Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kupatsa?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala opatsa. Koma limanena kuti tizichita zimenezi ndi zolinga zabwino komanso osati mokakamizika. Limasonyeza kuti kupatsa koteroko kumakhala ndi zotsatira zabwino kwa wolandira ngakhalenso kwa woperekayo. (Miyambo 11:25; Luka 6:38) Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Kupereka kumene Mulungu amasangalala nako
Mulungu amasangalala tikamapatsa ena zinthu mwa kufuna kwathu. Baibulo limanena kuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”—2 Akorinto 9:7.
Kupereka ndi mtima wonse ndi mbali ya “kupembedza” kumene Mulungu amavomereza. (Yakobo 1:27) Yehova amasangalala ndi munthu yemwe amathandiza anthu omwe akufunikira thandizo. Yehova amaona kuti munthuyo akumukongoza iyeyo. (Miyambo 19:17) Ndipo Baibulo limanena kuti Mulungu adzabweza yekha ngongoleyo.—Luka 14:12-14.
Kupereka kumene Mulungu sasangalala nako
Ngati munthu akupereka n’cholinga choti apezepo kenakake. Mwachitsanzo:
Pofuna kudzionetsera.—Mateyu 6:2.
Pofuna kuti nayenso adzapatsidwe kenakake.—Luka 14:12-14.
Pofuna kugula chipulumutso.—Salimo 49:6, 7.
Ngati akupereka pofuna kuthandizira zinthu zomwe Mulungu amadana nazo. Mwachitsanzo, si nzeru kupatsa munthu ndalama kuti akayendere juga kapena akagulire mankhwala osokoneza bongo komanso kuti akamwe mowa n’kuledzera. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1) Ndiponso si zomveka kupereka ndalama kwa munthu amene angathe kugwira ntchito n’kudzipezera yekha zinthu zofunika koma amachita ulesi.—2 Atesalonika 3:10.
Ngati zikulepheretsa woperekayo kusamalira banja lake. Baibulo limanena kuti amuna okwatira ayenera kusamalira mabanja awo. (1 Timoteyo 5:8) Choncho sizingakhale zoyenera kuti mwamuna azipereka zinthu zambiri kwa anthu ena mpaka banja lake kumasowa zinthu zina zofunikira. Ndipotu Yesu anadzudzula anthu amene ankalephera kusamalira makolo awo okalamba n’kumanena kuti chuma chawo chonse ndi “mphatso yoperekedwa kwa Mulungu.”—Maliko 7:9-13.