Kodi Ndi Ndani Amene Amapita Kumwamba
Yankho la M’Baibulo
Mulungu amasankha Akhristu okhulupirika ochepa kuti akadzamwalira adzaukitsidwe n’kukakhala ndi moyo kumwamba. (1 Petulo 1:3, 4) Koma Akhristuwa akasankhidwa, amafunika kupitiriza kukhala okhulupirika komanso kukhala ndi makhalidwe oyera n’cholinga choti asalephere kulandira mphoto yawo yokakhala ndi moyo kumwamba.—Aefeso 5:5; Afilipi 3:12-14.
Kodi Amene Adzapite Kumwamba Azikachitako chiyani?
Azikatumikira limodzi ndi Yesu monga mafumu ndi ansembe kwa zaka 1,000. (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Iwo adzapanga “kumwamba kwatsopano,” kapena kuti boma lakumwamba lomwe lidzalamulire “dziko latsopano” lomwe likuimira anthu omwe adzakhale padziko lapansi. Mafumuwa adzathandiza kuti zinthu padziko lapansili zidzakhalenso ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba.—Yesaya 65:17; 2 Petulo 3:13.
Kodi ndi anthu angati omwe adzaukitsidwe kuti apite kumwamba?
Baibulo limasonyeza kuti anthu 144,000 ndi amene adzaukitsidwe kuti akakhale ndi moyo kumwamba. (Chivumbulutso 7:4) Lemba la Chivumbulutso 14:1-3 limanena kuti mtumwi Yohane anaona masomphenya a “Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000.” M’masomphenyawa, “Mwanawankhosa” akuimira Yesu yemwe anaukitsidwa. (Yohane 1:29; 1 Petulo 1:19) “Phiri la Ziyoni,” likuimira udindo wapamwamba womwe Yesu ndi anthu 144,000 omwe akalamulire naye limodzi kumwamba adzapatsidwe.—Salimo 2:6; Aheberi 12:22.
Anthu omwe ‘anaitanidwa ndi kusankhidwa mwapadera’ kuti akalamulire ndi Khristu mu Ufumu wake, amatchedwa kuti “kagulu kankhosa.” (Chivumbulutso 17:14; Luka 12:32) Zimenezi zikusonyeza kuti iwo ayenera kukhala ochepa poyerekezera ndi nkhosa zonse za Yesu.—Yohane 10:16.
Maganizo olakwika amene anthu amakhala nawo okhudza amene adzapite kumwamba
Maganizo olakwika: Anthu onse abwino amapita kumwamba.
Zoona zake: Mulungu analonjeza kuti adzapereka moyo wosatha kwa anthu ambiri omwe ndi abwino ndipo adzakhala padziko lapansi pano.—Salimo 37:11, 29, 34.
Yesu ananena kuti: “Palibe munthu amene anakwera kumwamba” (Yohane 3:13) Apatu iye anasonyeza kuti anthu abwino omwe anamwalira iyeyo asanabwere pa dzikoli, sanapite kumwamba. Anthuwa ndi monga Abulahamu, Mose, Yobu ndi Davide. (Machitidwe 2:29, 34) M’malomwake, anthu amenewa anali ndi chiyembekezo choti adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi.—Yobu 14:13-15.
Baibulo limati kuukitsidwa kuti munthu akakhale kumwamba ndi “kuuka koyamba.” (Chivumbulutso 20:6) Izi zikusonyeza kuti padzakhalanso kuuka kwina ndipo anthu amene adzaukitsidwewo adzakhala padziko lapansi.
Baibulo limaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Izi zikuyenera kudzachitika padziko lapansi chifukwa kumwamba kulibe imfa.
Maganizo olakwika: Aliyense amasankha yekha kuti adzapite kumwamba kapena adzakhale padziko lapansi.
Zoona zake: Mulungu ndi amene amasankha kuti Akhristu ena okhulupirika alandire “mphoto ya chiitano . . . chopita kumwamba” kutanthauza kuti akakhale ndi moyo kumwamba. (Afilipi 3:14) Pa nkhaniyi palibe munthu aliyense amene amachita kusankha yekha.—Mateyu 20:20-23.
Maganizo olakwika: Anthu onse amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi ndi otsika ndipo ndi osayenera kupita kumwamba.
Zoona zake: Mulungu amatchula anthu amene adzakhale padziko lapansi kuti “anthu anga osankhidwa mwapadera” komanso “odalitsidwa ndi Yehova.” (Yesaya 65:21-23) Iwo adzakhala ndi mwayi wokwaniritsa cholinga cha Mulungu chomwe anali nacho poyamba. Cholingachi ndi choti anthu akhale ndi moyo wosatha komanso wangwiro m’paradaiso padziko lapansi.—Genesis 1:28; Salimo 115:16; Yesaya 45:18.
Maganizo olakwika: Nambala ya 144,000, yomwe imatchulidwa m’buku la Chivumbulutso si imanena za chiwerengero chenicheni cha anthu.
Zoona zake: N’zoona kuti m’buku la Chivumbulutso mumapezeka manambala omwe amaimira zinthu zina, koma manambala ena amanena za kuchuluka kwa zinthu zenizeni. Mwachitsanzo, bukuli limanena za “mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:14) Tiyeni tione umboni wosonyeza kuti nambala ya 144,000, imanena za chiwerengero chenicheni cha anthu.
Lemba la Chivumbulutso 7:4 limanena za “chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo [kapena kuti amene anatsimikiziridwa kuti adzapita kumwamba], anthu okwana 144,000.” Kenako mavesi otsatira a lembali amanena za gulu lachiwiri kuti ndi “khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga.” Nawonso a “khamu lalikulu” adzapulumutsidwa ndi Mulungu. (Chivumbulutso 7:9, 10) Nambala ya 144,000 ikanakhala kuti sinena za chiwerengero chenicheni cha anthu, zikanakhala zovuta kusiyanitsa magulu awiriwa.a
Komanso Baibulo limati anthu a 144,000 “anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira.” (Chivumbulutso 14:4) Mawu akuti “zipatso zoyambirira” amanena za chiwerengero chochepa cha anthu ochita kusankhidwa. Choncho mawuwa amanena za anthu omwe akalamulire kumwamba ndi Khristu ndipo adzalamulira anthu okhala padziko lapansi omwe chiwerengero chawo sichikudziwika.—Chivumbulutso 5:10.
a Pulofesa wina dzina lake Robert L. Thomas, analemba zokhudza nambala ya 144,000 imene imatchulidwa pa Chivumbulutso 7:4. Iye anati: “Nambala yotchulidwa palembali ndi ya chiwerengero chenicheni cha anthu mosiyana ndi anthu otchulidwa pa Chivumbulutso 7:9 omwe chiwerengero chawo sichikudziwika. Nambalayi ikanakhala kuti si chiwerengero chenicheni cha anthu, ndiye kuti manambala onse otchulidwa m’bukuli sakanakhalanso onena za ziwerengero zenizeni.”—Chivumbulutso 1–7: Buku Exegetical Commentary, tsamba 474.