MBIRI YA MOYO WANGA
“Ndaphunzira Zambiri Kuchokera kwa Ena”
USIKU umenewo kunali mdima wandiweyani ndipo ndinali kumapiri a ku Algeria, limodzi ndi asilikali anzanga a ku France. Pa nthawiyo, nkhondo inali itafika povuta kwambiri. Mfuti yanga ili m’manja, ndinali ndekhandekha pamalo amene tinkalondera, nditabisala kuseri kwa matumba a mchenga. Mwadzidzidzi, panayamba kumveka kuti chinachake chikubwera komwe ndinali. Ndinachita mantha kwambiri. Ndinali nditangokwanitsa kumene zaka za m’ma 20 ndipo sindinkafuna kupha munthu kapena kuphedwa. Choncho ndinafuula kupempha Mulungu kuti andithandize.
Zinthu zomwe zinachitika tsiku limeneli zinachititsa kuti ndiyambe kufuna kudziwa Mlengi. Koma ndisanafotokoze zinanso zimene zinachitika usiku umenewo, ndifotokoze kaye zimene zinachitika ndili mwana zomwe zinandithandiza kuti ndiyambe kufuna kudziwa Mulungu.
ZIMENE NDINAPHUNZIRA KWA BAMBO ANGA
Ndinabadwa mu 1937 ku Guesnain, tauni ina yakumpoto kwa France komwe kuli migodi. Ndinaphunzira kufunika kogwira ntchito mwakhama kwa bambo anga, omwe ankagwira ntchito mumgodi wamalasha. Ndinatengeranso mtima wawo wokonda chilungamo, womwe unkawachititsa kuti azimenyera ufulu anthu ogwira ntchito m’migodi, omwe ankagwira ntchito m’malo oopsa komanso ankachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Pofuna kuthandiza anthuwa, bambo analowa m’mabungwe omenyera ufulu wa anthu ogwira ntchito m’migodi. Iwo ankakhumudwanso chifukwa cha chinyengo chimene ansembe ankachita. Ansembe ambiri ankakhala moyo wofewa, koma ankapempha chakudya komanso ndalama kwa anthuwa, omwe ankavutika kupeza zofunika pa moyo. Bambowa anakwiya kwambiri ndi zimene ansembe ankachitazi, moti sanandiphunzitse chilichonse chokhudza zachipembedzo. Ndipotu sindinakambiranepo nawo zokhudza Mulungu.
Pamene ndinkakula, inenso ndinayamba kudana ndi zinthu zopanda chilungamo. Zinthu zopanda chilungamo zimenezi zikuphatikizapo tsankho limene ena ankachitira anthu a m’mayiko ena omwe ankakhala ku France. Ndinkasewera mpira ndi ana a anthu ochokera m’mayiko ena komanso ndinkasangalala kucheza nawo. Kuwonjezera apo, mayi anga anali a ku Poland, osati ku France. Choncho ndinkafunitsitsa kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana azikhala limodzi mwamtendere ndiponso azichitiridwa zinthu mofanana.
NDINAYAMBA KUGANIZIRA KWAMBIRI ZOKHUDZA MOYO
Ndinalowa usilikali mu 1957 mogwirizana ndi malamulo a boma. N’chifukwa chake ndinapezeka usiku ndili kumapiri a Algeria monga ndafotokozera kumayambiriro kuja. Nditafuula kupempha Mulungu kuti andithandize, ndinaona kuti chimene chinkabwera komwe ndinali, si msilikali wa m’gulu la adani, koma mbidzi. Pamenepa mtima wanga unakhala m’malo. Zimenezi komanso nkhondo imene inkachitikayo, zinandithandiza kuti ndiganizire kwambiri zokhudza moyo. Mwachitsanzo, ndinayamba kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Kodi Mulungu amatiganizira? Kodi zidzatheka kukhala ndi mtendere padzikoli?’
Kenako nditapita kutchuthi kwa makolo anga ndinakumana ndi wa Mboni za Yehova. Iye anandipatsa Baibulo lomwe ndinayamba kuliwerenga nditabwerera ku Algeria. Lemba limene linandikhudza kwambiri linali la Chivumbulutso 21:3, 4, lomwe limanena kuti: “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”a Mawu amenewa anandidabwitsa kwambiri moti ndinadzifunsa kuti, ‘Koma zimenezi zingakhale zoona?’ Pa nthawiyi sindinkadziwa chilichonse chokhudza Mulungu komanso Baibulo.
Nditamaliza nthawi yanga yogwira ntchito yausilikali mu 1959 ndinakumana ndi wa Mboni wina dzina lake François, yemwe anandiphunzitsa mfundo zambiri za m’Baibulo. Mwachitsanzo, anandisonyeza kuchokera m’Baibulo dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova. (Sal. 83:18) François anandifotokozeranso kuti Yehova adzachititsa kuti padzikoli pakhale chilungamo, adzasintha dziko kuti likhale paradaiso komanso adzakwaniritsa mawu a pa Chivumbulutso 21:3, 4.
