MUTU 4
Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani?
1, 2. (a) Kodi kungodziwa dzina la munthu winawake wotchuka ndiye kuti mukumudziwadi munthuyo? Fotokozani. (b) Kodi anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana otani onena za Yesu?
PADZIKO lapansili pali anthu ambiri otchuka. Mwina inuyo mumadziwa dzina la munthu winawake wotchuka. Koma kungodziwa dzina lake sikutanthauza kuti mukumudziwa bwinobwino. N’kutheka kuti simukudziwa mbiri yake, khalidwe lake komanso kuti amachita zotani.
2 N’kutheka kuti munamvapo za Yesu Khristu, ngakhale kuti anakhala padzikoli zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Komatu anthu ambiri sadziwa kuti Yesu anali munthu wotani. Ena amati anali munthu wabwino chabe, ena amati anali mneneri, pamene ena amakhulupirira kuti ndi Mulungu. Koma kodi zimenezi ndi zoona?—Onani Mawu Akumapeto 12.
3. N’chifukwa chiyani muyenera kudziwa Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu?
3 Mukufunika kumudziwa Yesu molondola chifukwa Baibulo limati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Lembali likusonyeza kuti ngati mutadziwa Yehova ndi Yesu molondola, mukhoza kudzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Yohane 14:6) Kudziwa Yesu kungakuthandizeninso chifukwa iye ndi chitsanzo chabwino cha mmene tiyenera kukhalira ndi anthu ena. (Yohane 13:34, 35) M’mutu woyamba, tinaphunzira za Mulungu. Tsopano tiphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu.
IFETU TAPEZA MESIYA
4. Kodi mawu akuti “Mesiya” ndi “Khristu” amatanthauza chiyani?
4 Zaka zambirimbiri Yesu asanabadwe, Baibulo linaneneratu kuti Yehova adzatumiza Mesiya, kapena kuti Khristu. Mawu akuti “Mesiya” ndi achiheberi, ndipo mawu akuti “Khristu” ndi achigiriki. Mawu awiri onsewa amatanthauza kuti Mulungu ndi amene adzasankhe Mesiya ndipo adzamupatsa udindo wapadera. Mesiya ndi amene adzakwaniritse zinthu zonse zimene Mulungu analonjeza ndipo angakuthandizeninso ngakhale panopo. Koma Yesu asanabadwe anthu ambiri ankadzifunsa kuti, ‘Kodi Mesiya ameneyu adzakhala ndani?’
5. Kodi ophunzira a Yesu ankakhulupirira kuti iye analidi Mesiya?
5 Ophunzira a Yesu sankakayikira zoti iye ndi Mesiya amene Mulungu ananeneratu kuti adzabwera. (Yohane 1:41) Mwachitsanzo, Simoni Petulo anauza Yesu kuti: “Ndinu Khristu.” (Mateyu 16:16) Kodi n’chiyani chingatithandize kutsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya?
6. Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu okhulupirika kuti adziwe Mesiya?
6 Zaka zambirimbiri Yesu asanabadwe, aneneri a Mulungu analemba zinthu zambiri zokhudza Mesiya, zomwe zikanathandiza anthu kumudziwa mosavuta. Kodi zimenezi zikanawathandiza bwanji? Tiyerekeze kuti mwatumidwa kupita kudepoti ya basi, komwe kumakhala anthu ambirimbiri, kuti mukachingamire munthu amene simunamuonepo. Ngati munthu wina atakufotokozerani bwino zina ndi zina zokhudza munthuyo, mukhoza kukamuzindikira mosavuta. Mofanana ndi zimenezi, Yehova anagwiritsa ntchito aneneri pofuna kudziwitsa anthu zimene Mesiya adzachite komanso zomwe zidzamuchitikire. Kukwaniritsidwa kwa maulosi onsewo kumathandiza anthu okhulupirika kudziwa kuti Yesu ndi Mesiya.
