PHUNZIRO 26
N’chifukwa Chiyani Anthu Amavutika?
Zinthu zoipa zikachitika anthu amadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani zimenezi zachitika?” N’zosangalatsa kuti Baibulo limayankha funso limeneli.
1. Kodi Satana anachita chiyani kuti zoipa ziyambe kuchitika padzikoli?
Satana Mdyerekezi anapandukira Mulungu. Satana ankafuna kulamulira ena choncho anapusitsa anthu oyambirira, Adamu ndi Hava kuti nawonso apandukire Mulungu. Satana anachita zimenezi pouza Hava bodza. (Genesis 3:1-5) Anachititsa kuti Hava aziganiza kuti Yehova akumumana zinthu zinazake zabwino. Iye ankatanthauza kuti anthu akhoza kumakhala osangalala ngakhale atapanda kumvera Mulungu. Satana ananena bodza loyamba pouza Hava kuti sadzafa. N’chifukwa chake Baibulo limatchula Satana kuti “ndi wabodza komanso tate wake wabodza.”—Yohane 8:44.
2. Kodi Adamu ndi Hava anasankha kuchita chiyani?
Yehova anapatsa Adamu ndi Hava chilichonse chomwe ankafunikira. Iye anawauza kuti akhoza kudya zipatso za mtengo wina uliwonse wa m’munda wa Edeni kupatulapo umodzi wokha. (Genesis 2:15-17) Koma Adamu ndi Hava anasankha kudya zipatso za mtengo womwe anawaletsa. Hava “anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya.” Pambuyo pake, Adamu “nayenso anadya.” (Genesis 3:6) Onse sanamvere Mulungu. Chifukwa chakuti Adamu ndi Hava anali angwiro, zinali zosavuta kuti asankhe kuchita chabwino. Koma iwo anasankha kusamvera Mulungu. Pamene anachita zimenezi anachimwa ndipo anakana kuti Mulungu aziwalamulira. Zimene anachitazi zinawabweretsera mavuto aakulu.—Genesis 3:16-19.
3. Kodi zimene Adamu ndi Hava anasankha kuchita zinatikhudza bwanji?
Adamu ndi Hava atachimwa, anapatsira uchimowo ana awo onse. Ponena za Adamu Baibulo limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse.’—Aroma 5:12.
Anthufe timavutika pa zifukwa zosiyanasiyana. Nthawi zina timavutika chifukwa chakuti sitinasankhe zinthu mwanzeru. Nthawi zinanso timavutika chifukwa chakuti anthu ena asankha zinthu molakwika. Penanso timavutika chifukwa chakuti takumana ndi zinthu zosayembekezereka.—Werengani Mlaliki 9:11.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu si amene amachititsa kuti anthu tizivutika padzikoli komanso mmene amamvera tikamavutika.
4. Ndi ndani amene amachititsa kuti tizivutika?
Anthu ambiri amakhulupilira kuti Mulungu ndi amene akulamulira dzikoli. Kodi zimenezi ndi zoona? Onerani VIDIYO.
Werengani Yakobo 1:13 ndi 1 Yohane 5:19, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?
5. Kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji kungochokera pamene Satana anayamba kulamulira?
Werengani Genesis 3:1-6, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi bodza liti limene Satana ananena?—Onani vesi 4 ndi 5.
Kodi Satana anachititsa bwanji anthu kuganiza kuti Yehova amawamana zinthu zabwino?
Kodi zimene Satana ananena, zinasonyeza bwanji bodza lakuti anthu akhoza kumasangalalabe ngakhale Yehova atapanda kuwalamulira?
Werengani Mlaliki 8:9, kenako mukambirane funso ili:
Kungochokera pamene Yehova anasiya kulamulira anthu, kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji padzikoli?
Adamu ndi Hava anali angwiro ndipo ankakhala m’Paradaiso. Koma iwo anasankha kumvera Satana n’kupandukira Yehova
Adamu ndi Hava atapandukira Mulungu anthu onse anakhala ochimwa ndipo anayamba kuvutika komanso kumwalira
Yehova adzathetsa uchimo, kuvutika komanso imfa. Zimenezi zikadzachitika anthu adzakhala angwiro m’Paradaiso padziko lapansi
6. Anthufe tikamavutika Yehova zimamukhudza kwambiri
Kodi Mulungu zimamukhudza anthufe tikamavutika? Tiyeni tione zimene Mfumu Davide komanso mtumwi Petulo analemba. Werengani Salimo 31:7 ndi 1 Petulo 5:7, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti Yehova amaona mavuto amene timakumana nawo ndiponso amatisamalira?
7. Mulungu adzathetsa mavuto onse amene anthufe timakumana nawo
Werengani Yesaya 65:17 ndi Chivumbulutso 21:3, 4, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani n’zotonthoza kudziwa kuti Yehova adzathetsa mavuto onse amene tikukumana nawo?
Kodi mukudziwa?
Satana atanena bodza lake loyamba, anachititsa kuti anthu aziona ngati Yehova ndi woipa. Zimenezi zinawononga mbiri ya Yehova yemwe ndi wolamulira wabwino komanso wachikondi. Posachedwapa Yehova adzayeretsa dzina lake akadzathetsa mavuto onse amene anthu akukumana nawo. M’mawu ena tingati adzasonyeza kuti ulamuliro wake wokha ndiwo wabwino kwambiri. Kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri m’chilengedwe chonse.—Mateyu 6:9, 10.
ZIMENE ENA AMANENA: “Ndi cholinga cha Mulungu kuti tizivutika.”
Kodi mungayankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Satana Mdyerekezi komanso Adamu ndi Hava ndi amene anayambitsa mavuto onse amene akuchitika padzikoli. Komabe Yehova amakhudzidwa kwambiri tikamavutika ndipo posachedwapa adzathetsa mavuto onse.
Kubwereza
Kodi ndi bodza liti limene Satana Mdyerekezi anauza Hava?
Kodi kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunakhudza bwanji tonsefe?
Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amatidera nkhawa tikamakumana ndi mavuto?
ONANI ZINANSO
Onani zimene mawu oti tchimo amatanthauza m’Baibulo.
Werengani kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhani imene Satana Mdyerekezi anayambitsa m’munda wa Edeni.
“N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthufe Tizivutika?” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2014)
Fufuzani mayankho otonthoza a funso lovuta kwambiri.
Onani mmene Baibulo linathandizira munthu wina amene anakumana ndi mavuto pa moyo wake.