Zimene ankaphunzitsazi ndinaona kuti n’zomveka, ndipo zinandifika pamtima. Koma ndinakwiyanso kwambiri ndi ansembe moti ndinkafuna kuwadzudzula chifukwa chophunzitsa zinthu zosemphana ndi Baibulo. Zikuoneka kuti ndinali ndidakali ndi maganizo a bambo anga aja ndipo sindinkachita zinthu moleza mtima. Ndinkafunitsitsa kuchitapo kanthu nthawi yomweyo.
François ndi anzanga ena atsopano a Mboni anandithandiza kuti ndichite zinthu moleza mtima. Anandiuza kuti ntchito yathu monga Akhristu si kuweruza anthu, koma kuwapatsa chiyembekezo powauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Imeneyi ndi ntchito yomwe Yesu ankagwira komanso imene anauza otsatira ake kuti azichita. (Mat. 24:14; Luka 4:43) Ndinkafunikanso kuphunzira kulankhula ndi anthu mokoma mtima komanso mwanzeru ngakhale pamene sindikugwirizana ndi zimene amakhulupirira. Baibulo limati: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.”—2 Tim. 2:24.
Ndinasintha zinthu pa moyo wanga ndipo ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova mu 1959 pamsonkhano wina wadera. Pamsonkhanowu ndinakumananso ndi mlongo wina dzina lake Angèle, amene ndinakopeka naye. Ndinayamba kumapita kumpingo womwe ankasonkhana, ndipo kenako tinakwatirana mu 1960. Angèle ndi mkazi wabwino kwambiri, moti ndimaona kuti ndi mphatso yamtengo wapatali yomwe Yehova anandipatsa.—Miy. 19:14.
NDINAPHUNZIRA ZINTHU ZOCHULUKA KWA ABALE ANZERU KOMANSO ODZIWA ZAMBIRI
Pazaka zonsezi, ndakhala ndikuphunzira mfundo zofunika kuchokera kwa abale anzeru ndiponso odziwa zambiri. Imodzi mwa mfundo zofunikazi ndi iyi: Kuti tichite bwino pa utumiki uliwonse wovuta, tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumatsatira malangizo anzeru opezeka pa Miyambo 15:22, omwe amati: “Aphungu akachuluka [zolingalira] zimakwaniritsidwa.”
Mu 1964, ndinayamba kuona kuti mawu ouziridwa amenewa ndi oonadi. M’chaka chimenecho ndinayamba kutumikira monga woyang’anira dera ndipo ndinkachezera mipingo kuti ndilimbikitse abale komanso kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Komabe pa nthawiyi, ndinali ndi zaka 27 zokha, ndipo sindinkadziwa zambiri. Choncho ndinkalakwitsa zinthu zambiri. Koma ndinkayesetsa kuphunzirapo kanthu pa zimene ndalakwitsazo. Koposa zonse, ndinaphunzira zinthu zambiri zofunika kwa “aphungu” odziwa zinthu zambiri.
Ndikukumbukira zimene zinachitika nditangoyamba kumene kutumikira monga woyang’anira dera. Nditamaliza kuchezera mpingo ku Paris, m’bale wina wolimba mwauzimu anandipempha ngati tingakambirane zinthu zina pambali. Ndinamuuza kuti, “N’zotheka.”
Ndiyeno anandifunsa kuti, “M’bale Louis, kodi dokotala amathandiza ndani, anthu odwala kapena abwinobwino?”
Ndinayankha kuti, “odwala.”
Iye anati, “Mukunena zoona. Koma ndaona kuti mukumakonda kucheza ndi anthu amene akuchita bwino kale m’choonadi monga woyang’anira mpingo. Mumpingo wathu muli abale ndi alongo amene ndi ofooka, atsopano kapenanso amanyazi. Akhoza kuyamikira kwambiri mutacheza nawo, komanso ngakhale kupita kunyumba kwawo kukadya.”
Ndinayamikira malangizo abwino amene m’baleyo anandipatsa. Zinandikhudza kwambiri kuona kuti iye ankakonda nkhosa za Yehova. Ngakhale kuti zinali zovuta kuvomereza kuti ndinkalakwitsa, koma mwamsanga ndinayamba kugwiritsa ntchito malangizo akewo. Ndimathokoza Yehova chifukwa chokhala ndi abale ngati amenewa.
Mu 1969 ndi 1973, ndinaikidwa kuti ndiziyang’anira dipatimenti yoona za zakudya pa misonkhano iwiri ya mayiko yomwe inachitikira ku Colombes, mumzinda wa Paris. Pamsonkhano wa mu 1973, anthu pafupifupi 60,000 ankafunika kupatsidwa chakudya kwa masiku 5. Kunena zoona, sindinkadziwa kuti tikwanitsa bwanji zimenezi. Pa nthawi imeneyinso, mfundo ya pa Miyambo 15:22, yoti tizipempha malangizo kwa anthu anzeru inandithandiza kwambiri. Choncho ndinapempha malangizo kwa abale olimba mwauzimu, omwe anachitapo utumikiwu kwa nthawi yaitali. Ena mwa abalewa anali oti amadziwa kupha nyama, kulima masamba, kuphika ndiponso kugula zinthu. Tonse pamodzi tinakwanitsa kuchita utumiki wovutawu.
