Hoseya
11 “Pa nthawi imene Isiraeli anali mnyamata ndinamukonda,+ ndipo ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.+
2 “Pamene iye anali kuitanidwa kwambiri,+ m’pamenenso anapitiriza kuchoka.+ Anayamba kupereka nsembe kwa zifaniziro za Baala+ ndipo anayamba kufukiza nsembe zautsi kwa zifaniziro zogoba.+ 3 Koma ine ndine amene ndinaphunzitsa Efuraimu kuyenda,+ amenenso ndinamunyamula m’manja mwanga+ koma iye sanavomereze kuti ndinamuchiritsa.+ 4 Ndinali kuwakoka mokoma mtima ndi mwachikondi,*+ moti kwa iwo ndinakhala ngati wochotsa goli m’khosi*+ mwawo ndipo mwachikondi ndinali kubweretsera aliyense wa iwo chakudya.+ 5 Iwo sadzabwerera kudziko la Iguputo, koma Asuri adzakhala mfumu yawo,+ chifukwa iwo anakana kubwerera kwa ine.+ 6 Lupanga lidzazungulira m’mizinda yake+ ndipo lidzawononga mipiringidzo yake ndi kupha+ anthu a m’mizindayo chifukwa cha zinthu zoipa zimene anali kufuna kuchita.+ 7 Anthu anga atsimikiza kuti akhale osakhulupirika kwa ine.+ Akuwaitana kuti abwerere kwa amene ali wokwezeka, koma palibe ngakhale ndi mmodzi yemwe amene akuimirira.
8 “Kodi ndikusiyirenji iwe Efuraimu?+ Kodi ndikuperekerenji kwa adani iwe Isiraeli?+ Kodi ndikusandutsirenji ngati Adima?+ Kodi ndikuchitirenji zofanana ndi zimene ndinachitira Zeboyimu?+ Mtima wanga wasintha+ ndipo pa nthawi imodzimodziyo wadzaza ndi chisoni. 9 Sindidzasonyeza mkwiyo wanga woyaka moto.+ Sindidzawononganso Efuraimu+ pakuti ndine Mulungu+ osati munthu. Ndine Woyera pakati panu+ ndipo sindidzabwera kwa inu nditakwiya. 10 Iwo adzayenda motsatira Yehova+ amene adzabangula ngati mkango.+ Inde adzabangula,+ ndipo ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.+ 11 Iwo adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Iguputo.+ Adzabweranso akunjenjemera ngati njiwa kuchokera kudziko la Asuri+ ndipo ndidzawachititsa kukhala m’nyumba zawo,” watero Yehova.+
12 “Efuraimu amalankhula mabodza okhaokha kwa ine.+ Kulikonse kumene ndingayang’ane ndikuona chinyengo cha Isiraeli, koma Yuda akuyendabe ndi Mulungu+ ndipo iye ndi wokhulupirika kwa Woyera Koposa.”