MUTU 14
“Anthu Ochuluka Anabwera kwa Iye”
1-3. Kodi chinachitika n’chiyani makolo atabweretsa ana awo kwa Yesu, ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu adziwe kuti Yesu ndi wotani?
YESU ankadziwa kuti pangotsala milungu yowerengeka chabe kuti aphedwe, koma anali ndi ntchito yambiri yoti achite. Choncho iye ankalalikira limodzi ndi atumwi ake ku Pereya, dera la kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. Iwo ankalalikira akupita cha kum’mwera, ku Yerusalemu kuti Yesu akachite nawo komaliza mwambo wapadera komanso wosaiwalika wa Pasika.
2 Yesu atamaliza kukambirana nkhani yofunika kwambiri ndi atsogoleri ena achipembedzo, anthu anayamba kumusokoneza chifukwa ankabweretsa ana awo kuti adzamuone. Zikuoneka kuti ana amenewa anali a misinkhu yosiyanasiyana, chifukwa mawu amene anawamasulira kuti ana m’mavesi amenewa, angatanthauze ana kuyambira akhanda mpaka a zaka 12. (Luka 18:15; Maliko 5:41, 42; 10:13) N’zodziwikiratu kuti anawa ankachita phokoso lalikulu ndiponso ankayendayenda chifukwa ndi zimene ana amachita. Koma ophunzira a Yesu anadzudzula makolo a anawo mwina poganiza kuti Mbuye wawo anali ndi ntchito yambiri ndipo anawo ankamusokoneza. Kodi Yesu anatani?
3 Yesu ataona zimene zinkachitikazo, anakwiya kwambiri. Kodi ndi ndani anamukwiyitsa? Kodi anali anawo kapena makolo awo? Ayi ndithu, ophunzira akewo ndi amene anamukwiyitsa. Yesu anati: “Asiyeni anawo abwere kwa ine, musawaletse. Chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu ngati amenewa. Ndithu ndikukuuzani, aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa n’komwe mu Ufumuwo.” Ndiyeno Yesu ananyamula anawo “m’manja mwake” n’kuyamba kuwadalitsa. (Maliko 10:13-16) Mawu amene Maliko anagwiritsa ntchito palembali angasonyeze kuti Yesu anakumbatira anawo mwachikondi ndipo malinga ndi zimene womasulira wina ananena, mwina ana ena anawanyamula “m’manja mwake.” N’zoonekeratu kuti Yesu amakonda kwambiri ana. Komabe, pamenepa tikuphunziraponso mfundo ina yakuti Yesu anali munthu wosavuta kumufikira.
4, 5. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu anali munthu wosavuta kumufikira? (b) Kodi m’mutu uno tikambirana mafunso ati?
4 Yesu akanakhala kuti anali munthu wovuta, wosachezeka komanso wonyada, n’zodziwikiratu kuti anawo sakanamuyandikira ndipo makolo awonso sakanamasuka kupita kwa iye. Mukamaganizira za nkhaniyi, n’zosakayikitsa kuti mungaone m’maganizo mwanu makolo akusangalala pamene munthu wachifundoyu ankadalitsa ana awo ndi kusonyeza kuti amawakonda ndiponso kuti Mulungu amawawerengera ndi kuwakonda. Ndithudi, ngakhale kuti pa nthawiyi Yesu anali ndi udindo waukulu kwambiri woti akwaniritse, iye anapitiriza kukhalabe munthu wosavuta kumufikira.
5 Kodi ndi anthu enanso ati amene ankamasuka kupita kwa Yesu? N’chifukwa chiyani anthu ankamasuka kupita kwa Yesu? Ndipo kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani imeneyi? Tiyeni tione.
Kodi ndi Ndani Amene Ankamasuka Kupita kwa Yesu?
6-8. Kodi nthawi zambiri ndi anthu ati amene ankapita kwa Yesu, nanga iye ankasiyana bwanji ndi mmene atsogoleri achipembedzo ankaonera anthuwo?
6 Mukamawerenga nkhani za m’Mauthenga Abwino, mungadabwe kuona kuti anthu ambiri ankapita kwa Yesu momasuka. Nthawi zambiri timawerenga kuti pamene panali Yesu pankakhalanso “gulu lalikulu la anthu.” Mwachitsanzo, timawerenga kuti “anthu ambirimbiri ochokera ku Galileya,” anamutsatira. Timawerenganso kuti “gulu lalikulu la anthu linasonkhana pamene iye anali,” “anthu ochuluka anabwera kwa iye” komanso kuti “gulu lalikulu la anthu linkayenda limodzi ndi Yesu.” (Mateyu 4:25; 13:2; 15:30; Luka 14:25) Izi zikusonyeza kuti nthawi zambiri pamene panali Yesu pankakhalanso anthu ambiri.