7. Kodi ndi maulosi awiri ati omwe amatsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya?
7 Tiyeni tikambirane maulosi awiri onena za Mesiya. Choyamba, kudakali zaka 700 kuti Yesu abadwe, Mika ananeneratu kuti Mesiya adzabadwira m’tawuni yaing’ono ya Betelehemu. (Mika 5:2) Ndipo Yesu anabadwiradi kumeneko. (Mateyu 2:1, 3-9) Chachiwiri, Danieli ananeneratu kuti Mesiya adzaonekera m’chaka cha 29 C.E. (Danieli 9:25) Zimene takambiranazi ndi zitsanzo ziwiri zokha za maulosi ambirimbiri amene amatsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya amene Mulungu ananeneratu kuti adzabwera.—Onani Mawu Akumapeto 13.
8, 9. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachitika pamene Yesu ankabatizidwa zimene zimasonyeza kuti iye ndi Mesiya?
8 Yehova anapereka umboni wokwanira wotsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya. Mulungu analonjeza Yohane M’batizi kuti adzamupatsa chizindikiro chomuthandiza kudziwa Mesiya. M’chaka cha 29 C.E., Yesu atapita kwa Yohane kuti akabatizidwe mumtsinje wa Yorodano, Yohane anaona chizindikirocho. Baibulo limanena kuti: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera. Panamvekanso mawu ochokera kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.’” (Mateyu 3:16, 17) Yohane ataona komanso kumva zimenezi, anadziwa kuti Yesu ndi Mesiya. (Yohane 1:32-34) Patsiku limeneli, Yehova atamudzoza ndi mzimu woyera, m’pamene Yesu anakhala Mesiya, kutanthauza kuti anasankhidwa ndi Mulungu kukhala Mtsogoleri ndiponso Mfumu.—Yesaya 55:4.
9 Kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo, mawu amene Yehova analankhula ndiponso chizindikiro chomwe anapereka pa nthawi imene Yesu ankabatizidwa, zimatsimikizira kuti Yesu analidi Mesiya. Koma kodi Yesu anachokera kuti, nanga anali munthu wotani? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi.
KODI YESU ANACHOKERA KUTI?
10. Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani ponena za moyo wa Yesu asanabwere padziko lapansi?
10 Baibulo limanena kuti Yesu anakhala ndi moyo kumwamba kwa zaka zambiri asanabwere padziko lapansi pano. Mika ananena kuti Mesiya “wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira.” (Mika 5:2) Yesu ananenanso yekha maulendo angapo kuti ankakhala kumwamba asanabwere padziko lapansi pano. (Werengani Yohane 3:13; 6:38, 62; 17:4, 5.) Yesu ankagwirizana kwambiri ndi Yehova kuyambira adakali kumwamba.
11. N’chifukwa chiyani Yesu ali Mwana wapadera kwambiri wa Yehova?
11 Yesu ndi Mwana wapadera kwambiri wa Yehova. Izi zili choncho chifukwa Mulungu anamulenga asanalenge angelo, anthu komanso zinthu zina zonse. N’chifukwa chake Yesu amatchedwa “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”a (Akolose 1:15) Pali chifukwa chinanso chimene chimapangitsa Yesu kukhala wapadera kwa Yehova. Chifukwa chake n’choti ndi Yesu yekha amene analengedwa ndi Mulungu mwiniwake osagwiritsira ntchito winawake. N’chifukwa chake amatchedwa kuti ndi “Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Ndi Yesu yekhanso amene Mulungu anagwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse. (Akolose 1:16) Komanso ndi Yesu yekha amene amatchedwa “Mawu,” chifukwa Yehova ankamugwiritsa ntchito popereka mauthenga ndi malangizo kwa angelo ndi anthu.—Yohane 1:14.
12. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu si wofanana ndi Mulungu?
12 Anthu ena amakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu ndi munthu mmodzi. Komatu Baibulo silinena zimenezi. Baibulo limanena kuti Yesu anachita kulengedwa, kutanthauza kuti poyamba kunalibe. Koma Yehova, yemwe analenga zinthu zonse, wakhala alipo kuyambira kalekale. (Salimo 90:2) Yesu sanayambe waganizapo zofuna kukhala wofanana ndi Mulungu. Baibulo limanena momveka bwino kuti Atate ndi wamkulu kuposa Mwana. (Werengani Yohane 14:28; 1 Akorinto 11:3.) Yehova yekha ndi amene ali “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 17:1) Iye ndi wamkulu komanso wamphamvu kuposa wina aliyense.—Onani Mawu Akumapeto 14.
