitachita a nkhondo.
Kodi pangafunikire zowonjezereka kukwaniritsira mbali imeneyi ya ulosi? Pali zida zankhondo za nyukliya zikwi makumi ambiri zachire kugwiritsiridwa ntchito msanga. Asayansi otchuka anena kuti ngati mitundu itati igwiritsire ntchito ngakhale nusu ya nkhokwe zawo za zida za nyukliya, chitaganya chonse, mwinamwake mafuko onse a anthu akawonongedwa. Koma zimenezo sindizo chotulukapo chimene ulosi wa Baibulo umasonyako.
‘Kudzakhala njala . . . m’malo akutiakuti’ (Mat. 24:7)
Pakhala nthaŵi zambiri zanjala m’mbiri ya anthu. Kodi zaka za zana la 20 zakanthidwa nayo kumlingo wotani? Nkhondo yadziko inachititsa kufalikira kwa njala ku Ulaya ndi Asia. Afirika wakanthidwa ndi chirala, chikumachititsa kupereŵera kwa chakudya kwakukulu. Chakumapeto kwa 1980 Gulu la Chakudya ndi Malimidwe linayerekezera kuti anthu mamiliyoni 450 anali anjala kufikira pakumatofa nayo, ndipo ofika biliyoni imodzi analibe chakudya chokwanira. Mwa amenewa okwanira mamiliyoni 40 chaka chirichonse amafa kwenikweni—m’zaka zina ofikira mamiliyoni 50—chifukwa cha kupereŵera kwa chakudya.
Kodi pali chachilendo chiri chonse ponena za kupereŵera kwa zakudya kumeneko? Chivumbulutso 6:6 chinasonyeza kuti muyezo waung’ono wa zakudya zazikulu monga tirigu kapena balere zikagulitsidwa pamtengo wamalipiro a tsiku lupiya latheka (wonani Mateyu 20:2) koma zinthu zonga mafuta a azitona ndi vinyo zogwiritsiridwa ntchito ndi anthu okhuphuka sizikaipitsidwa. Chotero mwachiwonekere ambiri akakanthidwa ndi kusoŵa pamene ena akakhalabe akupeza zimene anafuna. Mkhalidwewu suulinso malo amodzi, koma dziko lonse. Mu 1981 The New York Times inasimba kuti: “Kupititsa patsogolo miyezo ya moyo ndi kufunika kwa chakudya komakulakula kuzungulira dziko kwaika chitsenderezo pamitengo ya zakudya, kukumapangitsa kukhala kuvutirapo kwa maiko osauka koposa kugula zofunika zawo za chakudya kuchokera kumaiko akunja.” M’maiko ochuluka kutulutsidwa kwa chakudya, ngakhale mwachithandizo cha sayansi yamakono, sikunakhoze kuyenderana ndi kuwonjezereka kwa chiŵerengero chonse cha anthu. Akatswiri amakono a chakudya sakuwona njira yeniyeni yothetsera vutoli.
‘Kudzakhala zivomezi zazikulu’ (Luka 21:11)
Ndizowona kuti panali zivomezi zazikulu m’zaka za mazana apita; ndiponso, mogwiritsira ntchito makina awo amphamvu tsopano asayansi amadziŵa zivomezi zoposa miliyoni imodzi pachaka. Koma sipamafunikira makina apadera kuti anthu adziŵe kuti kuli chivomezi chachikulu.