7 N’zodziwikiratu kuti amenewa anali anthu wamba amene atsogoleri achipembedzo ankawanyoza kuti ndi anthu osaphunzira. Afarisi ndi ansembe ankanena poyera kuti: “Gulu lonse la anthu osadziwa Chilamulowa ndi lotembereredwa.” (Yohane 7:49) Patapita nthawi, zimene arabi analemba zinasonyeza kuti Afarisi ndi ansembe ankaona anthu mwanjira imeneyi. Atsogoleri ambiri achipembedzo ankaona anthu amenewa ngati onyozeka, ndipo ankakana kudya nawo limodzi, kugula zinthu zawo, kapena kucheza nawo. Ndipotu anafika powaona kuti anthu amenewa sadzaukitsidwa chifukwa sadziwa malamulo amene atsogoleriwo anapanga okha. N’kutheka kuti anthu wamba ambiri sankayandikira atsogoleri oterewa ndipo sankayerekeza n’komwe kuwapempha kuti awathandize mwanjira ina iliyonse, koma Yesu anali wosiyana ndi atsogoleri amenewo.
8 Yesu ankachita zinthu momasuka ndi anthu wamba, monga kudya nawo, kuwachiritsa, kuwaphunzitsa komanso kuwauza uthenga wopatsa chiyembekezo. Komabe, Yesu ankadziwa kuti anthu ambiri adzakana mwayi wotumikira Yehova. (Mateyu 7:13, 14) Ngakhale zinali choncho, iye ankaona kuti munthu aliyense angasinthe n’kuyamba kutumikira Mulungu komanso ankaona kuti anthu ambiri akhoza kusintha n’kuyamba kuchita zabwino. Pamenepa Yesu anasonyeza kuti anali wosiyana kwambiri ndi ansembe komanso Afarisi omwe anali ouma mtima. N’zochititsa chidwi kuti ngakhale ansembe ndi Afarisi ankapita kwa Yesu ndipo ena mwa iwo anasintha n’kuyamba kumutsatira. (Machitidwe 6:7; 15:5) Ngakhalenso ena mwa anthu olemera ndiponso olamulira ankapita kwa Yesu momasuka.—Maliko 10:17, 22.
9. N’chifukwa chiyani akazi ankapita kwa Yesu momasuka?
9 Nawonso akazi ankapita kwa Yesu momasuka. Iwo ayenera kuti nthawi zambiri ankanyozedwa ndi atsogoleri achipembedzo. Komanso arabi ankadana ndi aliyense wophunzitsa akazi. Ndipotu akazi sankaloledwa kuchitira umboni pa milandu chifukwa ankawaona kuti ndi mboni zosadalirika. Arabi anali ndi pemphero lawo loyamikira Mulungu chifukwa chakuti iwowo anabadwa aamuna. Koma akazi ankaona kuti Yesu sanali munthu wotero ndipo ambiri ankapita kwa iye kuti awaphunzitse. Mwachitsanzo, timamva za Mariya, mchemwali wake wa Lazaro, amene anakhala pansi pafupi ndi Ambuye Yesu, n’kumawamvetsera pamene m’bale wake Marita anatanganidwa kwambiri ndi kukonza chakudya. Ndipotu Yesu anayamikira Mariya chifukwa chosankha zinthu zabwino.—Luka 10:39-42.
10. Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo, kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi anthu odwala?
10 Nthawi zambiri atsogoleri achipembedzo ankaona kuti anthu odwala ndi osafunika, koma anthu odwalawo ankapita kwa Yesu. Chilamulo cha Mose chinkanena kuti odwala khate azikhala kwaokha kuti asapatsire anzawo, koma zimenezi sizinkatanthauza kuti anthu aziwachitira nkhanza. (Levitiko, chaputala 13) Kenako arabi analemba malamulo awo ndipo anaikamo mfundo yakuti anthu akhate ndi onyansa ngati chimbudzi cha munthu. Atsogoleri ena achipembedzo anafika mpaka pomagenda anthu akhate kuti asawayandikire. Zikanakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu amene zimenezi zinawachitikira alimbe mtima n’kupita kwa mphunzitsi aliyense. Komabe akhate ankapita kwa Yesu momasuka ndipo wakhate wina ananena mawu odziwika bwino osonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro akuti: “Ambuye, ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” (Luka 5:12) M’mutu wotsatira tikambirana zimene Yesu anachitira munthu ameneyu. Koma zimenezi zikutipatsa umboni wokwanira wosonyeza kuti anthu ankamasuka kupita kwa Yesu.
11. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti anthu amene ankavutika mumtima chifukwa cha machimo awo ankapita kwa Yesu momasuka, nanga tikuphunzirapo chiyani?
11 Anthu amene ankadzimva kuti ndi ochimwa ankapitanso kwa Yesu momasuka. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika pamene Yesu ankadya kunyumba kwa Mfarisi wina. Mkazi wina amene ankadziwika kuti ndi wochimwa anafika n’kugwada pafupi ndi mapazi a Yesu, akulira modzimvera chisoni kuti ndi wochimwa. Mayiyo ananyowetsa mapazi a Yesu ndi misozi ndipo ankawapukuta ndi tsitsi lake. Mfarisi amene anaitana Yesu uja ananyansidwa ndipo anamuweruza mumtima mwake chifukwa cholola mayiyu kumuyandikira. Koma Yesu anayamikira mayiyu mokoma mtima chifukwa choti analapa kuchokera pansi pa mtima ndipo anamutsimikizira kuti Yehova wamukhululukira. (Luka 7:36-50) Masiku anonso, anthu amene akuvutika mumtima chifukwa cha machimo amene anachita, amafunika kupita kwa anthu amene angawathandize kukhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ankamasuka kupita kwa Yesu?
N’chifukwa Chiyani Anthu Ankamasuka Kupita kwa Yesu?
12. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti anthu ankamasuka kupita kwa Yesu?
12 Kumbukirani kuti Yesu ankatsanzira ndendende Atate wake wokondedwa wa kumwamba. (Yohane 14:9) Baibulo limatiuza kuti Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” nthawi zonse amakhala pafupi ndi atumiki ake okhulupirika ndiponso aliyense amene amamufunafuna ndi mtima wonse kuti amutumikire. (Salimo 65:2) N’zosangalatsa kudziwa kuti mungathe kufika momasuka kwa munthu wamphamvu ndiponso wofunika kwambiri kuposa wina aliyense m’chilengedwe chonse. Yesu amakonda anthu ngati mmene Atate wake amachitira. M’mitu yakutsogoloku, tikambirana za chikondi chosaneneka chimene Yesu anali nacho. Komabe anthu ankapita kwa Yesu momasuka mwina chifukwa chakuti ankaona mosavuta kuti amawakonda. Tiyeni tione zina mwa zinthu zimene Yesu anachita posonyeza kuti amakonda anthu.
13. Kodi makolo angatsanzire bwanji Yesu?
13 Anthu ankaona mosavuta kuti Yesu amachita chidwi ndi munthu aliyense payekha, ndipo iye sanasinthe ngakhale pamene anali wotanganidwa kwambiri. Monga mmene taonera, makolo aja atabwera ndi ana awo kwa Yesu, iye anawalandirabe ngakhale kuti anali wotanganidwa kwambiri komanso anali ndi udindo waukulu woti akwaniritse. Iye anapereka chitsanzo chabwino kwa makolo. N’zoona kuti kulera ana ndi kovuta kwambiri masiku ano. Komabe n’zofunika kuti ana azitha kulankhula ndi makolo awo momasuka. Ngati ndinu makolo, mwina nthawi zina mumatanganidwa kwambiri moti zimakhala zovuta kucheza ndi ana anu. Koma ngati mwana wanu akukufunani, mungachite bwino kumuuza kuti adikire pang’ono mpaka mutamaliza zomwe mukuchitazo. Mukamachitadi zimene mwamulonjezazo, mwana wanuyo adzaphunzira kukhala woleza mtima. Komanso adzadziwa kuti angathe kubwera nthawi iliyonse kudzakuuzani zimene akufuna kuti mumuthandize.
14-16. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti Yesu achite chozizwitsa chake choyamba, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zinali zodabwitsa kwambiri? (b) Kodi chozizwitsa chimene Yesu anachita ku Kana chimasonyeza kuti iye anali wotani, nanga makolo angaphunzirepo chiyani?
