Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi ndi liti pamene ulamuliro wa Britain ndi America unakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa 7 wotchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo?
▪ Chifaniziro chachikulu chimene Mfumu Nebukadinezara inalota sichiimira maulamuliro onse amphamvu apadzikoli. (Dan. 2:31-45) Chimangoimira maulamuliro asanu amene analamulira kuyambira nthawi ya Danieli, omwe analowerera kwambiri pa zochita za anthu a Mulungu.
Zimene Danieli anafotokoza pomasulira chifanizirocho zinasonyeza kuti ulamuliro wa Britain ndi America udzachokera mu ulamuliro wa Roma osati kuugonjetsa. Danieli anaona kuti miyendo ya chifanizirochi inali yachitsulo ndipo chitsulocho chinafika mpaka kumapazi ndi kuzala zakumapazi. (Koma chitsulo cha kumapazi ndi zala chinasakanizidwa ndi dongo.)a Zimenezi zinasonyeza kuti ulamuliro wa Britain ndi America udzachokera m’miyendo yachitsulo. Mbiri yakale ikusonyeza kuti izi n’zimene zinachitikadi. Dziko la Britain linali mu ulamuliro wa Roma ndipo linayamba kukhala lamphamvu chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700. Kenako dziko la United States nalonso linakhala lamphamvu. Koma pa nthawiyi, ulamuliro wamphamvu padziko wa 7 wotchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo unali usanayambe. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa pa nthawiyi mayiko a Britain ndi United States anali asanachitire limodzi zinthu zikuluzikulu. Koma anachitira limodzi zinthu pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse.
Pa nthawi imeneyo, “ana a ufumu” ankagwira ntchito yawo makamaka m’dziko la United States. Likulu lawo linali m’dzikoli, ku Brooklyn ku New York. (Mat. 13:36-43) Koma Akhristu odzozedwa ankalalikiranso m’mayiko amene ankalamulidwa ndi ufumu wa Britain. Pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, dziko la Britain linachita mgwirizano wapadera ndi dziko la United States pomenyana ndi adani awo. Chifukwa cha nkhondoyo, kunali mzimu wokonda kwambiri dziko ku Britain ndi ku United States. Zimenezi zinachititsa kuti mayikowa ayambe kudana ndi anthu omwe anali mbali ya mbewu ya “mkazi” wa Mulungu. Analetsa mabuku awo ndipo anamanga anthu amene ankatsogolera pa ntchito yolalikira.—Chiv. 12:17.
Malinga ndi zimene ulosi wa m’Baibulo umanena, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa 7 unali usanakhazikitsidwe pamene dziko la Britain linayamba kukhala lamphamvu chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700. M’malomwake, unakhazikitsidwa chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye.b
[Mawu a M’munsi]
a Ulamuliro wa Britain ndi America uli ngati chitsulo. Koma dongo limene linasakanizidwa ndi chitsulocho likuimira zinthu zimene anthu ena amene ali pansi pa ulamulirowu akuchita. Dongoli lakhala likuchititsa kuti ulamulirowu usakhale wamphamvu kwambiri.
b Zimenezi zikusintha zimene zinalembedwa m’buku la Ulosi wa Danieli patsamba 57, ndime 24, komanso zimene zili patchati cha patsamba 56 ndi 139.
[Chithunzi patsamba 19]
Abale 8 omwe ankatumikira ku likulu ku Brooklyn anamangidwa mu June 1918