Kodi kwakhaladi chiŵerengero chenicheni chapadera cha zivomezi zazikulu chiyambire 1914? Ziŵerengero zopezedwa kuchokera ku National Geophysical Data Center m’Boulder, Colorado, zochirikizidwa ndi mabukhu angapo a maumboni, mapendedwe anachitidwa mu 1984 amene anaphatikizapo zivomezi zokha zimene zinalemera 7.5 kapena kuposa pasikelo yotchedwa Richter, kapena zimene zinawonongetsa madola mamiliyoni asanu (U.S.) kapena kuposa a chuma, kapena zimene zinapha anthu 100 kapena kuposa. Kunaŵerengeredwa kuti panali zivomezi zotero 856 mkati mwa zaka 2 000 isanafike 1914. Kuŵerengera kumodzimodziko kunasonyeza kuti m’zaka 69 zokha pambuyo pa 1914 panali zivomezi zotero 605. Zimenezi zitanthauza kuti poyerekezera ndi zaka 2 000 zapitazo avereji pachaka yakwera kuŵirikiza nthaŵi 20 kuyambira 1914.
‘Kudzakhala miliri m’malo akutiakuti’ (Luka 21:11)
Pamapeto a nkhondo yoyamba yadziko folowenza Yaspanya inalipo padziko lonse, ikumapha anthu oposa mamiliyoni 20 paliŵiro losafanana ndi lina lirilonse m’mbiri ya nthenda. Mosasamala kanthu za kupita patsogolo m’sayansi yamakhwala, chiŵerengero chachikulu chimaphedwa chaka chiri chonse ndi kensa, nthenda ya mtima, nthenda zambiri zopatsirana mwa kugonana, kutupa kwachiŵindi (multiple sclerosis), malungo, khungu lochititsidwa ndi ntchentche zakuda, ndi thenda ya Chagas.
‘Kusayeruzika kowonjezereka kotsagana ndi kuzirala kwa chikondi kochitidwa ndi chiŵerengero chokulirapo’ (Mat. 24:11, 12)
Katswiri wamkulu wodziŵa zaupandu amati: “Chinthu chimodzi chimene mumawona pamene muyang’ana upandu pamlingo wa dziko lonse ndicho kuwonjezeka kokulira ndi kosalekeza kulikonse. Zochitika zapadera zoterezi ziri zachilendo, ndipo zingakokololedwe mwamsanga ndi pfunde lomakulakula.” (The Growth of Crime, New York, 1977, Sir Leon Radzinowicz ndi Joan King, pp. 4, 5) Chiwonjezeko chiri chenicheni; siiri kokha nkhani ya kuchitira lipoti bwino. Nzowona, mibadwo yapita nayonso inali ndi apandu, koma ndi kale lonse upandu sunakhale wofalikira monga momwe uliri tsopano lino. Anthu okalamba amadziŵa zimenezo mwa zimene akumana nazo iwo eniwo.
Kusayeruzika kotchulidwa mu ulosiko kumaphatikizapo kunyoza malamulo odziŵika a Mulungu, kudziŵerengera mmalo mwa kuŵerengera Mulungu m’moyo wa munthuyo. Monga chotulukapo cha mkhalidwe umenewu, ziŵerengero za zisudzulo zikukwera, kugonana ndi osakwatirana nawo ndi kugonana kwa a ziŵalo zofanana kukuvomerezedwa mofala, ndipo mimba zokwanira mamiliyoni makumi ambiri zimatayidwa chaka chirichonse. Kusayeruzika kotero nkogwirizanitsidwa (m’Mateyu 24:11, 12) ndi chisonkhezero cha aneneri onyenga, amene amaika Mawu a Mulungu pambali moyanja ziphunzitso za iwo eni. Kulabadira nthanthi zawo mmalo mwa kuumilira ku Baibulo kumachititsa kukhalako kwa dziko lopanda chikondi. (1 Yoh. 4:8) Ŵerengani malongosoledwe ake pa 2 Timoteo 3:1-5.
“Anthu akukomoka ndi mantha ndi chiyembekezo cha zinthu zakudza padziko lapansi lokhalidwa ndi anthu” (Luka 21:25, 26, “NW”)
“Chenicheni nchakuti lerolino lingaliro limodzi lalikulu koposa limene limalamulira miyoyo yathu ndiro mantha.” inatero U.S. News & World Report. (October 11, 1965, p. 144) “Ndi kale lonse anthu sanakhale amantha motero monga lerolino,” anasimba motero magazine Achijeremani otchedwa Hörzu.—No. 25, June 20, 1980, p. 22.