13. N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Yesu ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo”?
13 Yehova ndi Mwana wake, Yesu, ankagwira ntchito limodzi mogwirizana kwa zaka mabiliyoni ambirimbiri zinthu zakumwamba ndiponso padziko lapansi zisanalengedwe. Iwo ayenera kuti ankakondana kwambiri. (Yohane 3:35; 14:31) Yesu ankatsanzira kwambiri makhalidwe a atate wake moti Baibulo limamutchula kuti ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.”—Akolose 1:15.
14. Kodi zinatheka bwanji kuti Mwana wapadera wa Yehova abadwe ngati munthu?
14 Mwana wapadera wa Yehovayu analolera kuchoka kumwamba n’kudzabadwa padziko lapansi ngati munthu. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Yehova anapanga zinthu zodabwitsa chifukwa anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba n’kuuika m’mimba mwa namwali wina, dzina lake Mariya. Panalibe mwamuna amene anagona naye. Zimenezi zinachititsa kuti Mariya abereke mwana wopanda uchimo, ndipo anam’patsa dzina lakuti Yesu.—Luka 1:30-35.
KODI YESU ANALI MUNTHU WOTANI?
15. Kodi n’chiyani chingatithandize kumudziwa bwino Yehova?
15 Mukhoza kudziwa zinthu zimene Yesu ankachita ndiponso makhalidwe ake ngati mutawerenga mabuku a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Popeza Yesu ali ndi makhalidwe ofanana ndi a Atate wake, zimene mungawerengezo zingakuthandizeni kuti mumudziwe bwino Yehova. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.”—Yohane 14:9.
16. Kodi Yesu ankaphunzitsa za chiyani? Nanga zomwe ankaphunzitsazo ankazitenga kuti?
16 Anthu ambiri ankamutchula Yesu kuti “Mphunzitsi.” (Yohane 1:38; 13:13) Chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene ankaphunzitsa chinali “uthenga wabwino wa ufumu.” Kodi Ufumu umenewu ndi uti? Ndi boma la Mulungu lakumwamba limene lizidzalamulira dziko lonse lapansi ndipo lidzabweretsa madalitso ambiri kwa anthu amene amamvera Mulungu. (Mateyu 4:23) Zinthu zonse zimene Yesu ankaphunzitsa zinkachokera kwa Yehova. Iye anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.” (Yohane 7:16) Yesu ankadziwa kuti Yehova akufuna kuti anthu amve uthenga wabwino woti Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi.
17. Kodi Yesu ankaphunzitsa kuti? Nanga n’chifukwa chiyani ankadzipereka kwambiri pophunzitsa ena?
17 Kodi Yesu ankaphunzitsa kuti? Kulikonse kumene kunkapezeka anthu. Ankaphunzitsa m’mizinda, m’midzi, m’misika, m’malo opemphereramo ndiponso m’nyumba za anthu. Sankayembekezera kuti anthu abwere okha kumene iye ali. Nthawi zambiri iyeyo ndi amene ankapita kumene kuli anthuwo. (Maliko 6:56; Luka 19:5, 6) Nthawi zonse Yesu ankamvera Atate wake moti ankadzipereka kwambiri pogwira ntchito yophunzitsa anthu chifukwa ankadziwa kuti ndi zimene Mulungu akufuna kuti azichita. (Yohane 8:28, 29) Koma palinso chifukwa china chimene chinkachititsa Yesu kuti azilalikira. Iye ankamvera chisoni anthu. (Werengani Mateyu 9:35, 36.) Yesu ankaona kuti atsogoleri achipembedzo sankaphunzitsa anthu awo zinthu zoona zokhudza Mulungu ndiponso Ufumu wake. Choncho iye ankafunitsitsa kuthandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wabwino.
