Nkhawa
Kodi muli ndi nkhawa chifukwa choopa mavuto monga umphawi, njala ndi kusowa pokhala?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mlr 3:19—Mneneri Yeremiya limodzi ndi anthu ena ambiri anasowa pokhala mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa
2Ak 8:1, 2; 11:27—Akhristu a ku Makedoniya anali pa umphawi wadzaoneni, mtumwi Paulo nayenso ankasowa zinthu monga chakudya, zovala ndi pokhala
Malemba otonthoza:
Onaninso De 24:19
Kodi muli ndi nkhawa chifukwa choopa kuti simungapeze anzanu, muzingokhala nokhanokha kapenanso simungakondedwe?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Mf 18:22; 19:9, 10—Mneneri Eliya ankaona kuti watsala yekhayekha monga mtumiki wokhulupirika wa Yehova
Yer 15:16-21—Mneneri Yeremiya ankadziona kuti ali yekhayekha pakati pa anthu omwe ankakonda kumangosangalala m’malo momvetsera uthenga wake
Malemba otonthoza:
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
1Mf 19:1-19—Yehova anathandiza mneneri Eliya pomupatsa madzi ndi chakudya, kumumvetsera pamene ankafotokoza nkhawa zake, komanso kumulimbikitsa pomukumbutsa kuti Iye ndi wamphamvu
Yoh 16:32, 33—Yesu ankadziwa kuti otsatira ake adzamusiya yekhayekha koma ankadziwanso kuti Yehova ali naye nthawi zonse