Zinthu zambiri zimachititsa mkhalidwe wa mantha umenewu padziko lonse; upandu wachiwawa, ulova, kusakhazikika kwa mkhalidwe wazachuma chifukwa chakuti mitundu yochuluka kwambiri iri ndi ngongole mopanda chiyembekezo, kuipitsidwa kwa malo okhala kwa dziko lonse, kusoŵeka kwa zomangira zamphamvu ndi zachikondi zabanja, ndi lingaliro lamphamvu lakuti anthu ali pafupi kwambiri ndi upandu wakupululutsidwa ndi nyukliya. Luka 21:25 amatchula ‘zizindikiro m’dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi ndi kukokoma kwa nyanja’ zogwirizanitsidwa ndi kuvutika maganizo kwamitundu. Kaŵirikaŵiri kutuluka kwa dzuŵa kumachititsa, osati chiyembekezo chachimwemwe, koma mantha a chimene tsikulo lidzabweretsa; pamene mwezi ndi nyenyezi ziŵala, kuopa upandu kumachititsa anthu kukhala m’nyumba zokhomedwa maloko. M’zaka za zana la 20, koma osati nthaŵiyo isanafike, ndege ndi zida zoponya zagwiritsiridwa ntchito kulakatitsira zopululutsa kuchokera m’lengalenga. Ngalaŵa za m’madzi zonyamula akatundu azida zaupandu zoti nkuponyedwa zakupha zimayendayenda pansi panyanja, ngalaŵa imodzi yokha yotero ikumakonzekeretsedwa kuwononga mizinda 160. Nposadabwitsa kuti mitundu ikuvutika maganizo!
‘Otsatira owona a Kristu akakhala odedwa ndi mitundu yonse kaamba kwa dzina lake’ (Mat. 24:9)
Chizunzo chimenechi sichiri chifukwa cha kuloŵerera m’ndale zadziko koma ‘kaamba ka dzina la Yesu Kristu,’ chifukwa chakuti otsatira ake amamamatira kwa iye monga Mfumu Yaumesiya ya Yehova, chifukwa cha kumvera kwawo Kristu kuposa wolamulira aliyense wa dziko lapansi, chifukwa cha kukhulupirika kwawo kumamatira ku Ufumu wake ndi kusaphatikizidwa m’zochitika za maboma a anthu. Monga momwe mbiri yamakono ikuchitira umboni, zimenezo zakhala zokumana nazo za Mboni za Yehova m’mbali zonse za dziko lapansi.
‘Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu ikalalikidwa mu dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni’ (Mat. 24:14, “NW”)
Uthenga umene ukalalikidwa ngwakuti Ufumu wa Mulungu mmanja mwa Yesu Kristu wayamba kulamulira kumwamba, kuti posachedwa udzathetsa dongosolo lonse la zinthu loipali, kuti muulamuliro wake anthu adzafikitsidwa kuungwiro ndipo dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Kuti mbiri yabwino ikulalikidwa lerolino m’maiko oposa 200 ndi m’zirumba, kufikira malekezero a dziko lapansi. Mboni za Yehova zimathera maora mamiliyoni mazana ambiri kuntchitoyi chaka chirichonse, zikumapanga maulendo obwerezabwereza kunyumba ndi nyumba kotero kuti munthu aliyense wothekera apatsidwe mwaŵi wakumva.
Kodi zochitika za “masiku otsiriza” zonsezi zikusonya ku chiyani?
