1 Mbiri
14 Hiramu+ mfumu ya Turo anatumiza anthu oti akapereke uthenga kwa Davide. Anatumizanso matabwa a mkungudza, anthu oswa miyala ndi kumanga makoma ndiponso akalipentala kuti akamangire Davide nyumba.*+ 2 Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike mu Isiraeli,+ popeza ufumu wakewo unakwezedwa kwambiri chifukwa cha anthu a Mulungu, Aisiraeli.+
3 Ku Yerusalemu, Davide anakwatiranso akazi ena+ ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+ 4 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo+ ndi awa: Samuwa, Sobabu, Natani,+ Solomo,+ 5 Ibara, Elisua, Elipeleti, 6 Noga, Nefegi, Yafiya, 7 Elisama, Beliyada ndi Elifeleti.
8 Afilisiti atamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Aisiraeli onse,+ Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide.+ Davide atamva zimenezi, anapita kukamenyana nawo. 9 Kenako Afilisitiwo anayamba kuukira anthu okhala mʼchigwa cha Arefai.+ 10 Ndiyeno Davide anafunsira kwa Mulungu kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anauza Davide kuti: “Pita, amenewa ndiwaperekadi mʼmanja mwako.”+ 11 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Ndiyeno Davide anati: “Mulungu woona wawononga adani anga ngati madzi achigumula pogwiritsa ntchito dzanja langa.” Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Baala-perazimu.* 12 Afilisiti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide atalamula, milunguyo anaitentha pamoto.+
13 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso nʼkuyamba kuukira anthu okhala mʼchigwacho.+ 14 Ndiyeno Davide anafunsiranso kwa Mulungu ndipo Mulungu woonayo anamuyankha kuti: “Usapite kukakumana nawo. Uwazembere kumbuyo nʼkuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 15 Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za bakazo, ukatuluke nʼkuyamba kumenyana nawo chifukwa Mulungu woona adzakhala atatsogola kukapha asilikali a Afilisiti.”+ 16 Choncho Davide anachitadi zimene Mulungu woona anamulamula,+ moti iwo anapha asilikali a Afilisiti kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri.+ 17 Davide anatchuka mpaka mbiri yake inamveka kumayiko onse ndipo Yehova anachititsa kuti anthu a mitundu yonse azimuopa Davideyo.+