Mu 1973, ine ndi mkazi wanga tinaitanidwa kuti tikatumikire pa Beteli ku France. Utumiki woyamba umene ndinapatsidwa unalinso wovuta kwambiri. Ndinkafunika kumatumiza mabuku m’dziko la Cameroon ku Africa, kumene ntchito yathu inali yoletsedwa kuyambira mu 1970 mpaka 1993. Apanso ndinkaona kuti sindingathe kuchita zimenezi. N’kutheka kuti m’bale amene ankayang’anira ntchito yathu ku France anazindikira mmene ndinkamvera chifukwa anandilimbikitsa pondiuza kuti: “Abale athu ku Cameroon akufunikira kwambiri mabuku athu choncho tiyenera kumawatumizira.” Ndipo tinkawatumiziradi.
Ndinayenda maulendo angapo kupita ku mayiko oyandikana ndi dziko la Cameroon kuti ndikakumane ndi akulu ochokera m’dzikoli. Abale anzeru komanso olimba mtima amenewa anandithandiza kuti tipeze njira yoti tizitumizira mabuku nthawi zonse m’dziko la Cameroon. Yehova anadalitsa khama lathu chifukwa kwa zaka 20, abale ndi alongo ankalandira Nsanja ya Olonda komanso Utumiki Wathu wa Ufumu.
NDINAPHUNZIRA ZAMBIRI KWA MKAZI WANGA WOKONDEDWA
Kungoyambira pamene tinayamba chibwenzi, ndinaona kuti Angèle ankakonda kwambiri Yehova. Zimenezi zinaonekeranso kwambiri titakwatirana. Mwachitsanzo, madzulo a tsiku la ukwati wathu, iye anandipempha kuti popemphera nditchule zimene tinkafuna, zoti banja lathu lizitumikira Yehova nthawi zonse. Ndipo Yehova anayankha pemphero lathu.
Angèle wandithandizanso kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, mu 1973 titaitanidwa kuti tikatumukire pa Beteli, ndinkazengereza chifukwa ndinkakonda kwambiri utumiki woyang’anira dera. Koma Angèle anandikumbutsa kuti tinadzipereka kwa Yehova, choncho tiyenera kuchita chilichonse chimene gulu lake latiuza kuti tichite. (Aheb. 13:17) Pamenepa sindikanatsutsa, moti tinapita ku Beteli. Mkazi wanga ndi wanzeru, woganiza bwino komanso amakonda kwambiri Yehova. Zimenezi zatithandiza kuti tikhale ndi banja lolimba komanso tizisankha zinthu mwanzeru.
Panopa ndife achikulire, koma Angèle akupitiriza kundithandiza kwambiri. Mwachitsanzo, kuti tilowe sukulu zophunzitsa utumiki zomwe nthawi zambiri zimachitika m’Chingelezi, ine ndi Angèle tinayamba kuphunzira chilankhulochi. Zimenezi zinaphatikizapo kuyamba kusonkhana mpingo wa Chingelezi, ngakhale kuti pa nthawiyo tinali ndi zaka za m’ma 70. Popeza ndimatumikira mu Komiti ya Nthambi ku France, sizinali zophweka kupeza nthawi yophunzira chilankhulo china. Koma ine ndi Angèle tinkathandizana. Panopa tili ndi zaka za m’ma 80, koma timakonzekerabe misonkhano yathu m’Chingelezi ndiponso Chifulenchi. Timayesetsanso mmene tingathere kuti tizisonkhana komanso kulalikira ndi mpingo wathu. Yehova watidalitsa chifukwa choyesetsa kuphunzira Chingelezi.
Mu 2017, tinalandiranso madalitso ena aakulu. Ine ndi Angèle tinali ndi mwayi wolowa Sukulu ya Abale A m’Komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo, yomwe imachitikira ku likulu la maphunziro la Watchtower ku New York.
Kunena zoona, Yehova ndi Mlangizi Wamkulu. (Yes. 30:20) Choncho n’zosadabwitsa kuti iye amapereka maphunziro abwino kwambiri kwa atumiki ake, posatengera msinkhu wawo. (Deut. 4:5-8) Ndaona kuti achinyamata amene amamvetsera zimene Yehova komanso abale ndi alongo odziwa zambiri amanena, amasankha zinthu mwanzeru ndipo amadzakhala atumiki okhulupirika a Yehova. Lemba la Miyambo 9:9 limatikumbutsa kuti: “Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake. Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira.”
Nthawi zina ndimaganizira zimene zinachitika usiku uja ndili ku Algeria zaka pafupifupi 60 zapitazo. Usiku umenewo sindinkadziwa kuti ndingadzakhale ndi moyo wosangalala chonchi. Ndaphunzira zinthu zambiri kuchokera kwa ena. Yehova wathandiza ineyo ndiponso Angèle kukhala ndi moyo wabwino komanso wokhutiritsa kwambiri. Choncho ndife otsimikiza kuti tipitiriza kuphunzira zinthu kwa Atate wathu wakumwamba komanso abale ndi alongo odziwa zambiri amene amamukonda.
a Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.