Luka 21:31, 32: “Pakuwona zinthu izi ziri kuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi [ndiko kuti, nthaŵi pamene udzawononga dziko loipa liripoli ndipo uwo udzatenga ulamuliro wokwanira wa zinthu za padziko lapansi]. Indetu ndinena ndi inu, mbadwo uno sudzapitirira kufikira zonse zitachitika.” (“Mbadwo” umene unali moyo kuchiyambi kwa kukwaniritsidwa kwa chizindikiro mu 1914 tsopano wakalamba kwambiri. Nthaŵi yotsala iyenera kukhala yaifupi kwambiri. Mikhalidwe yadziko ikupereka chisonyezero chirichonse chakuti ziridi choncho.)
Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimanena kuti munali mu 1914 pamene “masiku otsiriza” anayamba?
Chaka cha 1914 nchodziŵika ndi ulosi wa Baibulo. Kaamba ka maumboni onena za kuŵerengera nthaŵi, wonani tsamba 231-233, pamutu waukulu wakuti “Madeti.” Kulondola kwa chakacho kwasonyezedwa ndi chenicheni chakuti mikhalidwe yadziko yonenedweratu kusonyeza nthaŵi ino yachitika monga momwedi kunanenedweratu kuyambira 1914. Maumboni olembedwa pamwambapa akusonyeza zimenezi.
Kodi ndimotani mmene olemba mbiri yadziko amawonera chaka cha 1914?
“Kuyang’ana mmbuyo kuchokera panthaŵi yosaiŵalika yamakono tikuwona bwino lomwe lerolino kuti kuulika kwa Nkhondo Yadziko I kunayambitsa ‘Nthaŵi ya Mavuto’ m’zaka za zana la makumi aŵiri—mwa mawu omvekera bwino a wolemba mbiri Wachibritishi Arnold Toynbee—m’zimene chitaganya chathu sichinatulukemobe konse. Mwachindunji kapena mosakhala mwachindunji zipwirikiti zonse za theka lotsirizira la zaka zana zinayamba mu 1914 muja.”—The Fall of the Dynasties: The Collapse of the Old Order (New York, 1963), Edmond Taylor, p. 16.
“Anthu a mbadwo wa Nkhondo Yadziko II, mbadwo wanga, nthaŵi zonse adzakumbukira nkhondo yawo monga masinthiro okulira amakono. . . . Tiyenera kuloledwa kuvomereza mkhalidwe wathu wopanda pake, kukhala kwathu ndi malo m’mbiri. Koma tiyenera kudziŵa kuti, mwa mawu a anthu, masinthidwe otsimikizirika kwambiri anadza ndi Nkhondo Yadziko I. Panali panthaŵiyo pamene madongosolo andale zadziko ndi a anthu, zinalinkudza zaka mazana ambiri, anagaŵanika—nthaŵi zina mkati mwa milungu yochepa chabe. Ndipo ena anasinthidwa kwachikhalire. Munali m’Nkhondo Yadziko I pamene zinthu zotsimikizirika kwa nthaŵi yaitali zinataika. . . . Nkhondo Yadziko II inapitiriza, inakulitsa ndi kutsimikizira masinthidwe amenewa. Mwa lingaliro la makhalidwe a anthu Nkhondo Yadziko II inali nkhondo yotsiriza ya Nkhondo Yadziko I.”—The Age of Uncertainty (Boston, 1977), John K. Galbraith, p. 133.
“Zaka zokwanira theka la zana zapita, komabe chipsera chimene tsoka la Nkhondo Yaikulu [Nkhondo Yadziko I, imene inayamba mu 1914] inasiya pathupi ndi moyo wa mitundu sichinazimiririke . . . ukulu wakuthupi ndi wamakhalidwe wa vutoli unali wakuti panalibe chinthu chimene chinasiyidwa monga momwe chinaliri kale. Chitaganya chonse: madongosolo a boma, malire autundu, malamulo, magulu a ankhondo, maunansi apakati pamaiko, komanso malingaliro, moyo wabanja, chuma, maudindo, maunansi a anthu—kanthu kalikonse kanasinthidwa kuyambira pamwamba mpaka pansi. . . . Potsirizira anthu anatayikiridwa ndi kukhazikika kwawo, sanadzachirenso kufikira lerolino.”—General Charles de Gaulle, polankhula mu 1968 (Le Monde, Nov. 12, 1968, p. 9).