14 Yesu ankasonyeza kuti amakhudzidwa kwambiri ndi zinthu zimene anthu ankada nazo nkhawa. Mwachitsanzo, takumbukirani chozizwitsa choyamba chimene Yesu anachita. Iye anapita kuphwando la ukwati ku Kana, tauni imene inali ku Galileya. Kenako vinyo anatha ndipo zimenezi zinali zochititsa manyazi kwambiri. Zitatero Mariya, mayi a Yesu, anauza mwana wawo zimene zinachitikazo. Kodi Yesu anachita chiyani? Iye anauza anthu amene ankatumikira kuti adzadze madzi m’mbiya zamwala zokwanira 6. Atatunga pang’ono n’kukapatsa woyang’anira phwando, anadabwa kuona kuti anali vinyo wabwino kwambiri. Kodi zimenezi zinali zenizeni kapena kunali kungophimba anthu m’maso? Ayi ndithu, madziwo ‘anawasandutsadi vinyo.’ (Yohane 2:1-11) Kwa nthawi yaitali, anthu akhala akulakalaka kusandutsa zinthu zina kuti zikhale zimene akufuna. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri, akatswiri ena akhala akuyesa kusandutsa mtovu kuti ukhale golide, koma analephera. Nanga bwanji kusandutsa madzi kuti akhale vinyo? Munthu angaone kuti n’zosatheka kusandutsa madzi kuti akhale vinyo chifukwa ndi zinthu zosiyana kwambiri. Koma Yesu anachita chozizwitsa chapadera kwambiri chimenechi paphwando la ukwati, pofuna kuthetsa vuto limene lingaoneke ngati laling’ono. Kodi n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
15 Vuto limeneli silinali laling’ono kwa mkwati ndi mkwatibwi paphwando limeneli. Kale ku Isiraeli, nkhani yochereza alendo inali yofunika kwambiri. Kutha kwa vinyo pa ukwati inali nkhani yaikulu kwa akwatiwo komanso chinali chinthu chochititsa manyazi kwambiri, ndipo zimenezi zikanachititsa kuti asamasangalale akakumbukira tsiku la ukwati wawo. Vuto limeneli linawakhudza kwambiri ndiponso Yesu linamukhudza, n’chifukwa chake anachita chozizwitsacho. Zimenezitu zikutithandiza kudziwa chifukwa chake anthu ankapita kwa Yesu momasuka akakhala ndi mavuto.
16 Apanso makolo angaphunzirepo mfundo yofunika kwambiri. Kodi mumatani mwana wanu akakupezani ndi kukuuzani vuto limene likumudetsa nkhawa? Mwina mungangonyalanyaza vuto lakelo n’kumaganiza kuti ndi laling’ono. Mwinanso mungaone kuti ndi nkhani yoseketsa. Vuto la mwanalo lingaoneke laling’ono mukaliyerekezera ndi mavuto anu. Komabe, kumbukirani kuti vutolo si laling’ono kwa mwanayo. Ngati vutolo likumudetsa nkhawa munthu amene mumamukonda, kodi silingakhalenso lodetsa nkhawa kwa inu? Mukamasonyeza mwana wanu kuti mumakhudzidwa kwambiri ndi zinthu zimene zikumudetsa nkhawa, mwanayo adzaona kuti angathe kukuuzani chilichonse momasuka.
17. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yokhala munthu wofatsa, ndipo n’chifukwa chiyani munthu wofatsa amakhala wolimba mtima kwambiri?
17 Monga mmene tinaonera m’Mutu 3, Yesu anali wofatsa ndiponso wodzichepetsa. (Mateyu 11:29) Kufatsa ndi khalidwe labwino kwambiri ndipo munthu amene ali nalo amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa. Limeneli ndi limodzi mwa makhalidwe amene munthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu ndipo aliyense amene ali ndi khalidwe limeneli amasonyeza nzeru zochokera kwa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23; Yakobo 3:13) Yesu ankakhalabe wofatsa ngakhale pamene anthu amuputa dala. Kufatsa kwake sikunasonyeze kuti anali wosalimba mtima. Pofotokoza khalidwe limeneli katswiri wina anati: “Munthu wofatsa amakhala wolimba mtima kwambiri.” Ndithudi pamafunika kulimba mtima kuti tisapse mtima munthu akatiputa ndiponso kuti tichite zinthu mofatsa. Koma mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kutsanzira Yesu posonyeza kufatsa ndipo zimenezi zidzathandiza kuti anthu azibwera kwa ife momasuka.
18. N’chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti Yesu anali wololera, nanga khalidwe limeneli lingathandize bwanji kuti anthu azibwera kwa ife momasuka?
