Yambani Kuwerenga Baibulo
Mukhoza kumasangalala powerenga Baibulo. Mfundo zotsatirazi zikuthandizani kudziwa mmene mungayambire. Sankhani nkhani imene ikukusangalatsani kenako werengani malemba omwe asonyezedwawo.
Anthu Otchuka Komanso Nkhani Zawo
Nowa komanso Chigumula: Genesis 6:9–9:19
Mose ali pa Nyanja Yofiira: Ekisodo 13:17–14:31
Rute ndi Naomi: Rute machaputala 1 mpaka 4
Davide ndi Goliati: 1 Samueli chaputala 17
Abigayeli: 1 Samueli 25:2-35
Danieli ali m’dzenje la mikango: Danieli chaputala 6
Elizabeti ndi Mariya: Luka chaputala 1 ndi 2
Nzeru Zothandiza pa Moyo Wathu
Moyo wa banja: Aefeso 5:28, 29, 33; 6:1-4
Mabwenzi: Miyambo 13:20; 17:17; 27:17
Pemphero: Salimo 55:22; 62:8; 1 Yohane 5:14
Ulaliki wa Paphiri: Mateyu machaputala 5 mpaka 7
Ntchito: Miyambo 14:23; Mlaliki 3:12, 13; 4:6
Nkhani Zomwe Zingakuthandizeni . . .
Mukakhumudwa: Salimo 23; Yesaya 41:10
Mukaferedwa: 2 Akorinto 1:3, 4; 1 Petulo 5:7
Mukamadziimba mlandu: Salimo 86:5; Ezekieli 18:21, 22
Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya . . .
Masiku otsiriza: Mateyu 24:3-14; 2 Timoteyo 3:1-5
Chiyembekezo cha m’tsogolo: Salimo 37:10, 11, 29; Chivumbulutso 21:3, 4
ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Kuti muone nkhani yonse, muziwerenga chaputala kapena machaputala onse osati kungowerenga mavesi omwe asonyezedwa okhawo. Chongani chaputala chilichonse chomwe mwamaliza kuwerenga pogwiritsa ntchito tchati chakuti, “Chongani Machaputala Omwe Mwawerenga” chimene chili kumapeto kwa bukuli. Khalani ndi cholinga chowerenga Baibulo tsiku lililonse.