Kodi padzakhala munthu aliyense wamoyo pambuyo pa mapeto a dongosolo la dziko liripoli?
Ndithudi adzakhalapo. Mapeto a dongosolo la dziko lonse liripoli adzadza, osati chifukwa cha kuphedwa kosasankha m’nkhondo ya nyukliya, koma mu chisautso chachikulu chimene chimaphatikizapo “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chiv. 16:14, 16) Nkhondo imeneyo siidzawononga dziko lapansi, ndiponso siidzawononga anthu onse.
Mat. 24:21, 22, NW: “Panthaŵi imeneyo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso. Kunena zowona, ngati akadapanda kufupikitsidwa masiku amenewo, palibe munthu aliyense amene akadapulumutsidwa; koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.” (Chotero “anthu,” ena mwa anthu, adzapulumuka.)
Miy. 2:21, 22: “Owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiŵembu adzazulidwamo.”
Sal. 37:29, 34: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha. Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko; pakudulidwa oipa udzapenya.”
Kodi nchifukwa ninji Mulungu amaloleza nthaŵi yaikulu motere kupita asanawononge oipa?
2 Pet. 3:9, NW: “Yehova saali wozengereza ponena za lonjezo lake, monga momwe ena amalingalirira kuzengereza, koma ngwoleza mtima ndi inu chifukwa chakuti samafuna kuti alionse awonongedwe, koma amafuna kuti onse afikire kulapa.”
Marko 13:10: “Ndipo uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.”
Mat. 25:31, 32, 46: “Pamene Mwana wa munthu [Yesu Kristu] adzadza mu ulemelero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo adzakhala pachimpando cha kuŵala kwake; ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu amitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; ndipo amenewa [okana kuvomereza abale auzimu a Kristu monga oimira Mfumu mwiniyo] adzachoka kunka kuchilango cha nthaŵi zonse; koma olungama kumoyo wa nthaŵi zonse.”
Wonaninso tsamba 354, 355 ndi 184-186.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Mikhalidwe siiri yoipirapo kwambiri lerolino; nthaŵi zonse kwakhala nkhondo, njala, zivomezi ndi upandu’
Mungayankhe kuti: ‘Ndingathe kumvetsetsa chifukwa chimene mukulingalilira motero. Tinabadwira m’dziko limene zinthu zimenezi ziri zochitika za tsiku ndi tsiku. Koma olemba mbiri akufotokoza kuti pali kanthu kena kosiyana kwambiri ponena za zaka za zana la 20. (Ŵerengani mawu ogwidwa patsamba 266, 267.)’
Kapena munganene kuti: ‘Sichiri kokha chowonadi chakuti kwakhala nkhondo, njala, zivomezi, ndi upandu zimene ziri zapadera. Kodi munadziŵa kuti chizindikiro chimene Yesu anapereka chinali chachiungwe?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Iye sananene kuti chochitika chimodzi chirichonse mwa icho chokha chikatsimikizira kuti tinali mu “masiku otsiriza.” Koma pamene chizindikiro chathunthu chiwoneka, mpamene chiri chapadera—ndipo makamaka pamene chiwonekera pamlingo wa padziko lonse ndi kuyambira m’chaka chotsimikizira ndi kaŵerengedwe ka zaka ka Baibulo.’ (Wonani tsamba 261-266, ndiponso tsamba 231-233.)
‘Mudziŵa bwanji kuti mbadwo wamtsogolo sudzayenerana ndi ulosiwu bwino kwambiri kuposadi uno?’