18 Yesu anali wololera. Pa nthawi ina Yesu ali mumzinda wa Turo, mayi wina anabwera kwa iye kudzamudandaulira kuti mwana wake wamkazi ‘anagwidwa ndi chiwanda chimene chinkamuzunza mwankhanza.’ Katatu konse Yesu anasonyeza kuti sankafuna kumuthandiza. Koyamba, sanamuyankhe chilichonse, kachiwiri anamuuza chifukwa chake samayenera kuchita zimene anamupemphazo ndipo kachitatu, anamuuza fanizo limene linamuthandiza kuti amvetse chifukwa chake sankafuna kumuthandiza. Kodi pamenepa Yesu anasonyeza kuti anali wovuta komanso wosalolera? Kodi Yesu anasonyeza kuti mayiyu wapalamula mlandu poumirira kuti Yesu, yemwe anali mphunzitsi wofunika kwambiri, amuchitire zimene iye akupemphazo? Ayi, mayiyu sankaona choncho koma ankadziwa kuti Yesu amuchitira chifundo. Iye sanangopempha kuti amuthandize, koma anaumirira ngakhale kuti Yesu ankaoneka kuti sakufuna kumuthandiza. Yesu anaona kuti mayiyu anali ndi chikhulupiriro chachikulu chimene chinamupangitsa kuti apitirizebe kupempha, ndipo iye anachiritsa mwana wakeyo. (Mateyu 15:22-28) Ndithudi, anthu ankapita kwa Yesu momasuka chifukwa anali wololera ndiponso ankafunitsitsa kumvetsera anthu akamalankhula.
Kodi Anthu Angabwere kwa Inu Momasuka?
19. Kodi tingadziwe bwanji ngati anthu ena angathe kubweradi kwa ife momasuka?
19 Anthu ambiri amaganiza kuti ndi omasuka ndipo amaona kuti anthu ena angapite kwa iwo mosavuta. Mwachitsanzo, anthu ena audindo, amanena kuti khomo lawo ndi lotseguka ndipo anthu amene akuwayang’anira angathe kuwapeza nthawi iliyonse. Koma Baibulo limatichenjeza mwamphamvu kuti: “Anthu ambiri amanena kuti ali ndi chikondi chokhulupirika, koma ndi ndani amene angapeze munthu wokhulupirika?” (Miyambo 20:6) Zimakhala zosavuta kungonena kuti anthu ena angabwere kwa ife momasuka, koma kodi timatsanziradi Yesu mokhulupirika amene ankasonyeza chikondi m’njira imeneyi? Anthu ena amene amatidziwa bwino ndi amene anganene zoona osati mmene ifeyo timadzionera. Paulo anena kuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Choncho aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu ena amaona kuti ndine wotani? Kodi ndili ndi mbiri yotani?’
20. (a) N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti akulu aziyesetsa kuti anthu azitha kulankhula nawo momasuka? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyembekezera zinthu zimene akulu mumpingo sangakwanitse?
20 Akulu mumpingo amayesetsa kuti anthu azipita kwa iwo momasuka. Iwo amafunitsitsa kuti azikwaniritsa zimene lemba la Yesaya 32:1, 2, limanena kuti: “Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo, malo obisalirapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.” Mkulu angateteze, angatsitsimule ndiponso angalimbikitse ena ngati anthu amatha kupita kwa iye momasuka. N’zoona kuti kuchita zimenezi nthawi zina kumakhala kovuta chifukwa chakuti akulu ali ndi udindo waukulu m’nthawi yovuta ino. Komabe, iwo amayesetsa kuti asaoneke ngati atanganidwa kwambiri moti sangathe kusamalira nkhosa za Yehova. (1 Petulo 5:2) Abale ndi alongo enanso mumpingo amayesetsa kukhala ololera moti sayembekezera zinthu zimene akulu sangakwanitse. Abale ndi alongo akamachita zimenezi amasonyeza kuti ndi odzichepetsa komanso omvera.—Aheberi 13:17.
21. Kodi makolo angatani kuti ana awo azitha kulankhula nawo momasuka, nanga tikambirana chiyani m’mutu wotsatira?
21 Makolo amayesetsa kuti nthawi zonse ana awo azitha kulankhula nawo momasuka ndipo zimenezi n’zofunika kwambiri. Iwo amafuna kuti ana awo adziwe kuti angakhale omasuka kuuza bambo kapena mayi awo zakukhosi kwawo. Choncho, makolo a Chikhristu ayenera kuyesetsa kukhala odekha, ololera ndiponso kuti asamapse mtima msanga mwana wawo akaulula zinazake zimene analakwitsa kapena akanena maganizo olakwika. Makolo akamaphunzitsa ana awo mofatsa, amayesetsa kuti anawo azikhala omasuka kulankhula nawo nthawi iliyonse. Ndipotu, tonsefe timafunitsitsa kuti anthu azitha kubwera kwa ife momasuka ngati mmene zinalili ndi Yesu. M’mutu wotsatira, tikambirana za chifundo, chimene ndi limodzi mwa makhalidwe akuluakulu a Yesu, amene ankachititsa kuti anthu azipita kwa iye momasuka.