18. Kodi ndi makhalidwe ati a Yesu omwe amakusangalatsani kwambiri?
18 Yesu anali munthu wachikondi komanso woganizira ena. Anali wokoma mtima komanso wochezeka, moti ngakhale ana ankamukonda. (Maliko 10:13-16) Yesu sankachita zinthu mokondera, moti ankadana ndi katangale ndiponso zinthu zopanda chilungamo. (Mateyu 21:12, 13) Pa nthawi imeneyo akazi analibe ufulu wambiri ndipo sankalemekezedwa. Koma Yesu ankawalemekeza kwambiri. (Yohane 4:9, 27) Yesu analinso wodzichepetsa kwambiri. Mwachitsanzo, tsiku lina anasambitsa mapazi a ophunzira ake ndipo ntchito imeneyi nthawi zambiri inkagwiridwa ndi wantchito wamba.—Yohane 13:2-5, 12-17.
19. Kodi ndi chitsanzo chiti chomwe chikusonyeza kuti Yesu ankadziwa zomwe anthu amafunikira ndiponso ankafunitsitsa kuwathandiza?
19 Yesu ankadziwa zomwe anthu amafunikira ndipo ankafunitsitsa kuwathandiza. Iye anasonyeza zimenezi pamene anagwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anam’patsa pochiritsa anthu odwala. (Mateyu 14:14) Mwachitsanzo, munthu wina wakhate anabwera kwa Yesu n’kunena kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” Yesu anakhudzidwa kwambiri poganizira ululu umene munthuyo ankamva. Chifukwa chomumvera chisoni, iye anatambasula dzanja lake n’kumugwira, kenako anamuuza kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo munthu wodwalayo anachira. (Maliko 1:40-42) Kodi mukuganiza kuti munthuyu anamva bwanji atachiritsidwa?
ANALI WOKHULUPIRIKA KWA ATATE WAKE MOYO WAKE WONSE
20, 21. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yokhala wokhulupirika kwa Mulungu?
20 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yokhala wokhulupirika kwa Mulungu. Iye anakhalabe wokhulupirika kwa Atate wake ngakhale pamene adani ake ankamutsutsa komanso kumuzunza. Mwachitsanzo iye sanakopeke pamene Satana ankayesetsa kumunyengerera. (Mateyu 4:1-11) Pa nthawi ina, abale ake ena sankakhulupirira kuti iye ndi Mesiya ndipo ankamunena kuti “wachita misala,” koma iye anapitirizabe kugwira ntchito imene Mulungu anam’patsa. (Maliko 3:21) Pamene adani ake ankamuchitira zinthu zankhanza, Yesu anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ndipo sanabwezere.—1 Petulo 2:21-23.
21 Yesu anakhalabe wokhulupirika ngakhale pamene adani ake ankamuzunza mpaka kumupha mwankhanza. (Werengani Afilipi 2:8.) Taganizirani zimene zinamuchitikira tsiku limene anaphedwa. Anamangidwa, anthu ankamunenera zinthu zabodza, oweruza achinyengo anamugamula kuti ndi wolakwa, anthu ambirimbiri ankamuseka ndiponso asilikali anamuzunza kenako n’kumukhomerera pamtengo. Ndipo pamene ankamwalira anafuula kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” (Yohane 19:30) Patapita masiku atatu, Yehova anamuukitsa ndipo anakhalanso mzimu ngati mmene analili poyamba. (1 Petulo 3:18) Patapita milungu ingapo, Yesu anabwerera kumwamba ndipo “anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu” kuyembekezera kuti Mulungu am’patse Ufumu.—Aheberi 10:12, 13.
22. Kodi tili ndi mwayi wotani chifukwa choti Yesu anakhalabe wokhulupirika kwa Atate wake?
22 Chifukwa choti Yesu anakhalabe wokhulupirika kwa Atate wake, panopa tili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso monga mmene Yehova ankafunira. M’mutu wotsatira tikambirana mmene imfa ya Yesu inathandizira kuti zimenezi zikhale zotheka.
a Yehova amatchedwa Atate chifukwa ndi Mlengi. (Yesaya 64:8) Yesu amatchedwa Mwana wa Mulungu chifukwa analengedwa ndi Yehova. Angelo ndiponso anthu amatchedwanso ana a Mulungu.—Yobu 1:6; Luka 3:38.