Mungayankhe kuti: ‘Limenelo liri funso lokondweretsa, ndipo yankho likugogomezera chenicheni chakuti tikukhaladi mu “masiku otsiriza.” Motani? Eya, mbali ya chizindikiro choperekedwa ndi Yesu imaphatikizapo nkhondo pakati pa mitundu ndi maufumu. Koma kodi nchiyani chimene chikachitika ngati kukwaniritsidwa kwa chizindikiro kunafunikiritsa kuti tiyembezere kufikira pamene nkhondo ina yotheratu ikaulika pakati pamaulamuliro aakulu? Nkhondo yotero ikasiya opulumuka oŵerengeka ngati akakhalapo. Chotero, mukuwonatu, chifuno cha Mulungu chakuti pakhale opulumuka chimasonyeza kuti tsopano ife tiri pafupi kwambiri ndi mapeto a dongosolo lakale la zinthu limeneli.’
Kapena munganene kuti: ‘Kuyerekezera zochitika za dziko ndi ulosi umenewu kuli kofanana ndi kuyerekezera chidindo cha zala ndi mwini wake. Sipadzakhala wina aliyense wokhala ndi chidindo chotero. Mofananamo, chitsanzo cha zochitika zimene zinayamba mu 1914 sichidzabwerezedwa mu mbadwo wina mtsogolo.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kanthu kalikonse kamene kamachitika kupanga chizindikiro kali kuwoneka bwino.’ (2) ‘Ndithudi sitimafuna kukhala ofanana ndi anthu a m’tsiku la Nowa. (Mat. 24:37-39)’
‘Sitidzawona mapeto m’nthaŵi ya moyo wathu’
Mungayankhe kuti: ‘Koma inu mumakhulupirira kuti Mulungu adzaloŵerera panthaŵi ina, kodi sichoncho?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Njira yokha imene aliyense wa ife akadziŵira pamene zidzachitika ndiyo ngati Anachititsa chidziŵitso kupezeka kwa ife. Tsopano, Yesu anafotokoza momvekera bwino kuti palibe munthu amadziŵa tsiku kapena ora, koma anafotokoza mwa tsatanetsatane zinthu zimene zikachitika mkati mwa mbadwo pamene zikachitika.’ (2) ‘Malongosoledwe amenewo amaphatikizapo zochitika zimene inu mwini muli wozoloŵerana nazo. (Ngati kuli kotheka, longosolani tsatanetsatane wa chizindikiro, mukumagwiritsira ntchito mfundo zoperekedwa pamasamba apitaŵa.)’
‘Sindidera nkhaŵa ndi zinthuzi; ndimakhala ndi moyo tsiku limodzi panthaŵi imodzi’
Mungayankhe kuti: ‘Ndithudi nkwabwino kusakhala wodera nkhaŵa mopambanitsa ndi mtsogolo. Koma tonsefe timayesa kulinganiza miyoyo yathu mwanjira yakuti tidzitetezere ife ndi okondedwa athu. Kulinganiza kwanzeru nkopindulitsa. Baibulo limasonyeza kuti mtsogolomu muli zinthu zabwino kwambiri, ndipo ndife anzeru ngati tilinganiza mwanjira yakuti tipindule nazo. (Miy. 1:33; 2 Pet. 3:13)’
‘Sindimadzivutitsa kusinkhasinkha pamikhalidwe yoipa yonseyi; ndimakonda kukhala ndi chiyembekezo chakuti zidzakhala bwino mtsogolo’
Mungayankhe kuti: ‘Mokondweretsa, Yesu adanena kuti pakakhala chifukwa chabwino kaamba ka otsatira ake chokhalira ndi chiyembekezo chakuti zidzakhala bwino m’tsiku lathu. (Luka 21:28, 31)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Koma wonani kuti iye sakuŵauza kunyalanyaza zimene zikuchitika m’dziko ndi kukhala achimwemwe. Iye akunena kuti chiyembekezo chawo chakuti zidzakhala bwino chikakhala ndi chifukwa chabwino; chikakhala chifukwa chakuti anazindikira tanthauzo la zochitika za dziko nadziŵa chimene chikakhala chotulukapo.’