PHUNZIRO 25
Kodi Cholinga cha Mulungu Ndi Choti Tikhale Ndi Moyo Wotani?
Baibulo limanena kuti munthu “amakhala ndi moyo waufupi, wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Kodi Mulungu amafuna kuti tizikhala ndi moyo woterewu? Ngati si choncho, nanga cholinga chake ndi chotani? Kodi cholinga chakechi chidzakwaniritsidwa? Baibulo lili ndi mayankho otonthoza a mafunso amenewa. Tiyeni tiwaone.
1. Kodi Yehova amafuna kuti tizikhala ndi moyo wotani?
Yehova amafuna kuti tizikhala moyo wabwino kwambiri. Iye atalenga Adamu ndi Hava omwe ndi anthu oyambirira, anawaika m’Paradaiso wokongola, wotchedwa munda wa Edeni. Kenako “Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.’” (Genesis 1:28) Yehova ankafuna kuti iwo abereke ana, asamalire dziko lonse lapansi kuti likhale paradaiso ndiponso kuti azisamalira zinyama. Cholinga chake chinali chakuti anthu onse akhale ndi thanzi labwino n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale.
Ngakhale kuti masiku ano anthu sitikukhala ndi moyo umene Mulungu ankafunawu,a cholinga chake sichinasinthe. (Yesaya 46:10, 11) Mulungu amafunabe kuti anthu amene amamumvera adzakhale ndi moyo wopanda mavuto mpaka kalekale.—Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.
2. Tingatani kuti tizisangalala ndi moyo panopa?
Yehova anatilenga m’njira yakuti tizitha kuzindikira “zosowa zathu za uzimu,” kutanthauza kuti timakhala ndi mtima wofuna kumudziwa ndi kumulambira. (Werengani Mateyu 5:3-6.) Iye amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba, ‘tiziyenda m’njira zake zonse, kumukonda’ komanso kumutumikira ‘ndi mtima wathu wonse.’ (Deuteronomo 10:12; Salimo 25:14) Zimenezi zingatithandize kuti tizisangalala ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. Tikamatumikira Yehova timakhala ndi moyo watanthauzo chifukwa chakuti timachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza chikondi chachikulu chimene Yehova anasonyeza pamene ankalenga dzikoli kuti anthufe tikhalemo komanso zimene Mawu ake amanena zokhudza cholinga cha moyo.
3. Yehova amafuna kuti anthu azikhala moyo wabwino kwambiri
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansi lokongola chonchi?
Werengani Mlaliki 3:11, kenako mukambirane funso ili:
Malinga ndi lembali, mwaphunzira zotani zokhudza Yehova?
4. Cholinga cha Yehova sichinasinthe
Werengani Salimo 37:11, 29 ndi Yesaya 55:11, kenako mukambirane funso ili:
Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga cha Yehova chokhudza anthufe sichinasinthe?
5. Tikamalambira Yehova timakhala ndi moyo wosangalala
Kudziwa cholinga cha moyo, kumatithandiza kuti tizikhala mosangalala. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi kudziwa kuti moyo uli ndi cholinga kunathandiza bwanji Terumi?
Werengani Mlaliki 12:13, kenako mukambirane funso ili:
Tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova pa zinthu zabwino zambiri zimene watichitira?
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?”
Mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova amafuna kuti tizikhala moyo wabwino kwambiri wopanda mavuto padziko pano. Tikamamulambira ndi mtima wonse timakhala ndi moyo wosangalala kwambiri ngakhale panopa.
Kubwereza
Kodi Yehova ankafuna kuti Adamu ndi Hava azikhala moyo wotani?
Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga cha Mulungu chokhudza anthu sichinasinthe?
Mungatani kuti muzikhaladi moyo wosangalala?
ONANI ZINANSO
Onani umboni wosonyeza kuti munda wa Edeni unalipodi.
“Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2011)
Onani chifukwa chake sitikayikira kuti dzikoli lidzakhalapo mpaka kalekale.
Onani mmene Baibulo lingakuthandizireni kudziwa cholinga cha moyo.
Munthu yemwe ankaganiza kuti ali ndi chilichonse pa moyo anazindikira kuti ankasowekera chinachake. Onani chimene chinamuthandiza kudziwa cholinga cha moyo.
a M’phunziro lotsatira, mudzaphunzira chifukwa chake masiku ano anthufe timakumana ndi mavuto.