1 Mbiri
14 Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo+ anatumiza amithenga kwa Davide. Anatumizanso matabwa a mkungudza,+ anthu omanga makoma, ndi anthu a ntchito zamatabwa kuti akamangire Davide nyumba.+ 2 Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike+ mu Isiraeli, pakuti ufumu wake unakwezedwa kwambiri chifukwa cha anthu ake Aisiraeli.+
3 Davide anatenganso akazi ena+ mu Yerusalemu, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+ 4 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo ndi awa: Samuwa,+ Sobabu,+ Natani,+ Solomo,+ 5 Ibara,+ Elisua, Elipeleti,+ 6 Noga, Nefegi,+ Yafiya, 7 Elisama,+ Beliyada, ndi Elifeleti.+
8 Tsopano Afilisiti anamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli yense.+ Choncho Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide.+ Davide atamva zimenezi, anapita kukamenyana nawo. 9 Afilisitiwo anafika ndi kuyamba kufunkha m’chigwa cha Arefai.+ 10 Ndiyeno Davide anafunsira kwa Mulungu+ kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwaperekadi m’manja mwanga?” Pamenepo Yehova anauza Davide kuti: “Pita, amenewa ndiwaperekadi m’manja mwako.” 11 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu,+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero, Davide anati: “Mulungu woona wawononga adani anga ngati madzi achigumula pogwiritsa ntchito dzanja langa.” N’chifukwa chake malowo+ anawatcha Baala-perazimu. 12 Pa nthawiyi Afilisiti anasiya milungu yawo kumeneko.+ Ndiyeno Davide atalamula, milunguyo anaitentha pamoto.+
13 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso ndi kuyamba kufunkha m’chigwacho.+ 14 Pamenepo Davide anafunsiranso+ kwa Mulungu ndipo Mulungu woonayo anamuyankha kuti: “Ayi usapite kukakumana nawo. Koma uwazembere ndipo ukawaukire kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 15 Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka,+ ukatuluke n’kumenyana nawo+ chifukwa Mulungu woona adzakhala atatsogola+ kukapha gulu lankhondo la Afilisiti.” 16 Choncho Davide anachitadi monga mmene Mulungu woona anamulamulira,+ moti iwo anapha asilikali a Afilisiti kuchokera ku Gibeoni+ mpaka kukafika ku Gezeri.+ 17 Chotero Davide anatchuka+ mpaka mbiri yake inamveka kumayiko onse. Ndipo Yehova anachititsa kuti mitundu yonse iziopa Davide.+